Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Maulosi Onse a M’baibulo Amakwaniritsidwa
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 1
    • Maulosi Onse a M’baibulo Amakwaniritsidwa

      “Pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe.”​—YOSWA 23:14.

      KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? M’nthawi yakale, zimene ankanena olosera ambiri sizinkakwaniritsidwa ndipo n’chimodzimodzinso masiku ano. Anthu olosera amayesa kufufuza kuti adziwe zam’tsogolo potengera mmene zinthu zilili pa nthawiyo. Koma maulosi a m’Baibulo amafotokoza zinthu mwatsatanetsatane ndipo nthawi zonse amakwaniritsidwa, ngakhale zitakhala kuti zinthuzo zinanenedwa kutatsala zaka zambirimbiri kuti zichitike.​—Yesaya 46:10.

      CHITSANZO: M’zaka za m’ma 500 B.C.E., mneneri Danieli anaona masomphenya amene ananeneratu kuti ufumu wa Mediya ndi Perisiya udzagonjetsedwa ndi ufumu wa Girisi. Masomphenyawa anasonyezanso kuti mfumu ya Girisi ‘ikadzangokhala yamphamvu’ nthawi yomweyo ‘idzathyoledwa.’ Kodi ndani amene anali kudzalowa m’malo mwake? Danieli analemba kuti: “Pali maufumu anayi amene adzauke mu mtundu wake, koma sadzakhala ndi mphamvu ngati zake.”​—Danieli 8:5-8, 20-22.

      ZIMENE AKATSWIRI A MBIRI YAKALE ANENA: Patapita zaka zoposa 200 kuchokera m’nthawi ya Danieli, Alekizanda Wamkulu anakhala mfumu ya Girisi. Patangotha zaka 10, Alekizanda anagonjetsa ufumu wa Mediya ndi Perisiya ndipo ulamuliro wake unafika mpaka kum’tsinje wa Indase (kumene masiku ano ndi ku Pakistan). Koma ali ndi zaka 32 anamwalira mwadzidzidzi. Kenako zotsatira za nkhondo imene inachitikira m’mudzi wa Isasi ku Asia Minor zinachititsa kuti ufumu wa Girisi ugawikane. Anthu anayi amene anapambana pa nkhondoyi anagawana Ufumu wa Girisi. Komabe palibe amene anafanana mphamvu ndi Alekizanda.

      KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi palinso buku lina limene maulosi ake amakwaniritsidwa ngati Baibulo? Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?

      [Mawu Otsindika patsamba 4]

      “M’Baibulo muli maulosi . . . ambirimbiri moti n’zosatheka kuti maulosi onsewa akwaniritsidwe mwangozi.”​—A LAWYER EXAMINES THE BIBLE, LOLEMBEDWA NDI IRWIN H. LINTON

      [Mawu a Chithunzi patsamba 4]

      © Robert Harding Picture Library/​SuperStock

  • Nkhani Zomwe Zili M’baibulo Sinthano Chabe
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 1
    • Nkhani Zomwe Zili M’baibulo Sinthano Chabe

      “Ndafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi.”​—LUKA 1:3.

      KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? Nkhani zimene zimafotokozedwa m’mabuku a nthano zimakhala zoti sizinachitikedi. Mabukuwa satchulanso malo enieni amene zinthu zinachitikira, nthawi ngakhale mayina a anthu a m’mbiri yakale. Koma m’Baibulo muli nkhani zofotokozedwa mwatsatanetsatane ndipo zimenezi zimathandiza owerenga kukhulupirira kuti zimene Baibulo limanena “ndi choonadi chokhachokha.”​—Salimo 119:160.

      CHITSANZO: Baibulo limanena kuti “Nebukadinezara mfumu ya Babulo, . . . anatengera Yehoyakini [mfumu ya Yuda] ku Babulo.” Kenako “Evili-merodaki mfumu ya Babulo anakhala mfumu, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya Yuda ndi kumutulutsa m’ndende.” Komanso “tsiku lililonse [Yehoyakini] ankapatsidwa chakudya kuchokera kwa mfumuyo, masiku onse a moyo wake.”​—2 Mafumu 24:11, 15; 25:27-30.

      ZIMENE AKATSWIRI OFUFUZA ZINTHU ZAKALE APEZA: M’mabwinja a Babulo wakale, akatswiri ofukula zinthu zakale anapeza makalata a boma omwe analembedwa pa nthawi ya ulamuliro wa Nebukadinezara Wachiwiri. M’makalatawa analembamo zinthu zimene zinkaperekedwa kwa akaidi komanso anthu ena amene ankakhala kunyumba yachifumu. Ena mwa anthu amene anatchulidwa m’makalatawa anali “Yaukini [Yehoyakini],” amene anali “mfumu ya Yahudi (Yuda),” pamodzi ndi banja lake. Nanga kodi panapezeka umboni uliwonse wosonyeza kuti Evili-merodaki, yemwe analowa m’malo mwa Nebukadinezara, anakhalakodi? Mphika wa maluwa umene unapezedwa pafupi ndi mzinda wa Susa unali ndi mawu akuti: “Nyumba yachifumu ya Amil-Marduk [Evili-merodaki], Mfumu ya Babulo, mwana wa Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo.”

      KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi pali buku lililonse lachipembedzo limene limafotokoza mbiri yakale molondola ngati mmene Baibulo limachitira? Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?

      [Mawu Otsindika patsamba 5]

      “Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya nthawi imene zinthu zinachitika komanso malo amene zinachitikira, n’zolondola ndiponso zodalirika kuposa zimene mabuku ena akale amanena.”​—A SCIENTIFIC INVESTIGATION OF THE OLD TESTAMENT, LOLEMBEDWA NDI ROBERT D. WILSON

      [Chithunzi patsamba 5]

      Chikalata cha ku Babulo chimene chinatchula Mfumu Yehoyakini ya Yuda

      [Mawu a Chithunzi patsamba 5]

      © bpk, Berlin/​Vorderasiatisches Museum, SMB/​Olaf M. Tessmer/​Art Resource, NY

  • Baibulo Ndi Lolondola pa Nkhani Zaukhondo
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 1
    • Baibulo Ndi Lolondola pa Nkhani Zaukhondo

      “Kodi sindinakulembere zinthu zolangiza ndi zophunzitsa, n’cholinga chakuti ndikusonyeze kudalirika kwa mawu oona, kuti uthe kubwezera mawu oonadi?”​—MIYAMBO 22:20, 21.

      KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? Mabuku akale ambiri ali ndi mfundo zosadalirika zomwenso ndi zosagwirizana ndi njira zamakono zaukhondo. Masiku anonso nthawi ndi nthawi olemba mabuku amafunika kusintha zinthu zina ndi zina m’mabuku awo kuti zigwirizane ndi mfundo zimene zangotulukiridwa kumene. Koma Baibulo, popeza kuti linalembedwa ndi Mlengi, Mawu ake “amakhala kosatha.”​—1 Petulo 1:25.

      CHITSANZO: M’Chilamulo cha Mose, Aisiraeli analamulidwa kuti akafuna kudzithandiza azipita kumalo amene ankakhala “kunja kwa msasa” ndipo akamaliza azikwirira zonyansazo. (Deuteronomo 23:12, 13) Komanso Aisiraeli akakhudza nyama yakufa kapena mtembo wa munthu ankayenera kuchapa zovala zawo. (Levitiko 11:27, 28; Numeri 19:14-16) Pa nthawi imeneyo odwala khate ankakhala kwaokha mpaka wansembe atatsimikizira kuti khate lawo latha ndipo sangapatsirenso anthu ena.​—Levitiko 13:1-8.

      ZIMENE A ZAUMOYO APEZA: Kukhala ndi zimbudzi, kusamba m’manja, komanso kuika kwaokha anthu odwala matenda opatsirana, ndi njira zothandiza kwambiri kuteteza matenda. Ngati mukukhala pamalo oti palibe zimbudzi pafupi, bungwe lina la ku America loona za kapewedwe ka matenda osiyanasiyana linanena kuti: “Muzipita pamalo a mtunda wamamita 30 kuchokera pamene pali mtsinje, mjigo kapena chitsime, muzikumba n’kudzithandiza ndipo mukamaliza muzikwirira zonyansazo.” (U.S. Centers for Disease Control and Prevention) Malinga ndi zimene Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse limanena, kukhala ndi zimbudzi kumachepetsa matenda otsegula m’mimba. Komanso zaka zosachepera 200 zapitazo, madokotala anazindikira kuti anapatsira matenda anthu odwala ambiri chifukwa chosasamba m’manja atamaliza kugwira anthu amene amwalira. Bungwe la ku America lija linanenanso kuti kusamba m’manja ndi “njira yothandiza kwambiri pa njira zonse zopewera kutenga matenda.” Nanga bwanji za kuika kwaokha anthu akhate komanso odwala matenda ena opatsirana? Posachedwapa, magazini ina inati: “Mliri wa matenda ukangoyamba, kusunga kwaokha anthu amene akudwalawo ndi njira imene imathandiza kuti matenda asafalikire kwa ena.”​—Saudi Medical Journal.

      KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi palinso buku lina lachipembedzo limene mfundo zake zaukhondo zimagwirizana ndi mfundo zimene a zaumoyo apeza masiku ano? Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?

      [Mawu Otsindika patsamba 6]

      “Palibe amene sangachite chidwi akamawerenga malangizo okhudza nkhani zaukhondo amene anaperekedwa m’nthawi ya Mose.”​—MANUAL OF TROPICAL MEDICINE, LOLEMBEDWA NDI DR. ALDO CASTELLANI NDI DR. ALBERT J. CHALMERS

  • Nkhani za M’baibulo N’zogwirizana
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 1
    • Nkhani za M’baibulo N’zogwirizana

      “Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”​—2 PETULO 1:21.

      KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? Nkhani zambiri zofotokoza zinthu zimene zinachitika kale zimatsutsana ngakhale zitakhala kuti zinalembedwa nthawi yofanana. Komanso nthawi zambiri mabuku oti analembedwa ndi anthu osiyana, pamalo osiyana komanso zaka zosiyana sakhala ogwirizana. Komabe, chifukwa choti mabuku onse 66 a m’Baibulo anauziridwa ndi Mulungu, nkhani zake ndi zogwirizana.​—2 Timoteyo 3:16.

      CHITSANZO: Mose, yemwe anali m’busa wa nkhosa cha m’ma 1500 B.C.E., analemba zokhudza “mbewu” imene idzapulumutse anthu. Iye analemba zimenezi m’buku loyambirira la m’Baibulo. Kenako iye analembanso m’buku lomweli kuti mbewuyo idzakhala mbadwa ya Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. (Genesis 3:15; 22:17, 18; 26:24; 28:14) Patadutsa zaka 500, mneneri Natani ananena kuti mbewuyo idzachokera mu mzera wachifumu wa Davide. (2 Samueli 7:12) Patatha zaka 1,000 mtumwi Paulo ananena kuti Yesu limodzi ndi otsatira ake osankhidwa, ndi amene amapanga mbewu imeneyi. (Aroma 1:1-4; Agalatiya 3:16, 29) Ndiyeno chakumapeto kwa nthawi ya atumwi, buku lomaliza la m’Baibulo linalosera kuti ena mwa anthu amene ali mbali ya mbewu ija azidzachitira umboni za Yesu ndipo kenako adzaukitsidwa kupita kumwamba kumene adzalamulire ndi Yesu zaka 1,000. Mbewu imeneyi idzawononga Mdyerekezi ndi kupulumutsa anthu.​—Chivumbulutso 12:17; 20:6-10.

      ZIMENE AKATSWIRI A BAIBULO ANENA: Louis Gaussen atafufuza bwinobwino mabuku onse 66 a m’Baibulo, analemba zosonyeza kuti anachita chidwi kwambiri ndi “kugwirizana kwa nkhani za m’Baibulo, buku limene linalembedwa ndi anthu osiyanasiyana pa zaka 1,500.” Anachitanso chidwi poona kuti anthu amene analemba Baibulo “anali ndi cholinga chimodzi ndipo anayesetsa kuti chikwaniritsidwe ngakhale kuti sankadziwa zonse zokhudza cholingachi. Cholinga chimenechi ndi chokhudza kuwomboledwa kwa mtundu wonse wa anthu kudzera mwa Mwana wa Mulungu.”​—Theopneusty​—The Plenary Inspiration of the Holy Scriptures.

      KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi mungayembekezere kuti buku limene linalembedwa ndi anthu osiyanasiyana okwana 40 kwa zaka 1,500 lingakhale ndi nkhani zogwirizana? Komatu nkhani za m’Baibulo ndi zogwirizana ngakhale kuti linalembedwa ndi anthu 40 pa zaka 1,500. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?

      [Mawu Otsindika patsamba 7]

      “Mabuku onse a m’Baibulo ukawaphatikiza amapanga buku limodzi. . . Padziko lonse lapansi palibenso buku lofanana ndi limeneli.”​—THE PROBLEM OF THE OLD TESTAMENT, LOLEMBEDWA NDI JAMES ORR

  • Baibulo Lili Ndi Malangizo Othandiza
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 1
    • Baibulo Lili Ndi Malangizo Othandiza

      “Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, ndi kuwala kounikira njira yanga.”​—SALIMO 119:105.

      KODI BAIBULO NDI LOSIYANA BWANJI NDI MABUKU ENA? Pali mabuku ambiri otchuka komanso olembedwa mwaluso komabe mabuku amenewa samapereka malangizo othandiza pa moyo wa munthu. Mabuku ambiri a malangizo amafunika kukonzedwanso nthawi ndi nthawi. Koma Baibulo limanena kuti “zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.”​—Aroma 15:4.

      CHITSANZO: Ngakhale kuti cholinga chachikulu cha Baibulo sikupereka malangizo okhudza mmene tingakhalire ndi thanzi labwino, m’Baibulo muli malangizo abwino onena za zimene tingachite kuti tikhale ndi thanzi labwino. Mwachitsanzo Baibulo limanena kuti: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” (Miyambo 14:30) Limachenjezanso kuti: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (Miyambo 18:1) Ndiponso Baibulo limati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

      ZIMENE AKATSWIRI APEZA: Kudekha, kuwolowa manja komanso kukhala ndi mabwenzi abwino kungakuthandizeni kukhala ndi thanzi labwino. Magazini ina inanena kuti: “Azibambo amene amapsa mtima kwambiri amakhala pangozi yoti akhoza kudwala matenda a kufa ziwalo kuposa azibambo amene amaugwira mtima.” (The Journal of the American Medical Association) Pa kafukufuku amene anachitika kwa zaka 10 ku Australia anapeza kuti anthu achikulire amene “ankacheza pafupipafupi ndi anzawo komanso anali ndi anthu owauza nkhani zawo zachinsinsi,” ankakhala ndi moyo wautali. Zotsatira za kafukufuku amene anachitika ku Canada komanso ku America m’chaka cha 2008, zinasonyeza kuti “munthu amene amagwiritsa ntchito ndalama zake pothandiza ena amakhala wosangalala kuposa munthu amene amangogwiritsa ntchito ndalama zake pa zofuna zake.”

      KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi mungakhulupirire malangizo okhudza thanzi labwino opezeka m’buku lomwe linalembedwa zaka zoposa 2,000 zapitazo? Koma monga taonera, Baibulo lili ndi malangizo othandiza ngakhale kuti linalembedwa zaka zoposa 2,000 zapitazo. Kodi umenewu si umboni wosonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera?

      [Mawu Otsindika patsamba 8]

      “Ndimaona kuti Baibulo ndi buku lothandiza kwambiri . . . chifukwa lili ndi malangizo abwino pa nkhani yokhudza mmene munthu angakhalire ndi thanzi labwino.”​—HOWARD KELLY, M.D., MPHUNZITSI WA YUNIVESITE YA ZAMANKHWALA YA JOHNS HOPKINS

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena