NYIMBO 135
Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga Khala Wanzeru”
Losindikizidwa
1. Mwana wanga undipatse
Mtima wako.
Yemwe akunditonza
Aone yekha
Ukudziperekadi
Mofunitsitsa.
Anthu adziwe
Kuti umandikonda.
(KOLASI)
Mwana wanga wokondedwawe
Ukhale wanzeru chonde
Kuti uzinditumikira,
Inde mwakufuna kwako.
2. Uzinditumikira
Mosangalala.
Ngakhale ukapunthwa
Ndidzakudzutsa.
Ndipo ngati wina
wakukhumudwitsa,
Usadere nkhawa
Ndidzakhala nawe.
(KOLASI)
Mwana wanga wokondedwawe
Ukhale wanzeru chonde
Kuti uzinditumikira,
Inde mwakufuna kwako.
(Onaninso Deut. 6:5; Mlal. 11:9; Yes. 41:13.)