-
Chaka cha 1914 Ndi Chaka Chapadera KwambiriKodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
-
-
monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.a—Salimo 2:1-6; Danieli 7:13, 14.
Yesu ananeneratu kuti nthawi ya “kukhalapo” kwake idzadziwika ndi zinthu monga nkhondo, njala, zivomezi ndi miliri, ndipo zimenezi ndi zimene zakhala zikuchitika padziko lonse kuyambira mu 1914. (Mateyu 24:3-8; Luka 21:11) Zinthu zimene zakhala zikuchitikazi ndi umboni wokwanira wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unayambadi kulamulira kumwamba mu 1914 ndipo pamenepa ndi pamene “masiku otsiriza” a dziko loipali anayambira.—2 Timoteyo 3:1-5.
-
-
Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
-
-
ZAKUMAPETO
Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?
MNGELO wina amene amadziwika ndi dzina lakuti Mikayeli, satchulidwa kawirikawiri m’Baibulo. Koma nthawi iliyonse imene watchulidwa ndi dzina limeneli, amakhala akugwira ntchito inayake yapadera. M’buku la Danieli, Mikayeli amatchulidwa akulimbana ndi angelo oipa. M’kalata ya Yuda, amatchulidwa akukangana ndi Satana. Ndipo m’buku la Chivumbulutso, amatchulidwa ali pa nkhondo yomenyana ndi Satana ndi ziwanda zake. Mikayeli amagwira ntchito yolimbana ndi adani a Yehova komanso yotetezera Ufumu wa Mulungu, ndipo zimenezi n’zogwirizana ndi dzina lake, chifukwa limatanthauza kuti, “Ndani Ali Ngati Mulungu?” Koma kodi Mikayeli ameneyu ndi ndani?
Anthu ena amadziwika ndi mayina angapo. Mwachitsanzo, Yakobo amadziwikanso ndi dzina lakuti Isiraeli, ndipo mtumwi Petulo amadziwikanso kuti Simoni. (Genesis 49:1, 2; Mateyu 10:2) Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limasonyeza kuti Mikayeli ndi dzina lina la Yesu Khristu, lomwe ankadziwika nalo asanabwere padziko lapansi komanso atabwerera kumwamba. Tiyeni tikambirane malemba angapo omwe amatsimikizira zimenezi.
Mkulu wa Angelo. Mawu a Mulungu amanena kuti Mikayeli ndi “mkulu wa angelo.” (Yuda 9) Mmene dzina lakuti “mkulu wa angelo” limalembedwera zimasonyeza kuti akunena za munthu mmodzi. Zimenezi zikusonyeza pali mngelo mmodzi yekha amene ali ndi udindo umenewu. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti udindo umenewu ndi wa Yesu. Pofotokoza za Yesu Khristu ataukitsidwa, lemba la 1 Atesalonika 4:16 limanena kuti: “Ambuye . . . adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo.” Pa lemba limeneli, mawu a Yesu akufotokozedwa kuti ndi mawu a mkulu wa angelo. Choncho, Baibulo limasonyeza kuti Mikayeli mkulu wa angelo ndi Yesu.
Mtsogoleri wa Gulu Lankhondo. Baibulo limanena kuti “Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. . . . ndi angelo ake.” (Chivumbulutso 12:7) Choncho, Mikayeli ndi Mtsogoleri wa gulu lankhondo la angelo okhulupirika. Buku la Chivumbulutso limatchulanso kuti Yesu ndi Mtsogoleri wa gulu lankhondo la angelo okhulupirika. (Chivumbulutso 19:14-16) Ndipo mtumwi Paulo anatchula za “Ambuye Yesu” ndi “angelo ake amphamvu.” (2 Atesalonika 1:7) Choncho Baibulo limanena za Mikayeli ndi “angelo ake,” ndiponso Yesu ndi “angelo ake.” (Mateyu 13:41; 16:27; 24:31; 1 Petulo 3:22) Popeza Baibulo silisonyeza zoti pali magulu awiri a angelo okhulupirika, lina lotsogoleredwa ndi Mikayeli ndipo lina lotsogoleredwa ndi Yesu, n’zomveka kunena kuti Mikayeli ndi dzina la Yesu Khristu pa udindo umene ali nawo kumwamba.a
a Mfundo zina zosonyeza kuti Mikayeli ndi dzina lina la Mwana wa Mulungu zili m’buku la Samalani Ulosi wa Danieli!, tsamba 204-205, ndiponso m’buku la Chingelezi lakuti Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, tsamba 393-394. Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
-
-
Kodi “Babulo Wamkulu” N’chiyani?Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
-
-
ZAKUMAPETO
Kodi “Babulo Wamkulu” N’chiyani?
M’BUKU la Chivumbulutso muli mawu ambiri okuluwika. (Chivumbulutso 1:1) Mwachitsanzo, limafotokoza za mkazi wina yemwe analembedwa dzina lakuti “Babulo Wamkulu” pamphumi pake. Mkaziyu amamufotokoza kuti wakhala pa ‘makamu a anthu ndi mayiko.’ (Chivumbulutso 17:1, 5, 15) Popeza palibe mkazi aliyense amene angathe kuchita zimenezi, ndiye kuti mawu akuti Babulo Wamkulu ndi okuluwika. Ndiye kodi hule limeneli likuimira chiyani?
-