Lingaliro la Baibulo
Kodi Dziko Lapansi Lidzathera m’Moto?
KULIPSEREZA ndi chipululutso cha nyukiliya, kulitentha ndi dzuŵa lomatundumuka, kapena kunyeketsedwa ndi mulungu wokwiya—njira zake zingasiyane, koma anthu ambiri ndi otsimikizira kuti pulaneti Dziko Lapansi, mudzi wa anthu, lidzathera m’ng’anjo yonyeketsa, chiwonongeko chosakaza.
Ena amatchula malemba a Baibulo amene amachenjeza za moto wowononga wa Mulungu monga chilango pa anthu olakwira dziko lapansi. Ena amabwereza lingaliro la Paul Davis, profesa wa pa Yunivesite ya Adelaide, ku Australia, amene analemba za chimene amaona monga kuzimiririka kwa dziko kosapeŵeka m’chiwonongeko cha moto. M’buku lake lakuti The Last Three Minutes, analingalira kuti: “Mmene dzuŵa likupitirizabe kutundumuka, lidzakuta . . . Dziko Lapansi ndi moto wake. Pulaneti lathu lidzangonga khala lamoto.” Kodi choonadi nchiti ponena za chimene chidzachitikira dziko lapansi? Kodi tingawamvetsetse motani malemba a Baibulo amene akuchita ngati akulosera moto wofafaniza?
Kodi Mulungu Amasamala?
Pa Yeremiya 10:10-12, timauzidwa kuti: “Koma Yehova ndiye Mulungu woona . . . . Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake.” Mulungu anapanga dziko lapansi nalikhazikitsa molimba. Choncho mwa nzeru, chikondi, ndi luntha, analikonza dziko mosamala kuti likhalepo kosatha monga mudzi wokongola wa anthu.
Ponena za Mulungu polenga mtundu wa anthu, Baibulo limatiuza kuti: “Adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.”(Genesis 1:27, 28) Atatsiriza ntchito yake yolenga, analengeza mosakayikira kuti: “Zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Anafuna kuti zingokhala choncho. Monga mmene makolo oyembekezera kuona mwana amalinganiza ndi kukonza malo a mwana wawo woyembekezeredwayo, Mulungu anabzala munda wokongola nkumuika munthuyo Adamu momwemo kuti aukuze ndi kuusamalira.—Genesis 2:15.
Adamu anausiya ungwiro ndi ntchito yake yosamalira dziko lapansi. Koma kodi Mulungu anachisiya chifuno chake? Yesaya 45:18 amasonyeza kuti sanatero: “Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, . . . amene anaumba dziko lapansi . . ., Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.” (Onaninso Yesaya 55:10, 11.) Ngakhale kuti munthu ananyalanyaza ntchito yake yauyang’aniro, Mulungu anapitirizabe kukwaniritsa pangano lake ndi dziko lapansi ndi moyo umene ulipo. Lamulo limene linaperekedwa ku mtundu wa Aisrayeli akale linalolera “sabata la kupumula la dziko” chaka chachisanu ndi chiŵiri chilichonse. Linaphatikizapo malamulo achifundo amene anatetezera zifuyo. (Levitiko 25:4; Eksodo 23:4, 5; Deuteronomo 22:1, 2, 6, 7, 10; 25:4; Luka 14:5) Izi ndi zitsanzo zoŵerengeka za m’Baibulo zimene zimasonyeza mooneka bwino kuti Mulungu amasamala kwambiri za dziko lapansi ndi zonse zimene iyeyo anapatsa munthu kuti asamalire.
“Dziko Loyamba”
Tsopano tingagwirizanitse motani malemba a Baibulo amene akuchita ngati akutsutsana? Lemba lina loterolo ndilo 2 Petro 3:7, pamene, malinga ndi Revised Nyanja (Union) Version, pamati: “Koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” Lina ndilo Chivumbulutso 21:1, limene limati: “Ndipo ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka.”
Ngati mawu a Petro angatengedwe m’lingaliro lenileni kuti pulaneti Dziko Lapansi lidzathedwa ndi moto weniweni, pamenepo miyamba yeniyeniyo—nyenyezi ndi zakuthambo zina zidzawonongeka ndi moto. Komabe, lingaliro limeneli likuombana ndi chitsimikizo chopezeka m’malemba onga Mateyu 6:10: “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano,” ndi Salmo 37:29: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Ndiponso, kodi moto ungachitenji pa dzuŵa ndi nyenyezi zimene kale zikuyaka moto umene umatulutsa mphamvu yanyukiliya mosalekeza?
Ku mbali ina, Baibulo kaŵirikaŵiri limagwiritsira ntchito liwu lakuti “dziko lapansi” m’lingaliro lophiphiritsira. Mwachitsanzo, Genesis 11:1 amati: “Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi.” Panopa, liwu lakuti “dziko lapansi” likusonya ku mtundu wa anthu mwachisawawa, kapena chitaganya cha anthu. (Onaninso 1 Mafumu 2:1, 2; 1 Mbiri 16:31.) Nkhani ya pa 2 Petro 3:5, 6 ikutanthauza zofananazo potchula “dziko lapansi” mophiphiritsira. Imanena za tsiku la Nowa pamene chitaganya cha anthu oipa chinawonongedwa ndi Chigumula koma Nowa ndi banja lake ngakhalenso mbulunga yeniyeniyo anapulumutsidwa. (Genesis 9: 11) Mofananamo, pa 2 Petro 3:7, ikutero kuti amene adzawonongedwa ndiwo “anthu osapembedza.” Lingaliro limeneli likuvomerezana ndi mbali yonse yotsala ya Baibulo. Anthu oipa oikidwa chizindikiro cha chiwonongeko ndiwonso “dziko loyamba” lotchulidwa pa Chivumbulutso 21:1, chimene chagwidwa mawu poyamba.
Ndithudi, monga momwe atate wapadziko lapansi wosamala angatsimikizirire kuchita chilichonse chothekera kuti nyumba yake isawonongeke, Yehova Mulungu ali wodera nkhaŵa kwambiri za chilengedwe chake. Pa nthaŵi ina anaingitsa anthu oipa ndi achisembwere m’chigwa cha Yordano chachondecho ndipo analonjeza okhalamo atsopanowo amene anachita naye pangano, kuti ngati anasunga malamulo ake, ‘dziko silidzawasanza polidetsa iwo, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako asanafike iwo.’—Levitiko 18:24-28.
“Dziko Lapansi Latsopano”
Lerolino, anthu odetsedwa ndi chiwerewere, auchigaŵenga, ndi oipitsidwa mwa zandale adetsa dziko. Mulungu yekha ndiye angalipulumutse. Adzatero kumene. Pa Chivumbulutso 11:18, akulonjeza “kuwononga iwo akuwononga dziko.” M’dziko lapansi lobwezeretsedwa ndi lokonzedwanso mudzakhala anthu oopa Mulungu ndi okonda anthu anzawo moona mtima. (Ahebri 2:5; yerekezerani ndi Luka 10:25-28.) Masinthidwe amene adzachitika mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu adzakhala aakulu kwakuti Baibulo limanena za “dziko latsopano”—chitaganya cha anthu chatsopano.
Pamene tiŵerenga malemba onga Salmo 37:29 ndi kumvetsetsa mawu a Yesu pa Mateyu 6:10, timatsimikizira kuti mphamvu zachilengedwe mwa izo zokha kapena munthu ndi mphamvu yake yonse yakuwononga sangathe kuthetsa pulaneti lathu. Sadzalepheretsa chifuno cha Mulungu. (Salmo 119:90; Yesaya 40:15, 26) Mtundu wa anthu okhulupirika udzakhala ndi moyo padziko lapansi m’mikhalidwe yokongola mosaneneka ndi chisangalalo chosatha. Chimenecho ndicho choonadi ponena za mtsogolo mwa dziko lapansi, pakuti ichi ndi chimene chili—ndipo nthaŵi zonse ndicho chinali chifuniro cha Mlengi wa anthu wachikondi.—Genesis 2:7-9, 15; Chivumbulutso 21:1-5.