-
Kodi N’zotheka Mulungu Kukhala Mnzanu Wapamtima?Nsanja ya Olonda—2014 | December 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA
Kodi N’zotheka Mulungu Kukhala Mnzanu Wapamtima?
“Ukamadziwa kuti Mulungu ndi mnzako wapamtima, umaona kuti ndiwe wotetezeka ndipo umasangalala. Umaonanso kuti iye ndi wokonzeka kukuthandiza nthawi zonse kuti zinthu zizikuyendera bwino.”—CHRISTOPHER, MNYAMATA WA KU GHANA.
“Ukakhala pa mavuto, Mulungu amaona zonse ndipo amakuthandiza mwachikondi kuposa mmene umaganizira.”—HANNAH, MTSIKANA WAZAKA 13 WA KU ALASKA, U.S.A.
“Mulungu akakhala kuti ndi mnzako wapamtima, umamva bwino kwambiri komanso umasangalala.”—GINA, MAYI WAZAKA ZA M’MA 40 WA KU JAMAICA.
Si anthu atatu okhawa amene ali ndi maganizo amenewa. Pali anthu enanso ambiri amene amaona kuti Mulungu ndi mnzawo wapamtima. Kodi inunso mumaona choncho? Kapena mukufuna Mulungu atakhala mnzanu? Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi n’zothekadi munthu kukhala mnzake wapamtima wa Mulungu, yemwe ndi Wamphamvuyonse? Nanga munthu angatani kuti zimenezi zitheke?’
MULUNGU ANGATHE KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA
Baibulo limanena kuti n’zotheka Mulungu kukhala mnzathu wapamtima. Mwachitsanzo, limati Mulungu anatchula Abulahamu kuti, “bwenzi langa.” (Yesaya 41:8) Komansotu lemba la Yakobo 4:8 limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” Zimenezi zikusonyeza kuti n’zotheka ndithu Mulungu kukhala mnzathu wapamtima. Koma popeza Mulungu ndi wosaoneka, kodi ‘tingamuyandikire’ bwanji n’kukhala mnzathu wapamtima?
Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane zomwe zimachitika kuti anthu akhale mabwenzi apamtima. Choyamba anthuwo amauzana mayina. Ndiyeno akamalankhulana komanso kuuzana zakukhosi, amayamba kugwirizana kwambiri. Zikatere amayamba kupatsana mphatso kapena kuchitirana zinthu zosiyanasiyana. Izi zimapangitsa kuti azikondana kwambiri. Umu ndi mmenenso ubwenzi ndi Mulungu umayambira. Tiyeni tione mmene zimenezi zimachitikira.
-
-
Kodi Mumadziwa Ndiponso Kutchula Dzina la Mulungu?Nsanja ya Olonda—2014 | December 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA
Kodi Mumadziwa Ndiponso Kutchula Dzina la Mulungu?
Kodi muli ndi mnzanu wapamtima amene simudziwa dzina lake? Kunena zoona zimenezi sizingatheke. Ndiyetu n’chimodzimodzinso ndi Mulungu. Mayi wina wa ku Bulgaria, dzina lake Irina, anati: “N’zosatheka kuti Mulungu akhale mnzako wapamtima ngati sudziwa n’komwe dzina lake.” Koma monga taonera m’nkhani yapita ija, Mulungu amafuna kuti mudziwe dzina lake, kuti akhale mnzanu. Choncho kudzera m’Baibulo tingati iye wakuuzani dzina lake kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.”—Yesaya 42:8.
Kudzera m’Baibulo tingati Mulungu wakuuzani dzina lake kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.”—Yesaya 42:8.
Kodi Mulungu amaona kuti n’zofunika kuti mudziwe dzina lake ndiponso kuti muzilitchula? Inde. Mwachitsanzo, zilembo zomwe zimaimira dzina la Mulungu, zomwe zinkalembedwa popanda mavawelo, zinkapezeka pafupifupi ka 7,000 m’mipukutu yoyambirira ya Malemba Achiheberi. Apa ndiye kuti dzina la Mulungu linkapezeka m’Malemba kambiri kuposa dzina lililonse. Umenewutu ndi umboni woti Yehova amafuna kuti mudziwe dzina lake komanso muzilitchula.a
Kuti anthu akhale mabwenzi, amayamba ndi kuuzana mayina. Kodi inuyo mumadziwa dzina la Mulungu?
Komabe anthu ena angaganize kuti popeza Mulungu ndi woyera komanso Wamphamvuyonse, kutchula dzina lake ndi kupanda ulemu. N’zoona kuti n’zosayenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu molakwika, monga kulumbira potchula dzinali koma ukudziwa kuti zomwe ukunenazo n’zabodza. Izi n’zofanana ndi mmenenso zilili kuti sungamagwiritse ntchito dzina la mnzako pa zifukwa zosayenera. Komabe Yehova amafuna kuti anthu amene amamukonda azilemekeza dzina lake komanso azithandiza ena kudziwa dzinali. (Salimo 69:30, 31; 96:2, 8) Kumbukirani kuti Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ifenso tingathandizire kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe pouza ena za dzinali. Tikamachita zimenezi, ubwenzi wathu ndi Mulungu umalimba.
Baibulo limanena kuti ‘munthu akamaganizira za dzina la Mulungu,’ Mulunguyo amatchera khutu ndi kumvetsera. (Malaki 3:16) Ponena za munthu wotereyu, Yehova amalonjeza kuti: “Popeza wasonyeza kuti amandikonda, inenso ndidzamupulumutsa. Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa. Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha. Ndidzakhala naye m’nthawi ya masautso.” (Salimo 91:14, 15) Choncho, ngati tikufuna kuti Yehova akhale mnzathu wapamtima, tiyenera kudziwa dzina lake komanso kumalitchula.
a Ngakhale kuti dzina la Mulungu linkapezeka kambirimbiri m’Malemba Achiheberi, omwe ambiri amati Chipangano Chakale, n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri omasulira Mabaibulo sanaike dzinali m’Mabaibulo amene anamasulira. Pamene panali dzinali anaikapo mayina audindo monga akuti, “Ambuye” kapena “Mulungu.” Kuti mudziwe zambiri pa nkhaniyi, werengani tsamba 195 mpaka 197 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
-
-
Kodi Mumalankhulana ndi Mulungu?Nsanja ya Olonda—2014 | December 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA
Kodi Mumalankhulana ndi Mulungu?
Mabwenzi apamtima amalankhulana pafupipafupi. Amalankhulana kudzera pa foni, kalata, Intaneti kapena kutumizirana imelo. Ifenso kuti tikhale anzake apamtima a Mulungu, tiyenera kumalankhula naye pafupipafupi. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?
Tingalankhule ndi Yehova popemphera kwa iye. Komabe, tikamapemphera sitiyenera kulankhula motayirira ngati tikulankhula ndi munthu wamsinkhu wathu. Tiyenera kuzindikira kuti tikulankhula ndi Mlengi wathu, yemwe ndi Wamkulu m’chilengedwe chonse. Choncho, tiyenera kulankhula naye mwaulemu kwambiri. Komabe, pali zinthu zomwe tiyenera kuchita kuti Mulungu azimva mapemphero athu. Tiyeni tikambirane zitatu mwa zinthu zimenezi.
Choyamba, tiyenera kupemphera kwa Yehova Mulungu yekha basi, osati kwa Yesu, oyera mtima kapena kwa zifaniziro. (Ekisodo 20:4, 5) Pa nkhaniyi Baibulo limati: “Pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6) Chachiwiri, tiyenera kupemphera kudzera m’dzina la Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu. Yesu anati: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Chachitatu, mapemphero athu ayenera kukhala ogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Baibulo limati: “Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”a—1 Yohane 5:14.
Mabwenzi apamtima amalankhulana pafupipafupi
Komatu, ubwenzi sungapite patali ngati munthu mmodzi yekha ndi amene amalankhula. Anthu omwe ndi mabwenzi a pamtima amalankhulana ndipo zimenezi ndi zomwe zimalimbitsa ubwenzi wawowo. Choncho, nafenso tiyenera kulola Mulungu kuti azitilankhula ndipo tiyenera kumvetsera. Kodi mukudziwa njira imene Mulungu amagwiritsa ntchito akafuna kulankhula nafe?
Masiku ano, Yehova Mulungu amalankhula nafe kudzera m’Baibulo, lomwe ndi Mawu ake. (2 Timoteyo 3:16, 17) N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyerekeze kuti mwalandira kalata yochokera kwa mnzanu wapamtima. Mutawerenga kalatayo mungauze anthu ena nkhani imene ili m’kalatayo, ndipo munganene kuti: “Nkhani imeneyi wandiuza ndi mnzanga.” Komatu mnzanuyo sanakuuzeni nkhaniyo pamasom’pamaso, koma wachita kukulemberani kalata. Mofanana ndi zimenezi, mukamawerenga Baibulo, Yehova amakhala akulankhula nanu. N’chifukwa chake Gina, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, ananena kuti: “Ndimaona kuti, ngati ndikufuna kuti Yehova azindiona kuti ndine mnzake, ndiyenera kuwerenga Baibulo chifukwa ndi kalata imene wandilembera. Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kwandithandiza kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu.” Kodi inuyo mumalola kuti Yehova azilankhula nanu tsiku lililonse powerenga Baibulo tsiku ndi tsiku? Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muziona kuti Mulungu ndi mnzanu wapamtima.
a Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mmene pemphero limatithandizira kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu, werengani mutu 17 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
-
-
Kodi Mumachita Zomwe Mulungu Amafuna?Nsanja ya Olonda—2014 | December 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA
Kodi Mumachita Zomwe Mulungu Amafuna?
“Ukafuna kanthu uzingondiuza, ndizikupangira.” Kodi mungauze zimenezi munthu amene mwangokumana naye koyamba kapenanso amene simukumudziwa bwinobwino? Ayi, sizingatheke. Koma mukhoza kulankhula mawu amenewa kwa munthu amene ndi mnzanu wapamtima. Zili choncho chifukwa, mabwenzi amakonda kuchitirana zinthu zosiyanasiyana.
Baibulo limasonyeza kuti nthawi zonse Yehova amachita zinthu zomwe zingasangalatse atumiki ake. Mwachitsanzo Mfumu Davide, yemwe anali mnzake wapamtima wa Mulungu, anati: “Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa. . . . Zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.” (Salimo 40:5) Kuwonjezera apa, Yehova amachitiranso zabwino ngakhale anthu omwe samudziwa n’komwe. Iye ‘amadzaza mitima yawo ndi chakudya komanso chimwemwe.’—Machitidwe 14:17.
Anthu amene timawakonda timawachitira zinthu zabwino
Popeza Yehova amasangalala kuchita zinthu zomwe zimakondweretsa anthu, nayenso amafuna kuti anthu omwe akufuna kukhala anzake, azichita zinthu zomwe zingasangalatse ‘mtima wake.’ (Miyambo 27:11) Koma kodi tingatani kuti tisangalatse Mulungu? Baibulo limatiuza kuti: “Musaiwale kuchita zabwino ndi kugawana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotero Mulungu amakondwera nazo.” (Aheberi 13:16) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kuchitira ena zabwino, monga kuwapatsa zinthu, n’kokwanira?
Ayi, chifukwa Baibulo limanenanso kuti: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.” (Aheberi 11:6) Mwachitsanzo “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova,” ndipo kenako “anatchedwa ‘bwenzi la Yehova.’” (Yakobo 2:23) Yesu Khristu ananenanso kuti tiyenera ‘kukhulupirira Mulungu’ kuti atidalitse. (Yohane 14:1) Ndiye kodi mungatani kuti mukhale ndi chikhulupiriro chimene chingapangitse kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima? Nthawi zonse muyenera kuphunzira Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mudziwe “Mulungu molondola” komanso kuti “muzimukondweretsa pa chilichonse.” Mukadziwa zambiri zokhudza Yehova n’kumachita zimene mwaphunzirazo, mudzakhala ndi chikhulupiriro cholimba. Zimenezi zidzapangitsa kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima.—Akolose 1:9, 10.
-
-
Palibe Chinthu Chabwino Kwambiri Kuposa Kukhala pa Ubwenzi Ndi MulunguNsanja ya Olonda—2014 | December 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | MULUNGU AKHOZA KUKHALA MNZANU WAPAMTIMA
Palibe Chinthu Chabwino Kwambiri Kuposa Kukhala pa Ubwenzi Ndi Mulungu
Kodi mungatani kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima? Taona zinthu zingapo zimene mungachite. Zinthu zake ndi izi:
Muyenera kudziwa dzina la Mulungu n’kumatchula dzinali mukamanena za iye.
Muzilankhulana naye. Mungachite zimenezi popemphera kwa iye komanso kuphunzira Mawu ake, Baibulo.
Muzichita zimene iye amafuna.
Kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima muzitchula dzina lake mukamanena za iye, muzipemphera kwa iye, muziphunzira Baibulo komanso muzichita zimene iye amafuna
Mukaganizira mfundo zimenezi, kodi mukuona kuti mukuchita zonse zofunika kuti Mulungu akhale mnzanu wapamtima? Kodi pali zimene mukuona kuti mukufunika kukonza kuti ubwenzi umenewu utheke? N’zoona kuti pamafunika khama, koma zotsatira zake zimakhala zabwino.
Jennifer wa ku United States anati: “Pamafunika khama kuti Mulungu akhale mnzako wapamtima, koma mpake. Mulungu akakhala mnzako wapamtima, umamudalira, umamudziwa bwino komanso umamukonda. Ndisaname, palibe chinthu chabwino kwambiri kuposa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.”
Ngati mukufuna kuti nanunso Mulungu akhale mnzanu wapamtima, a Mboni za Yehova angakuthandizeni. Akhoza kumaphunzira nanu Baibulo kwaulere. Komanso, mungathe kupita ku Nyumba ya Ufumu yomwe ili m’dera lanu komwe a Mboni za Yehova amaphunzira nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo. Mukadzapita kumeneko, mudzasangalala kucheza ndi anthu amene amaona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri.a Nanunso mudzamva ngati mmene munthu wina amene analemba nawo masalimo anamvera. Iye anati: “Kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.”—Salimo 73:28.
a Kuti mupeze munthu woti aziphunzira nanu Baibulo kapena kuti mudziwe komwe Nyumba ya Ufumu ili m’dera lanu, lankhulani ndi munthu amene anakupatsani magaziniyi kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.pr2711.com/ny. Pitani pamene palembedwa kuti POYAMBIRA › TIPEZENI pamunsi pa tsambalo.
-