Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Pamene Panayambira Nkhaniyi
    Galamukani!—2003 | January 8
    • Pamene Panayambira Nkhaniyi

      TAUNI ya stratton, yomwe ili m’boma la ohio, ku united states ndi tauni yaing’ono imene ili pafupi ndi mtsinje wa Ohio, womwe uli malire a boma la Ohio ndi West Virginia. Tauniyi ili ndi anthu osakwana 300 ndipo ili ndi meya wake. Mu 1999 zinthu zinavuta m’tauniyi pamene akuluakulu a tauniyi anafuna kukhazikitsa lamulo loti anthu azikatenga kaye chilolezo kuboma akamayendera ena m’makomo. Lamuloli linakhudza Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito yawo youza ena uthenga wa m’Baibulo.

      Moti pamenepa pali nkhani? Inde, ndipo muona m’nkhani inoyo kuti kwenikweni boma litati likhazikitse lamulo lotere, Mboni za Yehova komanso anthu ena onse okhala ku United States sangamayankhule ndi ena mwaufulu.

      Chimene Chinatsitsa Dzaye

      Mboni za Yehova za mumpingo wa Wellsville m’tauni ya Stratton zakhala zikuchezera anthu a m’tauniyi kuyambira kalekale ndipo kungoyambira mu 1979 akuluakulu ena a kumeneko akhala akuzivutitsa chifukwa cha utumiki wawo wa kunyumba ndi nyumba. Kumayambiriro kwa m’ma 1990, wapolisi wina kumeneku anapirikitsa Mboni zina m’tauniyi, amvekere: “Zipitani; zaufulu wanuzo ine ndilibe nazo ntchito.”

      Komano nkhaniyi inafika pachiindeinde mu 1998 pamene meya weniweniyo anapezeketsa a Mboni za Yehova anayi. Iwo ankatuluka m’tauniyo pagalimoto yawo atachezamo ndi anthu ena amene anali ndi chidwi chokambirana za m’Baibulo. M’modzi wa azimayi amene anawapezeketsawo anati meyayo anawauza kuti bwenzi atawamangitsa kungoti achita mwayi poti si azibambo.

      Koma chimene chinabutsa nkhani yaposachedwapa ndi lamulo la tauniyi loletsa kupempha zinthu ndiponso kutsatsa malonda m’makomo mwa eniake popanda eniakewo kukuitanani. Lamuloli n’lakuti aliyense wofuna kuyenda khomo ndi khomo ayenera kukatenga kaye chilolezo kwa meya ndipo n’chaulere. Koma Mboni za Yehova zinaona kuti lamulo lotere n’loletsa anthu kuyankhulana, kupembedza, ndiponso kufalitsa nkhani mwaufulu. Motero tauniyi itakana kusintha lamuloli anaidulira chisamani ku khoti la m’bomalo.

      Pa July 27, 1999, jaji wamkulu wa khoti la kum’mwera kwa boma la Ohio anazenga mlanduwu. Iye anagamula kuti lamulo la tauniyo n’logwirizana ndi malamulo aboma. Kenaka pa February 20, 2001, khoti la apilo ku America linaugamulanso chimodzimodzi mlanduwu.

      Pofuna kuthetseratu nkhaniyi, bungwe la Watchtower Bible and Tract Society of New York mogwirizana ndi mpingo wa Mboni za Yehova m’tauniyi wotchedwa Wellsville anapempha kuti a khoti lalikulu kwambiri ku America auonenso mlanduwu.

  • Khoti Lalikulu Livomera Kumva Mlanduwu
    Galamukani!—2003 | January 8
    • Khoti Lalikulu Livomera Kumva Mlanduwu

      CHAPOSACHEDWAPA, Khoti lalikulu kwambiri ku United States lakhala likulandira milandu yopitirira 7000 pachaka ndipo pa milandu yonseyi lakhala likuvomera kuzengapo 80 kapena 90 yokha. Apa tingati linkangolola mlandu umodzi wokha pa milandu 100 iliyonse!

      M’mwezi wa May, 2001, Mboni za Yehova zinapempha Khoti Lalikululi kuti liuonenso mlandu wawo ndipo zinafunsa funso lakuti: “Kodi malamulo aboma amanena kuti anthu ochita ntchito ya m’Malemba imene inayamba kalekale, yoyenda khomo ndi khomo n’kumauza ena chikhulupiriro chawo kapena kuwagaŵira mabuku awo a Mawu a Mulungu popanda kuwalipiritsa, n’chimodzimodzi ndi anthu otsatsa malonda m’makomo, amene amayenera kukatenga kaye chilolezo kuboma?”

      Pa October 15, 2001, Dipatimenti yoona za milandu ya bungwe la Watchtower inauzidwa kuti Khoti Lalikulu ku United States lavomera kumva mlandu wawo umene ankaimba akuluakulu a tauni ya Stratton!

      Khotilo linavomera kumva mbali imodzi chabe ya mlanduwo yokhudza za ufulu woyankhula, yakuti, kodi Lamulo Loyamba Lowonjezera limakhudzanso za ufulu wouza anthu ena nkhani inayake popanda kudziŵitsa kaye boma?

      Zikatere, oweruza 9 akhotilo amayamba amvetsera kaye maganizo a amene adula chisamaniwo ndiponso amene akuimbidwa mlanduwo. A Mboni ali ndi maloya awo; nawonso a tauni ya Stratton ali ndi awo. Kodi pamenepa zinthu zithapo bwanji?

      [Bokosi patsamba 5]

      KODI LAMULO LOYAMBA LOWONJEZERA NDI LOTANI?

      “LAMULO LOYAMBA LOWONJEZERA (KUKHAZIKITSA CHIPEMBEDZO, UFULU WOPEMBEDZA, WOYANKHULA, WOFALITSA NKHANI, WOSONKHANA, WODANDAULA) Nyumba ya Malamulo siingapange lamulo lililonse loletsa kukhazikitsa chipembedzo chinachake, kapena loletsa chipembedzocho kuchita zinthu mwaufulu; kapena loletsa ufulu woyankhula kapena wofalitsa nkhani; kapenanso ufulu wakuti anthu asonkhane pamodzi mwabata, ndiponso ufulu wodandaulira boma kuti lisinthe chinthu chinachake.”—Amatero Malamulo a Dziko la United States.

      “Lamulo Loyamba Lowonjezera ndi limene pagona ufulu wonse wa anthu a ku United States. Lamulo limeneli sililola Nyumba ya Malamulo kukhazikitsa malamulo oletsa ufulu wa kuyankhula, kusonkhana, kapenanso kudandaula. Anthu ambiri amaona kuti ufulu woyankhula ngofunika kwambiri ndipo kuti ndiwo maziko a ufulu wina uliwonse. Lamulo Loyamba Lowonjezera limaletsanso Nyumba ya Malamulo kukhazikitsa chipembedzo cha boma kapena kuika malamulo ochepetsa ufulu wachipembedzo.” (Zachokera mu The World Book Encyclopedia) N’zochititsa chidwi kuti pa mlandu wina womwe chigamulo chake chinasintha zinthu wokhudzanso Mboni za Yehova wa Cantwell ndi boma la Connecticut, (mu 1940), Khoti Lalikulu ku United States linagamula kuti Lamulo Loyamba Lowonjezera sikuti limangoletsa “Nyumba ya Malamulo” yokha koma limaletsanso boma lililonse m’dzikolo kuika malamulo osemphana ndi ufulu wa anthu wotchulidwa m’Lamulo Loyamba Lowonjezera lija.

      [Zithunzi patsamba 5]

      Nkhani imeneyi ikukhudza kuyendera khomo ndi khomo pa zifukwa zosiyanasiyana

      [Mawu a Chithunzi patsamba 4]

      Photograph by Franz Jantzen, Collection of the Supreme Court of the United States

  • Choyamba Khoti Lalikulu Limva Mlanduwu
    Galamukani!—2003 | January 8
    • Choyamba Khoti Lalikulu Limva Mlanduwu

      TSIKU LOTI WOWERUZA wamkulu, Jasitisi William Rehnquist ndi oweruza ena 8 a Khoti Lalikulu amve mlanduwu, linali February 26, 2002. Mboni za Yehova zinali ndi maloya anayi.

      Loya wamkulu wa Mboni za Yehova anayamba kuyankhula ndi mawu ochititsa chidwi akuti: “Yerekezerani kuti ndi Loŵeruka m’maŵa, nthaŵi ili leveni koloko ndipo muli m’tauni ya Stratton. ‘Odi.’ [Kenaka anagogoda katatu, mokhala ngati akugogoda pachitseko.] ‘Muli bwanji? Malinga ndi nkhani zosautsa zimene zikuchitika masiku anozi, ndayesetsa kuti ndikupezeni kuti tikambiraneko zinthu zimene Mneneri Yesaya anati n’zabwino. Zinthu zake ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene Kristu Yesu ankauza anthu.’”

      Iye anapitiriza kunena kuti: “Kuyenda khomo ndi khomo m’tauni ya Stratton n’kumauza ena uthenga umenewu ndi mlandu ngati munthu sanakatenge chilolezo kwa akuluakulu a tauniyi.”

      ‘Mwati Simupempha Ndalama?’

      Woweruza wina, Jasitisi Stephen G. Breyer anafunsa maloya a Mboniwo mafunso osapita m’mbali. Iye anati: “Kodi n’zoona kuti a Mboni sapempha ndalama iliyonse, ingachepe bwanji, ndiponso kuti sagulitsa Mabaibulo, kapena china chilichonse, koma amangowauza anthu kuti, ‘Tikufuna tikambirane za Mawu a Mulungu’?”

      Loya wa Mboni anayankha kuti: “Bwana, iyi ndi nkhani yachidziŵikire m’tauni ya Stratton, Mboni za Yehova sizinapemphetsemo ndalama ayi. Ndipo m’madera ena n’zachidziŵikirenso kuti nthaŵi zina zimanena kuti ngati munthu akufuna angathe kupereka kangachepe. . . . Sikuti cholinga chathu n’kupemphetsa ndalama ayi. Timangofuna kukambirana ndi anthu za m’Baibulo basi.”

      Kodi M’pofunika Chilolezo cha Boma?

      Jasitisi Antonin Scalia anafunsa funso moganizadi ponena kuti: “Kodi mukutanthauza kuti mukafuna kuti muwauzeko nkhani inayake yosangalatsa anthu a kumene mumakhala, simuyenera kukapempha kaye kwa a meya, eti?” Ndiye loya wa a Mboni anayankha kuti: “Inde. Ifeyo tikuona kuti sibwino kuti khoti lino livomereze lamulo lakuti Boma lizifuna kuti nzika zake zizikapempha kaye chilolezo kuti zikauzane chinachake m’makomo mwawo.”

      Zinthu Zinatembenuka Itafika Nthaŵi ya Enawo

      Tsopano inafika nthaŵi yoti a tauniyo anene mbali yawo. Polongosola lamulo la tauniyo, loya wawo wamkulu anati: “Apatu tauni ya Stratton ikungogwiritsira ntchito mphamvu zake moyenerera pofuna kuteteza nzika zake kuti zizikhala mwaufulu, komanso popanda kuopa winawake. Lamulo loletsa kupempha zinthu m’makomo a eniake limangofuna kuti munthuyo akalembetseretu n’kumayenda ndi chikalata cha chilolezo akamayenda khomo ndi khomo.”

      Jasitisi Scalia anaboola mutu wa nkhaniyi mosachulutsa gaga m’diwa ndi funso lakuti: “Kodi anzanga mukukumbukira ngati ifeyo [a Khoti Lalikulu] tinaweruzapo mlandu wina uliwonse wokhudza lamulo lofika poterepa, lomaletsa anthu opita kunyumba ya wina, osati kukapempha ndalama kapena chinachake, kapenanso kukatsatsa malonda, koma wokhudza zakuti munthu wina ananena kuti, ‘Ndimafuna tikambiraneko za Yesu Kristu,’ kapena kungoti ‘Ndimafuna tikambirane zoteteza chilengedwe?’ Anzanga tanenani, kodi tinaweruzapo mlandu wotere ife?”

      Ndiye yekha anapitiriza kunena kuti: “Ine sindikudziŵapo za mlandu wina wotere m’zaka 200 zapitazi.” Pamenepa Jasitisi wamkulu Rehnquist anam’dula pakamwa n’kunena mongoseka, amvekere: “Simungadziŵedi chifukwa limenelo n’kale kwambiri, inuyo musanabadwe.” Ndiyetu mukhotimo anthu anaseka kwabasi. Koma Jasitisi Scalia anagogomezera mfundo yake ponena kuti: “Kwa ineyo n’kuyamba kumvapo mlandu wotere.”

      Kodi N’nzeru Ndithu?

      Jasitisi Anthony M. Kennedy anafunsa funso losapita m’mbali lakuti: “Kodi achikulire inuyo mukuona kuti n’nzeru ndithu kuti ndiziyamba ndapempha kaye chilolezo ku Boma ndikafuna kuyendako kamtunda pang’ono, kupita kwa anthu omwe ena sindidziŵana nawo, n’cholinga choti ndikawauze nkhani inayake, mwachitsanzo yokhudza kutaya zinyalala kaya ndi yokhudza phungu ku Nyumba ya Malamulo kapena china chilichonse chotere? Zoona ndipitire ku Boma zomwezi?” Ndiyeno anangoti, “Ayi ndithu, zina zinyanya.”

      Kenaka Jasitisi Sandra Day O’Connor naye anafunsapo kuti: “Nanga ana opemphetsa zinthu pa zikondwerero aja mutani nawo? Nawonso muzikawatengetsa chilolezo?” Jasitisi O’Connor ndi Scalia anapitiriza kugogomezera mfundo zimenezi. Kenaka Jasitisi O’Connor anafunsanso kuti: “Nanga bwanji ine n’kafuna kukapempha shuga kwa anthu amene ndayandikana nawo? Ndiye kuti ndiziyamba ndakatenga kaye chilolezo kuti ndipemphe shuga kwa anthu oyandikana nawo, eti?”

      Kodi a Mboni Ngopemphetsa?

      Jasitisi David H. Souter anafunsa kuti: “Kodi a Mboni za Yehova mukuwaikiranji m’gulu limeneli? Kodi a Mboni ngopemphetsa, otsatsa malonda, kapena ofunsira ganyu? A Mbonitu sali m’gulu limeneli ayi. Loya woimira tauniyo anaŵerenga mfundo za m’lamulolo mwatsatanetsatane n’kunena kuti khoti la m’boma lawo lija linaika Mboni za Yehova m’gulu la anthu opemphetsa. Atanena zimenezi Jasitisi Souter anayankha kuti: “Koma achikulire, ngati mukuika a Mboni za Yehova m’gulu la anthu opemphetsa, ndiye kuti kwa inuyo anthu opemphetsa alipo ambiritu.”

      Kenaka Jasitisi Breyer anaŵerenga tanthauzo la mawu akuti munthu wopemphetsa kuchokera m’buku lotanthauzira mawu pofuna kusonyeza kuti a Mboni sali m’gulu limeneli. Ndiyeno anati: “M’chikalata chanuchi sindinaŵerengemo chilichonse chonena za cholinga chokhazikitsira lamulo lakuti anthu [a Mboni za Yehova] ameneŵa azikatenga kaye chilolezo kwa akuluakulu a tauni yanu ngakhale kuti iwoŵa sapemphetsa ndalama, satsatsa malonda, ndiponso sapempha anthu kuti akavotere chipani chinachake. Kodi cholinga chanu n’chiyani makamaka?”

      Akuti “Mwayi” Woyankhula ndi Ena

      Kenaka loya wa tauniyo anatsutsa mfundozi ponena kuti “cholinga cha tauniyo ndicho kuthandiza anthu kuti wina asawasokoneze m’makomo mwawo.” Analongosolanso kuti tauniyo inkafuna kuteteza nzika zake kuti anthu achipongwe asaziyeretse m’maso kapena kuzichita chiwembu m’njira inayake. Ndiye Jasitisi Scalia anaŵerenga mawu a m’chikalata chofotokoza lamuloli osonyeza kuti meya angathe kufunsa munthu wofuna chilolezoyo mafunso okhudza zinan’zina komanso cholinga chake pofuna “kudziŵa mwayi umene angathe kum’patsa.” Kenaka ananenanso mosapita m’mbali kuti: “Mwati kuuza nzika zinzako nkhani inayake yoti aiganizirepo bwino ndi mwayi? Koma abale, zinazi n’zovuta kumvetsa ndithu.”

      Jasitisi Scalia sanalekere pomwepo ayi, anapitiriza kuti: “Moti inu mukufuna kuti munthu akafuna kugogoda pakhomo pa winawake, a Boma ayenera kuti am’dziŵe kaye? Mwa apo ndi apo, munthu angathedi kuchitidwa chipongwe panyumba pake, koma ndithu mpaka munthu akatengere chilolezo ku Boma asanagogode pakhomo lililonse chifukwa cha zomwezi? Ayi ndithu, n’zosamveka zimenezo.”

      Kodi Lamuloli Likutetezadi Nzika?

      Mphindi 20 zimene loya wa tauniyo anapatsidwa kuti ayankhulepo zitatha, anasiyira bwalo loya wamkulu wa boma la Ohio. Loya ameneyu ananena mfundo yakuti lamuloli n’loteteza anthu a m’tauniyo kwa anthu osawadziŵa, “amene angobwera panyumba pawo popanda kuwaitana . . . ” Ndiye anapitiriza kuti, “ndipo ineyo ndikuona kuti tauniyi siikulakwa kunena kuti, ‘Ife zimenezi zikutidetsa nkhaŵa.’”

      Kenaka Jasitisi Scalia anati: “Pamenepatu tauniyi ikunena kuti a Mboniŵa ayenera kukhala ndi chilolezo ngakhale poyankhula ndi anthu amene akuchita kufuna okha kuti awayendere chifukwa chosukidwa ndiponso kusoŵa munthu woti n’kucheza naye.”

      “Aka N’kalamulo Kakang’ono Chabe”

      Panthaŵi ya mafunso Jasitisi Scalia anatchula mfundo yosatsutsika pamene ananena kuti: “Tonsefe tikudziŵa bwino kuti mayiko amene ali ndi chitetezo chachikulu kwambiri ndi omwe amalamulidwa ndi maboma a mfundo zokhwima kwambiri. M’mayiko otere simuchuluka anthu ochita anzawo zachipongwe. Aliyense amadziŵa zimenezi, ndipo nthaŵi zina kuipa kokhala m’mayiko mmene anthu ali ndi ufulu wochita zimene akufuna n’kwakuti mumachuluka anthu ochita zinthu zoswa lamulo. Ndiye apa, nkhani yagona pakuti kodi tingachepetsedi zinthu zimenezi poika lamulo lakuti kugogoda pakhomo pa wina uchite kukhala mwayi wapadera?” Kenaka loya wamkulu wa boma la Ohio uja anayankha kuti “Komatu akuluakulu, aka n’kalamulo kakang’ono chabe.” Koma Jasitisi Scalia anayankha mom’pita pansi kuti n’zoona, kalamuloka n’kakang’onodi “moti palibe mlandu wina uliwonse wotere wonena za boma lililonse limene linakhazikitsapo lamulo langati limeneli. Lamulo laling’ono silikhala loteretu ayi.”

      Kenaka loya wamkulu wa bomayu posoŵa pothaŵira, jaji wina atam’panikiza nawo mafunso, anangovomera kuti: “Koma kungoti zoletseratu kugogoda m’makomozo ineyo si kuti ndinganene kuti n’zoyeneradi ayi.” Zonse zomwe ankafuna kunena zinathera pamenepa.

      Panthawi yonenapo zina ndi zina zimene sanagwirizane nazo, loya wa a Mboni ananena kuti lamulolo linalibe njira yodziŵira ngati munthu wofuna chilolezoyo akunenadi zoona. Iye anati: “Ineyo ndingathe kungopita kwa akuluakulu a tauniyo n’kukanena kuti ‘Ndine [wakutiwakuti],’ n’kundipatsa chilolezo n’kumayenda khomo ndi khomo.” Ananenanso kuti meyayo ali ndi mphamvu zotha kum’kaniza munthu chilolezocho ngati sali m’gulu linalake. Iye anati “Ifetu apa tikungoona kuti n’zachionekere kuti zingatengere ndi mmene meyayo akuonera,” ndipo anapitiriza kunena kuti: “Ndikunena mwaulemu wonse kuti ufulu wochita ntchito yathuyi ndi umene makamaka Lamulo Loyamba Lowonjezera limateteza.”

      Atangonena zimenezi, Jasitisi wamkulu Rehnquist anamaliza zonse ndi mawu aŵa: “Mlanduwu tavomera kuuzenga [m’Khoti lino].” Zonsezi zinangotenga nthaŵi yopitirira ola limodzi lokha basi. Kufunikira kwa zimene zinachitika pa ola limeneli kunadzadziŵika chikalata chogamula nkhaniyi chitatulutsidwa m’mwezi wa June.

      [Zithunzi patsamba 6]

      Jasitisi wamkulu Rehnquist

      Jasitisi Breyer

      Jasitisi Scalia

      [Mawu a Chithunzi]

      Rehnquist: Collection, The Supreme Court Historical Society/Dane Penland; Breyer: Collection, The Supreme Court Historical Society/Richard Strauss; Scalia: Collection, The Supreme Court Historical Society/Joseph Lavenburg

      [Zithunzi patsamba 7]

      Jasitisi Souter

      Jasitisi Kennedy

      Jasitisi O’Connor

      [Mawu a Chithunzi]

      Kennedy: Collection, The Supreme Court Historical Society/Robin Reid; O’Connor: Collection, The Supreme Court Historical Society/Richard Strauss; Souter: Collection, The Supreme Court Historical Society/Joseph Bailey

      [Chithunzi patsamba 8]

      Mkati mwa khotili

      [Mawu a Chithunzi]

      Photograph by Franz Jantzen, Collection of the Supreme Court of the United States

  • Khoti Lalikulu Ligamula Kuti Pakhale Ufulu Woyankhula
    Galamukani!—2003 | January 8
    • Khoti Lalikulu Ligamula Kuti Pakhale Ufulu Woyankhula

      TSIKU LA CHIGAMULO cha mlanduwu linali June 17, 2002, pamene Khoti Lalikulu linatulutsa chikalata chake. Kodi linagamula zotani? Zonse zinali m’mitu yankhani m’manyuzipepala. Nyuzipepala ya The New York Times inati: “Khoti Likana Zoletsa a Mboni za Yehova Kuyendera Ena.” The Columbus Dispatch ya ku Ohio inati: “Khoti Lalikulu Liletsa Lamulo Lotenga Kaye Chilolezo.” The Plain Dealer ya ku Cleveland, Ohio, inangonena momasula kuti: “Oyendera Anthu M’makomo Safunikira Chilolezo cha Boma.” Nkhani ina ya mu USA Today inati: “Ofuna Ufulu Woyankhula Zawayendera.”

      Oweruza 8 pa oweruza 9 anakana zimene khoti la apilo lija linagamula! Chikalata cha chigamulo cha khotilo, chomwe chinali ndi masamba 18, chinalembedwa ndi Jasitisi John Paul Stevens. Chigamulocho chinasonyezeratu kuti Lamulo Loyamba Lowonjezera likugwiritsidwabe ntchito kwambiri polola ntchito ya Mboni za Yehova. M’chigamulocho khotilo linafotokoza kuti a Mboniwo sanapemphe chilolezo chifukwa chakuti amaona kuti “Malemba ndi amene amawalamula kuti azilalikira.” Kenaka khotilo linatchulapo mawu a m’chikalata chodandaulira khotilo chimene Mbonizo zinalemba akuti: “Ifeyo timaona kuti kupempha chilolezo kuboma chakuti tizilalikira n’kunyoza Mulungu kumene.”

      Ndiyeno chikalata cha khotilo chinati: “Kwa zaka zoposa 50, khoti lino lakhala likukana zoletsa kuyenda khomo ndi khomo poyankhula ndi ena ndiponso pogaŵira timabuku. Sikuti zinkangochitika mwangozi kuti milandu yambiri yotere inali ya a Mboni za Yehova yokhudza za Lamulo Loyamba Lowonjezera, koma n’chifukwa chakuti kuyendera anthu khomo ndi khomo ndi lamulo la chipembedzo chawo. Tinaonanso m’landu wina wa Murdock ndi boma la Pennsylvania, . . . (wa mu 1943) ndipo tapeza kuti a Mboni za Yehova ‘amati amatsanzira Paulo, akamaphunzitsa “pabwalo ndi m’nyumba ndi m’nyumba.” Machitidwe 20:20. Amangotsatira ndendende lamulo la m’Malemba lakuti, “Mukani, kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.” Marko 16:15. Akamatero amakhulupirira kuti akutsatira lamulo la Mulungu.’”

      Kenaka chikalatacho chinatchulanso mfundo ya mlandu wa mu 1943 womwewu yakuti: “Mu Lamulo Loyamba Lowonjezera ntchito imeneyi n’chimodzimodzi ndi kupemphera m’matchalitchi ndi kulalikira kugome. Njofunikanso kuiteteza mofanana ndi mmene timatetezera zochitika zina zilizonse zodziŵika bwino za zipembedzo.” Potchulapo mfundo ya mlandu wina wa mu 1939, chikalatacho chinati: “Kuika lamulo lotenga kaye chilolezo komwe kumachititsa kuti anthu asathe kugaŵira timabuku mwaufulu ndiponso mosadodometsedwa n’kotsutsana kwambiri ndi ufulu umene malamulo a boma amapatsa anthu.”

      Kenaka khotilo linatchula mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Milandu yonseyi ikusonyeza kuti zimene Mboni za Yehova zakhala zikuyesa kuchita kuti anthu asamaletsedwe kuyankhula mwaufulu si zopindulitsa iwo okha.” Chikalatacho chinalongosola kuti a Mboni “si anthu wamba okhawo amene angaletsedwe kuyankhula mwaufulu chifukwa cha malamulo ngati a tauniyi.”

      Chikalatacho chinapitiriza kunena kuti, ponena kuti anthu akafuna kuyankhulana ndi anzawo mmene amachitira tsiku n’tsiku ayenera kuuza kaye boma kenaka n’kutenga chilolezo, lamuloli . . . “likunyoza mfundo zabwino zimene zili mu Lamulo Loyamba Lowonjezera komanso likunyoza ufulu umene anthu ayenera kukhala nawo. Lamulo lofuna kuti anthu azikatenga kaye chilolezo pofuna kuyankhulana motere n’losemphana kwambiri ndi chikhalidwe ndiponso malamulo amene dziko lathu lakhala likutsatira kuyambira kalekale.” Kenaka chikalatacho chinakamba za mmene “lamulo lotere lingaipitsire zinthu.”

      Kuopa Kuchitidwa Chipongwe

      Nanga bwanji zoti lamuloli n’loteteza anthu ku mbava ndi anthu achipongwe? Khotilo linati: “Inde, zimenezi n’zodetsadi nkhaŵa koma m’mbuyo monsemu khoti lino lakhala likuonetsetsa kuti lisachite zinthu monyanyira mwakuti n’kulanda nazo anthu ufulu wawo wolembedwa mu Lamulo Loyamba Lowonjezera.”

      Chikalatacho chinapitiriza kunena kuti: “N’zokayikitsa kuti lamuloli lingachititse anthu achipongwe kusiya kugogoda m’makomo kapena kuyankhula ndi anthu m’njira zina zimene sizinatchulidwe m’lamuloli. Mwachitsanzo iwo angathe kufunsira njira kapena kupempha kuti aimbe nawo telefoni, . . . kapenanso angathe kukalembetsa dzina labodza kuboma popanda wodziŵa.”

      Pobwerera ku chigamulo cha m’mbuyomo m’ma 1940, khotilo linati: “Nthaŵi ndi nthaŵi anthu odandaula [a Watch Tower Society] zinthu zinkawayendera bwino pa timilandu tosadziŵika bwino m’nthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse ndipo zinkatero chifukwa cha mmene khoti lino linkaonera mfundo za mu Lamulo Loyamba Lowonjezera. Panonso mfundozi tikuziona chimodzimodzi.”

      Kodi khotilo linagamula kuti chiyani? “Takana chiweruzo cha khoti la apilo chija, ndipo mlanduwu tikuubweza ku khotili kuti akauonenso malingana ndi mfundo tanenazi. Ifeyo talamula zimenezi.”

      Motero, mapeto a nkhaniyi anali akuti “Khoti Linaikira Kumbuyo Mboni za Yehova,” monga mmene inanenera nyuzipepala ya Chicago Sun-Times. Ndipo oweruza 8 pa oweruza 9 anaikira kumboyo a Mboni.

      Nanga Bwanji Zam’tsogolo?

      Kodi a Mboni za Yehova a mpingo wakufupi ndi tauniyo wa Wellsville anaiona bwanji nkhani imeneyi ya kupambana mu Khoti Lalikulu? Palibe chifukwa chodzitamandira pofuna kuchititsa manyazi nzika za tauniyi. Mboni za Yehova zilibe nawo mlandu anthu abwino a m’tauniyi. Gregory Kuhar, yemwe ndi wa Mboni wa kumeneku anati: “Ifeyo sitikanapita n’komwe kukhoti kuja ayi. Kungoti lamulo lija linali lolakwika basi. Zimene tinachitazi sikuti n’zongopindulitsa ife tokha ayi, koma aliyense.”

      Ndithu, a Mboni anayesetsa kwambiri kuti asasokoneze anthu a m’tauniyi. Gene Koontz, yemwenso ndi wa Mboni, anafotokoza kuti: “Nthaŵi yotsiriza kulalikira ku Stratton inali pa March 7, 1998, moti patha zaka zinayi zathunthu.” Ndiye anapitiriza kunena kuti: “Ineyo anachita kundiuza kuti andimanga. M’mbuyo monsemu takhala tikumva nkhani zosiyanasiyana zoti apolisi anali kutiopseza kuti atimanga. Ndiye tikapempha kuti ationetse chikalata chosonyeza lamulolo, palibe chimene ankachitapo.”

      Koontz anatinso: “Ifeyo timakonda kukhala bwino ndi anthu anzathu. Ngati ena sakufuna kuti tiwachezere sitilimbana nawo. Koma pali ena amene zimawasangalatsa ndipo amafuna kukambirana za m’Baibulo.”

      Gregory Kuhar analongosola kuti: “Sikuti ifeyo tinasuma mlandu umenewu n’cholinga choyambana ndi anthu a ku Stratton. Tinkangofuna kukhala ndi ufulu woyankhula movomerezedwa ndi lamulo.”

      Iye anatinso: “Tikuona kuti tipitakonso ku Stratton. Ndingakonde kuti ineyo ndikakhale munthu woyamba kugogoda pakhomo la munthu tikapitako. Tiyenera kupitakonso basi chifukwa ndi lamulo limene Yesu anapereka.”

      Panopo chigamulo cha mlandu umenewu chinakhudza madera ambiri. Akuluakulu a maboma osiyanasiyana ku America atamva zimene Khoti Lalikulu linagamula anazindikira kuti malamulo awo alibenso mphamvu yoletsa ntchito ya Mboni za Yehova yofalitsa uthenga wabwino. Tikunena pano, mavuto a kulalikira khomo ndi khomo athetsedwa m’madera pafupifupi 90 ku United States.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena