Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 12/15 tsamba 19-24
  • “Opani Mulungu Ndipo Mpatseni Ulemerero”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Opani Mulungu Ndipo Mpatseni Ulemerero”
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zirombo Zamwano
  • Opani Mulungu​—Chifukwa Ninji?
  • Kugwa kwa Babulo Wamkulu
  • Chigololo cha Babulo Chivumbulidwa
  • “Yehova . . . Wolungama ndi Wowona”
  • Kulemekeza Mulungu Kosatha
  • Kulimbana ndi Zilombo Ziwiri Zoopsa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Kupha Babulo Wamkulu
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Zimene Zili M’buku la Chivumbulutso Zimakhudzanso Adani a Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 12/15 tsamba 19-24

“Opani Mulungu Ndipo Mpatseni Ulemerero”

“Opani Mulungu [ndipo] mpatseni ulemerero.”​—CHIBVUMBULUTSO 14:7.

1. Ndani amene tiyenera kuwopa, ndipo nchiyani chimene sitiyenera kuwopa?

NDANI AMENE TIYENERA KUWOPA? Ndithudi osati chinjoka chofiira, Satana, ndi unyinji wa ziwanda zake! Kristu Yesu anaponya awa kuchoka kumwamba kutsatira kubadwa kwa Ufumu mu 1914. Koma masomphenya a Apocalypse chotsatira avumbula gulu limene Satana akugwiritsira ntchito pano pa dziko lapansi m’kuyesera kwake komalizira kwa kuzimiriritsa zifuno za Mulungu. Zotchuka mu kuchitira chithunzi kumeneko ziri zirombo zaukali ziŵiri ndi mkazi wachigololo woledzera​—Babulo Wamkulu. Kodi tiyenera kuwopa izi? Kutalitali! M’malomwake, tiyenra kuwopa Yehova ndi Kristu wake, amene Ufumu wake tsopano wabweretsa dziko lowonongeka la Satana ku chiŵeruzo chake chomalizira.​—Miyambo 1:7; Mateyu 10:28; Chibvumbulutso 12:9-12.

Zirombo Zamwano

2. Nchirombo chotani chimene chikubwera mowonekera m’masomphenya a chisanu ndi chitatu, ndipo icho chikuimira chiyani?

2 Pamene masomphenya a chisanu ndi chitatu a Chibvumbulutso amasuka, chirombo chituluka kuchokera m’nyanja yosakhazikika ya mtundu wa anthu. Chiri ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi ndi nduwira za chifumu khumi, kusonyeza ulamuliro woyenera woperekedwa pa icho ndi Satana. Icho chichitira mwano Yehova, kuvulaza atumiki Ake monga mmene angachitire nyalugwe, chimbalangondo, kapena mkango; koma ulamuliro wake uli wa kanthaŵi, ukumachotsedwa kuchokera kwa chinjoka, Satana, amene chifanana naye kotheratu. Mneneri Danieli kumayambiriroko anali atalongosola maboma a ndale zadziko za pa dziko lapansi monga zirombo, ndipo maboma iwo eniwo kaŵirikaŵiri asankha zolengedwa za m’nkhalango monga ziphiphiritso zawo za utundu, monga ngati mkango wa Britain ndi chiwombankhanga cha America. (Danieli 8:5-8, 20-22) Tsopano, ngakhale ndi tero, tikuwona chirombo chokhala ndi zambiri, kukupatira mphamvu zonse za ndale zadziko za mbiri ya Baibulo zomwe kaŵirikaŵiri zinatsendereza atumiki owona a Mulungu pa dziko lapansi. “Mitu” yowonekera pakati pa izi yakhala Igupto, Asuri, Babulo, Medi-Perisiya, Grisi, Roma, ndipo pomalizira Mphamvu ya dziko ya Mbali Ziŵiri ya Anglo-America.​—Chibvumbulutso 13:1, 2; 12:3, 7-9.

3. (a) Ndimotani mmene umodzi wa mitu ya chirombo unalandirira “kulasidwa kwa lupanga”? (b) Ndimotani mmene chirombo cha nyanga ziŵiri chikutengera chitsogozo m’kupanga chifano kwa chirombo choyamba? (c) Nchiyani chomwe chiri dzina la chirombo choyamba ndi kupatulika kwa dzinalo?

3 Mkati mwa nkhondo ya dziko ya 1914-18, Great Britain, monga mphamvu ya dziko yachisanu ndi chiŵiri, inalandira “kulasidwa ndi lupanga” komwe kukanatsimikizira kukhala kwakupha. Koma United States of America inabwera ku chipulumutso chake. Chiyambire pamenepo, America ndi Britain agwirizana monga mphamvu ya dziko ya mbali ziŵiri, imene Yohane akupitirizabe kulongosola monga chirombo chokhala ndi nyanga ziŵiri, chobwera kuchokera ku chitaganya chokhazikitsidwa cha anthu, “dziko lapansi.” Chirombo cha nyanga ziŵiri chimenechi chikutenga chitsogozo m’kupanga chifano ku chirombo choyamba ndi kuika moyo mwa icho, kuimira mmene Mphamvu ya Dziko ya Anglo-American inakhalira wochirikiza wamkulu ndi wopatsa moyo ponse paŵiri ku Chigwirizano cha Mitundu ndi cholowa m’malo chake, Mitundu Yogwirizana. Chirombo choyamba chiri ndi dzina la chiŵerengero, 666. Chisanu ndi chimodzi chiri nambala yopanda ungwiro​—yoperewera pa chisanu ndi chiŵiri changwiro m’kawonedwe ka Baibulo​—kotero kuti chisanu ndi chimodzi kukwezedwa ku mlingo wachitatu kumasonyeza kupanda ungwiro kwa tsoka kwa olamulira a umunthu a lerolino. Ngakhale kuti Mboni za Yehova zimalemekeza boma ndipo ziri za chitsanzo m’kumvera malamulo a dziko mu limene zimakhala, izo molimba mtima zimakana kulambira “chirombo” kapena chifano chake.​—Chibvumbulutso 13:3-18; Aroma 13:1-7.

Opani Mulungu​—Chifukwa Ninji?

4. (a) Ndani omwe akuwonedwa ali chiimirire pa Phiri la Ziyoni wa kumwamba, ndipo ndani amene achitiridwa chithunzi ndi akulu 24 pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu? (b) Nkuti kumene kuli kusiyana pakati pa “nyimbo yatsopano” yoyimbidwa ndi odzozedwa ndi “nyimbo yatsopano” yoyimbidwa ndi khamu lalikulu?

4 Pa nthaŵi ino, zakwanira zirombo zimenezo! M’kusiyana kodzetsa mpumulo, masomphenya a chisanu ndi chinayi akulunjikitsa chidwi pa Mwanawankhosa. Iye waima pa Phiri la Ziyoni, ndi 144,000 amene akuwagula monga zipatso zoyambirira kuchokera pakati pa mtundu wa anthu. Ngakhale kuti ena a amenewa adakatumikirabe pa dziko lapansi, m’lingaliro lauzimu a 144,000 onse “ayandikira ku Phiri la Ziyoni ndi . . . Yerusalemu wa kumwamba.” (Ahebri 12:22) Moyenerera, akulu 24 akuwonedwanso pano pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, popeza kuti iwo amaimira gulu limodzimodzilo lodzozedwa kuchokera ku kawonedwe kosiyana​—monga owukitsidwa kale ndi kuikidwa monga mafumu ndi ansembe. A 144,000 amenewo akuyimba “nyimbo yatsopano.” Iyo ikuchokera ku chokumana nacho chawo chapadera m’kukhala ogulidwa kuchokera ku dziko lapansi kukhala olowa Ufumu. Khamu lalikulu nalonso “likuyimba kwa Yehova nyimbo yatsopano,” koma ichi chikusiyana m’chakuti iwo akuyimba m’chiyembekezo cha kupeza moyo wosatha m’mabwalo a dziko lapansi a Ufumuwo.​—Chibvumbulutso 7:9; 14:1-5; Salmo 96:1-10; Mateyu 25:31-34.

5. (a) Ndimbiri yotani imene ikulengezedwa ndi mngelo wowuluka pakati pa mlengalenga, ndipo nchifukwa ninji iyo iri yosatha? (b) Ndi lamulo lotani limene mngeloyo akupereka m’mawu okwezeka, ndipo nchifukwa ninji liri loyenerera chotero?

5 Masomphenyawo tsopano akufutukuka. Yohane akuwona mngelo wina akuwuluka pakati pa mlengalenga. Ndipo ndi uthenga wabwino wosatha wotani nanga umene ali nawo wa kulalikira! Iri mbiri yabwino yosatha, popeza kuti imatanthauza moyo wosatha kwa awo ochokera mu mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu omwe amamvera Mulungu mu ora limeneli la chiweruzo chake. Mosiyana ndi zirombo zowopsya zimene Yohane wangozilongosola kumene, nchifukwa ninji Mulungu wozizwitsa ameneyu sayenera kulambiridwa, inde, kukondedwa? Iye ali Uyo amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Iye ali Magwero a chirichonse chomwe chiripo, chamoyo ndi chopanda moyo. Pali chifukwa champhamvu, chotero, kaamba ka mngeloyo kulamula m’mawu okwezeka: “OPANI MULUNGU NDIPO MPATSENI ULEMERERO”! Mawu a mngelowo akumveka kuzungulira pa dziko lonse lapansi, ndipo Mboni za Yehova zikumveketsa chiitano chake chodzutsa maganizo kwa mtundu wonse wa anthu m’zinenero 200. ​—Chibvumbulutso 14:6, 7; Yesaya 45:11, 12, 18.

Kugwa kwa Babulo Wamkulu

6. Ndi mbiri yozizwitsa yotani imene mngelo wina akulengeza?

6 Mngelo wina akuwonekera. Wozizwitsa ndithudi uli uthenga umene iye akulengeza: “Wagwa! Wagwa Babulo Wamkulu, umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake!” (Chibvumbulutso 14:8) Ndani amene ali Babulo Wamkulu ameneyo, chakuti angafikire pa kunyenga mitundu ndi kuiledzeretsa iyo?

7. Kodi Babulo Wamkulu nchiyani, ndipo ndimotani mmene anayambira?

7 Babulo wakale anali maziko enieni a chipembedzo chonyenga, chomwe chinafutukuka ku dziko lonse lapansi kukhala ulamuliro wa dziko lonse lapansi wa uchiwanda, woikidwa chizindikiro moyenerera kukhala “Babulo Wamkulu.” M’kupita kwa nthaŵi, Roma anakhala wotchuka mu ufumu wa chipembedzo umenewo, popeza kuti panali pansi pa Roma pamene Chikristu cha mpatuko chinayambika. Roma akupitirizabe kukhala malo apakati a dziko lonse kaamba ka chipembedzo cha Chibabulo. Ichi chinawonekera bwino mu 1986 pamene atsogoleri a zipembedzo a dziko lonse anayankha chiitano cha papa wa ku Roma mwa kusonkhana limodzi naye pa Assisi, pafupi ndi Roma, kupempherera chaka cha Mtendere wa Mitundu Yonse cholengezedwa ndi Mitundu Yogwirizana.

8. (a) Ndimotani mmene Babulo Wamkulu anakumanizirana ndi kugwa kwakukulu, ndipo ndi kuyambira liti pamene ichi chakhala chowonekera? (b) Nchiyani chimene chikusonyeza kuti mapemphero a atsogoleri a chipembedzo kaamba ka mtendere amapita osayankhidwa?

8 Ngakhale kuli tero, Babulo Wamkulu wavutika ndi kugwa kwakukulu! Chiyambire 1919 ichi chakhala chowonekera m’chichirikizo chomacheperachepera kaamba ka chipembedzo chonyenga dziko lonse. Chikomyunizimu chosakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu tsopano chikulamulira magawo okulira a dziko lapansi. Achichepere a lerolino akuphunzitsidwa chisinthiko, chomwe chimatsutsana ndi Mawu a Mulungu. Mu Europe wa Chiprotestanti anthu ochepera amapezeka pa tchalitchi, ndipo papa woyendayendayo akulimbikira kusungirira pamodzi ufumu wa Chikatolika. Mapemphero ku unyinji wa milungu ya zipembedzo zadziko mwachidziŵikire amangopita osayankhidwa. Ruth L. Sivard anasimba kuti: “Nkhondo makumi aŵiri mphamvu ziŵiri zinachitika mu 1987, nkhondo zochulukira kuposa chaka china chirichonse chapitacho m’mbiri yolembedwa. Unyinji wa chiŵerengero chonse cha imfa mu nkhondo zimenezi kufikira pa nthaŵiyo chiri chifupifupi 2,200,000​—ndipo chikukwera mofulumira.’a Ndi mosapindulitsa chotani nanga mmene msonkhano wa pemphero wa pa Assisi unatsimikizira kukhala! Ndipo komabe papa anaika chizindikiro chikumbukiro cha 1987 cha kusonkhana kumeneko mwa kutulutsa medulo yokhala ndi chifanefane chake pa mbali imodzi ndi chizindikiro cha msonkhano wa pempherowo ku mbali ina. Iwo apitiriza kunena “kuti, ‘Mtendere! Mtendere!’ koma palibe mtendere.”​—Yeremiya 6:14.

Chigololo cha Babulo Chivumbulidwa

9. Atsogoleri a chipembedzo a Babulo Wamkulu akhala owuma mutu kaamba ka njira za chisembwere zotani?

9 Chibvumbulutso 14:8 chimasonyeza kuti Babulo Wamkulu ali wa chigololo. Atsogoleri ake a chipembedzo akhala owuma mutu kaamba ka njira zawo za chisembwere. Alengezi a pa TV adyerera nkhosa zawo m’mazana a mamiliyoni a madola, pamene kuli kwakuti pa nthaŵi imodzimodziyo anali kuchita mkhalidwe wa chisembwere wodzetsa manyazi. Unsembe wa Chikatolika ulinso wokaikirika koposa, monga mmene chasonyezedwera ndi ripoti lotsatirali mu The Beacon Journal ya ku Philadelphia, Pennsylvania, January 3, 1988: “Mazana a ana oipsyidwa ndi ansembe a Chikatolika mu United States mkati mwa zaka zisanu zapitazi avutika ndi kuwawidwa maganizo kowopsya, akutero makolo, akatswiri a za malingaliro, nduna za polisi ndi maloya okhudzidwa m’nkhanizo.” Mkhalidwe wa chisembwere cha kugonana wadetsa mbiri yabwino ya atsogoleri a chipembedzo a Babulo Wamkulu.

10. (a) Pa Chibvumbulutso 18:3, nchiyani chimene chikusonyezedwa ndi “chigololo” cha Babulo Wamkulu? (b) Monga mmene chadziŵitsidwira pa Chibvumbulutso 18:24, nchifukwa ninji atsogoleri a chipembedzo a Babulo Wamkulu akugawanamo mu liwongo lalikulu la mwazi?

10 “Vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake,” ngakhale ndi tero, ali ndi chilozero chachindunji ku kupalana ubwenzi kwa chipembedzo chonyenga ndi olamulira, kuchirikiza ndawala zawo za ndale zadziko ndi nkhondo, ndi kukakamiza anthu kulambira mbali zina za utundu za chirombo. Andale zadziko kaŵirikaŵiri apeza chipembedzo kukhala mnzawo wothandiza kupeza zofunikira zawo, monga mmene chingawonedwere m’kugwirizana kwa Hitler ndi Vatican mu 1933 ndi Nkhondo ya Chiweniweni ya ku Spain ya 1936-39. Mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II, atsogoleri a chipembedzo a Chikatolika, Chiprotestanti, chiBuddha, ndi zipembedzo zina ku mbali zonse ziŵiri anachita ngati kuti analedzera ndi chiyanjo cha utundu cha nkhondo. Iwo anatengako mbali mokulira pa liwongo la mwazi kaamba ka makumi a mamiliyoni a asilikali ndi anthu wamba omwe anafa mu nkhondo chiyambire 1914. Atsogoleri a chipembedzo omwe anachirikiza a Fascists ndi Nazis alinso ndi liwongo la mwazi chifukwa cha Mboni za Yehova, ndi ena, omwe anaphedwa kapena anafa m’misasa ya chibalo.​—Yeremiya 2:34; Chibvumbulutso 18:3, 24.

11. (a) Nchiyani chimene Akristu odzozedwa ndi khamu lalikulu akana kulambira? (b) Ndi ziyembekezo zokulira zotani zomwe zimapereka chifukwa champhamvu cha kuwopera Mulungu ndi kumpatsa ulemerero?

11 Mkati mwa zaka 74 zapitazo, Akristu odzozedwa okhulupirika, limodzi ndi ziŵerengero zomawonjezereka za khamu lalikulu, apitirizabe KUWOPA MULUNGU NDI KUMPATSA ULEMERERO. Ife takana moima nji kulambira mbali ya utundu iriyonse ya chirombo. Takana kulemekeza chifano cha chirombo​—Chigwirizano cha Mitundu ndi UN​—popeza timazindikira kuti “ufumu wa Ambuye wathu [Yehova] ndi wa Kristu wake” wokha ungabweretse mtendere wowona ndi chisungiko. Takhala ogamulapo kusunga “malamulo a Mulungu ndi chikhulupiriro cha Yesu.” Chipiriro chimenecho chiri ndi mphoto yake! Akristu odzozedwa omwe “afa m’chigwirizano ndi Ambuye” aŵerengedwa kukhala achimwemwe, chifukwa chakuti “ntchito zawo zitsatana nawo pamodzi.” Ponena za aliwonse a khamu lalikulu omwe angafe pansi pa zizunzo, matenda, kapena mwangozi, ubwenzi umene akulitsa ndi Mulungu umatsimikizira iwo za chiwukiriro choyambirira kulowa m’chitaganya cha “dziko lapansi latsopano.” Ziyembekezo zazikulu zimenezi zimapereka chifukwa champhamvu ndithudi cha KUWOPERA MULUNGU NDI KUMPATSA ULEMERERO.​—Chibvumbulutso 11:15, 17; 12:10; 14:9-13; 21:1.

12. Ndi kututa kuŵiri kuti komwe kukuchitika, ndipo liti?

12 Pamene chiŵeruzocho chikupitiriza, angelo akuitanira kaamba ka kututa kuŵiri. Wotuta wayamba ali mwachidziŵikire Yesu, woikidwa pa mpando wachifumu mu ulemerero wa Ufumu chiyambire 1914, popeza kuti iye akukwera pa mtamba woyera, wavekedwa chisoti chachifumu, ndipo ali “monga mwana wa munthu.” Tsopano, m’tsiku la Ambuye, iye akututa dziko lapansi, choyamba otsalira a Akristu odzozedwa ndipo kenaka mamiliyoni a khamu lalikulu. (Yerekezani ndi Mateyu 25:31-34; Yohane 15:1, 5, 16.) Mosiyana, kututa kwachiŵiri kuli kuja kwa “mphesa za dziko lapansi,” zomwe zikuponyedwa “moponderamo mphesa mwamkulu mwa mkwiyo wa Mulungu.” Ichi ndi chiŵeruzo choperekedwa pa Har–​Magedo, pamene chitaganya choipa, chopotoka cha mtundu wa anthu chizulidwa ndipo zipatso zake zopatsa ululu zikuphwanyidwa kukhala madzi. Lolani kuti Yehova alemekezedwe m’kuyeretsa dziko lapansi kuchotsapo mphesa zaululu zimenezi!​—Chibvumbulutso 14:14-20; 16:14, 16.

“Yehova . . . Wolungama ndi Wowona”

13. (a) Mu masomphenya a khumi, ndi nyimbo yotani imene odzozedwa owukitsidwa akuyimba, ndipo ndi ati omwe ali mawu ake? (b) Ndimotani mmene ziŵeruzo zolungama za Mulungu zikulongosoledwera mowonekera m’masomphenyawa?

13 Mu masomphenya a khumi a Chibvumbulutso, kachiŵirinso tikuwona zochitika za kumwamba pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu. Ndi chisangalalo chotani nanga chimene chikupezeka pa kukhalapo kwake! Owukitsidwa a odzozedwa​—omwe anabwera achipambano chifukwa CHOWOPA MULUNGU NDI KUMPATSA ULEMERERO​—akuyimba ‘nyimbo ya Mose ndi ya Mwanawankhosa’: “Ntchito zanu nzazikulu ndi zodabwitsa, [Yehova] Mulungu, Wamphamvuyonse. Njira zanu nzolungama ndi zowona, Mfumu inu wa nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu Yehova, chifukwa inu nokha muli woyera? Chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidawonetsedw.” Ziŵeruzo za Mulungu ziridi zolungama ndi zowona, monga mmene zalongosoledwera bwino lomwe mkati mwa masomphenya amenewa! Angelowo akutsanulira mbale zisanu ndi ziŵiri za mkwiyo wa Mulungu, kutsogolera ku kusonkhanitsidwa kwa mitundu yonse pa Har–​Magedo ndi chokumbutsa kuti “Babulo Wamkulu anakumbukiridwa pamaso pa Mulungu”! Cha panthaŵi yake ndithudi chiri chiitano cha KUWOPA MULUNGU NDI KUMPATSA ULEMERERO.​—Chibvumbulutso 15:1​—16:21.

14. Mu masomphenya 11 ndi 12, ndi mbali yotchuka yotani imene Babulo Wamkulu akuchita, ndipo nchifukwa ninji iri nthaŵi yofulumira kumuleka iye?

14 Babulo Wamkulu akutchulidwa mobwerezabwereza mu Chibvumbulutso. Tikumuwona iye kachiŵirinso monga mutu wa nkhani ya masomphenya a 11 ndi 12. Iye “wakhala pa madzi ambiri,” kulamulira anthu ndi kuwapangitsa iwo kuledzera ndi ululu wake, ziphunzitso zonama. Iyemwini waledzera ndi “mwazi wa oyera mtima,” amene anawapha mu zizunzo, ndipo ali ndi liwongo la mwazi m’chigwirizano ndi “onse amene anaphedwa pa dziko,” chifukwa cha kyambitsa nkhondo kwake kwa chinyengo. Kugwirizana kwake m’zamalonda ndi mabizinesi akulu ndi kukhetsa mwazi wa anthu kwa ndalama kwamubweretsera iye chuma chopezedwa molakwika. Choipitsitsa koposa chakhala kuchita chigololo kwake ndi ndale zadziko, ngakhale kufikira ku nsonga ya kudyerera kaamba ka kuchuka m’kukwera chirombo cha mtendere ndi chisungiko​—UN. Koma nyanga zokhala ndi zida za nkhondo za chirombo chimenecho ziri pafupi kumukhadzula ndi kumuwononga. Iri nthaŵi yofulumira kwa onse OWOPA MULUNGU NDI KUMPATSA ULEMERERO kusiyana naye, “pakuti machimo ake anawunjikizana kufikira kumwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.”​—Chibvumbulutso 17:1​—18:24.

15. Kuwonongedwa kwa mkazi wachigolo wamkulu kumatsogolera ku nyimbo za chitamando zotani ndipo kukutsatiridwa ndi chochitika china cha chimwemwe chotani?

15 Chotero, kuphedwa kwa Babulo Wamkulu kukubwera, monga chiŵeruzo cholungama kuchokera kwa Yehova. M’chiyamikiro cha ichi, ‘Aleluya’ akuyimbidwa, m’mwamba ndipo kenaka pa dziko lapansi, kupereka chipulumutso, ulemerero, ndi mphamvu kwa Yehova. Kuyimbidwa kumeneku kwa “Tamandani Ya, anthu inu!” kumasonyeza chimwemwe chokulira pa chiwonongeko chosatha cha mkazi wacigololo wamkulu. Kusakazidwa kwake kumasiyana chotani nanga ndi chochitika cha chimwemwe kwambiri m’mwamba​—ukwati wa Mwanawankhosa, Kristu Yesu, ndi mkwatibwi wake, olakika okhulupirika 144,000! Nyimbo ya bingu ya chitamando ikukwezedwa kwa “Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse,” inde, “tikondwere, tisekerere ndipo tipatse ulemerero kwa iye, pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa ndipo mkazi wake wadzikonzera”!​—Chibvumbulutso 19:1-10.

16. Mogwirizana ndi masomphenya 13, ndi nkhani yotani imene potsirizira pake idzakhazikitsidwa, ndipo motani?

16 Ngakhale kuli tero, ukwati wa kumwamba umenewo usanachitike, masomphenya 13 akusonyeza mmene nkhani yokhudza ulamuliro wa Yehova ikukhazikitsidwira. Mfumu yake ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye, Yesu, wotsagana ndi gulu la angelo, “aŵeruza nachita nkhondo molungama,” akumaponda moponderamo mphesa mwa ukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse. Mbali iriyonse yotsalira ya dongosololo dziko lapansi la Satana ikutswanyidwa kukhala zidutswa, kuperedwa! (Chibvumbulutso 19:11-21) Pamene tikumawona chipambano chomadza mofulumira chimenecho kupyolera m’masomphenya a Chibvumbulutso ndithudi tiri ndi chifukwa chirichonse cha KUWOPERA MULUNGU NDI KUMPATSA ULEMERERO!

Kulemekeza Mulungu Kosatha

17. Nchiyani chimene masomphenya 14 ndi 15 akuvumbula ponena za chotulukapo cha chimwemwe kwa awo owopa Mulungu ndi kumpatsa ulemerero?

17 Masomphenya 14 ndi 15 a Chibvumbulutso akuvumbula chotulukapo cha chimwemwe kwa awo omwe AMAWOPA MULUNGU NDI KUMPATSA ULEMERERO. Pokhala Satana ndi ziwanda zake atatsekeredwa ku phompho kwa zaka chikwi, ukwati wa kumwamba wa Mwanawankhosa ndi mkwatibwi wake uchitika, ndipo mafumu ndi ansembe 144,001 amenwa akulamulira kwa zaka chikwi pamene akubweretsa mtundu wa anthu ku ungwiro. Pamapeto pa chiyeso chomalizira, awo amene apitiriza KUWOPA MULUNGU NDI KUMPATSA ULEMERERO adzapambana ndi kukhala ovomerezedwa kaamba ka moyo wosatha. Awa adzaphatikizapo mabiliyoni a akufa owukitsidwa, “akulu ndi ang’ono,” omwe atsimikizira oyenera kukhala ndi maina awo atalembedwa m’bukhu la moyo. “Miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” zidzabweretsa madalitso osaneneka kwa mtundu wa anthu, madalitso omwe ali otsimikizirika, popeza kuti monga Mpangi wa “zinthu zonse zatsopano,” Yehova akulengeza kuti: “Talemba, pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi owona.”​—Chibvumbulutso 20:1​—21:8.

18. Mogwirizana ndi masomphenya 16, nchiyani chimene chiri chimake cha bukhu la Chibvumbulutso?

18 Masomphenya 16 abweretsa powonekera kufika pachimake kwa Chibvumbulutso. Kodi chimenecho nchiyani? Ali masomphenya a mzinda. Mzinda umenewu, Yerusalemu Watsopano, uli wosiyana kwambiri ndi wina uliwonse umene munthu anakhalapo atamanga pa dziko lapansi​—wosiyana kotheratu, kutalitali ndi Babulo Wamkulu, mzinda umene mpatuko wake, chisembwere chodetsedwa, ndi chigololo cha ndale zadziko sichinalemekeze Mulungu. Mzinda wopatulikawo uli woyera, wosadetsedwa, wa mtengo wake. Uli mkwatibwi wa Mwanawankhosa, m’nzake m’kupereka moyo wosatha ku dziko la mtundu wa anthu. (Yohane 3:16) Nchosadabwitsa kuti kuitanako kukumvekera mokwezeka, momvekera, kwa kutuluka mu mzinda wonyengawo, Babulo Wamkulu!​—Chibvumbulutso 18:4; 21:9​—22:5.

19. (a) Ndi chiitano chotani chomwe chikupangidwa kupyolera mwa gulu la mkwatibwi, ndipo ndimotani mmene ofatsa akuvomerezera? (b) Kupereka kwathu yankho lotsimikizirika ku lamulo la “Kuwopa Mulungu ndi kumpatsa ulemerero” kudzatulukapo chiyani?

19 Mzimu wamphamvu wa Yehova umagwira ntchito kupyolera mwa gulu la mkwatibwi chiitano chokakamiza: “Idzani!” Inde, nonsenu ofatsa amene mumakhumba moyo wosatha mu paradaiso wa pa dziko lonse, idzani ku “kasupe wa madzi a moyo,” kulandira makonzedwe onse a Yehova kupyolera mwa Kristu ndi mkwatibwi wake kaamba ka kupeza moyo wosatha! Ndi chiyembekezo chozizwitsa chotani nanga​—moyo waumunthu mu ungwiro pa dziko lapansi la paradaiso! Ikakhala mphoto kwa ambiri omwe amapereka yankho lovomereza ku lamulo lakuti “OPANI MULUNGU NDIPO MPATSENI ULEMERERO”!​—Chibvumbulutso 22:6-21, NW.

[Mawu a M’munsi]

a World Military and Social Expenditures 1987-88.

KODI MUKAYANKHA MOTANI?

□ Ndi chilengezo cha pa nthaŵi yake chotani chimene chiripo kaamba ka ife m’masomphenya a zirombo ziŵiri?

□ Ndimotani mmene tiyenera kuyankhira ku chilengezo cha mngelo wowuluka pakati pa mlengalenga?

□ Ndimotani mmene Babulo Wamkulu walowetsedwera m’chigololo, ndipo ndimotani mmene ichi chikulingaliridwira ndi awo owopa Mulungu?

□ Ndimotani mmene dziko lapansi likututidwira mkati mwa tsiku la Ambuye?

□ Ndi zochitika za chimwemwe zotani zomwe zikutseka Chibvumbulutso, ndipo ndimotani mmene anthu a Mulungu angagawaniremo?

[Chithunzi patsamba 23]

Medulo ya mkuwa iyi inatulutsidwa mu October 1987 pa chikondwerero cha Pemphero kaamba ka Mtendere pa Assisi. Ku mbali imodzi kuli chifanizo cha “Tate Woyera” mochizungulira pali deti ndi mawu ozokotedwa awa: “John Paul II Pontifex Maximus.” Ku mbali ina “Francis Woyera” akuitanira kaamba ka “Mtendere Mphatso ya Mulungu” pa Msonkhano wa Pemphero kaamba ka Mtendere pa Assisi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena