Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ufumu wa Mulungu Wabadwa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 7. Kodi Yohane anaonanso chizindikiro china chotani kumwamba?

      7 Kodi Yohane anaonanso chizindikiro china chotani? Iye anati: “Chizindikiro chinanso chinaoneka kumwamba, ndipo ndinaona chinjoka chachikulu chofiira, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10, ndipo pamitupo panali zisoti zachifumu 7. Mchira wake unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba n’kuzigwetsera kudziko lapansi. Ndipo chinjokacho chinangoimabe pamaso pa mkazi uja, amene anali pafupi kubereka, kuti akabereka chidye mwana wakeyo.”—Chivumbulutso 12:3, 4.

  • Ufumu wa Mulungu Wabadwa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 9. Kodi mfundo yakuti mchira wa chinjokacho “unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba” n’kuzigwetsera padziko lapansi, ikutanthauza chiyani?

      9 Chinjokachi chilinso ndi mphamvu pa zolengedwa zauzimu. Pogwiritsa ntchito mchira wake, ‘chinakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba.’ Nthawi zina nyenyezi zimaimira angelo. (Yobu 38:7) Choncho mfundo yakuti chinjokacho chinakokolola “gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi,” ikusonyeza kuti Satana anasocheretsa angelo ambiri ndithu. Angelo amenewa atayamba kulamuliridwa ndi Satana, zinali zosatheka kuti achoke mu ulamuliro wakewo. Sakanathanso kubwerera m’gulu loyera la Mulungu. Choncho iwo anakhala ziwanda ndipo tinganene kuti akukokedwa ndi Satana, yemwe ndi mfumu yawo kapena kuti wolamulira wawo. (Mateyu 12:24) Satana anagwetseranso nyenyezi zimenezi kudziko lapansi. Mosakayikira zimenezi zikuimira zomwe zinachitika Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chisanachitike. Pa nthawiyo Satana ananyengerera ana osamvera a Mulungu kuti abwere padziko lapansi kudzagona ndi ana aakazi a anthu. Mulungu analanga ‘angelo amene anachimwawa’ powachititsa kuti azikhala moyo wonyozeka wofanana ndi kukhala m’ndende, wotchedwa Tatalasi.—Genesis 6:4; 2 Petulo 2:4; Yuda 6.

      10. Kodi pali magulu awiri ati otsutsana, ndipo n’chifukwa chiyani chinjokacho chikufuna kudya mwana amene mkazi uja akufuna kubereka?

      10 Izi zachititsa kuti pakhale magulu awiri otsutsana. Gulu loyamba ndi mbali yakumwamba ya gulu la Yehova lomwe likuimiridwa ndi mkazi, ndipo gulu lachiwiri ndi la Satana ndi ziwanda zake lomwe likutsutsa ulamuliro wa Mulungu. Komabe nkhani yofunika kwambiri yakuti woyenera kulamulira ndani iyenera kuthetsedwa. Koma kodi idzathetsedwa bwanji? Satana, amene akukokabe ziwanda zija, ali ngati chilombo cholusa chimene chikufuna kudya winawake. Iye akuyembekezera kuti mkazi uja abereke. Satana akufuna kudya mwana wobadwa kumeneyu chifukwa akudziwa kuti iye pamodzi ndi dziko limene akulilamulirali, adzawonongedwa ndi mwana ameneyu.—Yohane 14:30.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena