-
Kuvutika Maganizo Chifukwa ChoferedwaGalamukani!—2018 | No. 3
-
-
MFUNDO ZOTHANDIZA AMENE AFEREDWA
Kuvutika Maganizo Chifukwa Choferedwa
A Kostas ananena kuti: “Ine ndi Sophiaa tinakhala m’banja zaka zoposa 39 kufikira pomwe Sophia anadwala kwa nthawi yaitali mpaka kumwalira. Mkazi wanga atamwalira, anzanga anandithandiza kwambiri komanso ndinkayesetsa kudzitangwanitsa ndi zinthu zina. Komabe ndinavutika kwambiri ndi chisoni kwa chaka chathunthu. Nthawi zina ndinkasangalala koma mosadziwika bwino ndinkangopezeka kuti ndakhumudwa. Ngakhale kuti padutsa zaka zitatu, nthawi zina ndimavutikabe maganizo.”
Kodi munaferedwapo? Ngati zinakuchitikiranipo, mwina mungamvetse mmene a Kostas amamvera. Kumwalira kwa mwamuna kapena mkazi wako, wachibale kapena mnzako, kumasokoneza maganizo kwambiri. Akatswiri ofufuza zomwe zimachitika munthu akaferedwa, amavomerezanso kuti zimenezi si zachilendo. Magazini ina inanena kuti: “Anthu akaferedwa munthu amene ankamukonda kwambiri, amamva kuti ataya munthu wofunika amene sadzamuonanso ndipo zimenezi zimawapweteka mumtima.” (The American Journal of Psychiatry) Chifukwa chovutika maganizo mwina mungamadzifunse kuti: “Kodi zinditengera nthawi yaitali bwanji ndikumva chonchi? Kodi ndingadzakhalenso wosangalala? Nanga ndingatani kuti ndisamavutike ndi maganizo?”
Magaziniyi ikuyankha mafunso amenewa. Nkhani yotsatirayi ikufotokoza zimene mungakumane nazo ngati munthu amene munkamukonda anamwalira chaposachedwapa. Nkhani zina za m’magaziniyi zikufotokoza njira zomwe mungatsatire kuti muchepetseko chisoni.
Tikukhulupirira kuti mfundo za m’magaziniyi, zikhala zolimbikitsa kwa aliyense amene akuvutika maganizo chifukwa choferedwa.
a Maina ena asinthidwa.
-
-
Mavuto Amene Mungakumane NawoGalamukani!—2018 | No. 3
-
-
MFUNDO ZOTHANDIZA AMENE AFEREDWA
Mavuto Amene Mungakumane Nawo
Akatswiri ena amanena kuti munthu aliyense amamva chisoni motsatira ndondomeko inayake. Komabe chomwe tikudziwa n’choti aliyense amamva chisoni mosiyana ndi wina. Popeza anthu amakhudzidwa mosiyana akaferedwa, kodi ndiye kuti ena amakhala ndi chisoni chochepa pomwe ena amachita zinthu mokokomeza? Ayi sitingatero. N’zoona kuti kulira kumathandiza munthu akaferedwa komabe sitinganene kuti pali njira inayake yabwino kwambiri yosonyezera chisoni. Nthawi zambiri anthu amasonyeza chisoni potengera chikhalidwe chawo, umunthu wawo, zimene anakumana nazo pa moyo wawo komanso mmene imfayo yachitikira.
ZIMENE MUNGALIMBANE NAZO
Anthu amene mnzawo kapena wachibale wawo wamwalira amasokonezeka ndipo sadziwa zoyenera kuchita. Komabe pali zinthu zina zomwe nthawi zambiri anthu omwe aferedwa amakonda kuchita ndipo zimenezi zimachitikiranso anthu ambiri. Mwachitsanzo zinthu zina zomwe zimakonda kuchitika ndi izi:
Kusokonezeka maganizo. Nthawi zambiri munthu akakhala ndi chisoni amangolira komanso amalakalaka ataonananso ndi womwalirayo. Nthawi zinanso amakhala wosangalala kapena kukwiya kwambiri. Zimenezi zimachitika akalota kapena kukumbukira zomwe womwalirayo ankachita. Wachibale kapena mnzathu akamwalira, zimakhala zovuta kukhulupirira komanso timasokonezeka maganizo. Tiina anafotokoza mmene anamvera mwamuna wake Timo, atamwalira mwadzidzidzi. Ananena kuti: “Thupi lonse linangoti zii moti poyamba sindinalire n’komwe. Ndinasokonezeka maganizo kwambiri ndipo ndinkangomva ngati mpweya wandithera. Sindinkamvetsa kuti chikuchitika n’chiyani.”
Kukhala ndi nkhawa, kukhumudwa komanso kudziimba mlandu. A Ivan ananena kuti: “Patangodutsa nthawi yochepa kuchokera pamene mwana wathu Eric anamwalira, ine ndi mkazi wanga Yolanda, tinkakhala okwiya kwambiri. Zimenezi zinali zachilendo kwambiri chifukwa tinali tisanazichitepo. Tinkadziimbanso mlandu komanso tinkaganiza kuti mwina panali zinazake zomwe tikanachita kuti timuthandize.” Mkazi wa Alejandro, anamwalira atadwala kwa nthawi yaitali. Izi zitachitika, Alejandro ananena kuti: “Poyamba ndinkaona kuti, ‘ngati Mulungu walola kuti ndikumane ndi zimenezi, ndiye kuti ndine munthu woipa kwambiri.’ Kenako ndinayamba kudziimba mlandu chifukwa choona kuti ndimaimba Mulungu mlandu wochititsa kuti mkazi wanga afe.” A Kostas omwe tawatchula koyambirira aja ananena kuti: “Nthawi ina ndinkaona kuti Sophia analakwitsa kumwalira. Kenako ndinadzayamba kudziimba mlandu chifukwa choganiza choncho. Ndipo kunena zoona sikuti iye anachita kufuna kuti amwalire.”
Kulephera kuganiza bwinobwino. Nthawi zina munthu amene ali ndi chisoni maganizo ake amasinthasintha ndipo zimakhala zovuta kumumvetsa. Mwachitsanzo, nthawi zina akhoza kunena kuti wamva mawu a womwalirayo kapena kumuona. Woferedwayo akhozanso kumavutika kuika maganizo ake pa zomwe akuchita komanso amaiwalaiwala. Tiina anafotokoza kuti: “Nthawi zina ndikamacheza ndi munthu wina ndinkapezeka kuti ndayamba kuganiza zina. Ndinkakumbukira zomwe zinkachitika pomwe mwamuna wanga Timo ankamwalira. Zinkandipweteka ndikamalephera kuika maganizo anga pa zomwe ndinkachita.”
Kufuna kukhala panokha. Anthu ena omwe ali ndi chisoni chifukwa choferedwa samasuka akakhala ndi anzawo. A Kostas ananena kuti: “Ndikamacheza pagulu lomwe anthu ake ndi mabanja, ndinkadziona ngati mlendo. Komanso ndikamacheza pagulu la anthu omwe sali pabanja, ndinkamvanso chimodzimodzi.” Nawonso a Yolanda anafotokozanso kuti: “Sindinkamva bwino ndikamacheza ndi anthu omwe ankadandaula za mavuto awo. Ndinkaona kuti mavuto awo ndi aang’ono ndikawayerekezera ndi athu. Nthawi zinanso anthu ena ankatiuza zinthu zabwino zomwe ana awo ankachita. Zinkandichititsa chidwi koma kwinaku ndinkamvanso kupweteka mumtima. Ngakhale kuti ine ndi mwamuna wanga tinkakambirana kuti, ‘basi madzi akatayika sawoleka, tingoyang’ana kutsogolo,’ zinkativuta kuvomereza komanso kukhala oleza mtima.”
Kusokonezeka kwa thanzi. Nthawi zambiri anthu amene ali ndi chisoni, salakalaka chakudya, amaonda komanso sagona mokwanira. Aaron anafotokoza zomwe zinkamuchitikira patadutsa chaka kuchokera pamene bambo ake anamwalira. Iye ananena kuti: “Ndinkalephera kugona. Usiku uliwonse ndinkadzuka, n’kuyamba kuganizira za bambo anga.”
Alejandro anafotokozanso kuti ankangomva ngati akudwala. Iwo ananena kuti: “Maulendo angapo omwe dokotala anandiyeza, ankapeza kuti ndilibe matenda aliwonse. Ndinaona kuti zimenezi zinkachitika chifukwa chosokonezeka ndi chisoni.” Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kupezanso bwino. Ndipotu Alejandro anachita bwino kwambiri kukaonana ndi dokotala. Chisoni chikhoza kuchepetsa chitetezo cha m’thupi, kuwonjezera vuto lomwe linalipo kale komanso kubweretsa mavuto ena m’thupi.
Kulephera kuchita zinthu zofunika. A Ivan ananenanso kuti: “Mwana wathu Eric atamwalira, tinkafunika kudziwitsa achibale, anzake komanso anthu ena. Tinkafunikanso kuuza abwana ake ndi a landilodi ake. Panalinso makalata ambiri a ku boma oti tisainire. Kenako tinayambanso kuonetsetsa kuti tasonkhanitsa zinthu zake zonse. Tinkafunika kuchita zonsezi ngakhale kuti tinali titasokonezeka maganizo.”
Kwa ena, chisoni chimawonjezereka kwambiri akafunika kuchita zinazake zomwe poyamba ankazichita ndi malemuyo. Zimenezi n’zomwe zinachitikira Tiina. Iye ananena kuti: “Mwamuna wanga Timo, ndi amene ankaonetsetsa mmene ndalama zathu zikuyendera ku banki komanso kuyang’anira bizinezi yathu. Tsopano mtolo wonsewu unagwera pa ine moti zinangondiwonjezera nkhawa. Ndiyeno ndinkadzifunsa kuti, ‘Koma ndikwanitsadi kupanga zimenezi pandekha?’”
Kuvutika maganizo, kusokonezeka kwa thanzi komanso mavuto ena omwe tawatchulawa, angachititse munthu amene ali ndi chisoni kuganiza kuti palibe chimene angachite kuti adzakhalenso wosangalala. N’zoona kuti munthu amene timamukonda akamwalira, zimakhala zopweteka kwambiri. Koma kudziwiratu zimene zimachitika kungatithandize kuti tithe kupirira. Komabe tisaiwale kuti zimene anthu ena amachita akakhala ndi chisoni, zimakhala zosiyana ndi ena. Anthu omwe aferedwa akhozanso kulimbikitsidwa akadziwa kuti kuvutika kwambiri ndi chisoni si nkhani yachilendo.
KOMA NDINGADZAKHALENSO WOSANGALALA?
Zimene zimachitika: Munthu akaferedwa, sikuti amangokhalabe ndi chisoni mpaka kalekale. Nthawi ikamapita, chisonicho chimachepa. Apa sizikutanthauza kuti munthu woferedwayo amaiwaliratu za womwalirayo. Komabe nthawi zina akakumbukira zomwe zinachitika nthawi ina kapena tsiku linalake lapadera likafika, akhoza kuyambanso kumva chisoni. Ndipotu pakapita nthawi, anthu ambiri amayambiranso kukhala osangalala n’kumachita zinthu monga mwa nthawi zonse. Izi zimatheka ngati woferedwayo akulimbikitsidwa ndi anzake kapena achibale komanso ngati akutsatira njira zomuthandiza kupirira.
Kodi zimatenga nthawi yaitali bwanji? Kwa anthu ena zimawatengera miyezi kuti aiwale. Ambiri zingawatengere chaka chimodzi kapena ziwiri. Koma pali enanso omwe zingawatengere nthawia ndithu. Alejandro ananena kuti: “Zinanditengera pafupifupi zaka zitatu ndikuvutikabe ndi chisoni.”
Muzichita zinthu modekha. Musamadzipanikize ndi zinthu zambiri ndipo muzikumbukira kuti nthawi ikamapita, chisoni chanu chidzachepa. Koma kodi pali zimene mungachite panopa kuti musamavutike kwambiri ndi chisoni komanso kuti chisakutengereni nthawi yaitali?
Si zachilendo kumva chisoni kwambiri mnzathu akamwalira
a Pali anthu ena omwe amakhala ndi chisoni kwa nthawi yaitali kwambiri mpaka kuyamba kuvutika maganizo. Anthu oterowo amafunika kukaonana ndi dokotala kuti akawathandize.
-
-
Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa—Zimene Mungachite PanopaGalamukani!—2018 | No. 3
-
-
MFUNDO ZOTHANDIZA AMENE AFEREDWA
Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa—Zimene Mungachite Panopa
Pali malangizo ambirimbiri othandizira anthu omwe aferedwa ndipo ena amakhala othandiza kuposa ena. Mwina zimenezi zili choncho chifukwa monga tinafotokozera poyamba paja, anthufe timasonyeza chisoni mosiyanasiyana. Choncho zomwe zingakhale zothandiza kwa wina sizingakhale zothandizanso kwa wina.
Komabe pali mfundo zina zomwe anthu ambiri anaziona kuti n’zothandiza. Mfundozi ndi zomwe kawirikawiri akatswiri othandiza anthu omwe aferedwa, amapereka ndipo zimagwirizana kwambiri ndi mfundo za m’Baibulo.
1: MUZICHEZA NDI ACHIBALE KOMANSO ANZANU
Akatswiri ena amaona kuti njira imeneyi ndi yabwino kwambiri ukafuna kuchepetsa chisoni. Komabe nthawi zina mungaone kuti ndi bwino kungokhala panokha. Mwinanso anthu ena akamakuthandizani mungamamve ngati akungokutopetsani. Umu ndi mmenenso ena amamvera.
Musaganize kuti mukufunika kukhala limodzi ndi anzanu nthawi zonse. Komanso sibwino kuwathamangitsa chifukwa nthawi ina mudzafuna thandizo lawo. Choncho muziwauza mwaulemu zimene mukufuna ndi zimene simukufuna pa nthawiyo.
Muyenera kugawa bwino nthawi yokhala ndi anzanu komanso yochita zinthu panokha mogwirizana ndi mmene mukumvera.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Awiri amaposa mmodzi . . . Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.”—Mlaliki 4:9, 10.
2: MUZIDYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI KOMANSO KUCHITA MASEWERA OLIMBITSA THUPI
Zakudya za magulu onse zingakuthandizeni kuti muthe kupirira mukakhala ndi chisoni. Muzidya zipatso, ndiwo zamasamba komanso zakudya zokhala ndi mapulotini.
Muzimwa madzi ambiri komanso zakumwa zina zopatsa thanzi.
Mukaona kuti simukulakalaka kudya, muzingodya pang’ono koma pafupipafupi. Mukhozanso kupempha a dokotala kuti akupatseni mankhwala othandiza kubwezeretsa zofunika m’thupi.a
Muziyenda mwandawala kapena kuchita masewera enaake olimbitsa thupi kuti muchepetseko nkhawa. Nthawi zina kuchita masewera olimbitsa thupi kungakupatseni mpata woganizira za womwalirayo kapenanso zinthu zina.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”—Aefeso 5:29.
3: MUZIGONA MOKWANIRA
Nthawi zonse kugona mokwanira n’kofunika kwambiri makamaka kwa anthu amene aferedwa. Tikutero chifukwa chisoni chimapangitsa munthu kumva kutopa mwachilendo.
Musamamwe kwambiri khofi kapena mowa chifukwa zakumwa zimenezi zimachititsa kuti munthu azisowa tulo.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.
4: MUZIUZA ENA MMENE MUKUMVERA
Muzikumbukira kuti anthufe timamva chisoni mosiyanasiyana. Ndiyeno mumafunika kudziwa njira yomwe ingakuthandizeni inuyo.
Anthu ena akakhala ndi chisoni amaona kuti amamvako bwino akauza ena mmene akumvera. Pomwe ena amaona kuti imeneyi si njira yabwino. Koma akatswiri ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Mukaona kuti mukufunika kuuza winawake mmene mukumvera koma mukukayikakayika, mukhoza kuyamba ndi kufotokoza zinthu zing’onozing’ono kwa mnzanu yemwe mumamudalira.
Anthu ena amaona kuti kulira kumawathandiza kuti achepetseko chisoni pamene ena sachita kufunika kuti alire kwambiri.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Mtima umadziwa kuwawa kwa moyo wa munthu.”—Miyambo 14:10.
5: MUZIPEWA ZINTHU ZOMWE ZINGAWONONGE THANZI LANU
Anthu ena akaferedwa amaganiza kuti kumwa mowa kwambiri komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kungawachepetsere nkhawa. Komatu zimenezi zimawononga thanzi lawo. Mtendere womwe amapezawo umangokhala wa kanthawi kochepa koma pamapeto pake zimawabweretsera mavuto aakulu. Choncho mukakhala ndi nkhawa muzipeza njira zabwino zomwe zingakuthandizeni.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi.”—2 Akorinto 7:1.
6: MUZIPEZA NTHAWI YOCHITA ZINTHU ZINA
Ena amaona kuti zimakhala zothandiza kuti pa nthawi imene ayamba kumva kwambiri chisoni, azichita zinazake zomwe zingawachititse kuti asamaganizire kwambiri za malemuyo.
Mukhozanso kuchepetsako nkhawa mukamacheza ndi anzanu, kupeza anthu atsopano ocheza nawo, kuphunzira zinthu zatsopano komanso kuchita zinthu zina zosangalatsa.
Nthawi ikamadutsa zinthu zimasintha ndipo mudzaona kuti mwayamba kuiwalako moti zikhoza kumakutengerani kanthawi kuti muyambirenso kuganizira za womwalirayo. Zikatere ndiye kuti chisoni chanu chayamba kuchepa.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . Nthawi yolira ndi nthawi yoseka. Nthawi yolira mofuula ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.”—Mlaliki 3:1, 4.
7: MUZICHITA ZINTHU MMENE MUNKACHITIRA POYAMBA
Musachedwe kuyambanso kuchita zinthu ngati kale.
Mukayambiranso kugona pa nthawi imene munkagona poyamba, kugwira ntchito komanso kuchita zinthu zina zomwe munkachita, sizingakuvuteni kuti muyambirenso kuzolowera.
Mukamatanganidwa ndi kuchita zinthu zofunika, mudzachepetsa chisoni chanu.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pakuti zowawa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukira kawirikawiri, chifukwa Mulungu woona akuchititsa kuti mtima wake uzisangalala.”—Mlaliki 5:20.
8: MUSAMAPUPULUME POSANKHA ZOCHITA PA NKHANI ZIKULUZIKULU
Anthu ambiri amene amasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu wokondedwa wawo atangomwalira kumene, amadzanong’oneza bondo.
Ngati n’kotheka muzidikira kaye kuti padutse nthawi yokwanira musanasamuke, kusintha ntchito yomwe munkagwira, kuwononga kapena kupatsa ena katundu wa malemuyo.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”—Miyambo 21:5.
9: MUZIKUMBUKIRA MALEMUYO
Anthu ambiri omwe anaferedwa, amamvako bwino akamachita zinthu zomwe zimawathandiza kukumbukira womwalirayo.
Zikhozanso kukuthandizani ngati mutasunga zithunzi komanso zinthu zina kuti muzikumbukirabe malemuyo. Mungakhalenso ndi buku loti muzilembamo nkhani zomwe mukufuna kuti muzizikumbukira.
Mungasungenso zinthu zomwe zingamakukumbutseni zinthu zabwino zokhudza malemuyo kuti mudzazione nthawi ina mtima ukadzakhala m’malo.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kumbukirani masiku akale.”—Deuteronomo 32:7.
10: MUTHA KUCHOKAPO KWA MASIKU ANGAPO
Mukhoza kukonza zoti mukapitidweko mphepo kwinakwake.
Ngati simungakwanitse kupita kwinakwake kwa masiku angapo, mukhoza kungochita zinthu zina zoti musangalale nazo kwa tsiku limodzi kapena awiri. Mwina mungapite kunyanja kapena kukaona malo enaake.
Ndipotu ngakhale kungochita zinthu zina zosiyana ndi zomwe mumachita nthawi zonse, kungakuthandizeni kuchepetsako chisoni.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”—Maliko 6:31.
11: MUZITHANDIZA ANTHU ENA
Muzikumbukira kuti nthawi iliyonse imene mukuthandiza ena, nanunso mumasangalala.
Mungayambe ndi kuthandiza anthu enanso omwe akhudzidwa ndi imfa ya wokondedwa wanuyo, monga achibale ndi anzanu.
Mukathandiza ena komanso kuwalimbikitsa pa nthawi yomwe muli ndi chisoni, zingakuthandizeni kuti muyambirenso kusangalala.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
12: MUZIONANSO BWINO ZIMENE MUMACHITA
Mukaferedwa, mumakhala ndi mpata woganizira zinthu zofunika kwambiri.
Muzipezeraponso mwayi woganizira zimene mumachita pa moyo wanu.
Ngati n’kotheka sinthani zina ndi zina zomwe mumachita.
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ndi bwino kupita kunyumba yamaliro kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyerero, chifukwa amenewo ndiwo mapeto a anthu onse. Chotero munthu amene ali moyo aziganizira zimenezi mumtima mwake.”—Mlaliki 7:2.
Kunena zoona, sizingatheke kuti chisoni chanu chidzatheretu. Komabe anthu ambiri amene okondedwa awo anamwalira, anapeza umboni woti kutsatira mfundo zoyenera monga zomwe zili m’nkhaniyi kumawathandiza kuti azisangalala. Ndipotu si kuti nkhaniyi yafotokoza njira zonse zomwe munthu angatsatire kuti achepetseko chisoni. Koma ngati mutayesa kugwiritsa ntchito mfundo zomwe zafotokozedwazi, mukhoza kuona kuti chisoni chanu chayamba kuchepa n’kuyambiranso kukhala osangalala.
a Magazini ya Galamukani! sisankhira anthu thandizo la mankhwala.
-
-
Mfundo Zofunika Kwambiri Kwa Anthu Omwe AferedwaGalamukani!—2018 | No. 3
-
-
MFUNDO ZOTHANDIZA AMENE AFEREDWA
Mfundo Zofunika Kwambiri Kwa Anthu Omwe Aferedwa
OCHITA KAFUKUFUKU AKHALA AKUFUFUZA NJIRA ZOTHANDIZIRA ANTHU OMWE AKUVUTIKA NDI IMFA YA WACHIBALE KAPENA MNZAWO. Komabe, monga mmene tinafotokozera m’nkhani yapitayi, mfundo zothandiza zomwe akatswiriwa amapereka zimagwirizana ndi zomwe Baibulo limanena. Ndipotu Baibulo limapereka malangizo othandiza kwambiri. Malangizo ake amakhala olimbikitsa anthu omwe aferedwa ndipo sitingawapeze kulikonse.
Timadziwa kuti achibale ndi anzathu omwe anamwalira sakuvutika
Pa Mlaliki 9:5, Baibulo limanena kuti: “akufa sadziwa chilichonse.” Limanenanso kuti: “zimene anali kuganiza zimatheratu.” (Salimo 146:4) Mogwirizana ndi mfundozi, Baibulo limayerekezera munthu amene wamwalira ndi amene ali m’tulo.—Yohane 11:11.
Timatonthozedwa kwambiri tikamakhulupirira Mulungu
Pa Salimo 34:15, Baibulo limati: “Maso a Yehovaa ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” Tikamapemphera kwa Mulungu ndi kumuuza mmene tikumvera mumtima, timamva bwino ndipo maganizo athu amayamba kukhala m’malo. Kupemphera kumatithandizanso kuti tikhale paubwenzi ndi Mlengi wathu amene amagwiritsa ntchito mphamvu zake potitonthoza.
Zinthu zabwino zomwe tikuyembekezera m’tsogolo
Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kudzaonanso anthu onse omwe anamwalira atakhalanso ndi moyo. Mavesi angapo m’Baibulo amafotokoza mmene zinthu zidzakhalire nthawi imeneyo. Mwachitsanzo, Baibulo limafotokoza kuti Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Anthu ambiri omwe amakhulupirira Yehova, amatonthozedwa chifukwa chokhala ndi chiyembekezo chakuti adzaonananso ndi okondedwa awo omwe anamwalira. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Ann amene mwamuna wake wazaka 65 anamwalira, ananena kuti: “Ndimalimbikitsidwa chifukwa Baibulo limanena kuti anthu omwe anamwalira sakuvutika komanso kuti Mulungu adzaukitsa anthu onse omwe akuwakumbukira. Mfundo zimenezi zimandilimbikitsa ndikayamba kuganiza za mwamuna wanga ndipo zimandithandiza kuti ndipirire.”
Tiina amene tamutchula m’nkhani yoyambirira, ananena kuti: “Kungochokera pomwe mwamuna wanga Timo anamwalira, Mulungu wakhala akundithandiza. Ndikasokonezeka kwambiri maganizo ndimaona kuti Yehova ali nane. Ndimayembekezera mwachidwi kudzaona akufa akuukitsidwa. Zimenezi zimandilimbikitsa kuti ndisafooke mpaka pomwe ndidzaonanenso ndi mwamuna wangayu.”
Kuwonjezera pa Ann ndi Tiina, palinso anthu ambiri omwe amakhulupirira kuti zomwe Baibulo limanenazi zidzachitikadi. Ngati mukuona kuti zimene Baibulo limanena ndi nthano kapena nkhambakamwa chabe, mutha kufufuza kuti mupeze umboni wotsimikizira kuti zomwe limanena zidzachitikadi. Mwina mwaona kale kuti lili ndi mfundo zothandiza anthu omwe aferedwa.
DZIWANI ZAMBIRI ZOMWE ZIDZACHITIKIRE ANTHU OMWE ANAMWALIRA
Onerani mavidiyo ogwirizana ndi nkhaniyi pa webusaiti ya jw.org
Baibulo limanena kuti m’tsogolomu tidzakumananso ndi okondedwa athu omwe anamwalira
KODI CHIMACHITIKA N’CHIYANI MUNTHU AKAMWALIRA?
Kodi chimachitika n’chiyani anthufe tikafa? Zomwe Baibulo limanena pa nkhaniyi zimatitonthoza
Onani pomwe alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO (Tsegulani Mbali Yakuti: Baibulo
KODI MUNGAKONDE KUMVA UTHENGA WABWINO?
Masiku ano nkhani zoipa zili ponseponse. Koma kodi uthenga wabwino tingaupeze kuti? Vidiyoyi ikufotokoza za kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu.
Onani pomwe alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO (Tsegulani Mbali Yakuti: Misonkhano ndi Utumiki Wathu
a Yehova ndi dzina la Mulungu lomwe limapezeka m’Baibulo.
-