-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1988 | June 1
-
-
Imodzi ya ndemanga yachindunji koposa iri mu Yuda 7. Yuda anali atangolankhula za (1) Aisrayeli owonongedwa kaamba ka kusoweka kwa chikhulupiriro, ndi (2) angelo omwe anachimwa ndipo ‘anasungidwa m’ndende zosatha kufikira chiŵeruziro cha tsiku lalikulu.’ Kenaka Yuda analemba kuti: “Monga Sodomu ndi Gomora . . . iyikidwa chitsanzo pa kuchitidwa chilango cha moto wosatha.” Lemba limeneli lagwiritsidwa ntchito ku mizinda yeniyeni kukhala ikuwonongedwa kosatha, osati anthu. Ngakhale kuli tero, m’chiyang’aniro cha Yuda 5 ndi 6, mwachiwonekere anthu ambiri akatenga versi 7 kutanthauza chilango cha chiŵeruzo cha munthu aliyense payekha. (Mofananamo, Mateyu 11:20-24 angamvedwe kukhala akusuliza anthu, osati miyala kapena nyumba.) M’chiwunikiro cha ichi, Yuda 7 akatanthauza kuti anthu oipa a Sodomu/Gomora anaŵeruzidwa ndi kuwonongedwa kotheratu.a
Tikumayang’ana kwinakwake, timapeza icho kukhala choyenera kuti koposa kamodzi Baibulo limagwirizanitsa Chigumula ndi Sodomu/Gomora. M’mawu ozungulira lemba otani?
Pamene anafunsidwa ponena za “mapeto a dongosolo la kachitidwe ka zinthu,” Yesu ananeneratu kudza kwa “mapeto” ndi “chisautso chachikulu monga sipadakhale chotero kuyambira chiyambi cha dziko.” (Mateyu 24:3, 14, 21) Iye anapitiriza kulankhula za “masiku a Nowa” ndi chimene “chinawoneka m’masiku a Loti” kukhala zitsanzo za anthu omwe sanazindikire za chenjezo lonena za kudza kwa chiwonongeko. Yesu anawonjezera kuti: “Momwemo kudzakhala tsiku la kuvumbuluka Mwana wamunthu.” (Luka 17:26-30; yerekezani ndi Mateyu 24:36-39.) Kodi Yesu anali kuchitira chitsanzo kokha mkhalidwe, kapena kodi mawu ozungulira lemba m’limene anagwiritsira ntchito zitsanzo zimenezo analingalira kuti ziŵeruzo zosatha zikuphatikizidwapo?
Pambuyo pake, Petro analemba ponena za ziŵeruzo za Mulungu ndi kulanga Kwake awo oyenera icho. Kenaka Petro anagwiritsira ntchito zitsanzo ziŵiri: Angelo omwe anachimwa, dziko lakale la nthaŵi ya Nowa, ndi awo omwe anawonongedwa mu Sodomu/Gomora. Chomaliziracho, Petro ananena kuti, ‘chinakhazikitsa chitsanzo kaamba ka anthu opanda umulungu za zinthu zomwe zirinkudza.’ (2 Petro 2:4-9) Pambuyo pake, iye anayerekeza chiwonongeko chimene anthu anavutika nacho mu Chigumula ndi kudza kwa “tsiku la chiŵeruziro ndi chiwonongeko cha anthu opanda umulungu.” Chimenecho chiri kutsogolo kwa miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zolonjezedwa.—2 Petro 3:5-13.
Mofananamo, pa mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu loipa, kodi awo amene Mulungu awaŵeruza akhala ndi chiŵeruzo chomalizira? Chimenecho ndi chimene chikusonyezedwa ndi 2 Atesalonika 1:6-9: “Popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso, koma, kwa inu akumva chisautso, mpumulo pamodzi ndi ife pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu m’lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osadziŵa Mulungu ndi osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu. Amene adamva chilango ndicho chiwonongeko chosatha chowasiyanitsa ku nkhope ya Ambuye, ndi ku ulemerero wa mphamvu yake.”
Pali kufanana kosangalatsa m’kagwiritsidwe ka mawu pakati pa kalongosoledwe kameneka ndi chimene Yuda ananena kuti chinachitika m’nkhani ya Sodomu. M’kuwonjezerapo, Mateyu 25:31-46 ndi Chivumbulutso 19:11-21 amasonyeza kuti “mbuzi” zodulidwa mu nkhondo ikudzayo ya Mulungu zidzakumana ndi “kudulidwa kosatha” mu “nyanja ya moto,” imene imaphiphiritsira kuchotsedwa kotheratu.b—Chivumbulutso 20:10, 14.
Mofananamo, m’kuwonjezera ku chimene Yuda 7 amanena, Baibulo likugwiritsira ntchito Sodomu/Gomora ndi Chigumula monga zitsanzo kaamba ka kutha kowononga kwa dongosolo loipa la kachitidwe ka zinthu liripoli. Chiri chodziŵikiratu, chotero, kuti awo amene Mulungu anawononga m’ziŵeruzo zapapitapo zimenezo anakumana ndi chiwonongeko chosakhoza kubwereranso. Ndithudi, aliyense wa ife angatsimikizire chimenecho mwa kutsimikizira kwake kukhala wokhulupirika kwa Yehova tsopano. M’njira imeneyo tidzayenerera kukhala ndi moyo m’dziko latsopano kudzawona awo amene iye adzawawukitsa ndi awo amene iye sadzatero. Tikudziŵa kuti ziŵeruzo zake ziri zangwiro. Elihu anatitsimikizira ife kuti: “Nkutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipsye mlandu.”—Yobu 34:10, 12.
-
-
Mafunso Ochokera kwa OŵerengaNsanja ya Olonda—1988 | June 1
-
-
a Pa Ezekieli 16:53-55, “Sodomu ndi [matauni ake oidalira, NW]” akutchulidwa, osati m’chigwirizano ndi chiwukiriro, koma mophiphiritsira m’chigwirizano ndi Yerusalemu ndi ana ake akazi. (Yerekezani ndi Chivumbulutso 11:8.) Onaninso Nsanja ya Olonda, June 1, 1952, tsamba 337, Chingelezi.
b Yerekezani ndi “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1980.
-