Masiku Otsiriza—Pali Umboni Wotani?
“Ndipo palibe mabelu aliwonse omwe analira ndipo palibe aliyense anasisima mosasamala kanthu za kutaikiridwa kwake chifukwa chakuti chifupifupi aliyense anayembekezera imfa. . . . Ndipo anthu ananena ndi kukhulupirira, ‘Awa ndiwo mapeto a dziko.’”—Katswiri wolemba mbiri yakale wa ku Italy akumalemba pa ziyambukiro za Black Death m’zana la 14.
ANTHU owona mtima m’mibadwo yapitayo molakwika anakhulupirira kuti ankakhala m’masiku otsiriza. M’nkhani yogwidwa mawu pamwambapo, unali mliri wa zironda zotupa pathupi umene unawonedwa monga chizindikiro cha mapeto a dziko. Oyerekeza ena akunena kuti unapha mmodzi mwa atatu a chiŵerengero cha anthu cha ku Europe. Koma mapetowo sanadze. Sinali nthaŵi ya kubwezera kwa Mulungu.
Chotero kodi aliyense angatsimikizire motani kuti Mboni za Yehova ziri zolondola m’kulengeza kuyandikira kwa mapeto a kachitidwe ka dziko kamakono ndi kukula kwa kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi? Kokha mwa kufufuza zonenera zawo ndi kulinganiza izo ndi zoneneratu za Baibulo. Nchiyani, kenaka, chimene chiri maulosi apadera omwe amalongosola zochitika zodziŵikitsa masiku otsiriza?
Nkhondo, Kusoweka kwa Chakudya, ndi Mliri
Zina za zochitika zazikulu za maulosi amenewo zalongosoledwa mwachidule m’masomphenya otchuka a amuna okwera pa akavalo a Chivumbulutso pa Chivumbulutso 6:1-8, ndipo izo ziri:
“Kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane.” Chonde dziŵani kuti wokwera pa kavalo ameneyu akachotsa mtendere kuchoka pa dziko lapansi, osati kokha kuchoka pa mitundu yoŵerengeka. Chotero, chimenecho chimachitira chitsanzo nthaŵi ya nkhondo ya dziko lonse ndi kuphana. Kodi tachiwona chimenecho mkati mwa zana la 20?
“Kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nawo muyeso m’dzanja lake.” Ichi moyenera chimachitira chitsanzo njala, kuperewera kwa chakudya, ndi kusoweka kwa chakudya. Kodi mikhalidwe imeneyi iripo mu mbadwo wathu?
“Kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo Hades anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinayi la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi [kusoweka kwa chakudya NW] ndi imfa, ndi zirombo za padziko.” Pano, imfa yosayembekezereka, kaya kaamba ka nkhondo, kusoweka kwa chakudya, mliri, kapena zirombo za mthengo, ikuwunjika minkhole yake yosayembekezereka m’manda (Hades). Kodi makumi a zikwi sanapite kumanda oterowo m’nthaŵi yathu?
Pamodzi ndi masomphenyawa pamabwera mikhalidwe imene Yesu ananeneratu, ina ya imene iri: “Mtundu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina. Kudzakhala kusoweka kwa chakudya ndi zivomezi . . . Aneneri onyenga ambiri adzawuka; nadzasokeretsa ambiri, ndipo ndi kuwonjezeka kwa kusayeruzika, chikondi mwa anthu ambiri chidzazilala.” (The Jerusalem Bible) Iye ananeneratunso ntchito yochitira umboni dziko lonse, kapena kulalikira kwa “mbiri yabwino ya Ufumu,” mapeto asanadze.
Kuwonjezerapo, mtumwi Wachikristu Paulo analongosola kuyankha kwa anthu, akumanena kuti mkati mwa masiku otsiriza “anthu sadzakonda chirichonse koma ndalama ndi iwo eni . . . opanda ulemu kwa makolo, osayamika.” Iye anawonjezera kuti, “Iwo adzakhala anthu omwe amaika zikondwerero m’malo mwa Mulungu, anthu omwe amasungirira kawonekedwe kakunja kachipembedzo, koma akukana zenizeni zake.”—The New English Bible.a
Tiyeni tikumbukire kuti pamene kuli kwakuti ulosi wa Yesu umasonyeza pachimake pa mbiri ya munthu pamene zochitika zonsezi zibwera pamodzi mu mbadwo umodzi, izo sizifunikira kukhala zazikulu m’chiŵerengero kapena zochulukira kuposa za mbadwo uliwonse wapita, ngakhale kuti chimenecho chingakhale tero.
Kodi inu mwawona zochitika zimenezi ndi mikhalidwe mkati mwa zana lino la 20, makamaka chiyambire 1914? Kodi mukuziwona izo ngakhale tsopano mu 1988? Monga chokumbutsa, lolani tibwerere ku zochitika zina zapadera zomwe zayambukira ndipo zikuyambukira mtundu wa anthu ndi kuyankha funso lakuti, Kodi izo zimasonyeza kuti nthaŵi ya kuloŵerera kwa Mulungu mwa Ufumu wake iri pafupi?—Luka 21:29-33.
[Mawu a M’munsi]
a Maulosi amenewa angapezedwe mwatsatanetsatane mu malemba otsatirawa a Baibulo: Mateyu 24; Luka 21; Marko 13; 2 Timoteo 3:1-5.
[Chithunzi patsamba 4]
Mawu ozokotedwa omwe ali pansi pa chikumbutso chenicheni cha Nkhondo ya Dziko I ichi amaŵerenga kuti: “Ku chikumbukiro chosatha cha akufa olemekezeka a ku Borough ya ku Evesham [England] omwe anapereka miyoyo yawo kaamba ka Dziko lawo mu Nkhondo Yaikulu.”