Khamu Lalikulu Lopereka Utumiki Wopatulika
“Amtumikira Iye usana ndi usiku m’Kachisi mwake.” —CHIVUMBULUTSO 7:15.
1. Kodi ndi kupita patsogolo kotani kwa kuzindikira kwauzimu kumene kunafikiridwa mu 1935?
PA May 31, 1935, panali chisangalalo chachikulu pakati pa nthumwi pamsonkhano wa Mboni za Yehova ku Washington, D.C. Kumeneko, kwa nthaŵi yoyamba, namtindi wamkulu (kapena, khamu lalikulu) wa pa Chivumbulutso 7:9 anadziŵikitsidwa bwino mogwirizana ndi Baibulo lonse ndiponso mogwirizana ndi zochitika zimene zinali zitayamba kale kuchitika.
2. Kodi nchiyani chimene chinasonyeza kuti anthu omawonjezerekawo anazindikira kuti Mulungu sanawaitanire kumoyo wakumwamba?
2 Pafupifupi milungu isanu ndi umodzi pasadakhale, pa chochitika cha Chakudya cha Madzulo cha Ambuye m’mipingo ya Mboni za Yehova, 10,681 a awo amene analipo (pafupifupi 1 mwa 6) sanadye zizindikiro za mkate ndi vinyo, ndipo 3,688 mwa ameneŵa anali olengeza okangalika a Ufumu wa Mulungu. Kodi nchifukwa ninji anapeŵa kudya zizindikirozo? Chifukwa cha zimene anaphunzira m’Baibulo, anazindikira kuti Mulungu sanawaitanire ku moyo wakumwamba koma kuti adzakhala ndi phande m’makonzedwe achikondi a Yehova mwanjira ina. Chotero pamsonkhanopo, pamene wokamba nkhani anapempha kuti: “Awo onse amene ali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi aimirire chonde,” chinachitika nchiyani? Zikwi zambiri zinaimirira, ndipo omvetsera anawomba m’manja kwanthaŵi yaitali.
3. Kodi nchifukwa ninji kudziŵikitsidwa kwa namtindi wamkulu kunapereka chisonkhezero chatsopano ku utumiki wakumunda, ndipo kodi ndimotani mmene Mboni zinaonera zimenezi?
3 Zimene nthumwizo zinaphunzira pamsonkhano umenewo zinapereka chisonkhezero chatsopano ku utumiki wawo kuposa ndi kale lonse. Anafikira pakuzindikira kuti tsopano lino, mapeto adongosolo lakale asanafike, si anthu zikwi zoŵerengeka chabe koma namtindi wamkulu wa anthu akapatsidwa mwaŵi wa kuloŵa m’makonzedwe a Yehova a kupulumutsa moyo, ndi cholinga cha kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la paradaiso. Unali uthenga wothutsa mtima chotani nanga umene unaperekedwa kwa okonda choonadi pamenepo! Mboni za Yehova zinazindikira kuti panali ntchito yaikulu yoti ichitidwe—ntchito yosangalatsa. Zaka zina pambuyo pake, John Booth, amene anadzakhala chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, anakumbukira kuti: “Msonkhano umenewo unatipatsa zinthu zochuluka zosangalala nazo.”
4. (a) Kodi kusonkhanitsidwa kwa khamu lalikulu kokhalapo chiyambire 1935 kwafikiradi pamlingo wotani? (b) Kodi ndi m’njira yotani imene a khamu lalikulu akuperekera umboni wakuti chikhulupiro chawo nchamoyo?
4 M’zaka zimene zinatsatira, chiŵerengero cha Mboni za Yehova chinawonjezereka kwambiri. Mosasamala kanthu za chizunzo chachiwawa chodzetsedwa pa iwo mkati mwa Nkhondo Yadziko II, ziŵerengero zawo zinaŵirikiza pafupifupi katatu m’zaka khumi. Ndipo ofalitsa 56,153 amene anali kulalikira poyera mu 1935 anawonjezereka, podzafika 1994, panali olengeza Ufumu oposa 4,900,000 okhala m’maiko oposa 230. Unyinji wa ameneŵa ukuyembekezera mwaphamphu kudzaphatikizidwa limodzi ndi awo amene Yehova adzawapatsa moyo wangwiro pa dziko lapansi la paradaiso. Powayerekezera ndi kagulu ka nkhosa, iwo akhaladi khamu lalikulu. Iwo sali mtundu wa anthu amene amanena kuti ali ndi chikhulupiriro komabe amene samachisonyeza. (Yakobo 1:22; 2:14-17) Iwo onse amauza ena mbiri yabwino yonena za Ufumu wa Mulungu. Kodi inu ndinu mmodzi wa a khamu lachimwemwe limenelo? Kukhala Mboni yokangalika kuli chizindikiro chofunika chokudziŵirani, komano pali zambiri zimene zikuloŵetsedwamo.
“Akuimirira ku Mpando Wachifumu”
5. Kodi nchiyani chimene ‘kuimirira ku mpando wachifumu’ kwa khamu lalikulu kumasonyeza?
5 M’masomphenya operekedwa kwa mtumwi Yohane, anawaona “akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9) Kuima kwawo ku mpando wachifumu wa Mulungu, monga momwe kwalongosoledwera m’mawu a nkhaniyo, kumasonyeza kuti amavomereza kotheratu ulamuliro wa Yehova. Zimenezi zimaphatikizapo zambiri. Mwachitsanzo: (1) Iwo amavomereza kuyenera kwa Yehova kusankhira atumiki ake chimene chili chabwino ndi chimene chili choipa. (Genesis 2:16, 17; Yesaya 5:20, 21) (2) Amamvetsera Yehova pamene alankhula nawo m’Mawu ake. (Deuteronomo 6:1-3; 2 Petro 1:19-21) (3) Amazindikira kufunika kwa kugonjera awo amene Yehova wawaikizira uyang’aniro. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:22, 23; 6:1-3; Ahebri 13:17) (4) Ngakhale kuti ali opanda ungwiro, amayesayesa mwakhama kuchita mogwirizana ndi chitsogozo cha teokrase, osati monyinyirika, koma mofunitsitsa, kuchokera mumtima. (Miyambo 3:1; Yakobo 3:17, 18) Aimirira ku mpando wachifumu kuti apereke utumiki wopatulika kwa Yehova, amene amamlemekeza kwambiri ndi amene amamkonda kwambiri. Ponena za khamu lalikulu limeneli, ‘kuimirira’ kwawo ku mpando wachifumu kumasonyeza kuti ali ndi chivomerezo cha Uyo wokhala pa mpando wachifumu. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 6:16, 17.) Chivomerezo pamaziko otani?
“Atavala Zovala Zoyera”
6. (a) Kodi ‘kuvala zovala zoyera’ kwa khamu lalikulu kumatanthauzanji? (b) Kodi ndimotani mmene khamu lalikulu limapezera kaimidwe kolungama pamaso pa Yehova? (c) Kodi ndi kufikira kumlingo wotani kumene chikhulupiriro m’mwazi wokhetsedwa wa Kristu chimayambukirira miyoyo ya khamu lalikulu?
6 Mafotokozedwe a mtumwi Yohane a zimene anaona amanena kuti ziŵalo za khamu lalikulu limeneli ‘zavala zovala zoyera.’ Zovala zoyera zimenezo zimaphiphiritsira kaimidwe kawo koyera, ndi kolungama pamaso pa Yehova. Kodi iwo anapeza motani kaimidwe koteroko? Taona kale kuti m’masomphenya a Yohane iwo anaimirira “pamaso pa Mwanawankhosa.” Amazindikira Yesu Kristu kukhala “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi.” (Yohane 1:29) Yohane anamva mmodzi wa akulu amene, m’masomphenyawo, anali pafupi ndi mpando wachifumu wa Mulungu akufotokoza kuti: “Anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa. Chifukwa chake ali ku mpando wachifumu wa Mulungu.” (Chivumbulutso 7:14, 15) Kunena mophiphiritsira, iwo atsuka zovala zawo mwa kusonyeza chikhulupiriro m’mwazi wa dipo wa Kristu. Samangovomereza ndi pakamwa ziphunzitso za Baibulo zonena za dipo. Kulizindikira kwawo kumayambukira umunthu wawo wamkati; motero, “ndi mtima” iwo amasonyeza chikhulupiriro. (Aroma 10:9, 10) Zimenezi zili ndi chiyambukiro chachikulu pa zimene amachita m’miyoyo yawo. Ndi chikhulupiriro, iwo amadzipatulira kwa Yehova pamaziko a nsembe ya Kristu, amasonyeza kudzipatulira kumeneko mwa kumizidwa m’madzi, amakhala mogwirizanadi ndi kudzipatulira kwawo, ndipo motero amakhala paunansi wovomerezedwa ndi Mulungu. Ha, ndi mwaŵi wabwino chotani nanga—woyenera kusungidwa mosamalitsa!—2 Akorinto 5:14, 15.
7, 8. Kodi ndimotani mmene gulu la Yehova lathandizira khamu lalikulu kusunga zovala zawo zili zosadetsedwa?
7 Pokhala ndi nkhaŵa yachikondi kaamba ka ubwino wawo wokhalitsa, gulu la Yehova lachenjeza mobwerezabwereza za mikhalidwe yamaganizo ndi khalidwe limene lingachititse banga, kapena kudetsa zovala za munthu zomdziŵikitsa kotero kuti, mosasamala kanthu za kudzinenera kwake kwakunja kokha, munthuyo sangayenerere mafotokozedwe aulosi a pa Chivumbulutso 7:9, 10. (1 Petro 1:15, 16) Pochirikiza zimene zinafalitsidwa poyambirira, The Watchtower, mu 1941 ndi pambuyo pake, mobwerezabwereza inasonyeza kuti kukakhala kosayenera konse kulalikira kwa ena ndiyeno, panthaŵi zina, kuloŵa m’khalidwe longa chisembwere ndi chigololo. (1 Atesalonika 4:3; Ahebri 13:4) Mu 1947 kunagogomezeredwa kuti miyezo ya Yehova ya ukwati Wachikristu imagwira ntchito m’maiko onse; mosasamala kanthu za zimene miyambo ya kumaloko imaloleza, awo amene anapitirizabe chizoloŵezi cha mitala sakanakhala Mboni za Yehova.—Mateyu 19:4-6; Tito 1:5, 6.
8 Mu 1973, Mboni za Yehova padziko lonse zinasonyezedwa kuti iwo onse ayenera kupeŵa kotheratu zizoloŵezi zilizonse zodetsa monga ngati kusuta fodya, mosasamala kanthu za kumene angakhale—osati m’Nyumba Yaufumu mokha kapena mu utumiki wakumunda komanso kuntchito kapena kumalo ena obisika kwa anthu onse. (2 Akorinto 7:1) Mu 1987 pamisonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova, Akristu achichepere analangizidwa mwamphamvu kuti, kuti asungebe kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu, ayenera kupeŵa kukhala ndi moyo wapaŵiri. (Salmo 26:1, 4) Mobwerezabwereza Nsanja ya Olonda yachenjeza za mbali zosiyanasiyana za mzimu wadziko chifukwa chakuti “mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate” amaphatikizapo kudzisungira mwini “wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.”—Yakobo 1:27.
9. Kodi ndani kwenikweni amene adzavomerezedwa kuimirira ku mpando wachifumu wa Mulungu pambuyo pa chisautso chachikulu?
9 Ali awo amene chikhulupiriro chawo chimawasonkhezera kukhala ndi moyo wosunga chiyero chauzimu ndi cha makhalidwe amene ‘adzaimirirabe ku mpando wachifumu’ monga atumiki ovomerezedwa a Mulungu pambuyo pa chisautso chachikulu chilinkudzacho. Ameneŵa ndi anthu amene samangoyamba chabe kukhala ndi moyo Wachikristu komanso amaumamatira mokhulupirika.—Aefeso 4:24.
“Makhwatha a Kanjedza m’Manja Mwawo”
10. Kodi makhwatha a kanjedza amene Yohane anaona ali m’manja mwa a khamu lalikulu ali ndi tanthauzo lotani?
10 Pakati pa zinthu zina zapadera za khamu lalikulu, monga momwe mtumwi Yohane anaonera, pali “makhwatha a kanjedza m’manja mwawo.” Kodi zimenezo zili ndi tanthauzo lotani? Mosakayikira makhwatha akanjedza amenewo anakumbutsa Yohane za phwando Lachiyuda la misasa, phwando la chisangalalo chachikulu koposa pa kalenda Yachihebri, lochitidwa motsatira kututa kwa m’chilimwe. Mogwirizana ndi Chilamulo, makhwatha a kanjedza, limodzi ndi makhwatha a mitengo ina, anagwiritsiridwa ntchito kupangira misasa yokhalamo mkati mwa phwando limeneli. (Levitiko 23:39-40; Nehemiya 8:14-18) Anagwedezedwanso ndi olambira pa kachisi poimba Hallel (Salmo 113-118). Kugwedeza makhwatha a kanjedza kochitidwa ndi khamu lalikulu mosakayikira kunakumbutsanso Yohane za chochitikacho pamene Yesu anakwera pabulu kuloŵa mu Yerusalemu pamene khamu la olambira linagwedeza makhwatha a kanjedza ndi kufuula mwachisangalalo kuti: “Wolemekezeka Iye wakudza m’dzina la Ambuye, ndiye Mfumu ya Israyeli.” (Yohane 12:12, 13) Chotero kugwedeza makhwatha a kanjedza kumasonyeza kuti khamu lalikulu likutamanda Ufumu wa Yehova ndi Mfumu yake yodzozedwayo mwachisangalalo.
11. Kodi nchifukwa ninji atumiki a Mulungu amapezadi chisangalalo m’kutumikira Yehova?
11 Uli mzimu wachisangalalo wotero umene khamu lalikulu likusonyeza ngakhale tsopano lino pamene likutumikira Yehova. Zimenezi sizimatanthauza kuti samakumana ndi mavuto kapena kuti samakhala ndi chisoni kapena zoŵaŵa. Koma chikhutiro chimene chimadza m’kutumikira ndi m’kukondweretsa Yehova chimawachotsera zinthu zimenezo. Motero, mmishonale wina amene anatumikira ndi mwamuna wake kwa zaka 45 ku Guatemala anasimba za mikhalidwe ina yachikale imene analimo, kugwira ntchito zolimba ndi maulendo owopsa amene anali mbali ya moyo pamene anali kuyesayesa kufikira midzi ya Aindiya ndi uthenga wa Ufumu. Iye anati: “Inali nthaŵi yosaiŵalika m’miyoyo yathu pamene tinalidi achimwemwe.” Ngakhale kuti kukalamba ndi kudwaladwala zinali kumsautsa, pakati pa zolemba zotsirizira za m’dayale yake panali mawu akuti: “Unali moyo wabwino, wofupa kwambiri.” Padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zimaona mofananamo utumiki wawo.
“Utumiki Wopatulika Usana ndi Usiku”
12. Kaya ndi usana kapena usiku, kodi nchiyani chimene Yehova amaona padziko lapansi pano?
12 Olambira achimwemwe ameneŵa amapereka kwa Yehova “utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kachisi mwake.” (Chivumbulutso 7:15, NW) Kuzungulira dziko lonse, mamiliyoni akukhala ndi phande mu utumiki wopatulika umenewu. Pamene uli usiku m’maiko ena ndipo anthu ali m’tulo kumeneko, m’maiko ena dzuŵa limakhala litatuluka ndipo Mboni za Yehova zimakhala zili zotanganitsidwa kuchitira umboni. Pamene dziko likuzungulira, mosalekeza, usana ndi usiku, izo zimaimba zitamando za Yehova. (Salmo 86:9) Koma utumiki wochitidwa usana ndi usiku wotchulidwa pa Chivumbulutso 7:15 umenewo umachitidwa ngakhale ndi munthu mwini payekha.
13. Kodi ndimotani mmene Malemba amasonyezera chimene chimatanthauzidwa ndi kutumikira “usana ndi usiku”?
13 Anthu amene amapanga khamu lalikulu amapereka utumiki wopatulika usana ndi usiku. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti zinthu zilizonse zimene amachita zimaonedwa kukhala utumiki wopatulika? Nzoona kuti mosasamala kanthu za chimene amachita, amaphunzira kuchita chinthucho m’njira imene imalemekeza Yehova. (1 Akorinto 10:31; Akolose 3:23) Komabe, “utumiki wopatulika” umagwira ntchito kokha pa zimene zimaloŵetsamo mwachindunji kulambira Mulungu kwa munthu mwini. Kugwira ntchitoyo “usana ndi usiku” kumatanthauza kuchita nthaŵi zonse kapena mosalekeza ndiponso mwakhama.—Yerekezerani ndi Yoswa 1:8; Luka 2:37; Machitidwe 20:31; 2 Atesalonika 3:8.
14. Kodi nchiyani chingapangitse utumiki wakumunda wa ife eni kukhala woyenerera mafotokozedwe a utumiki wa “usana ndi usiku”?
14 Pamene akutumikira m’bwalo lapadziko lapansi la kachisi wauzimu wamkuluyo wa Yehova, awo amene amapanga khamu lalikulu amayesayesa kukhala ndi phande nthaŵi zonse ndiponso mosalekeza mu utumiki wakumunda. Ambiri adziikira chonulirapo cha kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda mlungu uliwonse. Ena amayesetsa kutero monga apainiya okhazikika kapena apainiya othandiza. Kaŵirikaŵiri ameneŵa amakhala otanganitsidwa m’kuchitira umboni m’makwalala ndi m’masitolo mmamaŵa kwambiri. Kuti athandize okondwerera, Mboni zina zimachititsa maphunziro a Baibulo usiku kwambiri. Zimapereka umboni pamene zikugula zinthu, poyenda ulendo, mkati mwa nyengo za chakudya chamasana, ndipo mwa kuimba telefoni.
15. Kuwonjezera pa utumiki wakumunda, kodi nchiyaninso chimene chikuphatikizidwa mu utumiki wathu wopatulika?
15 Kukhala ndi phande m’misonkhano ya mpingo kulinso mbali ya utumiki wathu wopatulika; chimodzimodzinso ndi kuchita ntchito ya kumanga ndi m’kusamalira malo a misonkhano Yachikristu. Zoyesayesa zochitidwa kulimbikitsa ndi kuthandiza abale ndi alongo Achikristu a munthuwe, mwauzimu ndi mwakuthupi, kuti akhale amoyo mu utumiki wa Yehova nazonso zimaphatikizidwamo. Zimenezi zimaphatikizapo ntchito ya Makomiti athu Olankhulana ndi Chipatala. Utumiki wa pa Beteli m’mipangidwe yake yosiyanasiyana, ndiponso utumiki wodzifunira pamisonkhano yathu yachigawo, zonsezo ndizo utumiki wopatulika. Zoonadi, pamene miyoyo yathu isumikidwa pa unansi wathu ndi Yehova, imadzazidwa ndi utumiki wopatulika. Monga momwe lembalo likunenera, anthu a Yehova amapereka “utumiki wopatulika usana ndi usiku,” ndipo amapeza chisangalalo chachikulu m’kuchita motero.—Machitidwe 20:35; 1 Timoteo 1:11.
“Ochokera mwa Mtundu Uliwonse, ndi Mafuko ndi Anthu ndi Manenedwe”
16. Kodi zili zoona motani kuti khamu lalikulu likuchokera “mwa mtundu uliwonse”?
16 Awo a khamu lalikulu akuchokera m’mitundu yonse. Mulungu alibe tsankhu, ndipo makonzedwe a dipo opangidwa kupyolera mwa Yesu Kristu ngokwanira kupindulitsa iwo onse. Pamene khamu lalikulu linazindikiridwa kwa nthaŵi yoyamba Mwamalemba mu 1935, Mboni za Yehova zinali zokangalika m’maiko 115. Podzafika m’ma 1990, kufunafuna onga nkhosa kunali kutafutukukira m’maiko ena owonjezereka kuŵirikiza kuposa kaŵiri.—Marko 13:10.
17. Kodi nchiyani chimene chikuchitidwa kuthandiza anthu a ‘mafuko, anthu ndi manenedwe’ onse kuti aphatikizidwe ndi khamu lalikulu?
17 Poyesayesa kupeza oyembekezera kukhala ziŵalo za khamu lalikulu, Mboni za Yehova zasamalira osati kokha mitundu komanso mafuko ndi anthu ndi zinenero za mitunduyo. Kuti zifikire anthu ameneŵa, Mboni zimafalitsa mabuku ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 300. Zimenezi zimaloŵetsamo kuphunzitsa ndi kusamalira magulu a otembenuza zinenero okhoza bwino, kuwapatsa ziŵiya za makompyuta zokhoza kusamalira zinenero zonsezi, ndiponso kuchita ntchito yosindikiza yeniyeniyo. Mkati mwa zaka zisanu zokha zapitazo, zinenero 36, zolankhulidwa ndi anthu pafupifupi 98,000,000, zawonjezeredwa pa zinenero zinazo. Ndiponso, Mboni zimayesayesa kufikira mwaumwini anthu ameneŵa kukawathandiza kumvetsetsa Mawu a Mulungu.—Mateyu 28:19, 20.
“Akutuluka m’Chisautso Chachikulu”
18. (a) Pamene chisautso chachikulu chiulika, kodi ndani amene adzatetezeredwa? (b) Kodi ndi zilengezo zosangalatsa zotani zimene zidzaperekedwa panthaŵiyo?
18 Pamene angelo amasula mphepo za chiwonongeko zotchulidwa pa Chivumbulutso 7:1, si “akapolo a Mulungu wathu” odzozedwa okha amene adzatetezeredwa ndi Yehova mwachikondi komanso ndi khamu lalikulu limene lagwirizana nawo m’kulambira koona. Monga momwe mtumwi Yohane anauzidwira, awo a khamu lalikulu ‘adzatuluka m’chisautso chachikulu’ monga opulumuka. Adzafuula mothokoza ndi motamanda chotani nanga panthaŵiyo pamene adzalengeza kuti: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa”! Ndipo atumiki onse a Mulungu okhulupirika kumwamba adzawonjezera mawu awo m’kulengeza kuti: “Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthaŵi za nthaŵi. Amen.”—Chivumbulutso 7:10-14.
19. Kodi ndi m’ntchito yosangalatsa yotani imene opumuluka adzafunitsitsa kukhalamo ndi phande?
19 Imeneyo idzakhala nthaŵi yachimwemwe chotani nanga! Onse amene adzakhala ndi moyo adzakhala atumiki a Mulungu woona yekha! Chisangalalo chachikulu koposa chimenechi chidzakhala m’kutumikira Yehova. Padzakhala ntchito yochuluka yoti ichitidwe—ntchito yosangalatsa! Dziko lapansi lidzasandulizidwa kukhala Paradaiso. Mamiliyoni zikwi zambiri a akufa adzaukitsidwa ndiyeno kuphunzitsidwa njira za Yehova. Ha, kukhalamo ndi phande kudzakhala mwaŵi wosangalatsa chotani nanga!
Kodi Ndemanga Yanu Njotani?
◻ Kodi nchiyambukiro chotani chimene zochitika za mu 1935 zinali nacho pa utumiki wakumunda wa Mboni za Yehova?
◻ Kodi nchiyani chimene “kuimirira ku mpando wachifumu” kwa khamu lalikulu kumasonyeza?
◻ Kodi ndimotani mmene chiyamikiro cha mwazi wa Mwanawankhosa chiyenera kuyambukirira miyoyo yathu?
◻ Kodi kugwedeza kwawo makhwatha a kanjedza kumatanthauzanji?
◻ Kodi ndimotani mmene khamu lalikulu limaperekera utumiki wopatulika usana ndi usiku?
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Utumiki wawo wopatulika uli wanthaŵi zonse, wachangu, ndi wakhama