-
Kodi Mulungu Amakuganizirani?Nsanja ya Olonda—2014 | August 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?
Kodi Mulungu Amakuganizirani?
“Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka. Yehova amandiwerengera.”a—DAVIDE YEMWE ANKAKHALA KU ISIRAELI, M’ZAKA ZA M’MA 1000 B.C.E.
“Mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko.”—YESAYA 40:15
Kodi Davide ankanena zoona kuti Mulungu ankamuwerengera kapena kuti kumuganizira? Kodi inuyo mumaona kuti Mulungu amakuganizirani? Anthu ambiri zimawavuta kukhulupirira kuti Mulungu Wamphamvuyonse angamawaganizire. N’chifukwa chiyani?
Chifukwa amadziwa mfundo yoti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri kuposa anthufe. Mulungu akakhala kumwamba n’kumayang’ana anthu padzikoli, amaona kuti mitundu yonse ya anthu “ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko, ndipo kwa iye ili ngati fumbi pasikelo.” (Yesaya 40:15) Poganizira mfundo imeneyi munthu wina wolemba mbiri yakale ananena kuti: “Munthu amene amaganiza kuti Mulungu, yemwe ndi wapamwamba kwambiri, angamachite chidwi ndi zochita za iyeyo ndi wodzikuza kwambiri.”
Palinso anthu ena amene amaganiza kuti zochita zawo zimachititsa kuti Mulungu aziwaona kuti ndi osafunika. Mwachitsanzo, bambo wina dzina lake Jim, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkapemphera kwa Mulungu kuti andithandize kuti ndiziugwira mtima komanso ndizikhala mwamtendere ndi anthu. Koma pakangopita nthawi ndinkayambiranso kupsa mtima. Zimenezi zinandipangitsa kuganiza kuti ndine wokanika ndipo Mulungu sangandithandize.”
Popeza Mulungu ndi wapamwamba kwambiri, kodi ndiye kuti sachita chidwi ndi anthu? Nanga kodi iye amamva bwanji anthu akamalephera kuchita bwino zinthu chifukwa choti si angwiro? Palibe munthu amene angathe kudziwa mayankho a mafunso amenewa popanda kuthandizidwa ndi Mulungu. Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limatitsimikizira kuti ngakhale kuti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri, amachita chidwi ndi zimene zikuchitikira munthu aliyense payekha. Ndipotu Baibulo limati: “Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Machitidwe 17:27) M’nkhani zotsatirazi, tiona zimene Mulungu amatiuza zosonyeza kuti amachita chidwi ndi munthu aliyense payekha. Tionanso mmene anachitira zimenezi kwa anthu ena, zomwe zikusonyeza kuti amachitanso chidwi ndi inuyo.
a Mawuwa achokera pa Salimo 40:17. Yehova ndi dzina la Mulungu.
-
-
Mulungu Amaona Zomwe Zikuchitika pa Moyo WanuNsanja ya Olonda—2014 | August 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?
Mulungu Amaona Zomwe Zikuchitika pa Moyo Wanu
“Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse.”—YOBU 34:21.
Mwana wamng’ono amafunika chisamaliro chapadera
N’CHIFUKWA CHIYANI ENA AMAKAYIKIRA? Zotsatira za kafukufuku amene anachitika posachedwapa zinasonyeza kuti mlalang’amba wathu wokhawu uli ndi mapulaneti okwana 100 biliyoni. Poganizira zimenezi ndiponso kukula kwa chilengedwe chonse, anthu ambiri amafunsa kuti, ‘Zingatheke bwanji kuti Mlengi wachilengedwe chonsechi azichita chidwi ndi anthu okhala padzikoli n’kumadziwa zomwe zikuchitika pa moyo wawo?’
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Sikuti Mulungu anangotipatsa Baibulo n’kutisiya. M’malomwake Yehova amatitsimikizira kuti: “Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.”—Salimo 32:8.
Taganizirani zimene zinachitikira Hagara, mayi wa ku Iguputo yemwe anakhalako m’zaka za m’ma 1900 B.C.E. Hagara anali wantchito wa Sarai ndipo atayamba kuchita mwano Sarai anayamba kumuzunza. Zitatere Hagarayo anathawira m’chipululu. Kodi Mulungu anamutaya Hagara chifukwa choti anachitira mwano Sarai? Ayi, chifukwa Baibulo limati: “Mngelo wa Yehova anakapeza Hagara m’chipululu.” Mngeloyo anauza Hagara kuti: “Yehova wamva kulira kwako.” Kenako Hagara anauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”—Genesis 16:4-13.
Dziwani kuti “Mulungu amene amaona chilichonse,” amaonanso zimene zikuchitika pa moyo wanu ndipo amakuderani nkhawa. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tiyerekeze ndi zimene mayi wachikondi amachita. Iye amaonetsetsa zimene zikuchitikira ana ake, makamaka aang’ono, chifukwa amadziwa kuti mwana wamng’ono amafunika chisamaliro chapadera. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu amaonetsetsa zimene zikutichitikira, makamaka tikhala pa mavuto. Yehova ananena kuti: “Ndimakhala kumwamba pamalo oyera. Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa, kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.” —Yesaya 57:15.
Komabe mwina mungafunse kuti: ‘Kodi Mulungu amaona chiyani mwa ine? Kodi amandiweruza pongotengera maonekedwe anga, kapena amaona zimene zili mumtima mwanga ndipo amandimvetsa?’
-
-
Mulungu AmakumvetsaniNsanja ya Olonda—2014 | August 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?
Mulungu Amakumvetsani
“Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.”—SALIMO 139:1.
“Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” —SALIMO 139:16
N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMAKAYIKIRA? Anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu amangoona kuti anthu ndi ochimwa komanso odetsedwa ndipo alibe nawo ntchito. Mtsikana wina dzina lake Kendra, yemwe ankadwala matenda a maganizo, ankangokhalira kudziimba mlandu chifukwa ankaona kuti amalephera kuchita zonse zimene Mulungu amafuna. Iye ananena kuti zimenezi zinachititsa kuti asiye kupemphera.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Sikuti Yehova amangoona zimene mumalakwitsa. Iye amaonanso zimene zili mumtima mwanu ndipo amakumvetsani. Baibulo limanena kuti: “Akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” Komanso ‘satichitira mogwirizana ndi machimo athu,’ koma amatikhululukira tikalapa.—Salimo 103:10, 14.
Taganizirani zimene zinachitikira Davide yemwe anali mfumu ya Aisiraeli. Iye anapemphera kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. . . . Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga.” (Salimo 139:16, 23) Davide ankadziwa kuti ngakhale kuti pa nthawi ina anachitapo machimo akuluakulu, koma atalapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova anazindikira zimenezi ndipo anamukhululukira.
Dziwani kuti Yehova amakumvetsani kuposa munthu wina aliyense. Baibulo limati: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” (1 Samueli 16:7) Mulungu amadziwa zimene zimakupangitsani kuti muzichita zinazake. Kaya ndi chifukwa cha chibadwa chanu, mmene munaleredwera kapenanso kumene mukukhala, Mulungu amamvetsa zonsezo. Ngati mukuyesetsa kuti muzichita zabwino, iye amaona komanso amasangalala ngakhale kuti mumalakwitsa zinthu zina.
Popeza Mulungu amakumvetsani chonchi, kodi amakuthandizani bwanji pogwiritsa ntchito zomwe amadziwazo?
-
-
Mulungu Angakulimbikitseni ndi KukuthandizaniNsanja ya Olonda—2014 | August 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?
Mulungu Angakulimbikitseni ndi Kukuthandizani
“Mulungu, amene amalimbikitsa osautsika mtima, anatilimbikitsa.” —2 AKORINTO 7:6.
“Mwana wa Mulungu . . . anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” —AGALATIYA 2:20
N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMAKAYIKIRA? Anthu ena akakhala pa mavuto amaganiza kuti n’kudzikonda kupempha Mulungu kuti awathandize. Iwo amachita zimenezi ngakhale atasoweratu mtengo wogwira. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Raquel, ananena kuti: “Ndikaganizira mavuto amene anthu ambiri padzikoli akukumana nawo, ndimaona kuti mavuto anga ndi ochepa kwambiri moti palibe chifukwa choti ndizipempha Mulungu kuti andithandize.”
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Mulungu anapereka Mwana wake pofuna kutithandiza. Anthufe timabadwa ochimwa, ndipo zimenezi zimachititsa kuti tisamathe kuchita zonse zimene Mulungu amafuna popanda kulakwitsa. Komabe Mulungu “anatikonda ndi kutumiza Mwana wake [Yesu Khristu] monga nsembe yophimba machimo athu.” (1 Yohane 4:10) Kudzera mu nsembe ya Yesu, Mulungu amatikhululukira machimo, timakhala ndi chikumbumtima chabwino komanso timakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko latsopano lamtendere.a Komatu sikuti nsembe imeneyi imangosonyeza kuti Mulungu amakonda anthu onse monga gulu. Imasonyezanso kuti Mulungu amakukondani inuyo panokha.
Taganizirani zimene mtumwi Paulo ananena. Iye ankayamikira kwambiri nsembe ya Yesu moti analemba kuti: “Ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene anandikonda ndi kudzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agalatiya 2:20) Ngakhale kuti Yesu anafa Paulo asanakhale Mkhristu, iye ankaona kuti nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Mulungu anamupatsa iyeyo.
Inunso muziona kuti nsembe ya Yesu ndi mphatso imene Mulungu anakupatsani inuyo panokha. Mphatso imeneyi imasonyeza kuti Mulungu amakuonani kuti ndinu wofunika. Ingakupatseninso “chiyembekezo chabwino” ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuti muzichita zinthu zabwino.—2 Atesalonika 2:16, 17.
Komatu Yesu anapereka nsembe moyo wake zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Ndiye kodi masiku ano pali umboni uliwonse wosonyeza kuti Mulungu akufuna kuti mukhale naye pa ubwenzi?
a Kuti mudziwe zambiri zokhudza nsembe ya Yesu, werengani mutu 5 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
-
-
Mulungu Akufuna Kuti Mukhale Naye pa UbwenziNsanja ya Olonda—2014 | August 1
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?
Mulungu Akufuna Kuti Mukhale Naye pa Ubwenzi
“Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate.” —YOHANE 6:44.
N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMAKAYIKIRA? Pali anthu ambiri amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu, koma amaona kuti sali naye pa ubwenzi. Mwachitsanzo, mayi wina wa ku Ireland dzina lake Christina, ananena kuti: “Ndinkadziwa kuti Mulungu ndi amene analenga chilichonse. Komabe sindinkamudziwa bwinobwino komanso ndinkaona kuti iye si bwenzi langa lapamtima.”
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Tikalakwa, Yehova satopa nafe ndipo amapitirizabe kutithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi. Yesu anapereka fanizo losonyeza mmene Mulungu amachitira zimenezi. Iye anati: “Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusochera, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phiri ndi kupita kukafunafuna yosocherayo? . . . Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mateyu 18:12-14.
Zimenezi zikutiphunzitsa kuti Mulungu amaona kuti munthu aliyense ndi wofunika. Ndiye kodi Mulungu ‘amafunafuna’ bwanji anthu amene ali ngati nkhosa zosochera? Lemba la Yohane 6:44 limanena kuti Yehova amakokera anthuwa kwa iye.
Kodi ndani masiku ano amene amapita kunyumba za anthu kapena m’malo osiyanasiyana n’kumauza anthu uthenga wa m’Baibulo wonena za Mulungu?
Tiyeni tione mmene Mulungu anachitira zimenezi m’mbuyomu. M’nthawi ya atumwi, Mulungu anatumiza Filipo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, kukakumana ndi nduna ya ku Itiyopiya kuti akakambirane nayo tanthauzo la zimene ndunayi inkawerenga m’Malemba. (Machitidwe 8:26-39) Pa nthawi ina Mulungu anachititsa kuti mtumwi Petulo apite kunyumba kwa kapitawo wa gulu la asilikali a Roma, dzina lake Koneliyo, yemwe ankapemphera komanso kuyesetsa kulambira Mulungu. (Machitidwe 10:1-48) Pa nthawi inanso Mulungu anatsogolera mtumwi Paulo ndi anzake kuti apite m’mbali mwa mtsinje womwe unali kunja kwa mzinda wa Filipi. Kumeneko anapeza mayi wina dzina lake Lidiya, yemwe anali “wolambira Mulungu,” ndipo Mulungu “anatsegula kwambiri mtima wake kuti atchere khutu ku zimene Paulo anali kunena.”—Machitidwe 16:9-15.
Zitsanzo za anthu onsewa zikusonyeza kuti Yehova anaonetsetsa kuti anthu amene ankafunitsitsa kumudziwa, apeze mwayi wophunzira za iye. Kodi ndani masiku ano amene amapita kunyumba za anthu kapena m’malo osiyanasiyana n’kumauza anthu uthenga wa m’Baibulo wonena za Mulungu? Ambiri angayankhe kuti, “Ndi a Mboni za Yehova.” Ndiye dzifunseni kuti, ‘Kodi n’kutheka kuti Mulungu akugwiritsa ntchito anthu amenewa pofuna kundikokera kwa iye?’ Tikukulimbikitsani kuti mupemphere kwa Mulungu kuti akuthandizeni kuzindikira njira imene akugwiritsa ntchito kuti akukokereni kwa iye.a
a Kuti mudziwe zambiri, onerani vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? pa webusaiti yathu ya www.pr2711.com/ny.
-