Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kulibe Chinthu Chabwino Choposa Choonadi
    Nsanja ya Olonda—1998 | January 1
    • Kulibe Chinthu Chabwino Choposa Choonadi

      Yosimbidwa ndi G. N. Van Der Bijl

      Mu June 1941, anandipereka kwa a Gestapo ndipo ananditengera ku msasa wachibalo wa Sachsenhausen pafupi ndi Berlin, ku Germany. Ndinakhala kumeneko monga mkaidi nambala 38190 mpaka ulendo wa ku imfa woopsawo wa mu April 1945. Koma ndisanafotokoze zochitikazo, tandilolani ndifotokoze mmene ndinakhalira mkaidi.

      NDINABADWIRA ku Rotterdam, ku Netherlands, Nkhondo Yadziko I itangoyamba kumene, mu 1914. Atate anali kugwira ntchito zapanjanji, ndipo nyumba yathu yaing’ono inali pafupi ndi njanji. Chakumapeto kwa nkhondoyo mu 1918, ndinali kuona sitima zambiri za ambulansi zikudutsa mwaliŵiro. Mosakayikira zinali zodzaza asilikali ovulala amene anali kukawatula kwawo kuchokera kudera lankhondo.

      Pamene ndinali ndi zaka 12 zakubadwa, ndinasiya sukulu kukafunafuna ntchito. Patapita zaka zisanu ndi zitatu ndinaloŵa ntchito yotumikira apaulendo pasitima yapamadzi, ndipo pazaka zinayi zotsatira, ndinakhala ndikuyenda pamadzi pakati pa Netherlands ndi United States.

      Titafika ku doko la New York m’chilimwe cha mu 1939, nkhondo inanso yadziko inali pafupi kuyamba. Choncho pamene mwamuna wina analoŵa m’sitima yathu ndi kundigaŵira buku lakuti Government, limene linali kunena za boma lolungama, ndinalilandira mosangalala. Nditabwerera ku Rotterdam, ndinayamba kufunafuna ntchito yapamtunda, popeza kuti moyo wapamadzi sunaonekenso kukhala wachisungiko. Pa September 1, Germany anathira nkhondo dziko la Poland ndipo mitundu inaloŵa m’Nkhondo Yadziko II.

      Kuphunzira Choonadi cha Baibulo

      Tsiku lina pa Lamlungu mmaŵa m’March 1940, ndinali kucheza kwa mkulu wanga wokwatira pamene mmodzi wa Mboni za Yehova analiza belo la pachitseko. Ndinamuuza kuti ndinali kale ndi buku la Government ndipo ndinamfunsa ponena za kumwamba ndi amene amapitako. Ndinalandira yankho lomveka ndi lofotokozeka moti ndinati mumtima, ‘Choonadi nchimenechi basi.’ Ndinampatsa keyala yanga ndi kumpempha kuti adzafike kunyumba kwanga.

      Atangondichezera katatu, pamene tinakambitsirana nkhani zakuya za m’Baibulo, ndinayamba kutsagana ndi Mboniyo m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. Titafika kugawo, anandisonyeza poyambira, ndipo ndinali ndekha. Ndi mmene ambiri achatsopano anali kuyambira ntchito yolalikira m’masiku amenewo. Anandiuza kuti, nthaŵi zonse ndiyenera kuloŵa m’khonde pamene ndikugaŵira mabuku kuti odutsa mumsewu asandione. Tinayenera kukhala osamala kwambiri m’masiku oyambirira a nkhondo.

      Patapita milungu itatu, pa May 10, 1940, asilikali a Germany anathira nkhondo dziko la Netherlands, ndipo pa May 29, mkulu wa Reich Seyss-Inquart analengeza kuti gulu la Mboni za Yehova laletsedwa. Tinali kungokumana m’timagulumagulu, ndipo tinali kusamala kuti malo athu amisonkhano asadziŵike. Kuchezera kwa oyang’anira oyendayenda kunali kotilimbikitsa kwambiri.

      Ndinali kusuta fodya kwadzaoneni, ndipo pamene ndinafuna kugaŵira ndudu kwa wa Mboni amene anali kundiphunzitsa Baibulo ndi kuzindikira kuti sasuta, ndinati: “Sindingasiye kusuta fodya!” Komabe, patangopita nthaŵi yochepa, pamene ndinali kuyenda mumsewu, ndinayamba kuganiza kuti, ‘Ngati ndikufuna kukhala Mboni, ndiyenera kukhala Mboni yeniyeni.’ Choncho sindinasutenso.

      Kuima Kumbali ya Choonadi

      Mu June 1940, patapita miyezi pafupifupi itatu kuchokera pamene ndinakumana ndi Mboni ija kunyumba ya mkulu wanga, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa. Patapita miyezi yoŵerengeka, mu October 1940, ndinaloŵa mu utumiki wanthaŵi zonse monga mpainiya. Panthaŵiyo, ndinapatsidwa jekete lotchedwa kuti jekete la apainiya. Ilo linali ndi matumba ambiri oikamo mabuku ndi timabuku, ndipo tinali kulivala ndi kuvalanso khoti pamwamba pake.

      Kungoyambira pachiyambi cha kuloŵerera kwa Ajeremani, Mboni za Yehova anali kuzifunafuna mosamala ndi kuzimanga. Tsiku lina mmaŵa mu February 1941, ndinali mu utumiki wakumunda ndi Mboni zina zingapo. Pamene anali kufikira anthu kumbali ina ya mdadada wa nyumba, ineyo ndinali kumbali inanso ya mdadadawo kuti tikumane. M’kupita kwa nthaŵi, ndinapita kuti ndikaone chimene chikuwachedwetsa ndipo ndinakumana ndi mwamuna wina amene anandifunsa kuti, “Kodi inunso mungakhalenso ndi timabuku iti?”

      “Inde,” ndinayankha motero. Nditangotero anandigwira ndi kundipereka kupolisi. Ndinakhala kumeneko muukaidi pafupifupi milungu inayi. Apolisi ambiri anali aubwenzi. Malinga ngati munthu sanaperekedwe kwa a Gestapo, anali ndi mwaŵi wa kumasulidwa mwa kungosaina chivomerezo cholembedwa chakuti sadzagaŵiranso mabuku a Baibulo. Atandipempha kusaina chivomerezo chimenecho, ndinayankha kuti: “Ngakhale mutandiuza kuti mudzandipatsa ndalama mamiliyoni, sindingasainebe.”

      Nditakhala kumeneko kanthaŵi, anandipereka kwa a Gestapo. Kenako anandipereka kumsasa wachibalo wa Sachsenhausen ku Germany.

      Moyo mu Sachsenhausen

      Pamene ndinafika ku Sachsenhausen mu June 1941, kunali kale Mboni 150​—zambiri zachijeremani. Ifeyo akaidi atsopano anatipititsa kugawo la msasawo lotchedwa kuti Chilekanitso. Kumeneko abale athu achikristu anatisamalira ndi kutifotokozera zimene tiyenera kuyembekezera. Patapita mlungu umodzi gulu lina la Mboni zochokera ku Netherlands linafika. Poyamba anatiuza kuti tiimirire pamalo amodzimodzi kutsogolo kwa nyumba kuyambira 7 koloko mmaŵa mpaka 6 koloko madzulo. Nthaŵi zina akaidi anali kuchita zimenezo tsiku lililonse kwa mlungu umodzi kapena kuposerapo.

      Mosasamala kanthu za kuzunzidwa kumeneko, abale anadziŵa kufunika kwa kukhala ndi dongosolo labwino ndi kudya chakudya chauzimu. Tsiku lililonse wina anali kusankhidwa kuti akonze zonena zozikidwa pa lemba la m’Baibulo. Kenako, pabwalo losonkhanira, Mboni zinali kupita kwa ameneyo mmodzimmodzi ndi kumvetsera zimene wakonzekera. Mwa njira ina yake, mabuku anali kuloŵa mwakazembera mumsasawo nthaŵi zonse, ndipotu Lamlungu lililonse tinali kusonkhana ndi kuphunzira pamodzi mabuku ameneŵa ofotokoza Baibulo.

      Mwa njira ina yake buku lakuti Children, limene linatulutsidwa pamsonkhano waukulu ku St. Louis, United States, m’chilimwe cha mu 1941, linaloŵa mwakazembera mu Sachsenhausen. Kuti tichepetse ngozi yakuti bukulo angaligwire ndi kuliwononga, tinaligaŵagaŵa, ndipo abale anali kusinthana zigawo zakezo kuti aliyense aliŵerenge.

      Patapita kanthaŵi, akuluakulu a msasawo anadziŵa kuti tinali kuchita misonkhano. Choncho Mboni anazipatula ndi kuziika m’zigawo zosiyana. Zimenezo zinatipatsa mpata wabwino kwambiri wa kulalikira kwa akaidi ena, ndipo chifukwa cha zimenezo, Apolishi ambiri, Ayukreniya, ndi ena analandira choonadi.

      Anazi sanali kubisa zolinga zawo za kuswa chikhulupiriro kapena kupha a Bibelforscher, monga momwe ankatchera Mboni za Yehova. M’kupita kwa nthaŵi, anatitsendereza koopsa. Anatiuza kuti akhoza kutimasula ngati tasaina chivomerezo chakuti tasiya chikhulupiriro chathu. Abale ena anayamba kupeza zodzikhululukira kuti, “Ndikamasuka, ndidzachita zambiri mu utumiki wa Yehova.” Ngakhale kuti angapo anasaina, abale athu ambiri anakhalabe okhulupirika mosasamala kanthu za kumanidwa zinthu zofunika, kusautsidwa, ndi kuzunzidwa. Ena mwa awo amene anasaina sitinamvenso za iwo. Koma chosangalatsa nchakuti ena anawongokera ndipo adakali Mboni zachangu.

      Nthaŵi zonse anali kutikakamiza kupenyerera pamene akaidi ena anali kulangidwa mwankhanza, monga kukwapulidwa ndi mkwapulo nthaŵi 25. Nthaŵi ina, anatikakamiza kupenyerera kuphedwa kwa amuna anayi mwa kuwanyonga. Zochitika zimenezo zimamkhudzadi kwambiri munthu. Mbale wina, mwamuna wamtali ndi wokongola, amene ndinali kukhala naye m’chigawo chimodzi, anandiuza kuti: “Ndisanabwere kuno, ndinkati ndikangoona mwazi ndinkakomoka nthaŵi yomweyo. Koma tsopano ndalimba mtima.” Komabe, ngakhale kuti tinalimba mtima, sitinakhale ouma mtima. Kunena zoona, sindinawaganizirepo zachiŵembu otizunza kapena kuwada.

      Nditagwira ntchito ndi kommando (gulu logwirira ntchito pamodzi) kwa nthaŵi ina, anandigoneka m’chipatala nditadwala malungo. Dokotala wina wachifundo wa ku Norway ndi nesi wa ku Czechoslovakia anandithandiza, ndipo chifundo chawo chiyenera kuti chinathandiza kupulumutsa moyo wanga.

      Ulendo wa ku Imfa

      Podzafika mu April 1945, zinali zoonekeratu kuti Germany akugonja pankhondoyi. Maiko ogwirizana a kumadzulo anali kuyandikira mofulumira kuchokera kumadzulo, ndiponso Asovieti, kuchokera kummaŵa. Anazi sakanatha kupha anthu zikwi mazana ambiri amene anali m’misasa yachibalo ndi kutaya mitembo yawo m’masiku oŵerengeka popanda kusiya chizindikiro chilichonse. Choncho anaganiza za kupha odwala ndi kusamutsira akaidi otsala ku doko lapafupi. Iwo analinganiza kuti kumeneko adzawalonga m’masitima apamadzi ndi kumiritsa masitimawo panyanja.

      Ulendo wa akaidi 26,000 kuchokera ku Sachsenhausen unayamba usiku wa pa April 20. Tisananyamuke pamsasawo, tinachotsa abale athu odwala m’chipatala. Tinapeza ngolo yowanyamulirapo. Tonse pamodzi, tinali 230 ochokera m’maiko osiyanasiyana asanu ndi limodzi. Pakati pa odwalawo panali Mbale Arthur Winkler, amene anali atathandiza kwambiri pa kufutukula ntchito ku Netherlands. Mbonife tinali kuthungo paulendowo, ndipo tinalimbikitsana mosalekeza kuti tipitirizebe kuyenda.

      Poyamba, tinayenda kwa maola 36 popanda kuima. Pamene ndinali kuyenda, kwenikweni ndinali kugona chifukwa cha kuvutika kwakukuluko ndiponso kutopa. Koma kukhalira kumbuyo kapena kupumula kunali kosatheka chifukwa chakuti panali ngozi ya kuomberedwa ndi asilikali. Usiku tinali kugona pamtetete kapena m’nkhalango. Chakudya chinali chosoŵa zedi. Njala itandipweteka koopsa, ndinadya mankhwala otsukira mano amene a Red Cross ya ku Sweden anatipatsa.

      Penapake, chifukwa chakuti asilikali achijeremani sanadziŵe bwino kumene kunali asilikali a Russia ndi a United States, tinakhala m’nkhalango masiku anayi. Umenewu unali mwaŵi waukulu chifukwa chakuti zimenezo zinachititsa kuti tisafike ku Lübeck Bay panthaŵi yake kuti tikakwere sitima zapamadzi zimene zinayenera kutipereka kumanda athu apamadzi. Pomalizira pake, patapita masiku 12 ndipo titayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 200, tinafika ku Crivitz Wood. Kumeneku kunali kufupi ndi Schwerin, mzinda wokhala pamtunda wa makilomita pafupifupi 50 kuchokera ku Lübeck.

      Asovieti anali kudzanja lathu lamanja, ndipo Aamereka, kulamanzere. Tinadziŵa kuti tili pafupi ndi dera lankhondo chifukwa cha kulira kwa mfuti zazikulu ndi moto wazipolopolo wosalekeza. Asilikali achijeremani anatekeseka; ena anathaŵa, ndipo ena anavula mayunifomu awo ausilikali ndi kuvala aukaidi amene anavula akaidi akufa, nchiyembekezo choti asadziŵike. Pakati pa chipwirikiti chimenecho, Mbonife tinasonkhana ndi kupempherera chitsogozo.

      Abale otsogolera anaganiza kuti tinyamuke mmaŵa kwambiri tsiku lotsatira ndi kupita cha kumene kunali asilikali a ku United States. Ngakhale kuti akaidi pafupifupi theka la amene anayamba ulendo wa ku imfa umenewo anamwalira kapena anaphedwa paulendowo, Mboni zonse zinapulumuka.

      Asilikali ena a ku Canada anandinyamula popita ku mzinda wa Nijmegen, kumene mlongo wanga anali kukhala. Koma nditafika kumeneko, ndinapeza kuti anasamuka. Choncho ndinayamba ulendo wapansi wopita ku Rotterdam. Mwamwaŵi, panjira munthu wina anandinyamula pagalimoto lake kukanditula kumene ndinali kupita.

      Choonadi Chakhala Moyo Wanga

      Nditafika ku Rotterdam, ndinafunsiranso ntchito yaupainiya tsiku lomwelo. Patapita milungu itatu ndinali kugawo langa mumzinda wa Zutphen, kumene ndinatumikira chaka chimodzi chotsatira ndi theka. M’nthaŵi imeneyo, ndinapezanso nyonga yanga yakuthupi. Kenako ndinaikidwa kukhala woyang’anira dera, monga momwe timatchera atumiki oyendayenda. Patapita miyezi yoŵerengeka, ndinaitanidwa ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ku South Lansing, New York. Nditamaliza maphunziro m’kalasi la 12 la sukululo mu February 1949, ananditumiza ku Belgium.

      Ndatumikira m’mbali zosiyanasiyana za utumikiwu ku Belgium, kuphatikizapo zaka pafupifupi zisanu ndi zitatu paofesi yanthambi ndi zaka makumi ambiri m’ntchito yoyendayenda ponse paŵiri monga woyang’anira dera ndi woyang’anira chigawo. Mu 1958, ndinakwatira Justine, amene anakhala mnzanga woyenda naye maulendo. Tsopano, pamene ndikukalamba, ndikusangalalabe kutumikira pang’onopang’ono monga woyang’anira woyendayenda wogwirizira.

      Ndikakumbukira utumiki wanga, ndimanenadi kuti: “Kulibe chinthu chabwino choposa choonadi.” Nzoona kuti zinthu zakhala zovuta nthaŵi zina. Ndazindikira kufunika kwa kuphunzira pazophophonya zanga ndi kulephera kwanga. Choncho polankhula ndi achinyamata, kaŵirikaŵiri ndimawauza kuti: “Inunso mudzaphophonya mwinanso kuchita tchimo lalikulu, koma musaname pazimene mwachita. Kambitsiranani nkhaniyo ndi makolo anu kapena ndi mkulu, kenako mupange kuwongolera kofunika.”

      Pazaka zanga pafupifupi 50 za utumiki wanthaŵi zonse ku Belgium, ndakhala ndi mwaŵi woona anthu amene ndinawadziŵa akali ana akutumikira monga akulu ndi oyang’anira oyendayenda. Ndiponso ndaona olengeza Ufumu ngati 1,700 a m’dzikoli akuwonjezeka kukhala 27,000.

      Ndimafunsa kuti, “Kodi pangakhale njira inanso ya moyo yopatsa chimwemwe kwambiri kuposa kutumikira Yehova?” Siinakhaleko, kulibe tsopano, ndipo siidzakhalako. Ndikupemphera kuti Yehova apitirizebe kutitsogoza ndi kutidalitsa ineyo ndi mkazi wanga kuti tipitirizebe kumtumikira kosatha.

      [Chithunzi patsamba 26]

      Ndi mkazi wanga titangokwatirana kumene mu 1958

  • ‘Pangani Ophunzira mwa Anthu a Mitundu Yonse’
    Nsanja ya Olonda—1998 | January 1
    • ‘Pangani Ophunzira mwa Anthu a Mitundu Yonse’

      “CHIFUKWA chake mukani nimupange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, kuwabatiza iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.” Umu ndimo mmene Baibulo la New World Translation linatembenuzira lamulo la Yesu pa Mateyu 28:19. Komabe, kutembenuza kumeneku ena akutsutsa. Mwachitsanzo, kabuku kena kachipembedzo kanati: “Lemba lachigiriki limeneli lingamveke bwino kokha ngati litatembenuzidwa motere: ‘Pangani ophunzira mwa mitundu yonse.’” Kodi zimenezo nzoona?

      Mabaibulo ambiri anatembenuzadi choncho kuti, “Pangani ophunzira mwa mitundu yonse,” ndipo kumeneko kunali kutembenuza mwachindunji mawu achigiriki. Choncho, kodi pali chifukwa chotani choŵerengera kuti, “Pangani ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza”? Chifukwa cha nkhani yakeyo. Mawu akuti “kuwabatiza” kwenikweni akutanthauza anthu, osati mitundu. Katswiri wazamaphunziro wa ku Germany, Hans Bruns, anati: “[mawu] akuti ‘iwo’ sakutanthauza mitundu (Chigiriki chimasiyanitsa bwino), koma anthu a m’mitunduyo.”

      Ndiponso, tiyenera kulingalira mmene anthu anatsatira lamulo la Yesu limenelo. Ponena za utumiki wa Paulo ndi Barnaba ku Derbe, mzinda wa ku Asia Minor, timaŵerenga kuti: “Pamene analalikira Uthenga Wabwino pamudzipo, nayesa ambiri akuphunzira [napeza ophunzira oŵerengeka, NW], anabwera ku Lustra ndi Ikoniya ndi Antiokeya.” (Machitidwe 14:21) Taonani kuti Paulo ndi Barnaba sanapange onse mumzinda wa Derbe kukhala ophunzira, koma kuti ena mwa anthu a ku Derbe.

      Mofananamo, ponena za nthaŵi ya mapeto, buku la Chivumbulutso linaneneratu kuti si mitundu yonse yomwe idzatumikira Mulungu, koma ‘khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,’ ndiwo adzamtumikira. (Chivumbulutso 7:9) Choncho, tikuchirikiza Baibulo la New World Translation kuti nlodalirika chifukwa linatembenuza bwino ‘Lemba lililonse, limene adaliuzira Mulungu.’​—2 Timoteo 3:16.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena