Choonadi Ponena za Angelo
Kukhala wodziŵana ndi munthu wina kaŵirikaŵiri kumaphatikizapo kudziŵa kanthu kena ponena za banja la munthuyo. Zili chimodzimodzinso ndi kudziŵa Yehova Mulungu. Pali zambiri zimene zimaloŵetsedwamo kuposa kungodziŵa dzina lake. Tiyeneranso kudziŵa kanthu kena ponena za “banja” lake lakumwamba. (Yerekezerani ndi Aefeso 3:14, 15.) Baibulo limatcha angelo kukhala “ana” a Mulungu. (Yobu 1:6) Polingalira za mbali yawo yofunika m’Baibulo, tiyenera kufuna kudziŵa zambiri ponena za iwo kuti tidziŵe bwino malo awo m’chifuno cha Mulungu.
CHITAGANYA china cha anthu chikubuka. Si kokha kuti anthu ambiri akunena kuti amakhulupirira angelo; chiŵerengero chomakula chikunena kuti chinakhudzidwa nawo mwa njira ina yake. Pamene Aamereka 500 anafunsidwa kuti, “Kodi inu mwininu munayamba mwadziŵapo za kukhalapo kwa mngelo m’moyo wanu?” pafupifupi chigawo chimodzi mwa zitatu chinavomera kuti inde. Chodabwitsanso ndicho chiŵerengero cha achichepere amene amanena kuti amakhulupirira angelo—malinga ndi kufufuza kwina kwa ku United States, panali 76 peresenti! Mwachionekere, anthu ali ndi chidwi ndi angelo. Koma kodi ndimotani mmene kuganiza kwamakonoku ponena za angelo kukuonedwera ndi choonadi cha Baibulo?
Mbali Yodzibisa ya Satana
Pamene tilankhula za angelo, sitiyenera kunyalanyaza za angelo oipa, zolengedwa zakumwamba zimene Baibulo limati zinapandukira Mulungu. Wodziŵika kopambana ndiye Satana. Buku lina lotchuka lotchedwa Ask Your Angels limanena kuti Satana wangokhala “mbali ina ya Mulungu” amene amathandiza anthu kulimbitsa ‘nkhongono zawo zauzimu’ mwa kuwayesa nthaŵi zonse. Ngakhale kuti pali “zolinga zachikondi” za Satana, akutero olemba bukulo, kwa zaka mazana ambiri iyeyo wagwirizanitsidwa molakwika ndi kuipa. Akuwonjezera kuti Satana ndi Yesu, “pamene kuli kwakuti ali osiyana wina ndi mnzake, tingati iwo ali a mbali imodzi, mbali yofunika ya chinthu chimodzimodzicho.” Mawu ameneŵa ndi odabwitsa, koma kodi Baibulo limanenanji?
Baibulo limafotokoza bwino kuti Satana sali “mbali ina ya Mulungu” koma ndiye mdani wa Mulungu. (Luka 10:18, 19; Aroma 16:20) Amanyoza ulamuliro wa Yehova, ndipo zolinga zake kwa anthu sizili “zachikondi” konse. Mwankhanza amasonyeza mkwiyo wake pa atumiki a Mulungu a pa dziko lapansi. Amawaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku!a (Chivumbulutso 12:10, 12, 15-17) Satana amalingalira zowaipitsa mwa mtundu uliwonse. Kuzunza kwake kopanda chifundo Yobu munthu wolungamayo kunasonyeza mkhalidwe wake wankhanza pa kuvutika kwa munthu.—Yobu 1:13-19; 2:7, 8.
Posakhala “a mbali imodzi,” Satana ndi Yesu ngotsutsana kwambiri. Eya, mosakayikira Satana ndiye amene anasonkhezera Herode kupereka lamulo la kupha tiana tonse—zonsezo poyesayesa kupha kamwanako Yesu! (Mateyu 2:16-18) Ndipo kuukira kosalekeza kwa Satana kunapitiriza kufikira pa imfa ya Yesu. (Luka 4:1-13; Yohane 13:27) Motero, m’malo mwa kukhala “mbali yofunika ya chinthu chimodzimodzicho,” Yesu ndi Satana ngosiyana kotheratu. Ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti iwo amadana kwambiri. (Genesis 3:15) Moyenerera, Yesu woukitsidwayo ndiye amene adzawononga Satana m’nthaŵi ya Mulungu yokwanira.—Chivumbulutso 1:18; 20:1, 10.
Mapemphero Omka kwa Yani?
Ochirikiza magulu onena za angelo ena amalangiza za kusinkhasinkha ndi njira zina kuti munthu alankhulane ndi angelo. “Pempho loona mtima la kufuna kulankhulana ndi chiŵalo chilichonse cha banja lakumwamba silinganyalanyazidwe,” likutero buku lina. “Pemphani ndipo mudzayankhidwa.” Mikaeli, Gabrieli, Urieli, ndi Rafaeli ndiwo angelo ena amene bukulo likulangiza kuwapempha kulankhulana nawo.b
Komabe, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kwa Mulungu, osati kwa angelo. (Mateyu 6:9, 10) Mofananamo, Paulo analemba kuti: “M’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6) Chotero, m’mapemphero awo, Akristu samafikira m’pemphero wina aliyense kusiyapo Yehova, ndipo amatero m’dzina la Yesu Kristu.c—Yohane 14:6, 13, 14.
Angelo Opanda Chipembedzo?
Malinga ndi kunena kwa Eileen Elias Freeman, amene amayang’anira AngelWatch Network, “angelo ali okwezeka pa chipembedzo chilichonse, pa nzeru iliyonse, pa chikhulupiriro chilichonse. Kwenikweni, angelo alibe chipembedzo.”
Komabe, Baibulo, limasonyeza bwino kuti angelo okhulupirika ali ndi chipembedzo; amalambira Mulungu woona, Yehova, amene salekerera kupikisana ndi milungu ina. (Deuteronomo 5:6, 7; Chivumbulutso 7:11) Motero, mngelo wina anadzisonyeza kwa mtumwi Yohane kukhala ‘kapolo mnzawo’ wa awo amene amamvera malamulo a Mulungu. (Chivumbulutso 19:10) Palibe malo alionse m’Baibulo pamene timaŵerenga za angelo okhulupirika omachirikiza mtundu winanso wa kulambira. Iwo amalambira Yehova yekha.—Eksodo 20:4, 5.
“Atate Wake wa Bodza”
Kukumana ndi angelo kochuluka konenedwako kumaloŵetsamo kulankhulana ndi mizimu ya akufa. “Ndinkalingalira kuti amalume anali atapeza njira yondifikira ndi kundidziŵitsa kuti tsopano anali m’chimwemwe,” akutero mkazi wina wotchedwa Elise atalandira chimene analingalira kuti chinali chizindikiro. Mofananamo Terri akukumbukira za bwenzi lina lokondedwa limene linafa. “Sabata limodzi litapita pambuyo pa maliro,” iye akutero, “anandifikira mu mkhalidwe umene ndinaganiza kuti unali atulo. Anandiuza kuti ndisalire za kutisiya kwake, chifukwa chakuti anali m’chimwemwe ndi pa mtendere.”
Koma Baibulo limanena kuti akufa “sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Limanenanso kuti pamene munthu afa, “tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:4) Komabe, Satana, ndiye “atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Iye ndiye amene anayambitsa chinyengo chakuti moyo wa munthu sumafa pa imfa. (Yerekezerani ndi Ezekieli 18:4.) Lerolino anthu ambiri amakhulupirira zimenezi, zimene zimakhutiritsa cholinga cha Satana, pakuti zimathetsa kufunika kwa kukhulupirira chiukiriro—chiphunzitso chachikulu cha Chikristu. (Yohane 5:28, 29) Chotero, kupempha thandizo ku mizimu ya akufa kapena kulandira mauthenga kwenikweniko ku iyo kulinso mbali ina ya gulu lonena za angelo limene lili losavomerezedwa ndi Mulungu.
Kodi Ndiko Kufikira Angelo Kapena Ziŵanda?
Mbali yokulira ya gulu lokhulupirira za angelo lamakono imaloŵanso m’kupenduza. Talingalirani za chokumana nacho cha Marcia. “Kuyambira September mpaka December wa 1986,” iye akutero, “ndinayamba kulandira mauthenga ‘achilendo.’ Ndinkaona mizukwa ndipo ndinkalota maloto a ‘zinthu zakale’ achilendo. Ndinalankhulana ndi mabwenzi amene anafa kale ndipo ndinali ndi zokumana nazo zina zambiri zachilendo zimene zinandidziŵitsa zinthu za anthu ena amene ndinakumana nawo koyamba. Ndinapatsidwanso mphatso ya kulemba mabuku popanda kuganiza ndi kupereka mauthenga ochokera kwa anthu a mizimu. Ena a iwo amene sindinakumanepo nawo m’moyo wawo wa pa dziko lapansi, ankapereka mauthenga kwa ena kupyolera mwa ine.”
Kugwiritsiridwa ntchito kwa ula monga njira ya “kulankhulana” ndi angelo nkofala. Buku lina limalimbikitsa oŵerenga ake poyera kugwiritsira ntchito miyala ya matsenga, makhadi a tarot, makobili a I Ching, kuŵerenga mizera ya m’zikhatho, ndi kupenda nyenyezi. “Lolani mtima wanu kukutsogolerani kwa wonenerera wolondola,” alembi a bukulo akulemba motero, “ndipo khulupirirani kuti mngelo adzakumana nanu kumeneko.”
Komabe, malinga ndi Baibulo, aliyense amene “adzakumana nanu kumeneko” ndithudi sali mmodzi wa angelo a Mulungu. Chifukwa? Chifukwa chakuti mwachindunji Mulungu amatsutsa kuchita ula, ndipo olambira oona—kumwamba ndi pa dziko lapansi—amakupeŵa kotheratu. Eetu, mu Israyeli kuchita ula kunali kodzetsa chilango cha imfa! “Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye,” chinatero Chilamulocho.—Deuteronomo 13:1-5; 18:10-12.
“Mngelo wa Kuunika”
Sikuyenera kutidabwitsa kudziŵa kuti Mdyerekezi angachititse ula kuonekera ngati wopindulitsa, kapena ngati waungelo. Baibulo limanena kuti Satana “adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.” (2 Akorinto 11:14) Iye angathedi kusintha zinthu zina ndi kuzipangitsa kuchitika, akumanyenga oona kuti ayambe kuganiza kuti chinthucho nchochokera kwa Mulungu. (Yerekezerani ndi Mateyu 7:21-23; 2 Atesalonika 2:9-12.) Koma ntchito zonse za Satana—mulimonse mmene zingakhalire ngati zabwino kapena zoipa—zimakwaniritsa cholinga chake chimodzi kapena ziŵiri: kuchititsa anthu kupandukira Yehova kapena kungoti achititse khungu maganizo awo kotero kuti ‘chiwalitsiro cha uthenga wabwino wa Kristu chisawawalire.’ (2 Akorinto 4:3, 4) Njira yotsirizirayi ya chinyengo kaŵirikaŵiri ndiyo imene ili yamphamvu kwambiri.
Lingalirani za nkhani ya m’Baibulo ya namwali wina wantchito m’zaka za zana loyamba. Kunenera kwake kunabweretsa phindu lambiri kwa ambuye ake. Iye anatsata ophunzira masiku ambiri, akumati: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.” Mawu akewo anali oona. Komabe nkhaniyo imatiuza kuti iye anagwidwa ndi mzimu, osati ndi mngelo, koma ndi “mzimu wambwebwe.” Potsirizira pake, Paulo “[a]nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m’dzina la Yesu Kristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthaŵi yomweyo.”—Machitidwe 16:16-18.
Kodi nchifukwa ninji Paulo anathamangitsa mzimu umenewu? Ndi iko komwe, unapindula ndalama zambiri kwa ambuye a namwali wogwidwa nawowo. Pokhala ndi mphamvu zachilendo, namwali wantchitoyo mwina anauza alimi za nthaŵi ya kubzala mbewu, anamwali za nthaŵi yokwatiwa, ndi okumba miyala kumene angakafunefune golidi. Eya, mzimu umenewu unasonkhezeradi namwaliyo kunena mawu ena oona, akumatamanda poyera ophunzirawo!
Chikhalirechobe, umenewu unali “mzimu wambwebwe.” Popeza unali wotero, sunayenere kulengeza za Yehova ndi makonzedwe ake a chipulumutso. Mawu ake oyamikirawo, mwinamwake onenedwa kuti uchititse chivomerezo pa zonenera za namwaliyo, anacheukitsa maganizo a openyerera pa otsatira oona a Kristu. Pokhala ndi chifukwa chabwino, Paulo anachenjeza Akorinto kuti: “Simungathe kulandirako ku gome la [Yehova, NW], ndi ku gome la ziŵanda.” (1 Akorinto 10:21) Mposadabwitsa kuti m’zaka za zana loyamba Akristu anawononga mabuku awo onse amene anali amatsenga.—Machitidwe 19:19.
‘Mngelo wa Kuuluka Pakati pa Mlengalenga’
Monga momwe taonera, Baibulo limasonyeza zochuluka ponena za magulu okhulupirira za angelo amakono kukhala ogwirizana kwambiri ndi Mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi. Kodi zimenezi zimatanthauza kuti angelo oyera samaphatikizidwa m’zochitika za anthu? Kutalitali, iwo tsopano lino akuchita ntchito yamphamvu pa dziko lapansi. Kodi iyo njotani? Kuti tiyankhe, tiyenera kuŵerenga buku la Baibulo la Chivumbulutso. Angelo amatchulidwa m’buku limeneli nthaŵi zambiri kuposa m’buku lina lililonse la Baibulo.
Pa Chivumbulutso 14:6, 7, timaŵerenga za cholembedwa cha mtumwi Yohane cha masomphenya a ulosi umene analandira kuti: “Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo uthenga wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala pa dziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu; ndi kunena ndi mawu aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.”
Lemba limeneli limasonyeza za ntchito yofunika koposa ya angelo lerolino. Iwo ali mu utumiki wofunika koposa—uja wa kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Kunali ponena za ntchito imeneyi kuti Yesu analonjeza otsatira ake kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:18-20) Kodi Yesu ali nawo pamodzi motani otsatira ake? Njira imodzi ili mwa kuwapatsa thandizo la angelo kotero kuti ntchito yaikulu kwambiri imeneyi itsirizidwe.
Mboni za Yehova zimathera maola oposa mamiliyoni zikwi zambiri pachaka zikumalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Pamene zichita ntchito imeneyi, zimaona umboni wa chitsogozo chaungelo. Mu utumiki wawo wa kukhomo ndi khomo, kaŵirikaŵiri zachitika kuti zafikira anthu amene anali kupempherera munthu wina kuti afike kudzawathandiza kumvetsa zifuno za Mulungu. Chitsogozo chaungelo, limodzi ndi kuyamba kuchitapo kanthu kwa Mbonizo, zachititsa anthu zikwi mazana ambiri kudziŵa Yehova chaka chilichonse!
Kodi mukumvetsera mngelo amene akuuluka pakati pa mlengalenga? Bwanji osayesa kukambitsirana zambiri ponena za uthenga wa angelo pamene Mboni za Yehova zifika?
[Mawu a M’munsi]
a Mawuwo “Satana” ndi “Mdyerekezi” amatanthauza kuti “wotsutsa” ndi “woneneza.”
b Pamene kuli kwakuti Mikaeli ndi Gabrieli amatchulidwa m’Baibulo, maina akuti Rafaeli ndi Urieli amapezeka m’mabuku a Apocryphy, amene sali mbali yoona ya Baibulo.
c Onani kuti pemphero limapita kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu, osati kwa Yesuyo. Pemphero limaperekedwa m’dzina la Yesu chifukwa chakuti mwazi wake wotsanulidwa unatsegula njira yofikira Mulungu.—Aefeso 2:13-19; 3:12.
[Bokosi patsamba 8]
KODI ANGELO NDI AYANI?
MOSIYANA ndi zimene ambiri amakhulupirira, angelo saali mizimu ya anthu amene anafa. Baibulo limafotokoza bwino kuti akufa “sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Nangano, kodi nkuti kumene angelo anachokera? Baibulo limasonyeza kuti aliyense analengedwa payekha ndi Mulungu dziko lapansi lisanakhaleko. (Yobu 38:4-7) Banja la Mulungu lakumwamba lingafikire ku mamiliyoni mazana ambiri kukula kwake, kapenanso mamiliyoni zikwi kapena koposa pamenepo! Angelo ena anagwirizana ndi Satana m’chipanduko chake.—Danieli 7:10; Chivumbulutso 5:11;12:7-9.
Popeza kuti Yehova ndi Mulungu wadongosolo, nkosadabwitsa kuti banja lake lalikulukululo la angelo nladongosolo.—1 Akorinto 14:33, NW.
• Mngelo wokhala ndi malo aakulu koposa, ponse paŵiri mu mphamvu ndi mu ulamuliro, ndiye mngelo wamkulu, Yesu Kristu, wotchedwanso Mikaeli. (1 Atesalonika 4:16; Yuda 9) Pansi pa ulamuliro wake pali aserafi, akerubi, ndi angelo.
• Aserafi amatumikira ku mpando wachifumu wa Mulungu. Mwachionekere ntchito yawo imaphatikizapo kulengeza za chiyero cha Mulungu ndi kusunga anthu ake ali oyera.—Yesaya 6:1-3, 6, 7.
• Akerubi amakhalanso pamaso pa Yehova. Pokhala onyamula kapena oyendetsa mpando wachifumu wa Mulungu, amachirikiza ulemerero wa Yehova.—Salmo 80:1; 99:1; Ezekieli 10:1, 2.
• Angelo (kutanthauza kuti “amithenga”) ndi nthumwi ndi oimira Yehova. Amachita chifuniro cha Mulungu, kaya chikhale cha kupulumutsa anthu a Mulungu kapena cha kuwononga oipa.—Genesis 19:1-26.
[Zithunzi patsamba 7]
Kodi mukumvetsera mngelo amene akuuluka pakati pa mlengalenga?