Nyimbo 11
Tikondweretse Mtima wa Yehova
Losindikizidwa
1. M’lungu takulonjezani,
kuchita zofuna zanu.
Tidzagwira ntchito yanu
Mtima wanu ukondwere.
2. Kapolo wanu padziko,
Amapereka chakudya
Iye amatithandiza
Kuchita zofuna zanu.
3. Mutipatse mzimu wanu,
Kuti tikhulupirike
Inde tikutamandeni,
Mtima wanu ukondwere.
(Onaninso Mat. 24:45-47; Luka 11:13; 22:42.)