Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Tonse Timafunika Kulimbikitsidwa
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2016 | Na. 5
    • NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI NDANI ANGATITHANDIZE TIKAKHALA PA MAVUTO?

      Tonse Timafunika Kulimbikitsidwa

      Mayi akuthandiza mwana wake yemwe wavulala

      Kodi munayamba mwagwapo nthawi inayake muli mwana? N’kutheka kuti munavulala dzanja kapena bondo. Kodi mukukumbukira zimene mayi anu anachita pokuthandizani? Mwina anatsuka balalo n’kulimanga ndi kansalu. N’zosakayikitsa kuti munalira koma pasanapite nthawi munatonthola chifukwa mwina mayi anu anakukumbatirani ndiponso kukuuzani mawu olimbikitsa. N’zosachita kufunsa kuti pamene munali mwana simunkasowa anthu okulimbikitsani.

      Koma munthu akakula mavuto ake amakhalanso aakulu ndipo zimavuta kuti apeze munthu amene angamulimbikitse. Mavuto amene akuluakulu amakumana nawo sangathetsedwe msanga ngati mmene zimakhalira ndi mavuto a ana. Tiyeni tione zitsanzo za mavuto ena amene timakumana nawo.

      • Kodi nthawi ina munachotsedwapo ntchito? Bambo wina dzina lake Julian ananena kuti atachotsedwa ntchito anasokonezeka maganizo kwambiri. Ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ndikwanitsa bwanji kumasamalira banja langa? Ndakhala ndikugwira ntchito mwakhama kwa zaka zambiri pakampaniyi, ndiye n’chifukwa chiyani andichotsa ntchito ngati ndine wachabechabe?’

      • Mwinanso mukusowa mtengo wogwira chifukwa chakuti banja lanu linatha. Mayi wina dzina lake Raquel ananena kuti: “Mwamuna wanga anandithawa mwadzidzidzi ndipo panopa padutsa chaka ndi miyezi 6. Zinandipweteka kwambiri moti ngakhale m’thupi sindinkamva bwino. Ndinkachita mantha kuti zindiyambitsira mavuto ena.”

      • N’kutheka kuti mukudwala matenda enaake ndipo zikuoneka kuti simudzachira. Nthawi zina mungamve ngati mmene Yobu ankamvera. Iye anati: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Yobu 7:16) Mwinanso mumamva ngati mmene bambo wina wazaka za m’ma 80 dzina lake Luis amamvera. Iye anati: “Nthawi zina ndimaona ngati ndikungodikira imfa.”

      • Kapena mukhoza kumafuna kulimbikitsidwa chifukwa wachibale kapena mnzanu anamwalira. Bambo wina dzina lake Robert ananena kuti: “Mwana wanga atamwalira pa ngozi yandege sindinakhulupirire. Kenako ndinayamba kumva ululu waukulu kwambiri wofanana ndi ululu umene Baibulo limauyerekezera ndi umene munthu angamve atalasidwa ndi lupanga lalitali.”—Luka 2:35.

      Robert, Luis, Raquel ndi Julian atakumana ndi mavutowa analimbikitsidwa ndi Mulungu wamphamvuyonse, ndipo palibe wina amene akanawalimbikitsa bwino kuposa iyeyo. Kodi Mulunguyo amalimbikitsa bwanji anthu? Nanga kodi inuyo angakulimbikitseni?

  • Kodi Mulungu Amatilimbikitsa Bwanji?
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2016 | Na. 5
    • Yesu akugwira munthu wodwala khate asanamuchiritse

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI NDANI ANGATITHANDIZE TIKAKHALA PA MAVUTO?

      Kodi Mulungu Amatilimbikitsa Bwanji?

      Mtumwi Paulo ananena kuti Yehovaa ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Apa Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu akhoza kuthandiza munthu aliyense ndipo angamulimbikitse akakumana ndi vuto lina lililonse.

      Komabe pali zimene tiyenera kuchita kuti Mulungu azitilimbikitsa. Kodi dokotala angatithandize bwanji ngati titapanda kukonza zoti tionane naye? Mneneri Amosi anafunsa kuti: “Kodi anthu awiri amayenda pamodzi asanapangane ndi kukumana mogwirizana ndi pangano lawolo?” (Amosi 3:3) N’chifukwa chake Malemba amanena kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”​—Yakobo 4:8.

      Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu adzatiyandikiradi? Choyamba, tikudziwa chifukwa chakuti iye amatiuza mobwerezabwereza kuti amafuna kutithandiza. (Onani bokosi limene lili m’nkhaniyi.) Chachiwiri, tili ndi umboni wosonyeza kuti Mulungu ankathandiza anthu akale komanso akuthandizabe anthu masiku ano.

      Mofanana ndi anthu ambiri amasiku ano amene amafuna kuti Mulungu awathandize, Davide ankakumana ndi mavuto ambiri. Nthawi ina iye anapempha Yehova kuti: “Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize.” Kodi Mulungu anayankha pempheroli? Inde. Tikutero chifukwa Davide ananenanso kuti: “Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.”​—Salimo 28:2, 7.

      YESU ANAPATSIDWA UDINDO WOLIMBIKITSA ONSE OLIRA

      Mulungu anapatsa Yesu udindo woti azilimbikitsa anthu. Anamupatsa ntchito yoti ‘amange zilonda za anthu osweka mtima komanso kuti atonthoze anthu onse olira.’ (Yesaya 61:1, 2) Mogwirizana ndi ulosiwu, Yesu ankalimbikitsa kwambiri anthu “ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa.”​—Mateyu 11:28-30.

      Iye ankalimbikitsa anthu powapatsa malangizo anzeru, kuwachitira zinthu mokoma mtima komanso nthawi zina kuwachiritsa. Tsiku lina munthu wina wakhate anapempha Yesu kuti: “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” Yesu atagwidwa ndi chifundo, anayankha kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” (Maliko 1:40, 41) Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa.

      Panopa Mwana wa Mulungu sangatilimbikitse ngati mmene ankachitiramu chifukwa sali padziko lapansi pano. Koma Atate wake Yehova yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” akupitirizabe kuthandiza anthu omwe ali ndi mavuto. (2 Akorinto 1:3) Tiyeni tione njira 4 zikuluzikulu zimene Mulungu amagwiritsa ntchito polimbikitsa anthu.

      • Baibulo. “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”​—Aroma 15:4.

      • Mzimu Woyera wa Mulungu. Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Yesu anamwalira, mpingo wachikhristu unalowa m’nyengo yamtendere. Zimenezi zinatheka chifukwa choti “unali kuyenda moopa Yehova ndiponso kulimbikitsidwa ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 9:31) Mzimu woyera, kapena kuti mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito, ndi wamphamvu kwambiri. Mulungu angaugwiritse ntchito kuti alimbikitse munthu pa vuto lina lililonse.

      • Pemphero. Baibulo limatiuza kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse.” Ndipo “zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.”​—Afilipi 4:6, 7.

      • Akhristu Anzathu akhoza kutilimbikitsa kwambiri monga anzathu apamtima. Mtumwi Paulo ananena kuti anzake ‘ankamuthandiza ndi kumulimbikitsa’ pa nthawi imene anali “m’masautso.”​—Akolose 4:11; 1 Atesalonika 3:7.

      A Mboni za Yehova awiri akulimbikitsa Mkhristu mnzawo

      Koma mwina mukudzifunsa kuti, Kodi zinthu zimenezi zimathandizadi? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tionenso bwinobwino zitsanzo za anthu omwe tawatchula m’nkhani yapitayi. Mofanana ndi anthuwa, inunso mukhoza kuona umboni wakuti Mulungu amachitadi zimene analonjeza kuti: “Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu.”​—Yesaya 66:13.

      a Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.

      Kodi Timadziwa Bwanji Kuti Mulungu Amafunitsitsa Kutilimbikitsa?

      • “Inu Yehova mwandithandiza ndi kundilimbikitsa.”​—Salimo 86:17.

      • “‘Limbikitsani anthu anga. Ndithu alimbikitseni,’ akutero Mulungu wanu.”​—Yesaya 40:1.

      • “Yehova wanena kuti: . . . ‘Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani.’”​—Yesaya 66:12, 13.

      • “Odala ndi anthu amene akumva chisoni, chifukwa adzasangalatsidwa.”​—Mateyu 5:4.

      • ‘Mutulireni Mulungu nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7.

  • Zimene Zingakuthandizeni Mukamakumana ndi Mavuto
    Nsanja ya Olonda (Yogawira)—2016 | Na. 5
    • NKHANI YA PACHIKUTO | KODI NDI NDANI ANGATITHANDIZE TIKAKHALA PA MAVUTO?

      Zimene Zingakuthandizeni Mukamakumana Ndi Mavuto

      Mavuto amakhala osiyanasiyana ndipo n’zosatheka kufotokoza mavuto onse m’nkhaniyi. Koma tiyeni tikambirane mavuto 4 amene tatchula kale aja ndiponso mmene anthu omwe ankakumana ndi mavutowo analimbikitsidwira ndi Mulungu.

      NTCHITO IKATHA

      Jonathan akutsuka mawindo

      “Ndinayamba kugwira ntchito iliyonse yomwe inkapezeka komanso tinasiya kumangogula zinthu zosafunika kwenikweni.”​—Jonathan

      Mwamuna wina dzina lake Setha ananena kuti: “Ine ndi mkazi wanga tinachotsedwa ntchito nthawi yofanana. Kwa zaka ziwiri, tinkangodalira zimene achibale ankatipatsa komanso timaganyu tina ndi tina timene tinkapeza. Chifukwa cha zimenezi mkazi wanga Priscilla anayamba kudwala matenda ankhawa, pamene ine ndinkangodziona ngati wachabechabe.

      “Pali zinthu zingapo zimene zinkatithandiza kupirira mavutowa. Mwachitsanzo, Priscilla ankakonda kuganizira mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 6:34. Palembali Yesu ananena kuti tisamade nkhawa ndi zamawa chifukwa tsiku lililonse limakhala ndi zodetsa nkhawa zake. Mkazi wanga ankapempheranso mochokera pansi pa mtima ndipo zinkamuthandiza kuti asamangokhalira kudandaula. Ineyo ndinkalimbikitsidwa kwambiri ndi lemba la Salimo 55:22. Mofanana ndi wolemba salimoli, ndinkatulira Yehova nkhawa zanga ndipo iye ankandichirikiza. Panopa ndinapeza ntchito ina komabe timayesetsa kukhala ndi moyo wosalira zambiri mogwirizana ndi malangizo a Yesu a pa Mateyu 6:20-22. Koma chofunika kwambiri n’chakuti zimene tinkachita pa nthawiyi zinathandiza kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Mulungu komanso kuti ine ndi mkazi wanga tizigwirizana kwambiri.”

      Mwamuna winanso dzina lake Jonathan ananena kuti: “Bizinezi yathu itatha ndinkada nkhawa kuti zitithera bwanji. Tinali titagwira ntchito mwakhama mu bizineziyi kwa zaka 20, koma inangotha mwadzidzidzi chifukwa cha mavuto azachuma omwe anali m’dziko lathu. Izi zinachititsa kuti ine ndi mkazi wanga tiyambe kumakangana pa nkhani ya ndalama. Tinkaopanso kugula zinthu ndi khadi lathu logulira zinthu pa ngongole poganiza kuti kampani imene inatipatsa khadilo siingalole.

      “Komabe Mawu a Mulungu komanso mzimu wake zinatithandiza kuti tizisankha zinthu mwanzeru. Ndinayamba kugwira ntchito iliyonse yomwe inkapezeka komanso tinasiya kumangogula zinthu zosafunika kwenikweni. Popeza ndife a Mboni za Yehova, tinkathandizidwanso ndi a Mboni anzathu. Ankatilimbikitsa komanso kutipatsa zinthu pamene tavutika kwambiri.”

      BANJA LIKATHA

      Raquel amene tamutchula kale uja ananena kuti: “Mwamuna wanga atandithawa, zinandipweteka kwambiri komanso zinandikwiyitsa. Koma ndinkadalira Mulungu ndipo iye ankandilimbikitsa. Ndinkapemphera kwa iye tsiku ndi tsiku ndipo ankandithandiza kuti ndikhale ndi mtendere wamumtima. Zinali ngati wachiritsa mtima wanga.

      “Baibulo linkandithandizanso kuti ndisamakwiye kapena kusunga chakukhosi. Ndinkayesetsa kutsatira mawu a mtumwi Paulo a pa Aroma 12:21 akuti: ‘Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.’

      Wa Mboni za Yehova akumulimbikitsa Raquel pogwiritsa Baibulo

      “Pali nthawi imene tiyenera kungovomereza kuti zachitika basi. . . . Panopa ndimaganizira zinthu zimene zingandithandize kukhala wosangalala m’malo momangoganizira za mavuto anga.”​—Raquel

      “Mnzanga wina wanzeru anandithandiza kuzindikira kuti ndiyenera kusiya kumangoganizira zimene zandichitikira. Anandisonyeza lemba la Mlaliki 3:6, n’kundiuza kuti pali nthawi imene tiyenera kungovomereza kuti zachitika basi. Malangizowa anali ovuta kutsatira koma anandithandiza kwambiri. Panopa ndimaganizira zinthu zimene zingandithandize kukhala wosangalala m’malo momangoganizira za mavuto anga.”

      Mayi wina dzina lake Elizabeth ananena kuti: “Banja likatha umafunika kuti ena azikulimbikitsa. Ineyo ndinali ndi mnzanga wina yemwe ankandithandiza tsiku ndi tsiku. Ankalira nane limodzi, kundilimbikitsa komanso kundithandiza kuti ndizidzimva kuti ndine wofunika. Sindimakayikira kuti Yehova anamugwiritsa ntchito kuti achiritse mabala amene ndinali nawo mumtima.”

      PAMENE MUKUDWALA KAPENA MWAKALAMBA

      Luis, yemwe amagwiritsa ntchito makina othandiza kupuma, akuyang’ana kumwamba popemphera kwa Yehova

      “Ndikapemphera ndimamva kuti mzimu [wa Mulungu] ukundithandiza.”​—Luis

      Luis yemwe tamutchula m’nkhani yoyambirira uja ali ndi vuto la mtima ndipo kwa maulendo awiri anatsala pang’ono kufa. Panopa amafunika kugwiritsa ntchito makina othandiza kupuma kwa maola 16, tsiku lililonse. Iye anati: “Ndimapemphera kwa Yehova nthawi zonse. Ndikapemphera ndimamva kuti mzimu wake ukundithandiza. Kupemphera kumandithandiza kuti ndipirire chifukwa ndimakhulupirira kuti Mulungu amandikonda ndipo andithandiza.”

      Mayi wina wazaka za m’ma 80 dzina lake Petra ananena kuti: “Ndimafuna kuchita zinthu zambiri koma sindingakwanitse. Ndimadandaula ndikamaona kuti mphamvu zanga zikutha. Panopa ndimakhala wofooka ndipo ndimayenera kumwa mankhwala ambiri. Nthawi zambiri ndimaganizira zimene Yesu anachita popempha Atate wake kuti ngati n’zotheka asalole kuti akumane ndi vuto linalake. Yehova anapatsa Yesu mphamvu ndipo ndi zimenenso amandichitira ineyo. Ndimapemphera tsiku lililonse ndipo zimenezi zimandithandiza chifukwa ndikalankhula ndi Mulungu ndimamva bwino mumtima.”​—Mateyu 26:39.

      Julian yemwe tamutchula kale uja wakhala akudwala matenda ofooketsa ziwalo kwa zaka pafupifupi 30. Iye anati: “Kale ndinali munthu wamphamvu zake ndiponso wolemekezeka koma panopa ndimayenda pa njinga ya anthu olumala. Komabe ndimaona kuti moyo wanga ndi wofunika chifukwa ndimadzipereka pothandiza anthu ena. Kuthandiza ena kungakuthandizeni kuti musamangoganizira za mavuto anu. Komanso Yehova amakwaniritsa lonjezo lake lakuti adzatipatsa mphamvu pa nthawi ya mavuto. Mofanana ndi mtumwi Paulo, inenso ndinganene kuti: ‘Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.’”​—Afilipi 4:13.

      PAMENE WACHIBALE KAPENA MNZANU WAMWALIRA

      Munthu wina dzina lake Antonio ananena kuti: “Bambo anga atamwalira pa ngozi yapamsewu, poyamba sindinakhulupirire chifukwa iwo ankangodziyendera mumsewu ndipo sanalakwitse chilichonse. Koma palibe chimene ndikanachita. Asanamwalire anakhala masiku 5 ali chikomokere. Sindinkalira ndikakhala ndi mayi anga, koma ndikakhala ndekha ndinkalira kwambiri. Ndinkangokhalira kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zatichitikira?’

      “Pa nthawi yovutayi, ndinkapempha Yehova kuti andithandize kuti ndisamadandaule kwambiri komanso kuti andipatse mtendere wamumtima. Izi zinandithandiza kuti mtima ukhale m’malo. Ndinakumbukira zimene Baibulo limanena zoti ‘zinthu zosayembekezereka’ zikhoza kugwera munthu aliyense. Popeza Mulungu sanganame, sindikukayikira kuti ndidzaonananso ndi bambo anga akadzaukitsidwa.”​—Mlaliki 9:11; Yohane 11:25; Tito 1:2.

      Robert ndi mkazi wake akuona zithunzi

      ‘Panopa timakumbukirabe zinthu zosangalatsa zimene tinkachitira limodzi ndi mwana wathu.’​—Robert

      Nayenso Robert amene tamutchula m’nkhani yoyamba uja amaona kuti pemphero ndi lothandiza. Iye ananena kuti: “Ine ndi mkazi wanga tinakhala ndi mtendere wamumtima womwe umatchulidwa pa Afilipi 4:6, 7. Tinapeza mtenderewu chifukwa chopemphera kwa Yehova. Mtendere umenewu unkatithandiza kuti tizilankhula ndi atolankhani za chikhulupiriro chathu chakuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. Panopa timakumbukirabe zinthu zosangalatsa zimene tinkachitira limodzi ndi mwanayo ndipo timayesetsa kuganizira kwambiri zinthuzo.

      “A Mboni anzathu atatiuza kuti anationa pa TV tikufotokoza modekha zimene timakhulupirira, tinawauza kuti tinakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa anthu ambiri ankatipempherera. Ndimakhulupirira kuti Yehova ankatithandiza pogwiritsa ntchito mawu olimbikitsa omwe Akhristu anzathuwo ankatiuza.”

      Monga mmene taonera m’zitsanzozi, Mulungu amatha kulimbikitsa anthu akakumana ndi vuto lililonse. Nanga kodi inuyo angakulimbikitseninso? Kaya mukukumana ndi mavuto otani, dziwani kuti Mulungu akhoza kukulimbikitsani.b Choncho mungachite bwino kupempha Yehova kuti akuthandizeni. Paja iye ndi Mulungu amene “amatitonthoza m’njira iliyonse.”​—2 Akorinto 1:3.

      a Mayina ena asinthidwa m’nkhaniyi.

      b Ngati mukufuna kuti mukhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu kuti azikulimbikitsani, lankhulani ndi a Mboni za Yehova am’dera lanu kapena lembani kalata yopita ku ofesi yawo yam’dziko lanu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena