‘Mkazi Uja Yezebeli’
“KOMATU ndiri nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi uja Yezebeli, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasokeretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.” (Chibvumbulutso 2:20) Anatero Yesu kwa akulu Achikristu mu Tiyatira. Mpingowo unali wokangalika kwenikweni ndipo unali utasonyeza chikondi, chikhulupiriro, ndi chipiriro. Koma unali unalekerera chisonkhezero choipitsa cha Yezebeli. Chifukwa ninji? Ndipo kodi zofananazo zingachitike lerolino?—Chibvumbulutso 2:19.
Mwachiwonekere, palibe aliyense mu Tiyatira amene ankatchedwadi Yezebeli. Yesu anagwiritsira ntchito dzinalo kutikumbutsa za Mfumukazi Yezebeli wa m’mbiri, mkazi wa Mfumu Ahabu. Mkazi wouma khosi ameneyo anaipitsa anthu a Mulungu kotheratu pamene anayambitsa kulambiridwa kwa Bala wachisembwere mu Israeli, akumachita mkupiti wotsimikizirika wa kuthetsa kulambira kowona.—1 Mafumu 16:31-33; 21:1-7.
Yezebeli mu Tiyatira—kaya anali mkazi mmodzi kapena gulu la akazi—mofananamo analimbikitsa chisembwere ndi kulambira mafano pakati pa anthu a Mulungu. Ena anamulabadira mumpingomo, popeza kuti Yesu akutchula za “ana ake,” omwe mwachiwonekere anali atsatiri ake. (Chibvumbulutso 2:22, 23) Chisonkhezero chake chinawopseza kuipitsa mpingo wa ku Tiyatira monga mmene anachita Israeli m’tsiku la Ahabu.
Kodi ncifukwa ninji Yezebeli wa ku Tiyatira anali wosonkhezera chotero? Atasanthula kufanana kwake ndi Yezebeli wakale, ena aganiza kuti iye anali mkazi wa mkulu wotsogolera mu Tiyatira. Komabe, Baibulo, silimanena zimenezo. Mwachiwonekere kwambiri, umunthu wake wosonkhezerawo ndi chenicheni chakuti iye anadzinenera kukhala mneneri wachikazi zinampatsa dzina mumpingo.
Kwalingaliridwa kuti zizolowezi zolakwika zimene iye anapititsa patsogolo zinali za makampani amalonda. Mogwirizana ndi kunena kwa Dr. W. M. Ramsay, “makampani ochulukira amalonda ngodziŵidwa mu Tiyatira kuposa mzinda wina uliwonse wa ku Asia.” Ponena za izi, The Interpreter’s Dictionary of the Bible ikuti: “Kampani yamalonda iriyonse yoteroyo inali ndi mulungu wake woichilikiza, mapwando ake, nthaŵi zake za kucheza zimene nthaŵi zina zinali mapwando ochita chisembwere. ‘Yezebeli’ angakhale atatsutsa kuti mapwando . . . amenewa sanafunikire kutsutsidwa popeza kuti wantchito aliyense, kuti apeze zakudya, anafunikira kuloŵa m’kampani.” The Expositor’s Greek Testament ikuvomerezana ndi zimenezi, ikumanena kuti omwe anatsatira Yezebeli “ananyada ndi ufulu wawo wounikiridwawo.”
Kwenikweni, chiphunzitso cha Yezebeli mu Tiyatira chinafanana ndi “chiphunzitso cha Balamu” mu Pergamo. (Chibvumbulutso 2:14) Mpingo wa ku Pergamo unapirira chizunzo chokulira, koma ena kumeneko ankatsanzira Balamu wakale mwa kuchilikiza dama lachigololo ndi kulambira mafano. Kwalingaliridwa kuti mu Pergamo, chisonkhezero cha Balamu chinalimbikitsa kulolela ncholinga chakupewa chizunzo chokakala, pamene mu Tiyatira Yezebeli analimbikitsa kulolela kaamba ka zifukwa zamalonda. Muli monse mmene zinaliri, ziphunzitso zonsezo zinali zampatuko wochititsa imfa.
Kodi chisonkhezero cha Yezebeli—kapena Balamu—chingakhalepo lerolino? Inde, chiriko. Atsogoleri ambiri a Chikristu Chadziko amatsanzira Yezebeli m’kulekelera m’mipingo yawo kugonana kwenikweni kwa a ziwalo zofanana, dama lachigololo, chigololo, kutaya mimba, ndi zinthu zina zofananazo zotsutsidwa ndi Mulungu. Ngakhale mkati mwa mpingo Wachikristu, anthu oŵerengeka afunsira “ufulu” pa kulambira kowona, akumalimbikitsa Akristu kusamamatira kwambiri ku miyezo ya Baibulo ndi kupititsadi patsogolo chisembwere.
Onse omwe afuna kukondweretsa Yehova ayenera kupewa malingaliro oterowo, ngakhale ngati angaperekedwe ndi anthu—amuna kapena akazi—okhala ndi maumunthu okongola kapena osonkhezera. Maganizo amenewa ngodzetsa imfa lerolino monga mmene kunaliri m’zaka za zana loyamba.—Chibvumbulutso 2:22, 23.