-
Umodzi Umene Umadabwitsa DzikoGalamukani!—1994 | January 8
-
-
Umodzi Umene Umadabwitsa Dziko
DZIKO linadabwa kwambiri ndi kugwa kwa mwadzidzidzi kwa Chikomyunizimu ndipo posachedwapa ndi chiwawa cha mafuko chomawonjezereka nthaŵi zonse. Komabe, panthaŵi imodzimodziyi, mamiliyoni ku Eastern Europe adabwa ndi zochitika zosangalatsa ndi zogwirizana za kagulu kamene kagonjetsa maudani aufuko ndi utundu—Mboni za Yehova.
Mboni za Yehova zapambana pa kusunga kulambira kogwirizana ngakhale pamene nkhondo zakhala zikuchita mowazinga. Mu 1991, pamene khamu la anthu amitundu yonse la Mboni 14,684 linasonkhana m’Zagreb, ku Croatia, wapolisi wina anati: “Kungakhale bwino kusonyeza m’zoulutsira nkhani zimene zikuchitika m’stediyamu muno, munomo, mmene anthu a ku Serbia, Croatia, Slovenia, Montenegro, ndi ena akhala pamodzi mumtendere.”
Chaka chimodzimodzicho mtolankhani wina pamsonkhano wachigawo ku Siberia anaona anthu a ku Russia akukupatira munthu wongobatizidwa kumene wa fuko la Buryat. Pokhala wodziŵa kuti kaŵirikaŵiri sipamakhala ubwenzi pakati pa mafuko osiyana otero, iye anafunsa kuti: “Kodi munakhoza motani kugonjetsa zopinga zautundu zimenezi?”
Chilimwe chapitachi misonkhano yachigawo 45 inachitidwa ndi Mboni za Yehova ku Eastern Europe ndi Asia, imene inali ku Moscow ndi Kiev inali ya mitundu yonse. Onse pamodzi oposa 368,000 anapezeka pamisonkhano yachigawo 45 imeneyo—oposa 112,000 m’dziko lomwe kale linali Soviet Union ndipo pafupifupi 11,000 m’mizinda inayi ya dziko lomwe kale linali Yugoslavia.
Mosasamala kanthu ndi kumenyana kwa m’madera awo, pafupifupi Mboni 215 zinafika pamsonkhano wachigawo m’Belgrade, ku Serbia, pa August 19 mpaka 22. Opezekapo anali 3,241. Mtolankhani wina anati: “Magulu a m’Sarajevo mwenimwenimo anapezekapo. Iwo analipirira basi, ndipo 56 anabwera. Ameneŵa anachokera ku Lukavica, Pale, Ilidža, ndi Vogošća. Ndiponso anthu asanu anachokera ku Benkovac. Mfundo ina yofunikira kuidziŵa njakuti 23 mwa anthu 174 amene anabatizidwa pamsonkhano wachigawowo anachokera kumadera a chipolowe ameneŵa.”
Ku Moscow ndi Kiev
Pa July 28, 1993, tsamba loyamba la The New York Times linali ndi chithunzithunzi chachikulu cha Mboni za Yehova ku Moscow, ndi mawu akuti: “Kumasulidwa kwa chipembedzo m’Russia kubweretsa okhulupirira ambiri m’Locomotive Stadium ku Moscow kudzabatizidwa monga Mboni za Yehova.”
Magazini a Times anasimba kuti: “Ziŵalozo zikumagwetsa misozi zikupatira atsopano onyowa. Mosiyana ndi khalidwe lanthaŵi zonse ku Locomotive, palibe amene akusuta fodya, palibe amene akutukwana, palibe woledzera.” Kwa masiku anayi Mboni za m’Russia ndi za kumaiko ena oposa 30 zinadzaza stediyamu yonseyo, chiŵerengero chapamwamba cha opezekapo chikumakhala 23,743.
Msonkhano wamitundu yonse wokulirapo wa Mboni za Yehova unachitikira ku Kiev, likulu la Ukraine. Kunali chiŵerengero chapamwamba cha anthu opezekapo 64,714 amene anasonkhana m’Republican Stadium, imodzi ya mastediyamu aakulu koposa ku Eastern Europe. Chikuto cha Evening Kiev chinati: “Mboni za Yehova . . . zili zogwirizanitsidwa osati ndi mabaji abluu okha olembedwapo ‘Chiphunzitso Chaumulungu’ komanso ndi chikhulupiriro chowona.”
Mmene Umodzi Umapezedwera
Kutheka kwa umodzi wotero kunasonyezedwa bwino ndi Mboni yachikulire ya ku Ukraine pamsonkhano wachigawo wa ku Kiev. Iyo inaloza chala kumwamba niiti, “Yehova.” Ndiyeno, ikumatambasula mikono yake mozungulira, inatukula chala chimodzi. Uthenga wake unali womvekera bwino: ‘Tonsefe tili amodzi, ogwirizana kupyolera mwa chiphunzitso chaumulungu cha Yehova Mulungu.’
Mokondweretsa, Encyclopædia Britannica inasimba za Mboni za Yehova m’dziko lomwe kale linali Soviet Union, ikumasonyeza chifukwa chake Mboni zili zogwirizana. Inafotokoza kuti: “Zimadziŵa ziphunzitso zawo [zozikidwa m’Baibulo], zili otembenuza anthu achangu ndipo zimalinganiza moyo wawo wonse mogwirizana ndi zikhulupiriro zawo zachipembedzo.” Chotero, kunali koyenerera chotani nanga kuti mutu wa misonkhano ya Mboni za Yehova chilimwe chathacho unali wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu”!
Yesu Kristu, amene anachirikiza chiphunzitso chaumulungu, anasonyeza lamulo la mkhalidwe logwirizanitsa lofunika pamene anapemphera ponena za otsatira ake kuti: “Siali a dziko lapansi monga ine sindili wa dziko lapansi.” Inde, kaimidwe ka Mboni za Yehova kauchete kamazigwirizanitsa, monga momwedi Yesu anapempherera kuti: “Kuti onse akakhale amodzi, monga inu Atate mwa ine, ndi ine mwa inu, kuti iwonso akakhale mwa ife.”—Yohane 17:16-21.
Chokumana nacho cha nthumwi ya ku Spain chimasonyeza mmene kusakhala mbali ya dziko kumagwirizanitsira anthu a Mulungu. Ali paulendo wopita kumsonkhano ku Moscow, iye anakhala pafupi ndi munthu wina wochokera ku Afghanistan amene anafotokoza kuti ngakhale anthu a chipembedzo chimodzimodzi anali kuphana m’nkhondo yachiŵeniŵeni m’dzikolo. Ndiyeno anafunsa kuti: “Kodi nchipani chandale chiti chimene chipembedzo chanu chimachirikiza?” Yankho linali lakuti “Palibe.” Popeza kuti Mboni za Yehova zili zachete m’zandale, sizimaloŵetsedwa m’kumenyana kwaufuko, kumene kumachititsa anthu kumenyana.
Nthumwi zoyenda paulendo kuchokera ku lipabuliki la dziko limene kale linali Soviet Union zinaona mwachindunji mmene nkhondo ilili yowopsa. Sitima yawo inadzera pamalo pamene magulu omenyana anali kuwomberana mfuti. Zinali zachimwemwe chotani nanga kufika ku Kiev motetezereka ndi kusangalala ndi chikondi ndi umodzi pakati pa mafuko osiyanasiyana a kumaiko ambiri m’stediyamu!
Nthumwi zambiri za ku Germany ndi Russia zinayamikira kwambiri zimene chiphunzitso chaumulungu chinazichitira. Monga amuna achichepere zaka zambiri zapitazo, anali kuyesa kuphana m’Nkhondo Yadziko II. Koma pamsonkhano wachigawo ku Kiev, anali ogwirizana m’kulambira kowona, monga momwe mukuonera patsamba 23.
Openyerera Anadabwa
Papitapo, Moscow, mzinda wa anthu pafupifupi mamiliyoni asanu ndi anayi, unalibe mwaŵi waukulu wa kudziŵa bwino lomwe Mboni za Yehova. Zowona, ambiri anamvapo za chizunzo chawo ndi kuikidwa kwawo m’ndende muulamuliro wa Chikomyunizimu. Ndiponso, podzafika chilimwe cha chaka chatha, mipingo 18 inali itakhazikitsidwa m’Moscow ndi 13 ku Kiev kusamalira ziŵerengero zomakula za opezeka pamisonkhano ya Mboni. Koma tsopano anthu a kumaloko anaona nthumwi zikwi makumi ambiri zovala mabaji pamalo amsonkhano ndi m’mizinda yawo yonseyo! Openyerera ambiri anazizwa.
Mkulu woyang’anira zamoto ku Moscow anati: “Msonkhanowu ngwochititsa chidwi kopambana. Nkosangalatsa kuti anthu ambiri a mitundu yosiyanasiyana ali ndi chinenero chimodzi. Ndadabwa ndi udongo ndi dongosolo la anthu anu. Ndakhala ndikugwira ntchito pastediyamuyi kwazaka 20 ndipo sindinaonepo zonga zimenezi.”
Wotsogolera alendo wina anati: “Nthaŵi zambiri pamene nditsogolera gulu, kupanda kwake umodzi kumaoneka gululo litangochoka pabwalo landege. Sizinakhale choncho kwa Mboni za Yehova.” Mlendo wina kumsonkhano wa ku Kiev anafuula kuti: “Inu mulidi ogwirizana. Nkosiyana chotani nanga ndi mmene zinthu ziliri kunja kwa linga lastediyamu!”
Pamene msonkhano wa ku Moscow unayamba pa Lachinayi, July 22, antchito angapo amene anaimirira pamwamba panyumba yomwe anali kumanga chapafupipo anali kuwonedwa akumalekeza ntchito yawo kwakanthaŵi. Mwachionekere anachita chidwi ndi mawu a anthu oposa 23,000 oimba nyimbo. Iwo akanadabwa kwambiri ngati akanadziŵa kuti nyimbozo zinali kuimbidwa m’zinenero zoposa 12. Ngakhale Mboni zogontha zosakhoza kuimba ndi mawu awo “zinaimba” ndi manja awo mwa kugwiritsira ntchito chinenero cha manja.
Malo abwino osonkhanapo madzulo anali Red Square wamkulu ku Moscow, kunja kwenikweni kwa linga la Kremlin. Madzulo amenewo msonkhano usanayambe (sikunade kufikira 10 koloko itapyola), Mboni mazana ambiri zochokera m’mafuko ndi mitundu yosiyanasiyana zinali kumeneko zikumakupatirana mwachimwemwe. Mtolankhani wa Moscow Times anadzera pamenepo ndipo anachita chidwi. “Kodi mumaimira yani?” iye anafunsa motero. Atauzidwa, anati: “Sindinaonepo khamu lachimwemwe la anthu osanganikirana a mafuko osiyanasiyana ambiri chotero pa Red Square. Kaŵirikaŵiri gulu lalikulu motere limabwera kuno kudzachita chionetsero chotsutsa kanthu kena.”
Nzika za Moscow ndi Kiev yemwe zinachitadi chidwi ndi kupatsana moni, kukupatirana mwachisangalalo, ndi kuyesa kulankhulana wina ndi mnzake kwa nthumwi zikwi zambiri zovala mabaji. Mwinibizinesi wina wa ku Iran amene anali kucheza ku Kiev anafikira Mboni yochokera ku United States nati: “Muli ndi kanthu kena kabwino koposa. Ndakhala ndikukupenyererani anthunu kwa masiku angapo apitawa. Ndikufuna ena a mabuku anu m’Chingelezi oŵerenga.” Iye anafotokoza kuti ngati kuti sanali kupita ku Iran m’maŵa wotsatira, akanafika kumsonkhano wachigawo.
Mu Moscow ndi Kiev yense—makamaka m’makwalala, m’mabwalo, ndi m’masitima apansi panthaka—nthumwi za msonkhano wachigawo zinafikira anthu ndi kuwapatsa matrakiti ndi mabrosha onena za Baibulo. Madzulo alionse Mboni zinkawonedwa zitaimirira pafupi ndi Lenin’s Tomb m’Red Square zikumakambitsirana mwakachetechete ndi kugaŵira matrakiti. Nthaŵi zambiri chogaŵira chinatengedwa ndi anthu mosazengereza, kaŵirikaŵiri akumwetulira. Ngati chogaŵiracho chinagaŵiridwa m’sitima ya pansi panthaka, kaŵirikaŵiri munthu anayamba kuŵerenga panthaŵi yomweyo. Sikunali kwachilendo kuona anthu asanu kapena asanu ndi mmodzi m’sitima akuŵerenga matrakiti onena za Baibulo.
Pambuyo poŵerenga uthengawo, wapaulendo wa m’sitima ya pansi panthaka kaŵirikaŵiri anali kuyamikira. “Tinalibe mwaŵi wa kuphunzira zinthu zotere,” anafotokoza motero mwamuna wina wa zaka zapakati m’Chingelezi chopotoka. “Zikomo kwambiri.” Pachochitika china, mnyamata wina ndi amake anachita chidwi kwambiri ndi uthenga kwakuti anatsika m’sitima ya pansi panthaka pasteshoni yomwe nthumwi zamsonkhano wachigawo zinatsikira kuti apitirize kukambitsirana.
Kiev anadzala ndi nthumwi zoposa 50,000 zimene zinachokera kumaiko oposa 30, zonsezo zinafunikira malo ogona. Zambiri zinakhala m’mahotela, nyumba za anthu, ndi masukulu, koma pafupifupi 1,800 anapeza malo ogona m’mabwato asanu ndi limodzi. Wosamalira limodzi la mabwatowo anasiyira kakalata Mboni. Iye anati: “Kwa ine mukuoneka ngati kuti mwachokera kupulaneti lina. Ndinu abwino ndi ogwirizana kwambiri kwakuti mwabweretsa dalitso. Muyenera kukhala ana a Mulungu. Ndikuganiza zimenezi nthaŵi zonse.”
Kunali koyenera chotani nanga kuti Mboni za Yehova zinakhoza kuchita misonkhano yawo yaikulu ndi kuti akuluakulu aboma ndi anthu wamba omwe anaona mikhalidwe Yachikristu yabwino yotero ndi mayendedwe amene amalemekeza Mulungu! Akuluakulu aboma kumaloko amene anagwira ntchito limodzi ndi Mboni analibe chonena kusiyapo kuzithokoza kwambiri kaamba ka kuyendetsa bwino zinthu, ulemu, ndi kugwirizana kwawo bwino ndi oyang’anira stediyamu ndi madipatimenti ena a mzinda.
“Stediyamu sinayeretsedwepo bwino motere kwazaka 13,” anatero mkulu wina waboma ku Kiev. Wapolisi wina wakomweko anafuula kuti: “Ndinu anthu odabwitsa chotani nanga! Ndichita ngati kuti ndili m’dziko latsopano. Sinditha kumvetsetsa chifukwa chake anthu inu munali kuzunzidwa.”
Mbali Zapadera za Msonkhano Wachigawo
Kwa Mboni za ku Moscow ndi Kiev, mbali yaikulu yapadera mwinamwake inali kukhalapo kwa nthumwi zikwi zambiri zochokera kumaiko ena, kuphatikizapo ziŵalo za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Chisangalalo cha kungokhalira limodzi, ogwirizana m’kulambira kwamtendere ndi anthu ambiri a mitundu yosiyanasiyana kwambiri, chinali chosafotokozeka. Pamene wokamba nkhani womalizira ku Moscow ndi Kiev ananena kuti chiyamiko chathu chachikulu chikumka kwa Yehova Mulungu, amene anatheketsa msonkhano wachigawo, omvetsera ananyamuka nawomba m’manja mosalekeza kwa mphindi zingapo kufikira pamene wokamba nkhaniyo anapitiriza ndi nkhani yake.
Mbali zina zapadera za msonkhano zinali nkhani zokambidwa m’Chingelezi tsiku lililonse ndi ziŵalo za Bungwe Lolamulira ndi malipoti achidule operekedwa ndi nthumwi zochokera kumaiko osiyanasiyana. Nkhani za m’Chingelezi zimenezi zinali kumasuliridwa nthaŵi yomweyo m’zinenero zambiri. Mwachitsanzo, ku Kiev m’zinenero 16! Chotero mwa kukhala m’malo olinganizidwira anthu a chinenero chakutichakuti, nthumwizo zinamvetsera mbali imeneyo ya programu m’chinenero chawo.
Mbali inanso yapadera ya msonkhano inali kutulutsidwa kwa brosha latsopano lakuti Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? m’chinenero cha ku Russia ndi Ukraine. Chimene chinayamikiridwa kwambiri chinali kutulutsidwa kwa Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki m’chinenero cha ku Russia, limene limagwiritsiridwa ntchito kukonzekeretsa Mboni za Yehova kulalikira chowonadi cha Baibulo mogwira mtima kwambiri. Ndiponso limene linatulutsidwa m’chinenero cha ku Russia linali Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, buku lachidule la mbiri ya Baibulo, lofotokoza nkhani malinga ndi dongosolo la mmene zinthu zinachitira lolembedwera makamaka achichepere. Makope oposa mamiliyoni 36 a bukuli asindikizidwa kale m’zinenero zoposa 80.
Kubatizidwa kwa ophunzira atsopano ochuluka kunalidi mbali yapadera ya msonkhano wachigawo. Mfundo imene sinaphonyedwe njakuti ambiri mwa awo amene anabatizidwa anali achichepere. Pamsonkhano wa atolankhani ku Kiev, mtolankhani wa nyuzipepala yakuti Osvita anafunsa kuti: “Pamisonkhano yanu yachigawo pamapezeka chiŵerengero chachikulu cha achichepere. Iwo ali okoma mtima, aukhondo, ndi odzisungira. Kodi mumachita bwanji zimenezo? Kodi muli ndi malamulo apadera a achichepere? Ndimagwira ntchito ndi achichepere, ndipo ndingakonde kwambiri kudziŵa zimenezo.”
Ngakhale kuti kudzipatulira kwa Mulungu kuyenera kuzikidwa pa chidziŵitso, osati pa kutengeka maganizo, ubatizo weniweniwo ulidi nthaŵi ya kutengeka maganizo, yosonkhezera mtima. Ku Moscow khamulo linanyamuka ndi kuwomba m’manja kuyambira panthaŵi imene oyembekezera ubatizo 1,489 anayamba kupita kumaiŵe atatu obatizira kufikira onse atabatizidwa, ola limodzi litapyola.
Ku Kiev, kumene kunali anthu oposa 64,000, maiŵe asanu ndi limodzi aubatizo anaikidwa kumbali imodzi ya stediyamu. Ndi obatiza asanu ndi mmodzi kapena kuposapo m’dziŵe limodzi, anthu ochuluka okhoza kupanga mpingo waukulu bwino anabatizidwa m’mphindi ziŵiri zilizonse. Chikhalirechobe, ubatizowo unapitiriza kwa maola oposa aŵiri! Pa Msonkhano Wamitundu Yonse wa “Chifuniro Chaumulungu” wa 1958 ku New York, panabatizidwa anthu 7,136. Koma ku Kiev, Mboni za Yehova 7,402 zoikidwa chatsopano zochokera m’Ukraine ndi maiko amene kale anali malipabuliki a Soviet Union zinachititsa ubatizo Wachikristu umenewu kukhala waukulu koposa uliwonse umene unachitikapo. Ameneŵa anali anthu olankhula chinenero cha ku Russia a m’madera kumene Mboni za Yehova zinali zoletsedwa kwa zaka makumi ambiri kufikira posachedwapa!
Mbali yapadera ya msonkhano ku Belgrade inali kukhalapo kwa nthumwi za kumadera okanthidwa ndi nkhondo. “Nthaŵi zambiri nthumwi zimenezi zinasonyeza chiyamikiro chachikulu kaamba ka mwaŵi wopatsidwa kwa izo wa kufika pamsonkhanowo,” wogwira ntchito pamsonkhano anatero. “Komabe, tiganiza kuti amene analimbikitsidwa kwambiri ndife amene tinakumana nawo ndi kuona chikondi chawo ndi changu cha chowonadi cha Baibulo.”
Pa yambiri ya Misonkhano ya “Chiphunzitso Chaumulungu,” kalata yomvetsa chifundo yolembedwa m’chisanu chapita yochokera ku Sarajevo inaŵerengedwa. “Tempichala ili pafupifupi [-15 digiri Celsius],” anatero wolembayo. “Ndili ndi mkazi wanga ndi ana aamuna aŵiri ndipo tilibe magetsi ndi nkhuni zokwanira . . . Tikumva kulira kwa mfuti zachiwaya ndi kuphulika kwa mabomba. Koma mitima yathu ili yabata ndi yachimwemwe chifukwa cha chowonadi ndi chifukwa cha unansi wathu wabwino ndi Yehova. . . . Tikupemphani kupitiriza kupemphera kwa Yehova kuti atithandize kulimbikira ndi kupirira mavuto onseŵa, tili olimba m’chikhulupiriro. Tikukupemphererani!”
Kodi Pali Kusiyana Kotani?
Poyerekezeredwa ndi mkhalidwe wa kupanda umodzi wosonyezedwa pakati pa zipembedzo za dziko, mwachionekere Mboni zili zosiyana kotheratu. Komatu, kodi izo kwenikweni nzosiyana motani? Ponena za msonkhano wachigawo wa Mboni zaka zingapo zapitazo, nkhani ya mkonzi inati: “Nkokhutiritsa maganizo kunena kuti ngati dziko lonse likanakhala likutsatira zikhulupiriro [za Baibulo] za Mboni za Yehova kukhetsa mwazi ndi udani zikanatha, ndipo chikondi chikanalamulira monga mfumu.”
Komabe, unyinji wa anthu sunatsatire chiphunzitso chaumulungu. M’zaka za zana loyamba, iwo anakanadi kumvetsera kwa Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu. Chotero kodi nkuchita mopambanitsa kuyembekezera kuti tsiku lina tidzakhala m’dziko logwirizana? Kodi chinthu chotero nchotheka motani?
[Bokosi patsamba 22]
MISONKHANO KU EASTERN EUROPE NDI ASIA
Chiŵerengero
Dziko Chapamwamba Obatizidwa
Albania (msonkhano 1) 598 39
Bulgaria (msonkhano 1) 704 45
Czech Republic (misonkhano 2) 20,025 620
Yemwe kale anali Soviet Union
Estonia (misonkhano 2) 4,732 383
Russia (misonkhano 3) 32,582 2,454
Ukraine (misonkhano 2) 69,333 7,797
Kyrgyzstan (msonkhano 1) 5,678 604
Yemwe kale anali Yugoslavia
Croatia (msonkhano 1) 5,003 157
Macedonia (msonkhano 1) 642 27
Serbia (msonkhano 1) 3,241 174
Slovenia (msonkhano 1) 1,961 69
Hungary (misonkhano 5) 22,191 798
Poland (misonkhano 13) 152,371 4,352
Romania (misonkhano 9) 36,615 2,375
Slovakia (misonkhano 2) 13,215 473
ZIWONKHETSO: 368,891 20,367
[Chithunzi patsamba 23]
Oposa 64,000 anasonkhana m’Republican Stadium, ku Kiev
[Chithunzi patsamba 23]
Amene anali adani m’Nkhondo Yadziko II ochokera ku Germany ndi Ukraine agwirizanitsidwa ndi chowonadi cha Baibulo
[Zithunzi pamasamba 24, 25]
Olambira ogwirizana oposa 23,000 m’Locomotive Stadium, ku Moscow
7,402 anabatizidwa ku Kiev, ndipo 1,489 ku Moscow
Nthumwi za kumaiko ena zinabweretsa matani ambiri a chakudya cha osoŵa
Pamwamba ndi pakati: Mafuko ambiri anasonkhana muumodzi wamtendere Pansi: Kuchitira umboni pa Red Square
[Chithunzi patsamba 26]
Nthumwi za msonkhano zinasangalala kulandira buku la “Nkhani za Baibulo,” “Bukhu Lolangiza la Sukulu,” ndi brosha latsopano m’chinenero chawo
-
-
Mmene Dziko LidzagwirizanitsidwiraGalamukani!—1994 | January 8
-
-
Mmene Dziko Lidzagwirizanitsidwira
ZOYESAYESA za anthu za kudzilamulira iwo eni mwachipambano zalephera kotheratu nthaŵi zonse. Mosakayikira mukuvomereza mawu ouziridwa akuti: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.” (Mlaliki 8:9) Kodi nchifukwa ninji anthu alephera momvetsa chisoni kwambiri kudzilamulira?
Baibulo limapereka chifukwa, likumati: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Ayi, munthu alibe mphamvu, kapena kuyenera, kwa kudzilamulira iyemwini kapena anthu anzake. Kumeneko kuli kuyenera kwapadera kwa Yehova Mulungu, Mlengi wathu, amene timauzidwa za iye kuti: “Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu.”—Yesaya 33:22.
Ndikokha pamene anthu onse avomereza Yehova Mulungu monga Wolamulira pamene dziko lidzagwirizana. Koma kodi zimenezo zidzachitikadi? Kalekale mneneri wina wa Mulungu analankhula za “masiku otsiriza,” pamene anthu ambiri akayamba kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka malangizo.
-