Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ufumu wa Mulungu Wabadwa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 22, 23. (a) Kodi Yohane anati chinachitika n’chiyani chinjoka chija chitaponyedwa kudziko lapansi? (b) Kodi zikutheka bwanji kuti chinjokacho chizunze “mkazi amene anabereka mwana wamwamuna uja”?

      22 Kungochokera pamene Satana anachotsedwa kumwamba, iye wakhala akuzunza kwambiri abale ake a Khristu amene adakali padziko lapansi pano. Yohane analemba kuti: “Tsopano chinjoka chitaona kuti achigwetsera kudziko lapansi, chinazunza mkazi amene anabereka mwana wamwamuna uja. Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu kuti aulukire kuchipululu, kumalo ake aja. Kumeneko n’kumene akudyetsedwa kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi, kutali ndi njoka ija.”—Chivumbulutso 12:13, 14.

  • Ufumu wa Mulungu Wabadwa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
    • 24. Kodi Ophunzira Baibulo anakumana ndi zinthu zotani, zimene zinali zofanana ndi kupulumutsidwa kwa Aisiraeli kuchokera ku Iguputo?

      24 Pa nthawi imene nkhondo yoyamba yapadziko lonse inkamenyedwa, abale ake a Yesu anapitiriza kugwira mokhulupirika ntchito yawo yolalikira monga mmene akanathera. Iwo anachita zimenezi ngakhale kuti Satana ndi anthu ake ankhanza ankawazunza koopsa. Kenako ntchito yolalikira, yomwe Ophunzira Baibulo ankagwira, inatsala pang’ono kuimiratu. (Chivumbulutso 11:7-10) Zitatero, iwo anakumana ndi zinthu zofanana ndi zimene zinachitikira Aisiraeli ali ku Iguputo, amenenso ankazunzidwa kwambiri. Pa nthawiyo, Yehova anapititsa Aisiraeliwo mwamsangamsanga kuchipululu cha Sinai komwe kunali kotetezeka, ndipo anakhala ngati anawakweza pamapiko a ziwombankhanga. (Ekisodo 19:1-4) Mofanana ndi zimenezi, Mboni za Yehova zitazunzidwa koopsa mu 1918 mpaka mu 1919, Yehova anapulumutsa mbonizo, zomwe zinkaimira mkazi wake. Kenako anaziika pamalo auzimu amene anali otetezeka ngati mmene chipululu chija chinalili kwa Aisiraeli. Zimenezi zinali ngati yankho la mapemphero awo.—Yerekezerani ndi Salimo 55:6-9.

      25. (a) Kodi Yehova anapanga mtundu wotani mu 1919, mofanana ndi mmene anapangira Aisiraeli kukhala mtundu m’chipululu muja? (b) Kodi ndani amene ali mumtundu umenewu, ndipo Mulungu anawabweretsa m’malo otani?

      25 M’chipululu muja, Yehova anapanga Aisiraeli kukhala mtundu waukulu. Iye ankawasamalira mwauzimu ndiponso ankawapatsa zofunikira pa moyo wawo. Mofanana ndi zimenezi, kuyambira mu 1919, Yehova anapanga mbewu ya mkazi uja kukhala mtundu wauzimu. Tisasokoneze mtundu umenewu ndi Ufumu wa Mesiya, umene wakhala ukulamulira kuchokera kumwamba kuyambira mu 1914. Koma mtundu watsopanowu wapangidwa ndi mboni zodzozedwa zomwe zidakali padziko lapansi pano. Mulungu anabweretsa mbonizi m’malo auzimu aulemerero kuyambira mu 1919. Kuyambira nthawi imeneyi, iwo anayamba kupatsidwa “chakudya chokwanira pa nthawi yake,” ndipo zimenezi zinawapatsa mphamvu kuti athe kugwira ntchito imene ankafunikira kugwira.—Luka 12:42; Yesaya 66:8.

      26. (a) Kodi nthawi imene yatchulidwa pa Chivumbulutso 12:6 ndi 14 inali yaitali bwanji? (b) Kodi cholinga cha nthawi zitatu ndi hafu chinali chiyani? Nanga nthawiyi inayamba liti, ndipo inatha liti?

      26 Kodi nthawi imene mbewu ya mkazi wa Mulungu ija inakhala ikupezanso mphamvu inali yaitali bwanji? Lemba la Chivumbulutso 12:6 limati inali yokwana masiku 1,260. Ndipo lemba la Chivumbulutso 12:14 limati inali yokwana nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi, kutanthauza nthawi zitatu ndi hafu. Mavesi awiri onsewa akunena za nthawi imodzimodzi, yokwana zaka zitatu ndi hafu. Kumpoto kwa dziko lapansi, nthawi imeneyi inayamba cha mu March m’chaka cha 1919 n’kudzathera cha mu September m’chaka cha 1922. Imeneyi inali nthawi imene Akhristu odzozedwa anatsitsimulidwa mwauzimu n’kupezanso mphamvu, ndipo anakonzanso bwino gulu lawo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena