NYIMBO 147
Mulungu Watilonjeza Moyo Wosatha
Losindikizidwa
1. Mulungu watilonjeza
Moyo womwe sudzatha.
Anthu adzasangalala,
Zidzachitikadi.
(KOLASI)
Inde tidzakhala
Ndi moyo wosatha.
M’lungu walonjeza
Zidzachitika.
2. Mudziko latsopanolo
Uchimowu udzatha.
Mudzakhaladi mtendere
Wochoka kwa M’lungu.
(KOLASI)
Inde tidzakhala
Ndi moyo wosatha.
M’lungu walonjeza
Zidzachitika.
3. Akufawo adzauka,
Chisoninso chidzatha.
Mulungu adzapukuta
Misozi ya anthu.
(KOLASI)
Inde tidzakhala
Ndi moyo wosatha.
M’lungu walonjeza
Zidzachitika.
(Onaninso Yes. 25:8; Luka 23:43; Yoh. 11:25; Chiv. 21:4.)