Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Satana Alipodi?
    Nsanja ya Olonda—2014 | November 1
    • NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SATANA ALIPODI?

      Kodi Satana Alipodi?

      Chithunzi cha Satana atagwetsedwa kuchokera kumwamba

      Chipilala chomwe chili ku Madrid, m’dziko la Spain, chosonyeza Satana ngati mngelo woipa amene anagwetsedwa padziko lapansi

      “Ndili mwana, ine ndi makolo anga tinkakhala ku El Salvador. Ndikachita mwano, mayi ankakonda kundiuza kuti, ‘Satana abwera kudzakutenga.’ Koma ine ndinkawayankha kuti, ‘Abwere! Ine sindiopa Satana chifukwa ndimakhulupirira Mulungu.’”—ROGELIO.

      Kodi nanunso muli ndi maganizo ofanana ndi a Rogelio? Pa mfundo zomwe zili m’munsizi, ndi iti imene mukuona kuti ndi yolondola?

      • Satana ndi maganizo oipa amene munthu amakhala nawo mumtima mwake.

      • Satana alipodi, koma sachita chidwi kwenikweni ndi zochita za anthufe.

      • Satana ndi mngelo woipa yemwe amachititsa kuti anthu azichita zoipa.

      Ena amaona kuti mfundo yolondola ndi yoyambayo, ena amati yachiwiriyo ndipo ena amati yolondola ndi yomalizayo. Koma kodi kudziwa zoona pa nkhaniyi n’kofunika? Ngati Satana kulibe, ndiye kuti amene amakhulupirira kuti alipo amakhulupirira zabodza. Ngati Satana alipodi koma sachita chidwi kwenikweni ndi zochita za anthufe, ndiye kuti anthu amene amamuopa, amangoopa njokaluzi. Komanso ngati Satana ndi mngelo woipa, yemwe amachititsa kuti anthu azichita zoipa, ndiye kuti ndi woopsa kwambiri kuposa mmene ambiri amaganizira.

      Tiyeni tione zimene Mawu a Mulungu amanena pa mafunso otsatirawa: Kodi Satana ndi ndani? Kodi ndi maganizo oipa amene amakhala mumtima mwa munthu kapena ndi mngelo woipa? Ngati alipodi, kodi ndi woopsa? Nanga mungatani kuti mudziteteze?

  • Kodi Satana Ndi Maganizo Oipa Chabe?
    Nsanja ya Olonda—2014 | November 1
    • Satana akuyang’ana Yobu, yemwe wakumana ndi mavuto

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SATANA ALIPODI?

      Kodi Satana Ndi Maganizo Oipa Chabe?

      Anthu ambiri amaganiza kuti Satana amene amatchulidwa m’Baibulo ndi maganizo oipa chabe amene munthu amakhala nawo mumtima mwake. Koma kodi zimenezi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa? Ngati zimene anthu amaganizazi zili zoona, n’chifukwa chiyani Baibulo limasonyeza kuti Satana analankhulapo ndi Yesu Khristu komanso ndi Mulungu? Tiyeni tione zimene zinachitika.

      SATANA ANALANKHULA NDI YESU

      Yesu atangoyamba kumene utumiki wake, Satana anamuyesa maulendo atatu. Koyamba, anamuuza kuti agwiritse ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa pofuna kuthetsa njala yake. Kachiwiri, anamuuza kuti aike moyo wake pachiswe n’cholinga choti adzionetsere kuti ndi Mwana wa Mulungu. Ndipo kachitatu, anamuuza kuti amupatsa maufumu onse a padziko lapansi ngati atamugwadira kamodzi kokha. Koma Yesu anagwiritsa ntchito Malemba pokana mayesero onsewa.—Mateyu 4:1-11; Luka 4:1-13.

      Kodi pamenepa tingati Yesu ankalankhula ndi ndani? Kodi ankalankhula ndi maganizo oipa amene anali mumtima mwake? Ayi, chifukwatu Malemba amanena kuti Yesu “anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.” (Aheberi 4:15) Baibulo limanenanso kuti: “Iye sanachite tchimo, ndipo m’kamwa mwake simunapezeke chinyengo.” (1 Petulo 2:22) Yesu anakhalabe wokhulupirika ndipo sanachimwe komanso analibe maganizo oipa mumtima mwake. Choncho n’zoonekeratu kuti Yesu sankalankhula ndi maganizo oipa amene anali mumtima mwake. Koma ankalankhula ndi mngelo woipa yemwe ndi Satana.

      Zimene Satana anauza Yesu zimasonyezanso kuti Satanayo alipodi.

      • Kumbukirani kuti Satana anauza Yesu kuti amupatsa maufumu onse a padziko lapansi akamugwadira. (Mateyu 4:8, 9) Zomwe Satana ananenazi sizikanakhala zomveka, zikanakhala kuti Satanayo kulibeko. Komanso Yesu sanatsutse zoti maufumuwa ndi a Satana.

      • Yesu atakana mayeserowa, Satana “anamusiya kufikira nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Zimenezi zikusonyeza kuti Satana si maganizo oipa chabe koma ndi mngelo woipa amene amachititsa anthu kuchita zoipa.

      • Komanso Satana atamusiya Yesu, “kunabwera angelo ndi kuyamba kum’tumikira.” (Mateyu 4:11) Kodi angelowa analidi enieni? Inde. Popeza angelowa ndi enieni, ndiye kuti Satana ndi weniweninso osati maganizo oipa chabe.

      SATANA ANALANKHULA NDI MULUNGU

      Pa nthawi inanso, Satana analankhula ndi Mulungu kawiri ndipo anakambirana zokhudza Yobu, yemwe anali wokhulupirika. Pa maulendo onsewa, Mulungu ananena kuti Yobu ndi wokhulupirika. Koma Satana anati Yobu ankatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. Ananenanso kuti Mulungu ankamudalitsa Yobu n’cholinga choti azimumvera. Pamenepatu Mdyerekezi analankhula ngati kuti iyeyo ankamudziwa bwino Yobu kuposa Mulungu. Pofuna kusonyeza kuti Yobu sankamutumikira chifukwa cha dyera, Yehovaa analola Satana kuti awononge katundu yense wa Yobu, ana ake onse ngakhalenso thanzi lake. Patapita nthawi, zinadziwika kuti Yobu sankatumikira Yehova chifukwa cha dyera ndiponso kuti Satana ndi wabodza. Pamapeto pake Mulungu anadalitsa Yobu chifukwa cha kukhulupirika kwake.—Yobu 1:6-12; 2:1-7.

      Kodi pamenepa tingati Yehova ankalankhula ndi maganizo oipa amene anali mumtima mwake? Ayi, chifukwa Baibulo limati: “Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.” (2 Samueli 22:31) Limanenanso kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova Mulungu.” (Chivumbulutso 4:8) Mawu akuti woyera akutanthauza kuti Yehova ndi wosadetsedwa, wopatulika komanso alibe uchimo uliwonse. Choncho iye sangakhale ndi maganizo oipa mumtima mwake.

      Satana atanena kuti Yobu amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera, Mulungu anamulola kubweretsa mavuto kwa Yobu

      Komabe mwina ena anganene kuti Yobu sanali munthu weniweni, choncho zoti Satana analankhula ndi Mulungu ndi zongopeka. Koma kodi zimenezi n’zomveka? Baibulo limasonyeza kuti Yobu anali munthu weniweni. Mwachitsanzo, lemba la Yakobo 5:7-11 limanena kuti Yobu ndi chitsanzo chabwino kwa Akhristu pa nkhani ya kupirira mayesero. Nkhani ya Yobu imatithandizanso kudziwa kuti Yehova amadalitsa anthu amene amapirira mayesero. Kodi Yobu akanakhala bwanji chitsanzo cholimbikitsa zikanakhala kuti sanali munthu weniweni? Komanso zikanatheka bwanji kuti Satana awononge zinthu zonse za Yobu, zikanakhala kuti Yobuyo sanali munthu weniweni? Kuwonjezera pamenepa, palemba la Ezekieli 14:14, 20, Yobu akutchulidwa pamodzi ndi Nowa komanso Danieli, omwe anali anthu okhulupirika. Nowa ndi Danieli anali anthu enieni. Choncho nayenso Yobu anali munthu weniweni, yemwe ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Ngati Yobu anali munthu weniweni, kodi si pomveka kunena kuti Satana, yemwe ankamuyesa komanso kumuzunza, analinso weniweni?

      Apatu taona kuti Baibulo limasonyeza kuti Satana alipodi. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi Satana ndi woopsa?’

      ZIMENE SATANA AKUCHITA MASIKU ANO

      Yerekezerani kuti gulu la zigawenga lalowa m’dera lanu. Kodi mukuganiza kuti zotsatira zake zingakhale zotani? N’zoonekeratu kuti chitetezo cha m’deralo chikhoza kusokonekera ndipo anthu ena akhoza kuyamba kuchita makhalidwe oipa. Mofanana ndi zimenezi, Baibulo limanena kuti angelo oipa, omwe amatchedwa ziwanda, anaponyedwa padziko lapansi limodzi ndi Satana. Pa nkhaniyi Baibulo limati: “Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. . . . Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:9, 12) Zimenezi ndi zimene zimachititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambiri komanso kuti anthu azichita zinthu zoipa. Taganizirani zinthu zotsatirazi, zomwe timamva pa wailesi, kuwerenga m’nyuzipepala komanso kuonera pa TV.

      • Anthu akuchita makhalidwe oipa kwambiri komanso zinthu zachiwawa, ngakhale kuti mayiko ambiri akuyesetsa kuletsa zinthu zimenezi.

      • Zosangalatsa zolimbikitsa kukhulupirira mizimu zikuchuluka ngakhale kuti makolo ambiri sagwirizana nazo.

      • Ngakhale kuti mayiko ndi mabugwe akuyesetsa kuteteza zinthu zachilengedwe, anthu akupitirizabe kuwononga zinthuzi.

      Anthu ambiri akaganizira zimene zikuchitikazi amavomereza kuti Satana ndi amene akupangitsa zinthu zoipa zimene zikuchitika padzikoli.

      Popeza taona kuti Satana ndi woopsa, mwina mungadzifunse kuti: Kodi ndingatani kuti Satana asamandisocheretse? Funso limeneli ndi lofunika kwambiri ndipo nkhani yotsatira ifotokoza yankho lake.

      a Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

  • Kodi Satana Tizimuopa?
    Nsanja ya Olonda—2014 | November 1
    • NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SATANA ALIPODI?

      Kodi Satana Tizimuopa?

      Mwamuna ndi mkazi wake akuthawira panja pothawa mpweya wa poizoni

      Mpweya umene umatuluka m’makala komanso m’malasha suoneka koma ndi woopsa. Satana ali ngati mpweya umenewu

      Makala komanso malasha amatulutsa mpweya winawake wa poizoni. Mpweyawu suoneka ndiponso sukhala ndi fungo. Komatu anthu ambiri amafa chifukwa chopuma mpweyawu. Komabe sikuti palibe chimene munthu angachite kuti azindikire mpweyawu n’kudziteteza. Mwachitsanzo, ambiri amaika maalamu m’nyumba zawo n’cholinga choti mukakhala mpweyawu, maalamuwo azilira. Zimenezi zimathandiza kuti anthuwo adziteteze.

      Satana tingamuyerekezere ndi mpweya umenewu. Iye saoneka komanso ndi wovuta kumuzindikira. Komatu ndi woopsa kwambiri. Komabe Mulungu angatithandize kuti tithe kulimbana naye. Pali zinthu zotsatirazi zomwe Mulungu watipatsa zimene zingatithandize kuti Satana asatisocheretse.

      Mnyamata akuphunzira Baibulo kenako akupemphera ndiponso kutaya zinthu zokhudzana ndi zamizimu

      Yehova watipatsa zinthu zambiri zimene zingatithandize kuti Satana asatisocheretse

      Anatilenga moti tizitha kusankha zochita. Lemba la Yakobo 4:7 limati: “Tsutsani Mdyerekezi ndipo adzakuthawani.” Ngakhale kuti Satana ali ndi mphamvu, sangatikakamize kuchita zomwe ifeyo sitikufuna. Timasankha tokha kuchita zoipa kapena ayi. Lemba la 1 Petulo 5:9 limati: “Khalani olimba m’chikhulupiriro ndipo mulimbane naye [Mdyerekezi].” Komanso kumbukirani kuti Yesu atakana zofuna za Satana katatu konse, Satanayo anamusiya. (Mateyu 4:11) Choncho ifenso tingathe kukana zofuna za Satana.

      Tingathe kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Lemba la Yakobo 4:8 limatiuza kuti: “Yandikirani Mulungu.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti mukhale naye pa ubwenzi. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Choyamba, muyenera kuphunzira za iye kudzera m’Baibulo. (Yohane 17:3) Zimene mungaphunzire zokhudza Yehova, zingakuthandizeni kuti muyambe kumukonda. Chikondi chimenechi chingapangitse kuti muzichita zimene amafuna. (1 Yohane 5:3) Kodi Yehova amachita chiyani akaona kuti mukuyesetsa kuti mukhale naye pa ubwenzi? Lemba la Yakobo 4:8 lija limanena kuti: “Iyenso adzakuyandikirani.”

      Anatilonjeza kuti adzatiteteza. Lemba la Miyambo 18:10 limati: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.” Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu ayenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, loti Yehova, ngati chithumwa. Koma zikutanthauza kuti anthu amene amakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo amaona kuti dzina lake ndi lofunika, angathe kupemphera kwa iye nthawi iliyonse kuti awathandize.

      Watipatsa zitsanzo. Lemba la Machitidwe 19:19 limanena zimene anthu a ku Efeso anachita atangokhala Akhristu. Limati: “Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana 50,000.”a Akhristu amenewa anawotcha chilichonse chogwirizana ndi zamizimu, ngakhale kuti zinthuzo zinali za ndalama zambiri. Chitsanzo chawochi chingatithandize kwambiri masiku ano. M’dzikoli anthu ambiri amakhulupirira zamizimu komanso nkhani zokhudza ufiti. Kukhala ndi chilichonse chokhudza zamizimu komanso kuchita zamizimu kungapangitse kuti munthu azivutitsidwa ndi ziwanda. Choncho ndi bwino kupewa chilichonse chokhudzana ndi mizimu.—Deuteronomo 18:10-12.

      Rogelio, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, poyamba sankakhulupirira kuti kuli Satana. Koma ali ndi zaka 50 anayamba kukhulupirira kuti Satana alipo. Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti ayambe kukhulupirira zimenezi? Iye anati: “Ndinapeza Baibulo ndipo nditawerenga ndinazindikira kuti Satana alipo. Zimenezi zandithandiza kudziwa zoyenera kuchita kuti Satana asamandisocheretse.”

      “Zimene ndinawerenga m’Baibulo zinandithandiza kuzindikira kuti Satana alipo, ndipo zimenezi zandithandiza kudziwa zoyenera kuchita kuti Satana asamandisocheretse”

      Komatu sikuti Satana azingosocheretsa anthu mpaka kalekale. Baibulo linaneneratu kuti iye “adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule.” (Chivumbulutso 20:10) Popeza Satana ali ndi thupi lauzimu, ataponyedwa pamoto komanso sulufule sangapse. Choncho lembali likungotanthauza kuti iye adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso. Apatu anthu onse amene amakonda Mulungu adzasangalala kwabasi.

      Kodi mungakonde kudzakhalapo pa nthawi imene Satana adzakhale atawonongedwa? Dziwani kuti zimenezi n’zotheka. Panopa mungachite bwino kupitiriza kuphunzira za Yehova kuti mumudziwe bwino.b Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala ndi moyo pa nthawi imene Satana sadzakhalapo. Pa nthawiyi zidzakhala zoona tikamadzanena kuti “kulibe Satana.”

      a Ngati ndalama zasiliva zomwe zatchulidwa palembali zinali madinari achiroma, ndiye kuti zinali ndalama zochuluka kwambiri chifukwa zinali zofanana ndi ndalama zimene anthu 50,000 ankalandira akagwira ntchito tsiku lonse.

      b Kuti mudziwe zambiri zokhudza Satana komanso kukhulupirira mizimu, werengani mutu 10 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mungapemphe wa Mboni aliyense kuti akupatseni bukuli.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena