Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Nyanja ya Moto N’chiyani? Kodi ndi Yofanana ndi Gehena?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
      • Mdyerekezi. (Chivumbulutso 20:10) Popeza Mdyerekezi ali ndi thupi lauzimu, sangawotchedwe ndi moto weniweni.​—Ekisodo 3:2; Oweruza 13:20.

  • Kodi Nyanja ya Moto N’chiyani? Kodi ndi Yofanana ndi Gehena?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    • Kodi mawu akuti “adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya” akutanthauza chiyani?

      Ngati nyanja ya moto ikuimira chiwonongeko chotheratu, n’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Mdyerekezi, chilombo, ndiponso mneneri wonyenga “adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya”? (Chivumbulutso 20:10) Taonani zifukwa 4 zosonyeza kuti kuzunzidwa kumene kukutchulidwa palembali n’kophiphiritsa:

      1. Kuti Mdyerekezi azunzidwe kwamuyaya, zingafunike kuti akhale ndi moyo kwamuyayanso. Koma Baibulo limanena kuti iye adzawonongedwa, kapena kuti sadzakhalaponso.​—Aheberi 2:14.

      2. Moyo wosatha ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, osati chilango.​—Aroma 6:23.

      3. Chilombo ndiponso mneneri wonyenga ndi zinthu zophiphiritsa, choncho sizingazunzidwe.

      4. Baibulo limasonyeza kuti kuzunzidwa kwa Mdyerekezi kukutanthauza kuti adzawonongedwa kotheratu ndipo sadzavutitsanso anthu.

      Mawu amene m’Baibulo anawamasulira kuti “kuzunzidwa” angatanthauzenso “kulepheretsedwa kuchita zinazake.” Mwachitsanzo, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “oyang’anira ndende” palemba la Mateyu 18:34, amawamasuliranso kuti “azunzi” m’Mabaibulo ena. Zimenezi zikusonyeza bwino kugwirizana kumene kulipo pakati pa mawu akuti “kuzunzidwa” ndi “kulepheretsedwa kuchita zinazake.” Komanso nkhani yopezeka pa Mateyu 8:29 ndi pa Luka 8:30, 31, imasonyeza kugwirizana kwa mawu akuti ‘kuzunzidwa’ ndi ‘phompho.’ Mawu onsewa akuimira malo ophiphiritsira, kumene munthu sangathe kuchita chilichonse, kapena kuti imfa. (Aroma 10:7; Chivumbulutso 20:1, 3) Ndipotu m’buku la Chivumbulutso muli mawu angapo akuti “kuzunzidwa” ndiponso “zunza” omwe anawagwiritsa ntchito mophiphiritsa.​—Chivumbulutso 9:5; 11:10; 18:7, 10.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena