Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 12/1 tsamba 9-14
  • “Nkhani Zosangalatsa” za M’chivumbulutso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Nkhani Zosangalatsa” za M’chivumbulutso
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Olengeza Nkhani Zosangalatsa
  • Zimene Chivumbulutso Chikutiuza
  • Mwanawankhosa Woyenerera Ulemerero
  • “Maweruzo Ake Ali Oona ndi Olungama”
  • Ulamuliro wa Zaka Chikwi Waulemerero
  • Khalani Oŵerenga Achimwemwe a Buku la Chivumbulutso
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Dzina la Buku la M’Baibulo, Lakuti Chivumbulutso, Limatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Mmene Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Akukukhudzirani
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 12/1 tsamba 9-14

“Nkhani Zosangalatsa” za M’chivumbulutso

“Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire [monga nkhani zosangalatsa, NW] kwa iwo akukhala padziko.”​—CHIVUMBULUTSO 14:6.

1. Pamene kuli kwakuti Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti buku la Chivumbulutso n’louziridwa, n’chifukwa chiyani sizili “gulu lolengeza za tsiku lachiwonongeko”?

MOSIYANA kwambiri ndi nkhani zoŵaneneza, Mboni za Yehova sizili “gulu lolengeza za tsiku lachiwonongeko.” Komabe, iwo amavomereza kuti buku la Chivumbulutso ndi mbali ya Mawu ouziridwa a Mulungu. Zoonadi, buku la Chivumbulutso lilinso ndi mauthenga achiweruzo kwa oipa. Koma pochita umboni wawo wapoyera, atumiki a Mulungu amakonda kutchula kwambiri za chiyembekezo chosangalatsa kwambiri chimene chili m’Baibulo, kuphatikizapo m’buku la Chivumbulutso. Chotero, iwo sawonjeza kapena kuchotsa kalikonse m’mawu aulosi amene ali mmenemo.​—Chivumbulutso 22:18, 19.

Olengeza Nkhani Zosangalatsa

2. Kodi ndi malemba ena ati amene Mboni za Yehova zimaŵerenga pantchito yawo yolalikira?

2 Maziko a m’Malemba a utumiki wapoyera wa Mboni za Yehova amene amatchulidwa nthaŵi zambiri ndiwo mawu a Yesu akuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa (“udzalengezedwa,” NW, mawu am’tsinde) padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Nanga “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” ndiwo chiyani? Mboni zambiri zingayankhe mwa kutchula mawu a m’mavesi a machaputala 20 ndi 21 a m’Chivumbulutso amene amanena za Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi ndi boma lake la Ufumu ndi anthu okhala padziko lapansi, pamene “sipadzakhalanso” imfa, maliro, ndi zopweteka.​—Chivumbulutso 20:6; 21:1, 4.

3. Kodi utumiki wapoyera wa Mboni za Yehova ukugwirizana ndi ntchito iti?

3 Pokhala olengeza nkhani zosangalatsa zimenezi, Mboni za Yehova zili kwenikweni zolankhulira za mthenga wophiphiritsa wakumwamba amene ntchito yake ikulongosoledwanso m’buku la Chivumbulutso. “Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6) “Uthenga Wabwino wosatha” ukuphatikizapo chilengezo chakuti “Ufumu [kapena, ulamuliro] wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake” ndi kuti “nthaŵi” ya Yehova yafika ya “kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:15, 17, 18) Kodi umenewo si uthenga wabwinodi?

Zimene Chivumbulutso Chikutiuza

4. (a) Kodi m’chaputala 1 cha Chivumbulutso mwafotokozedwa mfundo ziti zazikulu za choonadi? (b) Kodi ofuna kupindula ndi nkhani zosangalatsa ayenera kuchitanji?

4 Chaputala choyambirira cha buku la Chivumbulutso chimatcha Yehova kukhala “Alefa ndi Omega, . . . amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.” Ndipo chimati Mwana wake, Yesu Kristu, ndi “mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi.” Chimanenanso za Yesu kukhala “Iye amene atikonda ife, natimasula ku machimo athu ndi mwazi wake.” (Chivumbulutso 1:5, 8) Chotero kungoyambira kuchiyambi, buku la Chivumbulutso limafotokoza mfundo zazikulu za choonadi chopulumutsa moyo. “Iwo akukhala padziko” sadzapindula ndi nkhani zosangalatsa zimene akuuzidwa pokhapokha atavomereza uchifumu wa Yehova, kukhulupirira mwazi wokhetsedwa wa Yesu, ndi kukhulupirira kuti Yehova anamuukitsa ndi kuti tsopano Kristu ndiye Wolamulira woikidwa ndi Mulungu.​—Salmo 2:6-8.

5. Kodi machaputala 2 ndi 3 a Chivumbulutso amasonyeza Kristu ali paudindo wotani?

5 Machaputala aŵiri otsatira amasonyeza Kristu Yesu monga Woyang’anira wachikondi wakumwamba wa mipingo ya ophunzira ake padziko lapansi. Mpukutu womwe analembera mipingo yachikristu isanu ndi iŵiri yosankhidwa imene inaliko ku Asia Minor m’zaka zana loyamba C.E. unali ndi chilimbikitso komanso uphungu wamphamvu wothandizabe lerolino. Mauthenga otumizidwa ku mipingoyo amayamba ndi mawu monga akuti “ndidziŵa ntchito zako” kapena “ndidziŵa chisautso chako.” (Chivumbulutso 2:2, 9) Inde, Kristu anali kudziŵa zonse zomwe zinali kuchitika m’mipingo ya ophunzira ake. Mipingo ina anaiyamikira chifukwa cha chikondi chawo, chikhulupiriro, ntchito yawo muutumiki, chipiriro, ndi kukhulupirika ku dzina lake ndi mawu ake. Ina anaidzudzula chifukwa chakuti chikondi chawo pa Yehova ndi Mwana wake chinazirala, kapenanso anagwera m’zachiwerewere, kupembedza mafano, kapena mpatuko.

6. Kodi masomphenya olembedwa m’chaputala 4 amathandiza anthu kumvetsa chiyani?

6 Chaputala 4 chikusimba za masomphenya ochititsa nthumanzi a mpando wachifumu wakumwamba wa Yehova Mulungu. Pamlingo waung’ono chikusonyeza ulemerero wa malo a Yehova ndi olamulira akumwamba amene iye adzagwiritsa ntchito. Olamulira ovala akorona ameneŵa, amene mipando yawo yachifumu imazungulira mpando wachifumu waukulu m’chilengedwe chonse, amagwadira Yehova ndi kulengeza kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”​—Chivumbulutso 4:11.

7. (a) Kodi mngelo akulamula okhala padziko lapansi kuti achite chiyani? (b) Kodi mbali yofunika ya ntchito yathu ndiyo kuchitanji?

7 Kodi zimenezi zili ndi tanthauzo lililonse kwa anthu lerolino? Ndithudi zilinalo. Ngati akufuna moyo mu Ufumu wa Zaka Chikwi, ayenera kumvera zimene ‘mngelo wouluka pakati pa mlengalenga’ akulengeza kuti: “Opani Mulungu, m’patseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.” (Chivumbulutso 14:6, 7) Chimodzi mwa zolinga za ntchito yophunzitsa Baibulo imene Mboni za Yehova zikuchita ndicho kuthandiza “iwo akukhala padziko” kuti adziŵe ndi kulambira Yehova, kuvomereza kuti ndiye Mlengi, ndi kugonjera uchifumu wake wolungama modzifunira.

Mwanawankhosa Woyenerera Ulemerero

8. (a) Kodi Kristu akusonyezedwa monga chiyani m’chaputala 5 ndi 6? (b) Kodi onse amene akumvetsera nkhani zosangalatsazi akuphunziraponji pa masomphenya ameneŵa?

8 Machaputala aŵiri otsatira, 5 ndi 6, amasonyeza Yesu Kristu monga Mwanawankhosa yemwe akupezeka kukhala woyenerera kutsegula buku la zizindikiro zisanu ndi ziŵiri, kuvumbula mwaphiphiritso zinthu zomwe zikuchitika m’tsiku lathu. (Yerekezani ndi Yohane 1:29.) Kwa Mwanawankhosa wophiphiritsa ameneyu, mawu akumwamba akunena kuti: “Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo mudaŵayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Masomphenya ameneŵa akutiphunzitsa kuti pamaziko a mwazi wokhetsedwa wa Kristu, anthu ena a m’mitundu yosiyanasiyana akuitanidwa kukakhala naye kumwamba ndi ‘kuchita ufumu padziko.’ (Yerekezani ndi Chivumbulutso 1:5, 6.) Chiŵerengero chawo chenicheni chikutchulidwa pambuyo pake m’buku la Chivumbulutso.

9. Kodi Kristu akusonyezedwa motani m’chaputala 6?

9 M’masomphenya ena, Kristu akusonyezedwa monga munthu wovala korona yemwe wakwera pakavalo woyera, amene ‘atulukira wolakika kuti alakike.’ Chosangalatsa n’chakuti adzagonjetsa zotsatirapo zoipa zosonyezedwa ndi apakavalo enanso atatu a m’Chivumbulutso, amene adzetsa nkhondo zoopsa, njala zazikulu, ndi imfa zosaneneka kwa mtundu wa anthu chiyambire chaka chosaiŵalikacho cha 1914. (Chivumbulutso 6:1-8) Ntchito yofunika zedi ya Kristu, Mwanawankhosa wa Mulungu, pa kupulumutsidwa kwa mtundu wa anthu ndi kukwaniritsidwa kwa zifuno zosangalatsa za Yehova ndiyo nkhani yaikulu m’ntchito yophunzitsa Baibulo ya Mboni za Yehova.

10. (a) Kodi ndi mfundo zofunika zotani zimene zikutchulidwa m’chaputala 7? (b) Kodi Kristu anati chiyani ponena za amene adzalandira Ufumu?

10 Chaputala 7 chili ndi nkhani zosangalatsadi. M’buku la Chivumbulutso mokha ndi mmene tikupeza chiŵerengero cha awo amene Yesu anawatcha kuti “kagulu kankhosa” kamene Atate wa Mwanawankhosayu akupatsa Ufumu. (Luka 12:32; 22:28-30) Ameneŵa amasindikizidwa chizindikiro ndi Yehova Mulungu mwa mzimu wake. (2 Akorinto 1:21, 22) Mtumwi Yohane amene analandira Chivumbulutso, akuvomereza kuti: “Ndinamva chiŵerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anayi mphambu anayi.” (Chivumbulutso 7:4) Chiŵerengero chenicheni chimenechi chikutchulidwanso m’chaputala china chapatsogolo kuti ndicho chiŵerengero chonse cha awo “ogulidwa kuchokera kudziko” kuti akalamulire ndi Mwanawankhosa pa Phiri la Ziyoni lakumwamba. (Chivumbulutso 14:1-4) Pamene kuli kwakuti matchalitchi achikristu amapereka mafotokozedwe osatsatirika bwino ndi osatsimikizirika ponena za chiŵerengero chimenechi, katswiri wa za Baibulo E. W. Bullinger anatchula mfundo yochititsa chidwi yakuti: “Ndi mfundo yotchulidwa mosapita m’mbali: chiŵerengero chodziŵikiratu mosiyana ndi chiŵerengero chosadziŵika m’chaputala chimenechi.”

11. (a) Kodi ndi nkhani zosangalatsa zotani zomwe zimapezeka m’chaputala 7? (b) Kodi a mu “khamu lalikulu” ali ndi tsogolo lotani?

11 Kodi Bullinger anali kunena za chiŵerengero chosadziŵika chiti? M’vesi 9, mtumwi Yohane analemba kuti: “Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Kodi a m’khamu lalikulu limeneli ndani, nanga Mulungu amaŵaona motani leroli, ndipo kodi ali ndi tsogolo lotani? Yankho la m’Chivumbulutso lili uthenga wabwino kwa anthu okhala padziko. Timaŵerenga kuti: “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” Mwa kukhulupirira mwazi wokhetsedwa wa Kristu, iwo adzatetezedwa pa “chisautso chachikulu.” Kristu ‘adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzaŵapukutira misozi yonse pamaso pawo.’ (Chivumbulutso 7:14-17) Inde, anthu mamiliyoni ambiri amene alipo lerolino angakhale mbali ya khamu losaŵerengeka limene lidzapulumuka mapeto a dongosolo loipa lilipoli la zinthu. Monga olamulidwa ndi Mfumu Yesu Kristu mu Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi, iye adzaŵatsogolera ku moyo wosatha padziko lapansi. Kodi umenewo si uthenga wabwino?

“Maweruzo Ake Ali Oona ndi Olungama”

12, 13. (a) Kodi machaputala 8 mpaka 19 amanena za chiyani? (b) N’chifukwa chiyani anthu oona mtima sayenera kuvutika maganizo ndi maulosi amenewo?

12 Machaputala 8 mpaka 19 ndiwo kwenikweni amene apangitsa anthu kuona buku la Chivumbulutso monga buku lolosera masoka oopsa. Machaputalawo ali ndi mauthenga amphamvu achiweruzo (ophiphiritsidwa ndi kulira kwa malipenga, miliri, ndi mbale za mkwiyo wa Mulungu) onenedwera mbali zosiyanasiyana za dongosolo la zinthu la Satana. Ziweruzo zimenezi zidzachitidwa, choyamba pa chipembedzo chonyenga (‘Babulo Wamkulu’), kenako pa madongosolo andale osaopa Mulungu, ophiphiritsidwa ndi zilombo.​—Chivumbulutso 13:1, 2; 17:5-7, 15, 16.a

13 Machaputala ameneŵa akusonyeza kuyeretsedwa kwa kumwamba, pamene Satana ndi ziwanda zake akuponyedwa pansi kudziko lapansi. Zimenezi zimapereka mafotokozedwe okha omveka a zomwe zachitika kuti kuyambira mu 1914 dziko likhale pamavuto amene sanayambe achitikapo. (Chivumbulutso 12:7-12) Mwa maphiphiritso, amafotokozanso za kuwonongedwa kwa dongosolo loipa la Satana padziko lapansi. (Chivumbulutso 19:19-21) Kodi anthu oona mtima angavutike maganizo ndi zochitika zimenezi? Iyayi, popeza pochitika ziweruzo za Mulungu, gulu lakumwamba likufuula kuti: “Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, n’za Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama.”​—Chivumbulutso 19:1, 2.

14, 15. (a) Kodi dongosolo loipa lilipoli lidzathetsedwa motani mwachilungamo? (b) N’chifukwa chiyani mbali imeneyi ya Chivumbulutso iyenera kukhala yosangalatsa kwa anthu oona mtima?

14 Yehova sadzadzetsa dongosolo lolungama la zinthu padziko lapansi popanda kuchotsapo oliwononga. (Chivumbulutso 11:17, 18; 19:11-16; 20:1, 2) Koma palibe munthu kapena boma lolamulidwa ndi andale limene lili ndi ulamuliro kapena mphamvu yochita zimenezi. Ndi Yehova yekha ndi Kristu Yesu, Mfumu yake ndi Woweruza wake woikidwa, amene angachite zimenezi mwachilungamo.​—2 Atesalonika 1:6-9.

15 Monga momwe Chivumbulutso chimasonyezera bwino lomwe, Yehova adzathetsa dongosolo loipa lilipoli. Mfundo imeneyi iyenera kusangalatsa amuna ndi akazi amene “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa.” (Ezekieli 9:4) Izi ziyenera kuwatsimikizira za kufunika kwa kulabadira mwamsanga chilengezo cha mngelo wolengeza nkhani zosangalatsa, chakuti: “Opani Mulungu, . . . pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo m’lambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda.” (Chivumbulutso 14:7) Anthu oterowo ayeneratu kutumikira Yehova limodzi ndi Mboni zake, ‘zimene zisunga malamulo a Mulungu, nizikhala nawo umboni wa Yesu.’​—Chivumbulutso 12:17.

Ulamuliro wa Zaka Chikwi Waulemerero

16. (a) N’chifukwa chiyani matchalitchi achikristu akana chiyembekezo cha Zaka Chikwi? (b) N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti pemphero lachitsanzo lidzayankhidwa?

16 Machaputala 20 mpaka 22 a buku la Chivumbulutso ndiwo maziko a m’Malemba a chiyembekezo cha Zaka Chikwi. Chimenechi ndicho chigawo chokha cha Baibulo chimene chimatchuliratu nyengo ya zaka chikwi imene idzalambule bwalo la umuyaya wachimwemwe kumwamba ndi padziko lapansi. Matchalitchi achikristu akana chiyembekezo cha Zaka Chikwi. Popeza kuti chiphunzitso cha matchalitchi chimati anthu olungama amapita kumwamba ndipo oipa amapita ku helo, sichitchula n’komwe za paradaiso wa padziko lapansi. Pemphero lachitsanzo, limene limapempha kuti “kufuna [kwa Mulungu] kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano,” lilibenso tanthauzo lililonse kwa mamembala ambiri a matchalitchi achikristu. (Mateyu 6:10) Koma si mmene zilili kwa Mboni za Yehova. Zimakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova Mulungu sanalenge dziko “mwachabe,” koma kuti “akhalemo anthu.” (Yesaya 45:12, 18) Chotero, ulosi wakale, pemphero lachitsanzo, ndi chiyembekezo cha m’Chivumbulutso cha Zaka Chikwi, zonsezi zikugwirizana. Mu Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi, Kristu adzaonetsetsa kuti chifuniro cha Yehova chachitidwa padziko lapansi, monga momwe chikuchitidwira kumwamba.

17. N’chiyani chimasonyeza kuti tiyenera kuona “zaka chikwi” kukhala zaka zenizeni?

17 Mawu akuti “zaka chikwi” akupezeka kasanu ndi kamodzi m’mavesi oyambirira asanu ndi aŵiri a Chivumbulutso chaputala 20. Chochititsa chidwi n’chakuti penapake mawu ameneŵa akutchulidwa kuti “zaka chikwizo,” kusonyeza kuti akunena za zaka zenizeni zokwanira chikwi, osati chabe nthaŵi yaitali yosadziŵika bwino, monga momwe othirira ndemanga ambiri a m’zipembedzo zachikristu amanenera. Kodi n’chiyani chidzachitike m’Zaka Chikwizo? Choyamba, Satana adzakhala wopanda mphamvu kwa nthaŵi yonseyo. (Chivumbulutso 20:1-3; yerekezani ndi Ahebri 2:14.) Uthengatu wabwino zedi umenewo!

18. (a) N’chifukwa chiyani Zaka Chikwi zingatchedwe kuti “tsiku” lachiweruzo? (b) Kodi n’chiyani chidzachitike pamapeto a zaka chikwizo?

18 Popeza kuti “chiweruziro” chapatsidwa kwa awo amene ‘adzachita ufumu pamodzi ndi Iye [Kristu] zaka chikwizo,’ nthaŵi imeneyi ndiyo, kwenikweni, “tsiku” lachiweruzo la zaka chikwi. (Chivumbulutso 20:4, 6; yerekezani ndi Machitidwe 17:31; 2 Petro 3:8.) Akufa adzaukitsidwa ndipo, pamodzi ndi opulumuka “chisautso chachikulu,” adzaweruzidwa molingana kudalira pa ntchito zawo, kapena kuti zochita zawo, za m’nthaŵiyo. (Chivumbulutso 20:12, 13) Pamapeto a zaka chikwi, Satana adzamasulidwa kwakanthaŵi kochepa kuti ayese mtundu wa anthu komaliza ndiyeno pambuyo pake iyeyo, ziwanda zake, ndi opanduka ena alionse padziko lapansi amene adzam’tsatira adzawonongedwa kosatha. (Chivumbulutso 20:7-10) Anthu amene adzapambana pachiyeso chimenechi mayina awo adzalembedwa “m’buku la moyo” ndipo sadzafafanizidwa. Kenako adzapatsidwa moyo wosatha wachimwemwe, kutumikira ndi kulambira Yehova padziko lapansi la paradaiso.​—Chivumbulutso 20:14, 15; Salmo 37:9, 29; Yesaya 66:22, 23.

19. (a) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti malonjezo osangalatsa otchulidwa m’buku la Chivumbulutso sadzalephera kukwaniritsidwa? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Zimenezi ndizo nkhani zosangalatsa za m’Chivumbulutso. Si malonjezo wamba a anthu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mawu aŵa ali okhulupirika ndi oona.” (Chivumbulutso 21:5) Kodi tingachitenji kuti tikhale ndi mbali pakukwaniritsidwa kwa nkhani zosangalatsa zimenezi? Buku la Chivumbulutso lili ndi uphungu wochuluka kwa awo ofuna kukondweretsa Mulungu. Kutsatira uphungu umenewo kudzatidzetsera chimwemwe chochuluka, tsopano ndiponso kosatha, monga momwe nkhani yotsatira idzasonyezera.

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mukufuna malongosoledwe onse a buku la Chivumbulutso, onani buku lakuti Revelation​—Its Grand Climax At Hand!, lomwe linafalitsidwa mu 1988 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Mfundo Zobwereza

◻ Kodi ndi mfundo zazikulu ziti za choonadi zopezeka m’machaputala 4 mpaka 6 a Chivumbulutso zimene zikupanga mbali yofunika ya nkhani zosangalatsa?

◻ Kodi ndi nkhani zosangalatsa zotani zomwe zikupezeka m’Chivumbulutso chaputala 7?

◻ N’chifukwa chiyani anthu oona mtima sayenera kuchita mantha ndi mauthenga achiweruzo omwe ali m’Chivumbulutso?

◻ Kodi Zaka Chikwi zidzakhala “tsiku” lachiweruzo m’njira zotani?

[Chithunzi patsamba 10]

Mfumu Yesu Kristu adzachotseratu nkhondo zonse, njala ndi imfa padziko lapansi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena