Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 10/8 tsamba 30
  • “Miliri m’Malo Akutiakuti”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Miliri m’Malo Akutiakuti”
  • Galamukani!—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Dziko Lopanda Matenda
    Galamukani!—2004
  • Miliri m’Zaka za Zana la 20
    Galamukani!—1997
  • Anthu Anayi Okwera Mahatchi Ali pa Liwiro
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Tizilombo Ta matenda Tibwezera Chilango
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 10/8 tsamba 30

“Miliri m’Malo Akutiakuti”

M’MAWU apamwamba ameneŵa, opezeka pa Luka 21:​11, kuwonjezereka kwa miliri kukuperekedwa monga chimodzi cha mbali za chizindikiro cha masiku otsiriza. Pa Chivumbulutso 6:​8, miliri imeneyo yaphiphiritsiridwa ndi kuthamanga kwa kavalo wotumbuluka, kavalo wachinayi wa Chivumbulutso chaputala 6. Wolemba nkhani m’nyuzipepala wina Lawrence Hall anapereka mfundo zazikulu zochokera m’buku latsopano lolembedwa ndi Andrew Nikiforuk lotchedwa The Fourth Horseman: A Short History of Epidemics, Plagues, Famine and Other Scourges. Izo zinatuluka m’danga la Hall mu Star-Ledger ya February 25, 1994, ya ku Newark, New Jersey. Mawu ogwidwa m’dangalo akutsatira.

“Wapakavalo Wachinayi wa Apocalypse akuthamanga zolimba m’nthaŵi zino za kuthedwa nzeru. Mtundu wa anthu uli pachiswe m’njira zambiri​—⁠ngakhale kuti pali luso lapadera lazopangapanga latsopano kwambiri ndi kupita patsogolo mu sayansi ya zamankhwala. Mankhwala ambiri opha tizilombo tamatenda m’thupi, amene kale anatamandidwa kukhala mankhwala ochiritsa kamodzi nkamodzi, sangathe kulimbana konse ndi matenda amakono. . . .

“ ‘Ngakhale kuti . . . mankhwala awo ndi akatemera angabweretse lingaliro lonyenga la kuchiritsa, miliri idzapitirizabe kukumbutsa anthu onse kuti sayansi yochepa kwambiriyo idakali m’theŵera, ndipo mwinamwakenso lakuda’ . . . Cholinga changa si cha kukuwopsezani ayi, koma Wapakavalo Wachinayi wophiphiritsirayo alidi weniweni. Nthenda ya [TB] yayambanso kufala. Kachilombo ka AIDS kakupitirizabe kupha zikwizikwi chaka chilichonse padziko lonse . . . Nthenda zina monga ngati typhoid, diphtheria, kolera, anthrax ndi malungo zikuwopseza kwambiri​—⁠mothetsa nzeru akatswiri azaumoyo ndi anthu onse. . . .

“Nyengo iliyonse ya mbiri ya mtundu wa anthu yatulutsa nthenda zatsopano. . . . Nyengo ya Maluso a Zopangapanga inali ndi chindoko, nthomba inatengeredwa ku Americas ndi Columbus, ndipo tsopano AIDS ikutiwopsezanso. . . . Chikhalirechobe, pali miliri ina yatsopano ndi matenda zimene zikubuka pamene mtundu wa anthu ukuonekera kukhala ukugonja pa nkhondo yake yolimbana ndi tizilombo tamatenda. . . . Chiŵerengero cha anthu a madongosolo athupi osakhoza kudzitetezera chikukula.” Nikiforuk akunenanso kuti “kunama kwina kwakukulu kwa zaka za zana la 20 [ndi] kwakuti mankhwala opha tizilombo m’thupi, akatemera ndi madokotala atipulumutsa ku miliri. . . .

“ ‘Mulimonse mmene tingayesere, sitingagonjetse matenda amakono, kunyenga Wapakavalo kapena kunyalanyaza za kusasintha kwa kukhalapo kwa miliri m’mbiri.’ ”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena