Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mbiri Yabwino Kaamba ka Mtundu Wonse wa Anthu!
    Nsanja ya Olonda—1990 | January 1
    • ‘NDIPO ndinawona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nayo Mbiri Yabwino yosatha, ailalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu onse.’ (Chibvumbulutso 14:6) Ndi mawu amenewo, mtumwi Yohane wokalambayo analongosola masomphenya ouziridwa aulosi, masomphenya amene akukwaniritsidwa m’tsiku lathu. Ndi mpumulo wotani nanga kudziŵa kuti pali mbiri yabwino mu mbadwo uno wa upandu, kuipitsa, uchigaŵenga, nkhondo, ndi kufalikira komakwerakwera ndi kusatsimikizirika kwa zachuma! Koma kodi ndi mbiri yotani imene ingakhale yabwino koposa kotero kuti ikufunikira mngelo kuilengeza? Kodi ndi mbiri yotani imene ingakhale yosangalatsa mokwanira kotero kuti iyenerere kulalikidwa ku mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu onse?

  • Mbiri Yabwino Kaamba ka Mtundu Wonse wa Anthu!
    Nsanja ya Olonda—1990 | January 1
    • Kubwerera mu zaka za zana loyamba, Yesu anakwaniritsa zifuno zambiri za Mulungu kaamba ka iye, koma panthaŵiyo anali asadaikidwe kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Monga mmene magazine ano asonyezera kaŵirikaŵiri, zimenezo sizinachitike kufikira 1914. Monga mmene kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewo kukusonyezera mowonekera, m’chaka chimenecho Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba. (Chibvumbulutso 12:10, 12) Ngakhale kuti kunali mbiri yoipa kwambiri mu 1914​—kuwulika kwa Nkhondo ya Dziko ya I​—kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu kunali mbiri yabwino koposa. Chimenecho ndicho chifukwa chake Yesu analosera kaamba ka tsiku lathu kuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse.”​—Mateyu 24:14, NW.

      Kodi ulosi wa Yesu wakwaniritsidwa? Yankho ndi lakuti inde! Ndipo masomphenya aulosi a Yohane akukwaniritsidwanso. Zowonadi, sitingamuwone mngelo wosawoneka amene Yohane anawona. Koma Mboni za Yehova zakhala zikuwoneka kwambiri pamene zikulalikira mbiri yabwino ya mngeloyo “kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” M’maiko ndi zisumbu za m’nyanja 212, mawu awo amvedwa. Ndipo makamu akuvomereza. Zokumana nazo za ena a ameneŵa zidzasonyeza mmene mbiri imeneyi yonena za Ufumu wa Mulungu iriri yabwino.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena