Nyimbo 45
Pitani Patsogolo
Losindikizidwa
1. Pita patsogolo kula mu mzimu!
Mulungu afuna tikhaledi aluso.
Sonyezatu luso muutumiki,
M’lungu adzadalitsa.
Utumikiwu ndi wa onse.
Yesu naye anauchita.
Dalira Mulungu kuti usagwe,
Limba pa chilungamo.
2. Pita patsogolo molimba mtima!
Lalika uthenga kwa anthu onse m’dziko.
Tamanda Yehova Mfumu yathuyo,
Polalikira nawo.
Adani angatiopseze.
Tisaleke, onse amvetu
Kuti Ufumu wa M’lungu wayamba.
Phunzitsa choonadi.
3. Pita patsogolo usabwerere,
Wonjezera luso ntchitoyi n’njaikulu.
Mzimu wa Mulungu ukuthandize,
Udzapeza chimwemwe.
Konda anthu omwe wapeza.
Bwerera, uwafike m’mtima.
Athandize apite patsogolo,
Cho’nadi chiziwala.
(Onaninso Afil. 1:27; 3:16; Aheb. 10:39.)