Mutu 7
Yambaninso Kukonda Mulungu Ngati Poyamba
EFESO
1. Kodi uthenga woyamba wa Yesu unapita kumpingo uti, ndipo oyang’anira anawakumbutsa chiyani?
UTHENGA woyamba wa Yesu unapita kumpingo wa ku Efeso. Mpingo umenewu unali mumzinda wotukuka kwambiri wa m’mbali mwa nyanja ku Asia Minor pafupi ndi chilumba cha Patimo. Yesu analamula Yohane kuti: “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Efeso, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena wonyamula nyenyezi 7 m’dzanja lake lamanja, woyenda pakati pa zoikapo nyale 7 zagolide.” (Chivumbulutso 2:1) Mofanana ndi mawu a m’mauthenga opita kumipingo ina 6 kutsogoloku, apa Yesu analankhula mosonyeza kuti ali ndi udindo. Yesu anakumbutsa oyang’anira a mumpingo wa ku Efeso kuti iye amayang’anira akulu onse komanso kuti amayendera mipingo yonse. Mpaka pano, iye akupitirizabe kutsogolera mpingo mokoma mtima ndi kuyang’anira akulu komanso kuweta mwachikondi anthu onse amene ali mumpingo wake. Nthawi ndi nthawi iye amasintha kayendetsedwe ka mpingo kuti kuunika kupitirize kuwala kwambiri. Zoonadi, Yesu ndi M’busa Wamkulu wa gulu la nkhosa za Mulungu.—Mateyu 11:28-30; 1 Petulo 5:2-4.
2. (a) Kodi Yesu anayamikira mpingo wa ku Efeso pa zinthu zabwino ziti? (b) Kodi zikuoneka kuti akulu a mpingo wa ku Efeso anatsatira malangizo ati a mtumwi Paulo?
2 Mauthenga asanu mwa mauthenga 7 a Yesu, anayamba ndi mawu olimbikitsa ndiponso oyamikira. Mpingo wa ku Efeso unali woyamba kuuyamikira, ndipo Yesu anauza Akhristu a kumeneko kuti: “Ndikudziwa ntchito zako, khama lako, ndi kupirira kwako, ndiponso kuti sungalekelere anthu oipa. Iwe unayesanso anthu amene amadzitcha atumwi pamene sanali atumwi, ndipo unapeza kuti ndi onama. Umaonetsanso kupirira, ndipo walimbana ndi mavuto osiyanasiyana chifukwa cha dzina langa, koma sunafooke.” (Chivumbulutso 2:2, 3) Zaka zingapo m’mbuyomo, mtumwi Paulo anachenjeza akulu a ku Efeso kuti kudzabwera “mimbulu yopondereza,” yomwe ndi anthu ampatuko amene adzasokoneze nkhosa. Iye anachenjezanso akuluwo kuti ‘akhale maso,’ potengera chitsanzo chake. (Machitidwe 20:29, 31) Zikuoneka kuti Akhristu amenewa anatsatira malangizowa chifukwa pa nthawiyi, Yesu anawayamikira chifukwa cha ntchito zawo, kupirira kwawo ndiponso khama lawo.
3. (a) Kodi “atumwi onama” amatani pofuna kusocheretsa anthu okhulupirika masiku ano? (b) Kodi Petulo anapereka chenjezo lotani lonena za anthu ampatuko?
3 “Atumwi onama” aonekeranso m’tsiku la Ambuye, ndipo iwo ‘akulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.’ (2 Akorinto 11:13; Machitidwe 20:30; Chivumbulutso 1:10) Atumwi onamawa amaona kuti zipembedzo zonse zampatuko n’zabwino, ngakhale kuti sizigwirizana. Iwo amanena kuti Mulungu alibe gulu limene akugwiritsa ntchito, ndipo amatsutsa zoti Yesu anakhala Mfumu mu 1914. Iwo amakwaniritsa ulosi umene uli pa 2 Petulo 3:3, 4 wakuti: “M’masiku otsiriza kudzakhala onyodola amene azidzatsatira zilakolako zawo, amene azidzati: ‘Kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi ngati mmene zakhalira kuyambira pa chiyambi cha chilengedwe.’”
4. (a) Kodi anthu onyoza asonyeza bwanji kuti ndi onyada ndiponso opanduka? (b) Mofanana ndi Akhristu a ku Efeso, kodi Akhristu masiku ano amatani ndi anthu otsutsa amene amafalitsa nkhani zabodza?
4 Onyoza amenewa anasiya choonadi chifukwa sagwirizana ndi mfundo yakuti ayenera kulengeza poyera chikhulupiriro chawo. (Aroma 10:10) Ndipo masiku ano amanyoza Akhristu oona mothandizidwa ndi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu ndiponso manyuzipepala ndi ma TV amene amafalitsa nkhani zabodza zokhudza Akhristu oonawo. Koma anthu okhulupirika amazindikira kuti anthu amenewa ndi achinyengo poona zochita ndi zolankhula zawo. Mofanana ndi Akhristu a ku Efeso, Akhristu masiku ano ‘salekelera anthu oipa,’ koma amawachotsa mumpingo.a
5. (a) Kodi Yesu ananena kuti Akhristu a ku Efeso anali ndi vuto lotani? (b) Kodi Akhristu a ku Efeso anayenera kukumbukira mawu ati?
5 Kenako, mofanana ndi mmene anachitira ndi mipingo isanu pa mipingo 7 ija, Yesu anatchula vuto lalikulu limene Akhristu a mpingo wa ku Efeso anali nalo. Iye anawauza kuti: “Komabe, ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya chikondi chimene unali nacho poyamba.” (Chivumbulutso 2:4) Iwo sanayenere kukhala ndi vuto limeneli chifukwa zaka 35 m’mbuyomo, Paulo anawalembera kalata yonena za ‘chikondi chachikulu cha Mulungu chimene anatikonda nacho,’ ndipo anawalimbikitsa kuti: “Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi, monganso Khristu anakukondani.” (Aefeso 2:4; 5:1, 2) Komanso mawu a Yesu otsatirawa anayenera kukhazikika m’mitima yawo. Iye anati: “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi. Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:29-31) Akhristu a mumpingo wa ku Efeso anasiya chikondi chimenechi, chimene anali nacho poyamba.
6. (a) Kaya tinayamba choonadi kalekale kapena tangoyamba posachedwapa, kodi tiyenera kupewa makhalidwe otani? (b) Kodi kukonda Mulungu kuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?
6 Kaya tinayamba choonadi kalekale kapena tangoyamba posachedwapa, tiyenera kusamala kuti tisasiye kukonda Yehova ngati mmene tinkamukondera titangophunzira kumene za iye. Kodi chingatichititse kuti tisiye kukonda Yehova n’chiyani? Zinthu monga kukonda kwambiri ntchito yathu, mtima wofuna ndalama zambiri, kapena kukonda kwambiri zinthu zosangalatsa pamoyo wathu zingatichititse kuti tisiye kukonda Yehova. Zimenezi zingatichititse kuti tizikonda kwambiri zinthu zakuthupi kuposa zinthu zauzimu. (Aroma 8:5-8; 1 Timoteyo 4:8; 6:9, 10) Kukonda Yehova kuyenera kutithandiza kusiya mtima wofuna zinthu zimenezi ndipo tiyenera ‘kupitiriza kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake.’ Tikamachita zimenezi ‘timaunjika chuma chathu kumwamba.’—Mateyu 6:19-21, 31-33.
7. (a) Kodi n’chiyani chiyenera kutilimbikitsa kutumikira Yehova? (b) Kodi Yohane ananena chiyani pa nkhani ya chikondi?
7 Tiyeni nthawi zonse tizitumikira Yehova chifukwa chomukonda kuchokera pansi pa mtima. Ndiponso tiziyamikira kwambiri zimene Yehova ndi Khristu atichitira. Pa mfundo imeneyi, Yohane analemba kuti: “Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda ndi kutumiza Mwana wake monga nsembe yophimba machimo athu.” Yohane anapitiriza kuti: “Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu amene amapitiriza kusonyeza chikondi, amakhalabe wogwirizana ndi Mulungu ndiponso Mulungu amakhala wogwirizana naye.” Choncho, tisalole kuti tisiye kukonda Yehova, Ambuye Yesu Khristu ndiponso Mawu a Mulungu amene ndi amoyo. Kuwonjezera pa kutumikira Mulungu mwakhama, tingasonyezenso kuti timam’konda mwakumvera “lamulo ili lakuti, munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.”—1 Yohane 4:10, 16, 21; Aheberi 4:12; onaninso 1 Petulo 4:8; Akolose 3:10-14; Aefeso 4:15.
‘Chita Ntchito za Poyamba’
8. Kodi Yesu ananena kuti Akhristu a ku Efeso anayenera kuchita chiyani?
8 Akhristu a ku Efeso anayenera kuyambiranso kukonda Mulungu kuti zinthu ziwayendere bwino. N’chifukwa chake Yesu anawauza kuti: “Choncho, kumbukira malo amene unali usanagwe, lapa ndi kuchita ntchito za poyamba. Ngati sutero, ndikubwera kwa iwe, ndipo ndidzachotsa choikapo nyale chako pamalo ake ngati sulapa.” (Chivumbulutso 2:5) Kodi Akhristu a mpingo wa ku Efeso anatani atauzidwa uthenga umenewu? Sitikudziwa zimene anachita. Koma tikukhulupirira kuti analapa ndipo anayambiranso kukonda Yehova. Iwo akanapanda kuchita zimenezi, nyale yawo ikanathimitsidwa ndipo choikapo nyale chawo chikanachotsedwa. Choncho akanataya mwayi wawo wowalitsa choonadi.
9. (a) Kodi Yesu anauza Akhristu a ku Efeso mawu olimbikitsa ati? (b) Yohane atamwalira, kodi mipingo inalephera bwanji kutsatira malangizo a Yesu opita kwa Akhristu a ku Efeso?
9 Ngakhale zinali choncho, Yesu anauza Akhristu a ku Efeso mawu olimbikitsa akuti: “Komabe, pali chinthu chimodzi chimene ukuchita bwino: Umadana ndi ntchito za mpatuko wa Nikolao, zimenenso ine ndimadana nazo.” (Chivumbulutso 2:6) Iwo anayesetsa kudana ndi mpatuko mofanana ndi mmene Ambuye Yesu Khristu amachitira. Koma patapita zaka zambiri, anthu a m’mipingo yambiri analephera kutsatira mawu a Yesu amenewa. Iwo analowa mumdima wauzimu chifukwa chakuti anasiya kukonda Yehova ndi choonadi ndiponso anasiya kukondana. Iwo anagawanika n’kupanga magulu ambirimbiri ampatuko omwe amangokhalira kukangana. Akhristu ampatuko amene sankakonda Yehova, anachotsa dzina la Mulungu pokopera Baibulo kuchokera ku mipukutu yachigiriki. Chifukwa choti anasiya kukonda Yehova, Akhristu onyengawo anayamba kuphunzitsa ziphunzitso zochokera ku Babulo ndi za Agiriki m’zipembedzo zawo. Zina mwa ziphunzitsozi ndi zoti kuli malo otchedwa puligatoliyo, zoti pali milungu itatu mwa mulungu mmodzi ndiponso zoti anthu oipa amakapsa kumoto. Chifukwa chosakonda Mulungu ndi choonadi, anthu amene amati ndi Akhristu anasiya kulalikira za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Iwo anayamba kulamulidwa ndi atsogoleri a chipembedzo odzikonda amene apanga ufumu wawo padziko lapansi lino.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 4:8.
10. Kodi m’chaka cha 1918 zinthu zinali bwanji m’Matchalitchi Achikhristu?
10 Chiweruzo chitayambira panyumba ya Mulungu mu 1918, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anapezedwa ndi mlandu wothandiza pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, mochita kudzionetsera. Iwo ankathandiza pa nkhondoyo polimbikitsa Akatolika ndi Apulotesitanti kuti aziphana. (1 Petulo 4:17) Pa nthawiyo, Matchalitchi Achikhristu ankachita zosiyana ndi zimene Akhristu a mpingo wa ku Efeso, omwe ankadana ndi mpatuko wa Nikolao, anachita. Matchalitchiwo ankaphunzitsa ziphunzitso zotsutsana ndiponso zonyoza Mulungu, ndipo atsogoleri awo ankagwirizana kwambiri ndi dzikoli, ngakhale kuti Yesu anauza ophunzira ake kuti asakhale mbali ya dziko. (Yohane 15:17-19) Mipingo yawo imene sidziwa mfundo yaikulu ya m’Baibulo, yomwe ndi Ufumu wa Mulungu, sinali ngati zoikapo nyale zimene zikuwalitsa choonadi cha m’Malemba. Ndipo anthu a m’mipingoyo sanali mbali ya kachisi wauzimu wa Yehova. Atsogoleri awo, amene ndi amuna ndi akazi omwe, sanali nyenyezi koma zinadziwika kuti ali m’gulu la “munthu wosamvera malamulo.”—2 Atesalonika 2:3; Malaki 3:1-3.
11. (a) M’chaka cha 1918, kodi ndi gulu liti la Akhristu limene linkatsatira uthenga wa Yesu wopita kwa Akhristu a ku Efeso? (b) Kodi Akhristu odzozedwa anachita zotani kuyambira mu 1919?
11 Ngakhale kuti zinthu zinali zovuta kwambiri pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, Akhristu odzozedwa anapitiriza kutumikira Yehova mwakhama pambuyo pa nkhondoyi chifukwa chomukonda ndiponso chifukwa chokonda choonadi. Iwo sanalekerere anthu amene ankafuna kuyambitsa mpatuko polambira Charles T. Russell, yemwe anali pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, atamwalira mu 1916. Akhristu okhulupirika amenewa ataphunzirapo kanthu chifukwa chozunzidwa ndiponso chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo, Mbuye wawo anawauza kuti ‘achita bwino kwambiri,’ ndipo anawauzanso kuti asangalale naye limodzi. (Mateyu 25:21, 23) Iwo anazindikira kuti zochitika za padziko komanso zinthu zimene zinawachitikira, zikukwaniritsa chizindikiro chimene Yesu anapereka chosonyeza kukhalapo kwake monga Mfumu. Kuyambira m’chaka cha 1919, iwo anachita khama pogwira ntchito yokwaniritsa ulosi waukulu umene Yesu ananena, wakuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 6:9, 10; 24:3-14) Ngati chikondi cha Akhristu okhulupirikawo pa Yehova chinali chitachepa pang’ono, zimene zinachitika pa nthawiyi zinawathandiza kuti chikondicho chiyambenso kukula.
12. (a) Kodi pamsonkhano wosaiwalika wa mu 1922 panaperekedwa chilengezo chotani? (b) Kodi Akhristu oona analandira dzina lotani m’chaka cha 1931, ndipo analapa chiyani?
12 Pa September 5 mpaka 13, m’chaka cha 1922, ku Cedar Point, m’chigawo cha Ohio, m’dziko la U.S.A., kunachitika msonkhano wosaiwalika. Pamsonkhanowu panasonkhana Akhristu okwana 18,000, ndipo panaperekedwa chilengezo chapadera chakuti: “Bwererani kumunda, inu ana nonse a Mulungu wam’mwambamwamba. . . . Dziko lonse lidziwe kuti Yehova ndiye Mulungu ndipo Yesu Khristu ndi Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. . . . Choncho lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi ufumu wake.” Dzina laulemerero la Yehova linayamba kukwezedwa kwambiri. M’chaka cha 1931 Akhristuwa anasonkhananso pamsonkhano wina umene unachitikira ku Columbus, Ohio, U.S.A. Pamsonkhano umenewu iwo anasangalala kwambiri chifukwa analandira dzina limene Mulungu anawapatsa lakuti, Mboni za Yehova, lotchulidwa mu ulosi wa Yesaya. (Yesaya 43:10, 12) Kuyambira ndi magazini ya March 1, 1939, gulu la Yehova linasintha dzina la magazini ake odziwika bwino kwambiri kuti akhale Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Cholinga chachikulu cha kusinthaku chinali kulemekeza Mlengi wathu ndi ufumu wake. Akhristu a Mboni za Yehova anayambanso kukonda kwambiri Yehova, ndipo analapa kuti akhululukidwe ngati analepherapo m’mbuyomu kulemekeza ndi kukweza dzina la Mulungu laulemerero ndiponso Ufumu wake.—Salimo 106:6, 47, 48.
“Wopambana pa Nkhondo”
13. (a) Kodi Akhristu a ku Efeso akanapeza madalitso otani ‘akanapambana pa nkhondo’? (b) Kodi Akhristu a ku Efeso anafunika kuchita chiyani kuti ‘apambane pa nkhondo’?
13 Pomaliza, monga mmene anachitira m’mauthenga ake ena, Yesu ananena kuti mzimu wa Mulungu, kudzera mwa iye, ukufotokoza za mphoto imene anthu okhulupirika adzalandire. Iye anauza Akhristu a ku Efeso kuti: “Ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti: Wopambana pa nkhondo, ndidzamulola kudya za mumtengo wa moyo, umene uli m’paradaiso wa Mulungu.” (Chivumbulutso 2:7) Anthu a mtima womvera ayenera kuti anatsatira uthenga wofunika umenewu, chifukwa chakuti Yesu sananene maganizo ake koma ananena zochokera kwa Yehova, yemwe ndi Ambuye Wamkulu Koposa. Mulungu anapereka uthengawo kudzera mwa mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito. Kodi Akhristu a ku Efeso ‘akanapambana bwanji pa nkhondoyo’? Akanapambana potsatira kwambiri Yesu, amene anatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika mpaka imfa, ndipo anatha kunena kuti: “Limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.”—Yohane 8:28; 16:33; onaninso 1 Yohane 5:4.
14. Kodi “paradaiso wa Mulungu” amene Yesu anamutchula akuimira chiyani?
14 Popeza kuti Akhristu a mumpingo wa ku Efeso komanso Akhristu odzozedwa masiku ano, sakuyembekezera kudzakhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi, n’chifukwa chiyani palembali akunena kuti ‘adzawalola kudya za mumtengo wa moyo, umene uli m’paradaiso wa Mulungu’? Paradaiso ameneyu sangakhale amene adzabwezeretsedwe padziko lapansi, popeza kuti Akhristu odzozedwa okwana 144,000, kuphatikizapo a mumpingo wa ku Efeso, anagulidwa kuchokera mwa anthu kuti akalamulire ndi Mwanawankhosa, Khristu Yesu, paphiri la Ziyoni la kumwamba, ngati ana auzimu. (Aefeso 1:5-12; Chivumbulutso 14:1, 4) Choncho paradaiso ameneyu ayenera kukhala malo akumwamba omwe ndi okongola kwambiri, kumene anthu opambana pa nkhondo amenewa adzakhale. Anthu amenewa adzadya za mumtengo wa moyo. Zimenezi zikutanthauza kuti adzapatsidwa moyo womwe sungafe ndipo adzakhalapo kwamuyaya “m’paradaiso wa Mulungu,” yemwe ali kumwamba. Choncho iwo adzakhala limodzi ndi Yehova.
15. N’chifukwa chiyani a khamu lalikulu masiku ano ayenera kuchita chidwi ndi mawu a Yesu olimbikitsa anthu kuti apambane pa nkhondo?
15 Nanga bwanji za anthu okhulupirika a padziko lapansi amene akugwirizana ndi gulu la Akhristu odzozedwa okwana 144,000? Khamu lalikulu la Mboni limeneli nalonso likupambana pa nkhondo. Koma iwo akuyembekezera kudzalandira paradaiso padziko lapansi. Iwo azidzamwa mu “mtsinje wa madzi a moyo” ndipo adzachiritsidwa ndi ‘masamba a mitengo’ yomwe ili m’mphepete mwa mtsinje umenewo. (Chivumbulutso 7:4, 9, 17; 22:1, 2) Ngati inuyo muli m’gulu la anthu amenewa yesetsani kusonyeza kuti mumakonda kwambiri Yehova ndipo yesetsani kumenyabe nkhondo kuti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba. Mukatero mudzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.—Yerekezerani ndi 1 Yohane 2:13, 14.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri za kuonekera kwa atumwi onama, onani buku la Kukambitsirana za m’Malemba, tsamba 196 mpaka 203, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Bokosi patsamba 36]
Kutamanda Yehova ndi Mwana Wake
M’buku la nyimbo limene anthu a Yehova anatulutsa m’chaka cha 1905, munali nyimbo zotamanda Yesu zochuluka kuwirikiza kawiri kuposa zotamanda Yehova Mulungu. M’buku lawo la nyimbo limene linatuluka m’chaka cha 1928, chiwerengero cha nyimbo zotamanda Yesu chinali chofananirako ndi cha nyimbo zotamanda Yehova. Koma m’buku la nyimbo latsopano, nyimbo zotamanda Yehova zilipo zochuluka kuwirikiza katatu kuposa zotamanda Yesu. Zimenezi n’zogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 14:28) Tiyenera kukonda kwambiri Yehova choyamba, kenako tizikondanso kwambiri Yesu ndipo tizisonyeza kuyamikira nsembe yake yamtengo wapatali ndiponso udindo wake monga Mkulu wa Ansembe wa Mulungu komanso Mfumu.
[Tchati patsamba 33]
Mmene Yesu Anaperekera Malangizo
(machaputala ndi mavesi a m’buku la Chivumbulutso)
Mipingo Udindo wake Mawu Vuto malangizo Madalitso
imene popereka oyamba lawo kapena mawu ake
inalandira Uphungu oyamikira lenileni olimbikitsa
uthenga
Efeso 2:1 2:2, 3 2:4 2:5, 6 2:7
Pegamo 2:12 2:13 2:14, 15 2:16 2:17
Tiyatira 2:18 2:19 2:20, 21 2:24, 25 2:26-28
Filadefiya 3:7 3:8 — 3:8-11 3:12
Laodikaya 3:14 — 3:15-17 3:18-20 3:21