Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mabuku, Mabuku, Mabuku!
    Nsanja ya Olonda—1997 | August 1
    • Mabuku, Mabuku, Mabuku!

      “Pakuti saleka kulemba mabuku ambiri,” inalemba motero Mfumu yanzeru Solomo ya nthaŵi zakale. (Mlaliki 12:12) M’chaka cha 1995 ku Britain, pa anthu 580 alionse, pafupifupi buku limodzi latsopano linalembedwa, zikumapangitsa dziko limenelo kukhala lotsogola pa maiko onse polemba mabuku atsopano. China, dziko lomwe lili ndi anthu ochuluka koposa padziko lonse lapansi, linali lachiŵiri ndi chiŵerengero cha 92,972 cha mabuku atsopano poyerekeza ndi chiŵerengero cha Britain cha 95,015. Germany anatsatira ndi (mabuku 67,206), ndiye kenako United States (49,276), kenaka France mabuku (41,234). “Chapangitsa kuti dziko la Britain likhale patsogolo nchakuti Chingelezi ndicho chilankhulo chofala padziko lonse.” inatero nyuzipepala ya The Daily Telegraph ya ku London.

      Malipoti amasonyeza kuti malonda amabuku akhala akuloŵa pansi pa zaka zingapo, ndipo tsopano ndi 80 peresenti yokha ya anthu akuluakulu m’Britain amagula buku limodzi kapena ochulukirapo pa chaka. Komabe kodi anthu amaŵerenga mabuku onse amene amagula?

      Buku lina limene likufalitsidwabe ndiponso kuŵerengedwa kwambiri ndi Baibulo, lomwe tsopano limapezeka m’zilankhulo 2,120, mbali zake chabe kapenanso lathunthu. Ngati inu simunapezebe Baibulo, fikani pa ofesi ya Watch Tower Society yomwe ili pafupi ndi kwanuko kuti mukagule lanu. Ngati muli nalo kale, litengeni ndipo yang’ananimo Malemba amene alembedwa mu nkhani za m’magazini ano. Mukatero, mudzapeza chidziŵitso chopereka moyo cha m’Baibulo.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1997 | August 1
    • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

      Popeza Mboni za Yehova zimayesetsa kuti zikhale zoona mtima ndipo zimakhulupirirana, nchifukwa ninji zimati nkofunika kulemba pangano pamene zikuchita malonda zokhazokha?

      Zimenezi ndi za m’Malemba, nzothandiza, ndipo nchikondi. Zili choncho bwanji? Chabwino, tiyeni tione mbali zimenezo m’mapangano.

      Baibulo limafotokoza mmene Mulungu anachitira ndi anthu ake a m’pangano, Aisrayeli. Limanenanso malonda a pakati pa olambira Yehova okhaokha. Genesis chaputala 23 ili ndi nkhani imodzi imene tingalingalirepo. Pamene wokondedwa wake Sara anamwalira, Abrahamu anafuna kugula malo poti amuike. Anayamba kukambitsirana ndi Akanani amene amakhala kufupi ndi Hebroni. Mavesi 7-9 amasonyeza kuti anatchula mtengo woyenera wa munda umene amafunawo. Vesi 10 limasonyeza kuti mtengo umenewu anaunena poyera pa chipata, ena onse a mumzindawo akumva. Vesi 13 limaonetsa kuti mwini mundawo anafuna kumpatsa Abrahamu waulere, koma iye ananena kuti adzautenga pokhapokha atagula. Ndipo mavesi 17, 18 ndi 20 amalongosola kuti umu ndimo mmene zinayendera, zinavomerezeka “pamaso pa ana a Heti, pa onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake.”

      Komabe, kodi zikanachitika mosiyanako kukanakhala kuti amene akugulitsanawo anali alambiri oona okhaokha? Yeremiya chaputala 32 amatipatsa yankho. Kuchokera mu vesi 6 kupita mtsogolo, timapeza kuti Yeremiya anafuna kugula munda kwa mwana wa mbale wa atate ake. Vesi 9 limasonyeza kuti anagwirizana mtengo woyenera. Tsopano ŵerengani mavesi 10-12: “Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m’miyeso. Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wovundukuka; ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamaso pa Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m’bwalo la kaidi.”

      Inde, ngakhale kuti Yeremiya amagulitsana ndi wolambira mnzake, komanso mbale wake, anatsata njira zoyenera mwalamulo. Makalata aŵiri analembedwa​—imodzi anaisiya yotseguka kuti azitha kuonapo mwamsanga, ndipo yachiŵiri anaitseka kuti idzakhale umboni ngati zitadzachitika kuti pakhala kukayikira za kalata yotsegukayo. Monga momwe vesi 13 limanenera, kugulitsana konseku kunachitika “pamaso pawo.” Motero zinali zapoyera, kugulitsana mwalamulo, pali mboni. Choncho, pali zitsanzo za m’Malemba zosonyeza kuti alambiri oona ayenera kuchita malonda m’njira yotsimikizika ndipo yakulemba.

      Ndiponso kumathandiza. Timazindikira kuona kwa mawu akuti “koma yense angoona zom’gwera m’nthaŵi mwake.” (Mlaliki 9:11) Izi zimachitikira ngakhale Akristu odzipereka ndi okhulupirika. Yakobo 4:13, 14 amanena kuti: “Nanga tsono, inu akunena, lero kapena maŵa tidzapita kuloŵa ku mudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kusatsa malonda, ndi kupindula nawo; inu amene simudziŵa chimene chidzagwa maŵa. Moyo wanu uli wotani?” Motero, tikhozadi kuyamba ntchito, monga ngati kuyamba kugula chinthu china, kapena kumvana kugwirira wina ntchito kaya utumiki wina wake, kapena kuchitira wina kanthu kena. Koma kodi nchiyani chidzachitika maŵa​—kapena mwezi wamaŵa kapena chaka cha maŵa? Bwanji ngati ifeyo kapena mnzathuyo ngozi imgwera? Zimenezi zikhoza kusonyezeratu kuti kusunga pangano lija sikutheka. Bwanji ngati sitingathenso kuchita ntchito ija kapena mnzathuyo wapeza kuti mwina sangathenso kubweza ngongole ija kapena kuchita zimene amayenera kuchita malinga ndi pangano? Ngati simunalemberane, zinthu zikhoza kuvuta kwambiri, zomwe sizikadavuta kuthetsa kapena zikadapewedwa ngati mukadakhala kuti munalemberana.

      Kuwonjezera apo, tisaiŵale kuti popeza sitidziŵiratu za mtsogolo ponena za moyo wathu, mwina wina adzafunikira kulipira ngongole yathu kapena ya winayo. Yakobo anawonjezera mu vesi 14: “Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthaŵi, ndi pamenepo ukanganuka.” Kunena zoona, tikhoza kufa mwadzidzidzi. Pangano lolembedwa, ndithudi likhoza kuthandiza otsala kupitiriza kusamalira nkhaniyo patachitika kanthu kena kosayembekezereka kwa aliyense wa opanganawo.

      Ndi ganizo limeneli, tikhoza kufikanso ku mfundo yachitatu​—mapangano olemba amasonyeza chikondi. Ndithudi, ngati mmodzi wafa kapena wachita ngozi moti sangathenso kulongosola zinthu, zingakhale chikondi kuti Mkristu akhale ndi pangano lolemba la ndalama zomwe amayembekezera kulandira. Ndipo kulemberana pangano sikuti ndi kusakhulupirirana ayi. Koma kumasonyeza chikondi kwa mbale wathu amene tikuchita naye malonda, chifukwa tidzalongosola bwino lomwe zimene ayenera kuchita kapena zimene ayenera kulandira. Kachitidwe kachikondi kameneka kadzapangitsa kuti pasabuke chizondi ngati mmodzi mwa anthu opanda ungwiro ameneŵa aiŵala mfundo zina kapena zimene amayenera kuchita. Ndipo ndani mwa ife amene sali wopanda ungwiro, wosaiŵala, amene nkosatheka kwa iye kumva molakwa mfundo zina kapena zolinga zake?​—Mateyu 16:5.

      Pali njira zina zimene kupanga mapangano olemba kumasonyezera chikondi kwa abale athu, mabanja athu, ndiponso mpingo wonse. Komabe ziyenera kukhala zoonekeratu kuti m’malo mongosonyeza chabe chikondi, mapangano olemba otero okhala ndi mfundo zonse zofunika amathandiza ndipo ali ogwirizana ndi Malemba.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena