Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chilango Chimene Chingabale Chipatso cha Mtendere
    Nsanja ya Olonda—1988 | April 15
    • Chilango Chimene Chingabale Chipatso cha Mtendere

      “Chilango chirichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.”​—AHEBRI 12:11.

      1, 2. (a) Molingana ndi Ahebri 12:9-11, kodi nchiyani chimene Mulungu mwachikondi amapereka? (b) Kodi ndi chitsanzo chimodzi chiti cha kupereka chilango, ndipo kodi nchiyani chimene chingatulukemo mwa ichi?

      TALINGALIRANI kumbuyo m’masiku a ubwana wanu. Kodi mungakumbukire makolo anu akukupatsani chilango? Ambiri a ife tingatero. Mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito chimenecho monga chitsanzo pamene anali kuchitira ndemanga pa chilango chochokera kwa Mulungu, monga mmene timaŵerengera pa Ahebri 12:9-11.

      2 Chilango cha Mulungu cha utate, chimene chingayambukire miyoyo yathu yauzimu, chingatenge mitundu yambiri. Umodzi uli makonzedwe ake akuchotsa mu mpingo Wachikristu munthu yemwe sakufunanso kukhala mwa miyezo ya Mulungu, kapena amene amakana kuchita tero. Munthu yemwe amapatsidwa nthyole motero kapena kulangidwa angalape ndi kutembenuka. M’kachitidweka, mpingo wa okhulupirira umalangidwanso popeza kuti amaphunzira kufunika kwa kumamatira ku miyezo yapamwamba ya Mulungu.​—1 Timoteo 1:20.

      3. Ndimotani mmene ena amachitira ku lingaliro la kuchotsa?

      3 ‘Koma,’ winawake angafunse, ‘kodi sichiri chowawa kuchotsa ndipo kenaka kukana kulankhula ndi munthu wochotsedwayo?’ Kawonedwe kotereka kanabuka mu mlandu wa posachedwapa wa mu bwalo lamilandu wokhudza mkazi yemwe analeredwa ndi makolo omwe anali Mboni za Yehova. Makolo ake anali atachotsedwa, iye sanatero, koma iye anadzilekanitsa mwaufulu iyemwini mwa kulemba kalata ya kuchoka mu mpingo. Mwatsatanetsatane, mpingo unangodziŵitsidwa kuti sanalinso mmodzi wa Mboni za Yehova. Iye anachokapo ndi kupita kutali, koma zaka zingapo pambuyo pake anabwereranso ndi kupeza kuti Mboni za kumaloko sizinakhoze kulankhula naye. Chotero anatenga nkhaniyo ku bwalo lamilandu. Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo, ndipo kodi ichi chikanakuyambukirani motani? Kuti timvetsetse nkhaniyi bwino, tiyeni tiwone chimene Baibulo limanena ponena za nkhani yokhudzidwayi ya kuchotsa.

      Nchifukwa Ninji Kaimidwe Kamphamvu Kameneka?

      4. Kodi nchiyani chimene chimachitika mwa kamodzikamodzi ndi ena mu mpingo? (Agalatiya 6:1; Yuda 23)

      4 Akristu owona ambiri amachirikiza Mulungu mokhulupirika ndi malamulo ake olungama. (1 Atesalonika 1:2-7; Ahebri 6:10) Mwakamodzikamodzi, ngakhale kuli tero, munthu amapatuka kuchoka pa njira ya chowonadi. Mwachitsanzo, mosasamala kanthu za chithandizo chochokera kwa akulu Achikristu, iye mosalapa angawukire malamulo a Mulungu. Kapena iye angakane chikhulupiriro mwa kuphunzitsa ziphunzitso zabodza kapena mwakudzilekanitsa iyemwini kuchoka mu mpingo. Kenaka kodi nchiyani chimene chingachitike? Zinthu zoterozo zinachitika ngakhale pamene atumwi anali ndi moyo; ndipo, tiyeni tiwone chimene iwo analemba ponena za ichi.

      5, 6. (a) Tiri ndi uphungu wanzeru wotani wonena za kuchita ndi awo amene amachita machimo aakulu ndipo ali osalapa? (Mateyu 18:17) (b) Kodi ndi mafunso otani amene tikuyang’anizana nawo?

      5 Pamene mwamuna wina mu Korinto anali wochita makhalidwe oipa wosalapa, Paulo anawuza mpingo kuti: “Musayanjane naye, ngati munthu wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kudya naye wotere, iai.” (1 Akorinto 5:11-13) Chotero chinkachitikanso kwa ampatuko, monga ngati Huminayo: “Munthu wopatukira chikhulupiriro, utamchenjeza kamodzi ndi kaŵiri, umkanize, podziŵa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa, nakhala wodzitsutsa yekha.” (Tito 3:10, 11; 1 Timoteo 1:19, 20) Kupewa koteroko kukakhala koyenera, nakonso, kaamba ka aliyense amene amakana mpingo: “Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti awonekere kuti sali onse a ife.”​—1 Yohane 2:18, 19.

      6 Mwachiyembekezo, wotereyu adzalapa kotero kuti angakhoze kulandiridwanso. (Machitidwe 3:19) Koma pa nthaŵiyo, kodi Akristu angakhale ndi kuyanjana naye kokhala ndi polekezera, kapena kodi kumupewa iye kosamalitsa kuli koyenerera? Ngati ndi tero, nchifukwa ninji?

      Kulekanitsidwa Kotheratu?

      7. Ndimotani mmene mkhalidwe wathu umasiyanirana ponena za magulu aŵiri a ochimwa?

      7 Akristu samadziika iwo eni kudzipatula kwa anthu. Timakhala ndi kuyanjana kwa nthaŵi zonse ndi anansi, ogwira nawo ntchito, ophunzira nawo, ndi ena, ndi kuchitira umboni kwa iwo ngakhale kuti ena ali ‘adama, aumbombo, olanda, kapena olambira mafano.’ Paulo analemba kuti sitingawapewe iwo kotheratu, ‘pakuti ngati ndi tero tikayenera kutulukamo m’dziko.’ Ngakhale kuli tero, iye analangiza kuti ichi chikayenera kukhala chosiyana ndi “mbale” yemwe akakhala tero: “Musayanjane naye wotchedwa mbale [amene abwerera ku njira zoterozo], kungakhale kudya naye, iai.”​—1 Akorinto 5:9-11; Marko 2:13-17.

      8. Kodi ndi uphungu wotani umene mtumwi Yohane anapereka pa kupewa?

      8 M’zolembera za mtumwi Yohane, timapezamo uphungu wofanana womwe umagogomezera mmene Akristu amafunikira kupewa oterowo mosamalitsa: “Yense wakupitirira, wosakhala m’chiphunzitso cha Kristu, alibe Mulungu . . . Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musamlankhule. Pakuti iye wakumlankhula [Chigriki, khaiʹro] ayanjana nazo ntchito zake zoipa.”a​—2 Yohane 9-11.

      9, 10. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa awo akuswa lamulo osalapa mu Israyeli, ndipo nchifukwa ninji? (b) Ndimotani mmene tingadzimverere ponena za makonzedwewo lerolino a kuchita ndi munthu wochotsedwa chifukwa cha chimo losalapa? (2 Petro 2:20-22)

      9 Nchifukwa ninji kaimidwe kolimba kotereka kali koyenera ngakhale lerolino? Chabwino, tangowunikira pa kulekanitsidwa kotheratu koikidwa mu lamulo la Mulungu kwa Israyeli. M’nkhani zosiyanasiyana zazikulu kwenikweni, olakwira lamulo mwadala anali kuphedwa. (Levitiko 20:10; Numeri 15:30, 31) Pamene chimenecho chinachitika, ena, ngakhale achibale, sanali okhoza kulankhula ndi munthu wakufa wolakwira lamuloyo. (Levitiko 19:1-4; Deuteronomo 13:1-5; 17:1-7) Ngakhale kuti Aisrayeli okhulupirika kumbuyoko anali anthu olongosoka okhala ndi zikhumbo zonga zathu, iwo anadziŵa kuti Mulungu ali wachilungamo ndi wachikondi ndi kuti Lamulo lake linachinjiriza kuyera kwa makhalidwe awo abwino ndi auzimu. Chotero anakhoza kulandira kuti kakonzedwe kake ka kuchotsa ochita zoipa kanali mwalamulo chinthu chabwino ndi cholondola.​—Yobu 34:10-12.

      10 Tingakhaledi mofananamo otsimikizira kuti makonzedwe a Mulungu akuti Akristu akane kuyanjana ndi winawake amene anachotsedwa kaamba ka chimo losalapira ali chinjirizo lanzeru kwa ife. “Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa.” (1 Akorinto 5:7) Mwakupewanso anthu omwe mwadala adzilekanitsa iwo eni, Akristu amachinjirizidwa ku kawonedwe koipa kothekera, kosayamikira, kapena ngakhale kampatuko.​—Ahebri 12:15, 16.

      Bwanji Ponena za Achibale?

      11, 12. (a) Kodi nchiyani chomwe chinali chotulukapo pa achibale a chiIsrayeli pamene ochita choipa analekanitsidwa? (b) Chitirani chitsanzo mapindu a kumvera.

      11 Mulungu motsimikizirika amazindikira kuti kunyamula malamulo ake olungama onena za kuchotsa ochita zolakwa kaŵirikaŵiri kumaphatikizapo ndipo kumayambukira achibale. Monga mmene kwatchulidwira pamwambapo, pamene m’Israyeli wochita zoipa anaphedwa, panalibe kuyanjana kwa banja komwe kunali kothekera. M’chenicheni, ngati mwana wamwamuna anali woledzera ndi wosusuka, makolo ake ankamubweretsa iye pamaso pa oŵeruza, ndipo ngati iye anali wosalapa, makolowo ankagawanamo m’kumupha kwachilungamo, ‘kuti achotse choipacho pakati pa Israyeli.’ (Deuteronomo 21:18-21) Mungayamikire kuti ichi sichinali chopepuka kwa iwo. Tangolingalirani, inunso, mmene abale a wochita zoipayo, alongo, kapena agogo anadzimverera. Komabe, kuika kwawo chikhulupiriro mwa Mulungu wawo wa chilungamo patsogolo pa chikondi cha banja kukakhala chopulumutsa moyo kwa iwo.

      12 Kumbukirani nkhani ya Kora, amene anali mtsogoleri mkuchimwira utsogoleri wa Mulungu wodzera mwa Mose. M’chilungamo chake changwiro, Yehova anawona kuti Kora akafunikira kufa. Koma okhulupirika onse analangizidwa kuti: “Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kawo kalikonse, mungawonongeke m’zochimwa zawo zonse.” Achibale omwe sanakhoze kulandira chenjezo la Mulungu anafa ndi opandukawo. Koma ena a achibale a Kora anasankha mwanzeru kukhala achikhulupiriro kwa Yehova, chimene chinapulumutsa miyoyo yawo ndi kutsogolera ku mtsogolo modalitsika.​—Numeri 16:16-33; 26:9-11; 2 Mbiri 20:19.

      13. Ndimotani mmene Akristu okhulupirika akavomerezera ngati chiwalo chapafupi cha banja chachotsedwa kapena kudzilekanitsa?

      13 Kuchotsedwa mu mpingo Wachikristu sikumaphatikizapo imfa ya mwamsanga, chotero mathayo a banja amapitirizabe. Chotero, munthu amene wachotsedwa kapena yemwe wadzilekanitsa iyemwini angapitirizebe kukhala panyumba ndi mkazi wake Wachikristu ndi ana ake achikhulupiriro. Ulemu kaamba ka ziŵeruzo za Mulungu ndi kachitidwe ka mpingo kudzasonkhezera mkazi ndi ana kuzindikira kuti mwanjira yake, iye anasintha chomangira chauzimu chomwe chinalipo pakati pawo. Komabe, popeza kuti kuchotsedwa kwake sikuthetsa chomangira chakuthupi kapena unansi wa ukwati, chikondi ndi zochita za banja za nthaŵi zonse zikapitirizabe.

      14. Kodi ndi uphungu waumulungu wotani umene uyenera kusonkhezera kugwirizana kwathu ndi wachibale wochotsedwa kapena wodzilekanitsa wokhala kunja kwa banja lachifupi?

      14 Mkhalidwe uli wosiyana ngati wochotsedwayo kapena wodzilekanitsayo ali wachibale wokhala kunja kwa banja ndi nyumba. Chingakhale chothekera kukhala chifupifupi ndi kusagwirizana kulikonse ndi wachibaleyo. Ngakhale ngati panali nkhani zina za banja zofunikira kukumana, ichi ndithudi chikafunikira kuchepetsedwa kwambiri, m’chigwirizano ndi prinsipulo la umulungu lakuti: “Musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira [kapena wa liwongo la chimo lina lalikulu], . . . kungakhale kudya naye wotere, iai.”​—1 Akorinto 5:11.

      15. Ndimotani mmene achibale angalamulire ziyambukiro za malingaliro m’zochitikazi? (Masalmo 15:1-5; Marko 10:29, 30)

      15 Mwachimvekere, ichi chingakhale chovuta chifukwa cha malingaliro ndi mathayo a banja, onga ngati chikondi cha agogo kaamba ka zidzukulu zawo. Komabe, ichi chiri chiyeso cha chikhulupiriro kwa Mulungu, monga momwe chalongosoledwera ndi mlongo wogwidwa mawu pa tsamba 26. Aliyense amene akudzimva wachisoni ndi kuwawa kumene wachibale wochotsedwa wapangitsa angapeze chitonthozo ndi kulimbikitsidwa ndi chitsanzo chosonyezedwa ndi ena a achibale a Kora.​—Masalmo 84:10-12.b

      Chogamulopo cha Bwalo Lamilandu

      16-18. Kodi ndi chigamulo chotani chimene chinafikiridwa mu mlandu wa mu bwalo lamilandu wotchulidwa poyambirirapo, ndipo kodi bwalo lamilandu linapereka lingaliro lowonjezereka lotani?

      16 Inu mungafune kudziŵa chotulukapo cha mulandu wa mu bwalo lamilandu wophatikizapo mkazi yemwe anakalipitsidwa chifukwa chakuti mabwenzi akale anali osakhoza kulankhulana naye pambuyo pa kusankha kwake kutaya chikhulupiriro, kudzilekanitsa iyemwini ndi mpingo.

      17 Mlandu usanapite kukuyesedwa, bwalo lalikulu lamilandu la m’deralo mwachidule linapereka chiŵeruzo motsutsana ndi iye. Chiŵeruzo chimenecho chinazikidwa pamaziko akuti mabwalo a milandu samadziloŵetsa mu nkhani zopereka chilango za tchalitchi. Mkaziyo kenaka anachita apilu. Chiŵeruzo chogwirizana cha bwalo lamilandu lalikulu la apiluc chinazikidwa pamaziko akulu a Kukonzedwanso Koyambirira kwa kuyenera (kwa Malamulo a ku U.S.): “Chifukwa chakuti kachitidwe ka kupeŵa kali mbali ya chikhulupiriro cha Mboni za Yehova, tapeza kuti mbali za ‘kachitidwe kaufulu’ ka Lamulo la mu United States . . . kaletsa [mkaziyo] kupitirizabe. Omwe apatsidwa mlanduwo ali ndi thayo lotetezera mwalamulo kudziloŵetsa m’kachitidwe ka kupeŵa. Mwatsatanetsatane, tigwirizana” ndi chiŵeruzo chapoyambirira cha bwalo lamilandu la kumaloko.

      18 Lingaliro la bwalo lamilandu linapitirizabe kuti: “Kupeŵa kali kachitidwe kochitidwa ndi otsatira a Mboni za Yehova ku kamasuliridwe kawo ka malemba a lamulo, ndipo sitiri aufulu kukonzanso lamulo limenelo. . . . Omwe apatsidwa mlandu ali oyenerera kuchita kachitidwe kaufulu ka zikhulupiriro za chipembedzo chawo. . . . Mabwalo a milandu mwachisawawa samaloŵereramo mosamalitsa mu unansi pakati pa ziwalo (kapena ziwalo zakale) za tchalitchi. Matchalitchi apatsidwa mbali yaikulu pamene apereka chilango ku ziwalo kapena ku ziwalo zakale. Tikuvomerezana ndi kawonedwe ka Woweruza Wamkulu [wakale wa bwalo lamilandu lalikulu la U.S.] Jackson kakuti ‘zochitachita za chipembedzo zimene zimangokhudza kokha ziwalo za chikhulupiriro chake ziyenera kukhala zaufulu​—kukhala chifupifupi zaufulu kwenikweni monga mmene chirichonse chingakhalire.’ . . . Ziwalo za Tchalitchi chimene [mkaziyo] anagamulapo kuleka zamaliza kuti sizikufuna nkomwe kuyanjana ndi iye. Ife tikugwirira ku chimenecho kuti iwo ali aufulu kupanga kusankha kumeneko.”

      19, 20. Nchifukwa ninji munthu wochotsedwa mu mpingo sali wokhoza kupezanso zowonongedwa za ndalama mu bwalo lamilandu?

      19 Bwalo lamilandu la apilu linavomereza kuti ngakhale kuti mkaziyo anadzimva wowawidwa chifukwa chakuti mabwenzi akale asankhapo kusalankhula naye, “kumlola iye kuchira kaamba ka kuvulazika kosayerekezeka kapena kwa malingaliro sikudzaletsa Mboni za Yehova mwalamulo kuchita kachitidwe ka chipembedzo mwaufulu. . . . Kutsimikizirika kwa lamulo kwa kachitidwe kaufulu ka chipembedzo kumafuna kuti chitaganya chilekerere mtundu wa kupweteka kumene [iye] anavutika nako monga mphoto yoyenerera kulipiridwa kuti ichinjirize kuyenera kwa kusiyana kwa chipembedzo kumene nzika zonse zimasangalala nako.” Chigamulo chimenechi, m’chenicheni, chalandira kuchirikiza kokulira kuyambira pamene chinaperekedwa. Tero motani? Mkaziyo pambuyo pake anapempha bwalo lalikulu lamilandu m’dzikolo kumvetsera ku nkhaniyo ndipo mwinamwake kuti asinthe chigamulo chodzetsedwa molimbana ndi iye. Koma mu November 1987, bwalo lamilandu lalikulu la United States linakana kuchita tero.

      20 Chotero, mlandu wofunika kwambiriwo unatsimikizira kuti munthu wochotsedwa kapena wodzilekanitsa sangachotsepo kuvulazika kuchokera kwa Mboni za Yehova mu bwalo lamilandu la lamulo kaamba ka kupeŵedwa.d Popeza kuti mpingo unali kuyankha ku zitsogozo zangwiro zimene tonsefe tingaŵerenge m’Mawu a Mulungu, ndi kuwagwiritsira ntchito, munthuyo akukumva kutaikiridwa kobweretsedwa pa iye ndi mwamunayo kapena kachitidwe ka iyemwini.

      Chilango​—Mapindu Ambiri

      21. Nchifukwa ninji kukhazikika kuli kofunika kulinga ku kuchotsa?

      21 Anthu ena akunja, pambuyo pa kumvetsera ku kuchotsedwa, amakhala okhoterera ku kumverera chisoni ochita choipa amene sangakhale okhoza kulankhuzana ndi ziwalo za mpingo Wachikristu. Koma kodi kumvera chisoni koteroko sikuchitidwa molakwa? Talingalirani madalitso okulira amene ochita zoipa ndi ena angalandire.

      22, 23. Chitirani chitsanzo kufunika ndi phindu la kumvera Mulungu m’kawonedwe kathu ka anthu ochotsedwa.

      22 Mwachitsanzo, pa tsamba 26 tawona ndemanga ya Lynette yonena za chosankha chake cha ‘kudzilekanitsa iyemwini kotheratu ku kuyanjana kulikonse’ ndi mng’ono wake wochotsedwa Margaret. Iye ndi achibale ake Achikristu ‘anakhulupirira kuti njira ya Yehova iri yabwino koposa.’ Ndipo iridi!

      23 Mng’ono wa Lynette pambuyo pake anamuuza iye kuti: ‘Ngati ukanawona kuchotsedwako mopepuka, ndikudziŵa kuti sindikanatenga kaimidwe kulinga ku kubwezeredwanso mwamsanga monga mmene ndachitira. Kuchotsedwa kotheratu kuchokera kwa okondedwa ndi kuyanjana kwathithithi ndi mpingo kunapanga chikhumbo champhamvu cha kulapa. Ndinazindikira kokha mmene njira yanga inaliri yolakwika ndi mmene kunaliri kolakwika kutembenukira Yehova.’

      24. Ndimotani mmene kuyankha kwa mlongo mmodzi kukuchotsedwa kunamuyambukirira iye ndi ena?

      24 Mu mlandu wina, makolo a Laurie anachotsedwa. Komabe iye anati: ‘Kuyanjana kwanga ndi iwo sikunaleke koma kunawonjezekabe. Pamene nthaŵi inapitiriza, ndinadzakhala wofooka mopitirizabe. Ndinafika ku nsonga ya kusapezeka ngakhale pa misonkhano.’ Kenaka iye anaŵerenga nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi 15, 1982, imene inagogomezera uphungu wa pa 1 Akorinto 5:11-13 ndi 2 Yohane 9-11. “Chinali monga kuti golobo ya magetsi inayatsidwa pa ine,” iye analemba tero. ‘Ndinadziŵa kuti ndikafunikira kupanga masinthidwe ena. Ndimamvetsetsa bwino lomwe tsopano tanthauzo la Mateyu 10:34-36. Chosankha changa sichinali chinthu chopepuka kaamba ka banja langa kuchitenga, kwa mwana wanga wa mwamuna, wa zaka zisanu, iye ali mnyamata yekha, ndipo anamkonda iye kwabasi.’ Chikuyembekezeredwa kuti kusowa kuyanjana koteroko kudzakhudza mitima ya makolo, monga mmene kunachitira kwa Margaret. Chikhalirechobe, chilango chophatikizidwapo chinathandiza Laurie: ‘Ndabwereranso kunja mu utumiki wa m’munda. Ukwati wanga ndi banja ziri zolimba kwambiri chifukwa cha kusintha kwanga, ndipo ine ndirinso tero.’

      25. Kodi ndi kawonedwe kotani kamene munthu wobwezeretsedwa anali nako ka chilango cha Mulungu?

      25 Kapena talingalirani kudzimva kwa wina amene anachotsedwa ndipo pambuyo pake anabwezeretsedwanso. Sandi analemba kuti: ‘Ndikufuna kukuyamikirani kaamba ka nkhani zothandiza kwenikweni ndi zophunzitsa [zotchulidwa pamwambapo] pa kudzudzula ndi kuchotsa. Ndiri wachimwemwe kuti Yehova amakonda anthu ake mokwanira ndi kuwona kuti gulu lake likusungidwa loyera. Chimene chingawonekere kukhala chowawa kwa akunja chiri ponse paŵiri choyenera ndipo kwenikweni chinthu cha chikondi kuchichita. Ndiri woyamikira kuti atate wathu wa kumwamba ali Mulungu wachikondi ndi wachikhululukiro.’

      26. Kodi ndi chipatso cholungama chotani chimene chingatulukepo kuchokera ku kulandira chilango? (Masalmo 94:10, 12)

      26 Chotero Mulungu wathu amene amafuna kuti wochita zoipa wosalapa achotsedwe mu mpingo amasonyezanso chikondi kuti wochita zolakwa angabwezeretsedwe mu mpingo ngati walapa ndi kutembenuka. (Anthu odzilekanitsa angafunse mofananamo kuti akhalenso mbali ya mpingo kachiŵirinso.) Pambuyo pake iye angatonthozedwe ndi Akristu omwe adzadziŵikitsanso chikondi chawo kaamba ka iye. (2 Akorinto 2:5-11; 7:8-13) Zowona, chiri monga mmene Paulo analembera kuti: “Chilango chirichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵeretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.”​—Ahebri 12:11.

      [Mawu a M’munsi]

      a Yohane pano anagwiritsira ntchito khaiʹro, komwe kunalinso kupatsa moni konga ngati “tikulandirani” kapena “tikuwoneni.” (Machitidwe 15:23; Mateyu 28:9) Iye sanagwiritsire ntchito a·spaʹzo·mai (monga mu versi 13), imene imatanthauza “kukumbatirana, mwakutero kupereka moni, kulonjera” ndipo chikanatanthauza kupatsa moni kotentha, ngakhale ndi kukupatirana. (Luka 10:4; 11:43; Machitidwe 20:1, 37; 1 Atesalonika 5:26) Chotero chitsogozo cha pa 2 Yohane 11 chikatanthauza bwino lomwe kusanena ngakhale “tikuwoneni” kwa oterewa.​—Onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 1986, tsamba 30.

      b Kaamba ka kukambitsirana kwa kuchotsedwa kwa wachibale, onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982, masamba 26-31.

      c 819 F.2d 875 (9th Cir. 1987).

      d Ngakhale kuti anthu osiyanasiyana apereka milandu ku bwalo lamilandu, palibe bwalo lamilandu lomwe lapereka chiŵeruzo motsutsana ndi Mboni za Yehova pa kachitidwe kawo kozikidwa m’Baibulo ka kupeŵa.

      Nsonga Zofunikira Kukumbukira

      ◻ Kodi ndi m’njira yotani mmene kuchotsedwa kungakhalire m’chitidwe wopereka chilango?

      ◻ Nchifukwa ninji mkhalidwe wa Mkristu kulinga kwa anthu ochotsedwa umasiyana ndi mkhalidwe wake kulinga kwa anthu ochimwa m’dziko?

      ◻ Kodi ndi zitsogozo zotani za Malemba zimene ziyenera kusungidwa m’malingaliro ngakhale kuti wachibale wachotsedwa?

      ◻ Kodi bwalo lamilandu la apilu linafikira mapeto otani mu mlandu womwe unabweretsedwa ndi munthu wodzilekanitsa?

      ◻ Kodi nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera ku kalongosoledwe kaumwini ponena za kuchotsedwa?

      [Mawu Otsindika patsamba 26]

      “Kudzilekanitsa ife eni kotheratu ku kuyanjana kulikonse ndi [mng’ono wanga wochotsedwa] Margaret kunayesa chikhulupiriro chathu ku makonzedwe a Yehova. Kunapatsa mwaŵi ku banja lathu kusonyeza kuti timakhulupiriradi kuti njira ya Yehova iri yabwino koposa.”​—Lynette.

      [Bokosi patsamba 30]

      Kuchotsa​—Kuli ndi Ziyambukiro Zotani?

      Wodziŵa za mbiri yakale wa Chingelezi Edward Gibbon analemba ponena za kulongosoka ndi zotulukapo za kuchotsedwa chifupifupi ndi nthaŵi za atumwi:

      “Kuli kuyenera kosakaikira kwa chitaganya chirichonse kuchotsa m’chigwirizano chake ndi mapindu otero pakati pa ziwalo zake amene akana kapena kulakwira malamulo amenewo omwe akhazikitsidwa ndi lamulo la onse. . . . Zotulukapo za kuchotsedwa zinali zosakhalitsa [pa dziko lapansi] kuphatikizaponso ndi nkhani yauzimu. Mkristu amene kachitidweka kanaperekedwako analandidwa mbali iriyonse ya kuchita zopereka za chikhulupiriro. Mathayo ponse paŵiri a chipembedzo ndi ubwenzi wamseri unathetsedwa.”

  • Kodi Mumakumbukira?
    Nsanja ya Olonda—1988 | April 15
    • Kodi Mumakumbukira?

      Kodi mwasangalala kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, onani ngati mungakhoze kuyankha mafunso otsatirawa:

      ◻ Kodi nchiyani chimene chiri mutu wa kulengeza kwamakono kwa m’Baibulo?

      Mutu wa uthenga wa alengezi owona lerolino uli mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu m’manja mwa wolamulira wake woikidwa, Yesu Kristu. Iwo umaphatikizapo chowonadi chonse chimene Yesu analankhula ndi chimene ophunzira ake anachilemba. (Mateyu 24:14; 28:19, 20)​—1/1, tsamba 4.

      ◻ Nchifukwa ninji chiri choyenerera kupitirizabe kulalikira mbiri yabwino m’magawo mmene muli zotulukapo zochepa kapena kulibiretu?

      Yehova, kupyolera mwa Kristu Yesu, walamulira kuti ‘mbiri yabwino imeneyi ilalikidwe m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu.’ (Mateyu 24:14, NW) Pamene anthu akana kumvetsera, ichi chimatipatsa ife mwaŵi wosonyeza kuzama kwa chikondi chathu ndi kudzipereka kwa Yehova mwa kuumirira kuchita chimene chiri chabwino. Ndiponso, chikondi chathu chimatisonkhezera ife kuchenjeza anansi athu ponena za chimene mtsogolo mwasunga kaamba ka mtundu wa anthu. (1 Yohane 5:3; 2 Timoteo 4:2)​—1/1, tsamba 26.

      ◻ Ndi mapindu otani amene utumiki wa nthaŵi zonse umabweretsa kwa olalikira Ufumu ambiri?

      Umawathandiza iwo kukulitsa mokwanira koposa chipatso cha mzimu, kusonyeza chikondi chochulukira cha anthu, kukhala okhutiritsa kwenikweni mu utumiki, ndi kukhulupirira Yehova ku mlingo wokulira. Chotero, iwo amasangalala ndi unansi wa thithithi ndi Yehova.​—1/15, tsamba 26.

      ◻ Ndi ku chitsogozo chiti ndi chifuno cha Mulungu kumene olemba Baibulo onse analoza mosasamala kanthu za kusiyana kwawo m’kaperekedwe?

      Iwo onse anasonyeza chimene Yehova Mulungu adzachita kupangitsa mtundu wa anthu kukhala wachimwemwe ndiponso chimene munthu aliyense payekha ayenera kuchita ndi cholinga chofuna kulandira chivomerezo cha Mulungu.​—2/1, tsamba 7.

      ◻ Ndi ziti zimene ziri mphatso zina ndi mapindu a kukhala owona mtima?

      Mkhalidwe wa kukhulupirira ndi kudalira umakulitsidwa, kutsogolera ku mkhalidwe waumoyo ndi maunansi. Kuwona mtima kumathandiziranso kukhala ndi chikumbumtima choyera, ndipo kumapereka mtendere wa maganizo, kotero kuti wina angayang’anizane ndi ena popanda mantha akuchititsidwa manyazi. (Ahebri 9:14; 1 Timoteo 1:19)​—2/15, tsamba 7.

      ◻ Ndi mapemphero andani amene Mulungu wamphamvuyonse amamva ndi kuyankha?

      Yehova amamva mapemphero operekedwa kwa iye kupyolera mu ngalande yoyenera, Yesu Kristu; mu mkhalidwe wabwino; ndipo ndi cholinga chabwino cha maganizo ndi mtima. Mulungu amayankha mapemphero oterowo mogwirizana ndi chifuno chake chaumulungu ndipo pa nthaŵi yake yosankhidwa.​—3/15, tsamba 7.

      ◻ Ndi chochitika chofunika chotani chimene chinawoneka mu chaka cha 20 cha kulamulira kwa Mfumu Aretasasta (455 B.C.E.)?

      Chilolezo chinaperekedwa kwa Nehemiya kubwerera ndi kukamanganso Yerusalemu ndi malinga ake. Lamulo limeneli linali chiyambi cha “milungu makumi asanu ndi aŵiri” a zaka za ulosi wa Danieli, kulozera kutsogolo ku kuwoneka kwa Yesu monga “Mesiya Mtsogoleri” pa nthaŵi yake m’chaka cha 29 C.E. (Danieli 9:24, 25; Nehemiya 1:1; 2:1-9)​—3/15, masamba 28, 29.

      ◻ Ndimotani mmene mavuto abanja amasamaliridwira bwino koposa?

      M’chikondi, popeza Baibulo limapatsa uphungu kuti, “Zanu zonse zichitike m’chikondi.” Ndiponso, “Chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” (1 Akorinto 16:14; 1 Petro 4:8) Ichi chiyenera kukhala chikondi chozama chomwe chiri chofunitsitsa kunyalanyaza kupanda ungwiro kwa ziwalo zina za banja zomwe mwa njira ina yake zingakwiitse kapena kukalipitsa ena.​—4/1, masamba 6, 7.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena