Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • re mutu 17 tsamba 100-104
  • “Miyoyo ya Amene Anaphedwa” Idzalandira Mphoto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Miyoyo ya Amene Anaphedwa” Idzalandira Mphoto
  • Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mkanjo Woyera
  • ‘Amene Anafa Adzauka Choyamba’
  • “Kuuka Koyamba” Kuli M’kati Panopa!
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Anthu Anayi Okwera Mahatchi Ali pa Liwiro
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Masomphenya Osangalatsa Omwe Amalimbitsa Chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
re mutu 17 tsamba 100-104

Mutu 17

“Miyoyo ya Amene Anaphedwa” Idzalandira Mphoto

1. Kodi tikukhala m’nyengo iti, ndipo pali umboni wotani wa zimenezi?

UFUMU wa Mulungu ukulamulira. Wokwera pahatchi yoyera watsala pang’ono kupambana pa nkhondo yolimbana ndi adani ake onse. Hatchi yofiira, yakuda, ndi yotuwa zili pa liwiro padziko lonse lapansi. N’zoonekeratu kuti maulosi amene Yesu ananena okhudza kukhalapo kwake monga mfumu akukwaniritsidwa. (Mateyu chaputala 24 ndi 25; Maliko chaputala 13; Luka chaputala 21) Zoonadi, tikukhala m’masiku otsiriza a nthawi yathu ino. (2 Timoteyo 3:1-5) Choncho tiyeni tikhale tcheru pamene Yesu Khristu, yemwe ndi Mwanawankhosa, akumatula chidindo chachisanu chomatira mpukutu uja. Kodi tiona masomphenya ena otani?

2. (a) Kodi Yohane anaona chiyani Yesu atamatula chidindo chachisanu? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuwerenga zoti kumwamba kuli guwa la nsembe lophiphiritsira?

2 Yohane anafotokoza masomphenya okhudza mtima kwambiri. Iye anati: “Atamatula chidindo chachisanu, ndinaona pansi pa guwa lansembe pali miyoyo ya amene anaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu, ndiponso chifukwa cha ntchito yochitira umboni imene anali nayo.” (Chivumbulutso 6:9) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yohane anaona guwa la nsembe lili kumwamba? Inde. Aka n’koyamba kuti Yohane atchule guwa la nsembe. Koma iye watchula kale za Yehova atakhala pampando wake wachifumu, akerubi amene azungulira mpando wachifumuwo, nyanja yoyera mbee! ngati galasi, nyale, ndiponso akulu 24 atanyamula zofukiza. Zinthu zonsezi n’zofanana ndi zinthu zimene zinali m’chihema cha padziko lapansi, chimene chinali malo opatulika olambirirako Yehova mu Isiraeli. (Ekisodo 25:17, 18; 40:24-27, 30-32; 1 Mbiri 24:4) Choncho sitiyenera kudabwa kuona kuti kumwambako kulinso guwa la nsembe lophiphiritsira.—Ekisodo 40:29.

3. (a) Pachihema chakale cha Ayuda, kodi miyoyo inkathiridwa bwanji “pansi pa guwa lansembe”? (b) N’chifukwa chiyani Yohane anaona miyoyo ya mboni zimene zinaphedwa ili pansi pa guwa la nsembe lophiphiritsa la kumwamba?

3 Pansi pa guwa la nsembe limeneli pali “miyoyo ya amene anaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu, ndiponso chifukwa cha ntchito yochitira umboni imene anali nayo.” Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Miyoyo imeneyi sikutanthauza mizimu ya anthu amene anafa, ngati imene Agiriki olambira mafano ankakhulupirira kuti imachoka mwa munthu akamwalira. (Genesis 2:7; Ezekieli 18:4) Koma Yohane ankadziwa kuti moyo umaimiridwa ndi magazi ndipo ansembe amene ankatumikira pachihema cha Ayuda akapha nyama kuti aipereke nsembe, ankawaza magazi ake “mozungulira guwa lansembe” kapena ankawathira “pansi pa guwa lansembe zopsereza.” (Levitiko 3:2, 8, 13; 4:7; 17:6, 11, 12) Choncho munthu akaona guwa la nsembe ankaganizira kwambiri za moyo wa nyamayo. Koma kodi n’chifukwa chiyani Yohane anaona miyoyo, kapena kuti magazi, a atumiki a Mulungu amenewa ali pansi pa guwa la nsembe lophiphiritsira kumwamba? N’chifukwa chakuti Mulungu amaona kuti imfa ya anthu amenewa ndi yansembe.

4. Kodi imfa ya Akhristu odzozedwa imakhala yansembe m’njira yotani?

4 Inde, anthu onse amene anadzozedwa ndi mzimu woyera n’kukhala ana auzimu a Mulungu amafa imfa yansembe. Chifukwa cha zimene akachite mu Ufumu wa Yehova wakumwamba, iwo amagwirizana ndi chifuniro cha Mulungu n’kusiya kukhala ndi chiyembekezo chilichonse chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Komanso, iwo amalola kufa imfa yansembe pofuna kusonyeza kuti akugwirizana ndi mfundo yakuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. (Afilipi 3:8-11; yerekezerani ndi Afilipi 2:17.) Zimenezi n’zimene zinachitikira anthu amene Yohane anaona miyoyo yawo ili pansi pa guwa la nsembe. Iwo ndi odzozedwa amene m’nthawi yawo anaphedwa chifukwa chochita utumiki mwakhama posonyeza kuti akugwirizana ndi Mawu a Yehova ndiponso ndi mfundo yakuti iye ndi woyenera kulamulira. ‘Miyoyo yawo inaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu, ndiponso chifukwa cha ntchito yochitira umboni imene anali nayo.’

5. Kodi miyoyo ya Akhristu okhulupirika amene anafa ikufuula mwa njira yotani popempha kuti anthu amene anawapha abwezeredwe?

5 Yohane anapitiriza kufotokoza masomphenyawo, kuti: “Iwo anafuula ndi mawu okweza akuti: ‘Mudzalekerera kufikira liti, Inu Ambuye Wamkulu Koposa, woyera ndi woona, osaweruza ndi kubwezera okhala padziko lapansi chifukwa cha magazi athu?’” (Chivumbulutso 6:10) Kodi miyoyo, kapena kuti magazi, a anthuwa angafuule bwanji popempha kuti amene anawapha abwezeredwe, popeza Baibulo limasonyeza kuti akufa sadziwa chilichonse? (Mlaliki 9:5) Kumbukirani kuti Abele, amene anali wolungama, ataphedwa ndi Kaini, magazi ake analirira Mulungu. Kenako Yehova anauza Kaini kuti: “N’chiyani chimene wachitachi? Tamvera tsono. Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.” (Genesis 4:10, 11; Aheberi 12:24) Sikuti magazi a Abele ankatulutsadi mawu enieni. Koma popeza Abele anaphedwa wosalakwa, kuti chilungamo chichitike, womuphayo ankafunika kuti alangidwe. N’chimodzimodzinso ndi Akhristu amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Iwo anaphedwa osalakwa, ndipo kuti chilungamo chichitike, owaphawo anayenera kubwezeredwa. (Luka 18:7, 8) Mawu opempha kuti owaphawo abwezeredwe ndi ofuula chifukwa chakuti Akhristu amene aphedwa pa chifukwa chimenechi ndi ambiri.—Yerekezerani ndi Yeremiya 15:15, 16.

6. Kodi ufumu wa Yuda unawonongedwa mu 607 B.C.E. pofuna kubwezera mlandu uti wokhetsa magazi?

6 Tingayerekezerenso zimenezi ndi zimene zinachitikira fuko la Yuda litasiya kulambira Yehova, pamene Mfumu Manase inayamba kulamulira mu 716 B.C.E. Manase anapha anthu ambiri osalakwa, ndipo zikuoneka kuti iye ‘anacheka pakati ndi macheka,’ mneneri Yesaya. (Aheberi 11:37; 2 Mafumu 21:16) Ngakhale kuti kenako Manase analapa n’kusintha, mlandu wa magazi amene iye anakhetsa unalipobe. Choncho Ababulo anawononga ufumu wa Yuda mu 607 B.C.E. “Zimenezi zinachitikira Yuda molamulidwa ndi Yehova, kuti achotse dzikolo pamaso pake chifukwa cha machimo a Manase, malinga ndi zonse zimene anachita, komanso chifukwa cha magazi osalakwa amene iye anakhetsa, moti anadzaza Yerusalemu ndi magazi osalakwa, ndipo Yehova sanalole kukhululuka.”—2 Mafumu 24:3, 4.

7. Kodi ndani amene ali ndi mlandu waukulu wokhetsa “magazi a oyera”?

7 Mofanana ndi kalelo, panopa anthu ambiri amene anapha mboni za Mulungu mwina anafa kalekale. Koma gulu limene linawachititsa kuti aphe anthu a Mulungu lidakalipobe ndipo lidakali ndi mlandu wa magazi. Gulu lake ndi la Satana lapadziko lapansi, kapena kuti mbewu yake yapadziko lapansi. Mbali yaikulu ya gulu limeneli ndi Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi.a Baibulo limafotokoza kuti Babulo Wamkulu ‘waledzera ndi magazi a oyera, ndiponso magazi a mboni za Yesu.’ Ndipo “mwa iye munapezeka magazi a aneneri, a oyera, ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” (Chivumbulutso 17:5, 6; 18:24; Aefeso 4:11; 1 Akorinto 12:28) Ndithudi, iye ali ndi mlandu waukulu zedi wa magazi. Kwa nthawi yonse imene Babulo Wamkulu akhalepo, magazi a anthu amene iye wapha apitirizabe kufuula popempha kuti chilungamo chichitike.—Chivumbulutso 19:1, 2.

8. (a) Kodi ndi anthu ati amene anaphedwa pa nthawi imene Yohane anali ndi moyo? (b) Kodi mafumu a Roma anazunza bwanji Akhristu?

8 Yohane anaona ndi maso ake pamene Satana, Njoka yankhanza ija, limodzi ndi mbewu yake yapadziko lapansi, ankapha Akhristu polimbana ndi mpingo wa Akhristu odzozedwa, womwe unali ukungoyamba kumene pa nthawiyo. Yohane anaona Ambuye wathu akupachikidwa komanso anapulumuka pamene Sitefano, Yakobo, amene anali m’bale wake wa Yohaneyo, ndiponso Petulo, Paulo, ndi anzake ena apamtima anaphedwa. (Yohane 19:26, 27; 21:15, 18, 19; Machitidwe 7:59, 60; 8:2; 12:2; 2 Timoteyo 1:1; 4:6, 7) Mu 64 C.E. Nero, mfumu ya Roma, ananamizira Akhristu kuti ndi amene anatentha mzindawo. Iye anachita zimenezi pofuna kuziziritsa mphekesera zimene zinkamveka zoti iyeyo ndi amene anatentha mzindawo. Wolemba mbiri Tacitus anati: “[Akhristu] ankaphedwa m’njira zosiyanasiyana zochititsa manyazi. Ena ankawaveka zikopa za nyama zakutchire n’kuwakhuwizira agalu kuti awakhadzulekhadzule. Ena [ankapachikidwa],b ndipo ena ankawotchedwa usiku kuti akhale ngati zounikira.” Akhristu ambiri anazunzidwanso pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Domitian (81-96 C.E.) ndipo n’chifukwa chake Yohane anamangidwa n’kuikidwa pachilumba cha Patimo. Izi zikungotsimikizira mawu amene Yesu ananena, akuti: “Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.”—Yohane 15:20; Mateyu 10:22.

9. (a) Chinyengo cha Satana chitafika pachimake, kodi iye anakhazikitsa chiyani pofika m’zaka za m’ma 300 C.E., ndipo kodi chimene anakhazikitsacho ndi mbali yaikulu ya chiyani? (b) Kodi olamulira ena a m’Mayiko Achikhristu anazunza bwanji Mboni za Yehova pa nkhondo ziwiri za padziko lonse?

9 Pofika m’zaka za m’ma 300 C.E., chinyengo cha Satana Mdyerekezi, yemwe ndi njoka yakale ija, chinafika pachimake pamene iye anakhazikitsa Matchalitchi Achikhristu, omwe ndi zipembedzo zampatuko. Zipembedzo zimenezi zimanamizira kuti ndi zachikhristu, koma kwenikweni ndi zachibabulo. Matchalitchi Achikhristu ndiwo mbali yaikulu ya mbewu ya Njoka ndipo alipo ambirimbiri, komanso ziphunzitso zawo n’zotsutsanatsutsana. Mofanana ndi fuko la Yuda lomwe linali losakhulupirika kwa Mulungu, Matchalitchi Achikhristu ali ndi mlandu waukulu wa magazi, chifukwa ankathandizira kwambiri mbali zonse zimene zinkamenyana pa nkhondo zonse ziwiri za padziko lonse. Atsogoleri ena a ndale a m’Mayiko Achikhristu anapezerapo mwayi pa nkhondo zimenezi n’kumapha atumiki odzozedwa a Mulungu. Pofotokoza mmene Hitler anazunzira Mboni za Yehova, buku lina lothirira ndemanga pa buku limene Friedrich Zipfel analemba (Kirchenkampf in Deutschland [Nkhondo ya Matchalitchi ku Germany]), linati: “Munthu mmodzi pa anthu atatu alionse [a Mboni] anaphedwa. Ena anachita kuphedwa mwachindunji, ena anaphedwa mwa njira zina zachiwawa, pamene ena anafa ndi njala, matenda, kapena chifukwa chogwiritsidwa ntchito mwankhanza. Palibenso chipembedzo china chimene chinazunzidwapo kwambiri chonchi chifukwa cha chikhulupiriro chake cholimba, chimene sichinkagwirizana ndi mfundo za chipani cha Nazi.” Ponena za Matchalitchi Achikhristu, komanso atsogoleri ake, tinganenedi kuti: “Pazovala zako papezeka madontho a magazi a anthu osauka osalakwa.”—Yeremiya 2:34.c

10. Kodi anyamata ena a m’khamu lalikulu azunzidwa motani m’mayiko ambiri?

10 Kuyambira mu 1935, anyamata okhulupirika a m’khamu lalikulu akhala akuzunzidwa kwambiri m’mayiko ochuluka. (Chivumbulutso 7:9) Mwachitsanzo, pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkatha ku Ulaya, m’tauni inayake imodzi yokha, anyamata ena a Mboni za Yehova okwana 14 ananyongedwa. Kodi iwo analakwa chiyani? Ananyongedwa chifukwa chokana ‘kuphunzira nkhondo.’ (Yesaya 2:4) Chaposachedwapa, anyamata ena ku mayiko a kum’mawa kwa Asia ndi ku Africa aphedwa pochita kumenyedwa kapena kuwomberedwa ndi mfuti chifukwanso chokana kupita kunkhondo. Tili ndi chikhulupiriro chonse kuti anyamata amenewa, omwe anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo pothandiza abale ake a Yesu odzozedwa, adzaukitsidwa n’kukhala m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.—2 Petulo 3:13; yerekezerani ndi Salimo 110:3; Mateyu 25:34-40; Luka 20:37, 38.

Mkanjo Woyera

11. Kodi Akhristu odzozedwa amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo amapatsidwa “malaya akunja oyera” m’njira yotani?

11 Mtumwi Paulo atalemba za chikhulupiriro cha anthu akale amene anatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, iye anafotokoza kuti: “Komabe onsewa, ngakhale kuti anachitiridwa umboni chifukwa cha chikhulupiriro chawo, sanaone kukwaniritsidwa kwa lonjezolo. Zinatero chifukwa chakuti Mulungu anaoneratu chinthu chabwino kwambiri choti atipatse, kuti iwo asakhale angwiro popanda ife.” (Aheberi 11:39, 40) Kodi “chinthu chabwino kwambiri” chimene Paulo ndi Akhristu ena odzozedwa ankayembekezera n’chiyani? Yohane anachiona m’masomphenyawa. Iye anati: “Aliyense wa iwo anapatsidwa mkanjo woyera, ndipo anauzidwa kuti apumulebe kanthawi pang’ono, kufikira chitakwanira chiwerengero cha akapolo anzawo, ndi abale awo amene anali pafupi kuphedwa monga mmene iwonso anaphedwera.” (Chivumbulutso 6:11) Kulandira “mkanjo woyera” kukutanthauza kuti iwo anaukitsidwa n’kupatsidwa moyo wauzimu umene sungafe. Iwo salinso pansi pa guwa la nsembe ngati miyoyo ya amene anaphedwa, koma anaukitsidwa n’kukhala nawo m’gulu la akulu 24 amene amalambira Mulungu kumpando wake wachifumu wakumwamba. Kumeneko, iwonso anapatsidwa mipando yachifumu, kutanthauza kuti tsopano ndi mafumu. Ndipo iwo avala “malaya akunja oyera,” kutanthauza kuti aweruzidwa kuti ndi olungama, oyenera kupatsidwa malo aulemu pamaso pa Yehova m’bwalo lake lakumwamba. Zimenezi zikukwaniritsanso lonjezo la Yesu kwa Akhristu odzozedwa okhulupirika a mumpingo wa ku Sade. Iye anawauza kuti: “Amene wapambana pa nkhondo adzavekedwa malaya akunja oyera.”—Chivumbulutso 3:5; 4:4; 1 Petulo 1:4.

12. Kodi odzozedwa amene anaukitsidwa ‘akupumulabe kanthawi pang’ono’ m’njira yotani, ndipo apumula mpaka liti?

12 Umboni wonse ukusonyeza kuti anthu anayamba kuukitsidwa n’kupita kumwamba mu 1918, pambuyo poti Yesu waikidwa pampando wachifumu mu 1914 ndipo wakwera pahatchi yake yoyera n’kupita kukagonjetsa adani ake monga mfumu. Iye anayamba ndi kuyeretsa kumwamba pochotsako Satana ndi ziwanda zake. Koma odzozedwa amene anaukitsidwa n’kupita kumwambawo anauzidwa kuti “apumulebe kanthawi pang’ono, kufikira chitakwanira chiwerengero cha akapolo anzawo.” Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi ayenera kusonyeza kuti akutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika pamene akuyesedwa ndi kuzunzidwa, ndipo ena mwa iwo mwina adzaphedwa. Koma pamapeto pake, Mulungu adzabwezera Babulo Wamkulu ndiponso andale amene amagwirizana naye, chifukwa cha magazi onse olungama amene iwo anakhetsa. Panopa, Akhristu amene anaukitsidwa ayenera kuti ndi otanganidwa ndi ntchito zosiyanasiyana kumwamba. Sikuti iwo akupumula pongokhala osachita chilichonse, koma kuti akudikirira moleza mtima tsiku limene Yehova adzapereke chilango kwa adani ake. (Yesaya 34:8; Aroma 12:19) Kupumula kwawo kudzatha akadzaona chipembedzo chonyenga chikuwonongedwa ndiponso pamene iwo monga “oitanidwa . . . amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika,” adzathandize Ambuye Yesu Khristu kupereka chiweruzo kwa mbali zina zonse za mbewu yoipa ya Satana padziko lapansi pano.—Chivumbulutso 2:26, 27; 17:14; Aroma 16:20.

‘Amene Anafa Adzauka Choyamba’

13, 14. (a) Malinga ndi zimene ananena mtumwi Paulo, kodi anthu anayamba liti kuukitsidwa n’kupita kumwamba, ndipo ndani amene anaukitsidwa? (b) Kodi odzozedwa amene anali ndi moyo mpaka m’tsiku la Ambuye anaukitsidwa liti kupita kumwamba?

13 Zimene tikuona Yesu atamatula chidindo chachisanu zikugwirizana ndendende ndi zimene malemba ena amanena zokhudza anthu amene amaukitsidwa n’kupita kumwamba. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti tikukuuzani izi mogwirizana ndi mawu a Yehova kuti, ife amoyofe amene tidzakhalapo pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, sitidzakhala patsogolo pa amene agona mu imfa. Chifukwa Ambuye mwini adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo, ndi lipenga la Mulungu. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba. Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwowo, tidzatengedwa m’mitambo kukakumana ndi Ambuye m’mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.”—1 Atesalonika 4:15-17.

14 Mavesi amenewa akutiuza zinthu zochititsa chidwi kwambiri. Abale ake a Yesu odzozedwa amene anakhalabe ndi moyo padziko lapansi mpaka pa nthawi ya kukhalapo kwake, popita kumwamba sanakhale patsogolo pa anthu amene anafa kale. Amene anafa kale ali ogwirizana ndi Khristu, nthawi ya kukhalapo kwa Yesu isanafike, anali oyambirira kuukitsidwa. Yesu anatsika, kutanthauza kuti anaika maganizo ake onse pa iwo, ndipo anawaukitsa kuti akhale ndi moyo wauzimu, kutanthauza kuti anawapatsa “mkanjo woyera.” Ndiyeno amene ali ndi moyo padziko lapansi amamaliza moyo wawo wapadziko lapansi, ndipo ambiri mwa iwo amaphedwa mwankhanza ndi adani awo. Koma iwo sagona mu imfa ngati mmene anachitira anzawo aja. M’malomwake, akamwalira nthawi yomweyo amasintha, “m’kuphethira kwa diso,” ndipo amatengedwa kupita kumwamba kuti akakhale ndi Yesu ndi anzawo ena amene ali ziwalo za thupi la Khristu. (1 Akorinto 15:50-52; yerekezerani ndi Chivumbulutso 14:13.) Choncho kuukitsidwa kwa Akhristu odzozedwa kunayamba okwera pamahatchi anayi a m’buku la Chivumbulutso atangoyamba kumene liwiro lawo.

15. (a) Kodi kumatulidwa kwa chidindo chachisanu kwapereka uthenga wabwino wotani? (b) Kodi liwiro la Wopambana pa nkhondo amene wakwera pahatchi yoyera lidzathera pati?

15 Kumatulidwa kwa chidindo chachisanu chomatira mpukutu uja kwapereka uthenga wabwino wokhudza Akhristu odzozedwa amene anatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika mpaka imfa, ndipo anapambana pa nkhondo ya chikhulupiriro chawo. Koma sikunapereke uthenga wabwino uliwonse wokhudza Satana ndi mbewu yake. Wopambana pa nkhondo amene wakwera pahatchi yoyera, yemwe sangagonjetsedwe, apitirizabe liwiro lake lokagonjetsa adani ake. Liwiroli lidzathera pa nthawi yopereka chilango ku dzikoli, limene “lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Zimenezi zikuoneka bwino pamene Mwanawankhosa akumatula chidindo cha 6.

[Mawu a M’munsi]

a Mfundo zotithandiza kudziwa kuti Babulo Wamkulu ndi ndani zafotokozedwa mwatsatanetsatane m’Mutu 33.

b Yerekezerani ndi Zakumapeto 9 mu Baibulo la Dziko Latsopano, patsamba 1947 pa kamutu kakuti, “Mtengo Wozunzikirapo.”

c M’Mutu 36 muli umboni watsatanetsatane wosonyeza kuti zipembedzo zili ndi mlandu wa magazi.

[Bokosi patsamba 102]

“Miyoyo ya amene anaphedwa”

Buku lina lolembedwa ndi McClintock ndi Strong linagwira mawu a Mpulotesitanti wina wa ku England dzina lake John Jortin, yemwe anakhalapo m’zaka za m’ma 1700, ndipo makolo ake anali Apulotesitanti ochokera ku France. Bukulo linati: “Anthu akayamba kuzunzidwa, Chikhristu chimatha . . . Chikhristu chitakhazikitsidwa monga chipembedzo cha boma mu ufumu [wa Roma] ndiponso atsogoleri ake atapatsidwa ulemu ndi chuma chambiri, Chikhristucho chinakula mphamvu n’kuyamba kuzunza mwankhanza kwambiri Akhristu amene ankatsatira mfundo za m’mabuku a Uthenga Wabwino.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia.

[Chithunzi patsamba 103]

“Aliyense wa iwo anapatsidwa mkanjo woyera”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena