Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tsiku Lopereka Chiweruzo la Mulungu Lidzabweretsa Madalitso Osangalatsa Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 7, 8. (a) Kodi panatsegulidwa mpukutu uti ndipo kenako chinachitika n’chiyani? (b) Kodi ndani amene sadzaukitsidwa?

      7 Yohane akupitiriza kuti: “Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo. Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake.” (Chivumbulutso 20:12b, 13) Zimenezi zidzakhala zochititsa chidwi kwambiri. ‘Nyanja, imfa ndi Manda’ zonse zikukhudzidwa, komabe sizikutanthauza kuti munthu amene wafera m’nyanja ndiye kuti sali m’Manda.a Mwachitsanzo, pamene Yona anali m’mimba mwa chinsomba m’nyanja, ananena kuti anali m’Manda. (Yona 2:2) Choncho ngati munthu wamwalira chifukwa cha uchimo wochokera kwa Adamu, ndiye kuti mwina ali m’manda a anthu onse, ndipo Mulungu akumukumbukirabe. Mawu aulosi amene ali pa Chivumbulutso 20:12, 13, akutipatsa umboni wamphamvu wotsimikizira kuti onse amene Mulungu akuwakumbukira adzaukitsidwa.

  • Tsiku Lopereka Chiweruzo la Mulungu Lidzabweretsa Madalitso Osangalatsa Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • a Anthu oipa omwe anafa pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa sali m’gulu la anthu amene adzaukitsidwe kuchokera m’nyanja. Chilango chimene anthu amenewo anapatsidwa n’chomaliza, mofanana ndi chilango chimene Yehova adzapereke poweruza anthu pa chisautso chachikulu.—Mateyu 25:41, 46; 2 Petulo 3:5-7.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena