Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Khamu Lalikulu Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 17. (a) Kodi mmodzi wa akulu 24 aja anafunsa funso lotani, ndipo mfundo yakuti mkuluyo ankadziwa yankho la funsolo ikusonyeza chiyani? (b) Kodi funso la mkuluyo linayankhidwa liti?

      17 Kuchokera m’nthawi ya mtumwi Yohane kudzafika m’tsiku la Ambuye, Akhristu odzozedwa sankalidziwa bwinobwino khamu lalikulu. Choncho m’pake kuti mmodzi wa akulu 24 aja, omwe akuimira Akhristu odzozedwa amene ali kumwamba, anam’thandiza Yohane kuti aganize pomufunsa funso lofunika kwambiri. Yohane anati: “Ndiyeno mmodzi wa akulu aja anandifunsa kuti: ‘Kodi amene avala mikanjo yoyerawa ndi ndani, ndipo achokera kuti?’ Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: ‘Mbuyanga, mukudziwa ndinu.’” (Chivumbulutso 7:13, 14a) Inde, mkulu ameneyu ankadziwa yankho la funso limeneli ndipo akanatha kumuuza Yohane. Zimenezi zikusonyeza kuti Akhristu odzozedwa amene anaukitsidwa kale ndipo ali m’gulu la akulu 24, mwina akugwira nawo ntchito yodziwitsa anthu choonadi cha Mulungu masiku ano. Akhristu odzozedwa amene ali padziko lapansi analidziwa khamu lalikululi poonetsetsa zimene Yehova ankachita pakati pawo. Iwo sanachedwe kumvetsetsa tanthauzo la kuwala kwamphamvu kochokera kwa Mulungu kumene kunaunikira bwino gulu lake mu 1935, pa nthawi ya Yehova yoyenerera.

  • Khamu Lalikulu Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 22. Kodi Yohane anauzidwa zinthu zinanso ziti zokhudza khamu lalikulu?

      22 Mulungu anauza Yohane zinthu zinanso zokhudza khamu lalikulu. Yohane anati: “Ndipo iye [mkulu uja] anati: ‘Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu, ndipo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa. N’chifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kachisi wake, ndipo wokhala pampando wachifumuyo adzatambasulira hema wake pamwamba pawo kuti awateteze.’”—Chivumbulutso 7:14b, 15.

      23. Kodi chisautso chachikulu chimene ‘mudzatuluke’ khamu lalikulu, n’chiyani?

      23 Nthawi inayake, Yesu ananena kuti kukhalapo kwake mu ulemerero wa Ufumu kudzathera pa “chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyu 24:21, 22) Pokwaniritsa ulosi umenewu, angelo adzasiya kugwira mphepo zinayi za dziko lapansi zija kuti ziwononge dziko la Satanali. Woyambirira kuwonongedwa adzakhala Babulo Wamkulu, amene ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi. Ndiyeno chisautsocho chikadzafika pachimake, Yesu adzapulumutsa a 144,000 amene adzakhale adakali ndi moyo padziko lapansi, pamodzi ndi khamu lalikulu kwambiri.—Chivumbulutso 7:1; 18:2.

      24. Kodi munthu aliyense amene ali m’khamu lalikulu amafunika kuchita chiyani kuti adzapulumuke?

      24 Kodi munthu aliyense amene ali m’khamu lalikulu amafunika kuchita chiyani kuti adzapulumuke? Mkulu uja anauza Yohane kuti anthu a m’khamu lalikulu “achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.” Zimenezi zikutanthauza kuti amakhulupirira kuti Yesu ndi amene anawaperekera dipo. Komanso iwo anadzipereka kwa Yehova ndipo anasonyeza kudzipereka kumeneko pobatizidwa m’madzi. Ndiponso ali ndi “chikumbumtima chabwino” chifukwa amachita zinthu zoyenera nthawi zonse. (1 Petulo 3:16, 21; Mateyu 20:28) Choncho Yehova amawaona kuti ndi oyera komanso olungama, ndipo iwo amayesetsa ‘kukhala opanda banga la dzikoli.’—Yakobo 1:27.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena