Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr18 July tsamba 1-6
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya July 2018

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya July 2018
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2018)
  • Timitu
  • JULY 2-8
  • CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 6-7
  • nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 6:38
  • nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 6:38
  • Kufufuza Mfundo Zothandiza
  • JULY 9-15
  • CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 8-9
  • Kufufuza Mfundo Zothandiza
  • JULY 16-22
  • nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 10:33, 34
  • Msamariya Anali Munthu Wachifundo
  • Kufufuza Mfundo Zothandiza
  • nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 11:5-9
  • JULY 23-29
  • CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 12-13
  • Kufufuza Mfundo Zothandiza
  • nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 13:33
  • JULY 30–AUGUST 5
  • Kufufuza Mfundo Zothandiza
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2018)
mwbr18 July tsamba 1-6

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya July 2018

JULY 2-8

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 6-7

“Muzikhala Owolowa Manja”

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 6:37

Pitirizani kukhululukira anthu machimo awo ndipo machimo anunso adzakhululukidwa: Kapena kuti “Pitirizani kumasula anthu kuti nanunso mudzamasulidwe.” Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti “kukhululukira” amatanthauza “kumasula munthu n’kumusiya kuti azipita (monga mmene zimakhalira ndi mkaidi).” Choncho popeza mavesiwa akunena kuti tiyenera kusiya kuweruza komanso kutsutsa ena, mawuwa ayenera akutanthauza kumasula kapena kuti kukhululukira munthu amene anali woyenera kupatsidwa chilango.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 6:38

Khalani opatsa: Kapena kuti “Musasiye kupereka kwa ena.” Mawu achigiriki omwe anagwiritsidwa ntchito pavesili angatanthauze kuchita zinthu mopitiriza.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 6:38

m’matumba anu: Mawu ake enieni m’chigiriki ndi “pachifuwa.” Koma muvesili, mawuwa amatanthauza chovala chakunja chimene munthu ankatha kuchipinda n’kukhuthulirapo zinthu. Pa nthawiyo ogulitsa malonda ankakonda ‘kukhuthulira zinthu pa malaya akunja a munthu amene akugula.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 7:35

zotsatira zake: Kapena “ana ake.” Pavesili, nzeru zikufotokozedwa ngati munthu amene ali ndi ana. Palemba la Mateyu 11:19, pomwe amafotokoza nkhani yomweyi, anagwiritsa ntchito mawu akuti “ntchito zake.” Choncho zotsatira kapena kuti ana, zomwe zikuimira zimene Yohane M’batizi komanso Yesu ankachita, zinasonyeza kuti zimene anthu ankawanena zinali zabodza. M’mawu ena tingati Yesu ankanena kuti: ‘Ingoonani ntchito zabwino zimene tikuchita ndipo mutsimikiza kuti zimene anthu akunena ndi zabodza.’

JULY 9-15

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 8-9

“Kodi Chofunika N’chiyani Kuti Munthu Akhale Wotsatira wa Yesu?”

it-2 494

Chisa

Mlembi wina anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.” Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zam’mlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti n’kutsamira mutu wake.”(Mat. 8:19, 20; Luka 9:57, 58) Palembali Yesu ankatanthauza kuti munthu amene akufuna kumutsatira, ayenera kudzimana zinthu zina zimene anthu ena ali nazo ndipo ayenera kudalira kwambiri Yehova. Mfundo imeneyi imaonekeranso bwino m’pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake. Iye anati: “Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.” Komanso anati: “Choncho, dziwani ichi, ndithu palibe aliyense wolephera kulekana ndi chuma chake chonse amene angathe kukhala wophunzira wanga.”​—Mat. 6:11; Luka 14:33.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 9:59, 60

kukaika maliro a bambo anga: Mawuwa sakutanthauza kuti bambo a munthuyu anali atamwalira. Zikanakhala choncho, munthuyu sakanapezeka pamalowa n’kumalankhula ndi Yesu. Kale ku Middle East, mwambo wa maliro unkachitika mofulumira kwambiri ndipo nthawi zambiri ankaika tsiku lomwelo. Choncho sikuti bambo ake a munthuyu anali atamwalira koma ayenera kuti amadwala kapena anali okalamba. Komanso Yesu sakanamuuza munthuyu kuti angosiya bambo ake akudwala kapena akuvutika. Payenera kuti panali anthu ena amene akanawasamalira. (Maliko 7:9-13) Tinganene kuti munthuyu ankauza Yesu kuti, ‘Ndidzakhala wotsatira wanu bambo anga akadzamwalira. Choncho dikirani kaye kuti amwalire kenako ndidzawaike m’manda.’ Koma Yesu ankaona kuti munthuyu akutaya mwayi woika Ufumu wa Mulungu pa malo oyamba m’moyo wake.​—Luka 9:60, 62.

Aleke akufa aike akufa awo: Monga mmene mfundo imene ili pamwambayi yasonyezera, bambo ake a munthu amene ankalankhula ndi Yesuyu ayenera kuti anali akudwala kapena anali okalamba, koma sikuti anali atamwalira. N’kunena kwina, Yesu ankamuuza kuti: ‘Asiye anthu akufa mwauzimu aike akufa awo.’ Zimenezi zikutanthauza kuti munthuyo ankafunika kusiya udindo wosamalira bambo akewo m’manja mwa achibale ake omwe akanawasamalira mpaka pamene adzamwalire. Munthuyu akanavomera kukhala wotsatira wa Yesu akanatha kupeza moyo wosatha ndipo sakanakhala ngati achibale ake aja omwe anali akufa mwauzimu pamaso pa Mulungu. Zimene Yesu anayankha zimasonyeza kuti kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba komanso kuuza ena za Ufumuwo n’kumene kumathandiza kuti munthu akhale wamoyo pamaso pa Mulungu.

nwtsty zithunzi ndi mavidiyo

Kulima pogwiritsa ntchito pulawo

Anthu ankalima pogwiritsa ntchito pulawo m’nyengo yamvula pamene nthaka imakhala yofewa. Kuchita zimenezi kumakhala kovuta m’nthawi yachilimwe chifukwa nthaka imakhala yolimba kwambiri chifukwa cha dzuwa. (sdg mutu 19.) Mapulawo ena ankakhala ndi thabwa losongoka ndipo nthawi zina kunsonga kwake ankaikako chitsulo. Thabwa limeneli linkalumikizidwa kuthabwa lina lomwe linkakokedwa ndi ng’ombe imodzi kapena zingapo. Munthu akamaliza kulima, ankadzala mbewu. Chifukwa chakuti anthu ambiri ankadziwa bwino mmene pulawo imagwirira ntchito, M’Malemba Achiheberi, pulawo samaifotokoza kwambiri. (Ower. 14:18; Yes. 2:4; Yer. 4:3; Mika 4:3) Yesu ankakonda kugwiritsa ntchito zitsanzo zokhudza ulimi akamaphunzitsa mfundo zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, iye ananena za ntchito yolima ndi pulawo pofuna kusonyeza kufunika kotumikira Mulungu ndi mtima wonse. (Luka 9:62) Ngati munthu amene akulima ndi pulawo akuyang’ana m’mbuyo, akhoza kulima mizere yopotoka. Mofanana ndi zimenezi, wophunzira wa Khristu amene wasokonezeka ndi zinthu zina samakhala woyenera Ufumu wa Mulungu.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 8:3

anali kutumikira: Kapena kuti “kuwathandiza.” Mawu achigiriki akuti di·a·ko·neʹo angatanthauze kuthandiza ena powapatsa chakudya, kuwaphikira komanso kuwachitira zinthu zina. Mawuwa anagwiritsidwa ntchito ponena za zinthu zimenezi pa Luka 10:40 (“wandilekerera ndekha ntchito”), Luka 12:37 (“adzawatumikira”), Luka 17:8 (“kunditumikira”) komanso pa Mac. 6:2 (“kugawa chakudya”). Komabe mawuwa angagwiritsidwenso ntchito ponena za zinthu zosiyanasiyana zomwe munthu angachitire ena. Choncho palemba la Luka 8:2, 3, azimayiwa ankathandiza Yesu ndi ophunzira ake kuti azichita bwino utumiki wawo. Zimene azimayiwa anachita zinalemekeza Mulungu ndipo iye anayamikira kwambiri kuwolowa manja kwawo polola kuti nkhani yawo ilembedwe m’Baibulo kuti anthu ena m’tsogolo adzawerenge. (Miy. 19:17; Aheb. 6:10) Mawu achigiriki aja anagwiritsidwanso ntchito ponena za azimayi otchulidwa pa Mat. 27:55 ndi Maliko 15:41.

JULY 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 10-11

“Fanizo la Msamariya Wachifundo”

nwtsty zithunzi ndi mavidiyo

Msewu Wochoka ku Yerusalemu Kupita ku Yeriko

N’kutheka kuti msewu (1) womwe wasonyezedwa m’vidiyoyi ndi umene unkachoka ku Yerusalemu kupita ku Yeriko. Msewuwo unali wa makilomita oposa 20 ndipo ukamatuluka mumzinda wa Yerusalemu unali wotsetsereka mtunda wa kilomita imodzi. Anthu achifwamba ankakonda kubisala mumsewu umenewu womwe unkadutsa m’mapiri. Asilikali ankakhala mumsewuwu nthawi zonse kuti aziteteza anthu odutsa. Mzinda wa Yeriko wa Aroma (2) unali pamene msewuwo unalowa m’chipululu cha Yudeya. Mzinda wakale wa Yeriko (3) unali pamtunda wamakilomita awiri kuchokera mumzinda wa Yeriko wa Aroma.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 10:33, 34

Msamariya wina: Ayuda ankakonda kunyoza Asamariya ndipo ankakana kuchita nawo zinthu limodzi. (Yoh. 4:9) Ayuda ena ankafika mpaka pomagwiritsa ntchito mawu akuti “Msamariya” ngati mawu onyoza komanso amwano. (Yoh. 8:48) Buku lina lotchedwa Mishna limanena kuti Rabi wina ananena kuti: “Munthu amene amadya mkate wophikidwa ndi Asamariya amafanana ndi munthu amene amadya nkhumba.” (Shebith 8:10) Ayuda ambiri sankavomereza umboni woperekedwa ndi Msamariya. Ankakananso Msamariya akamafuna kuwathandiza. Poganizira mmene Ayuda ankaonera Asamariya, Yesu anatchula mfundo yofunika kwambiri m’fanizo la Msamariya wachifundo.

anamanga komanso kuthira mafuta ndi vinyo m’mabalamo: Luka yemwe anali dokotala, anafotokoza fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo ndipo anatchula mwatsatanetsatane mmene anthu pa nthawiyo ankasamalirira munthu amene wavulala. Anthu ankagwiritsa ntchito mafuta ndi vinyo ngati mankhwala othira pabala. Nthawi zambiri mafuta ankathiridwa pabala kuti pafewe (yerekezerani ndi Yes. 1:6), ndipo vinyo ankathandiza kuti tizilombo tomwe tili pabalalo tife. Luka anatchulanso mmene anthu ankamangira pabala kuti lipole msanga.

kunyumba ya alendo: Mawuwa m’Chigiriki amanena za “malo omwe kumapita aliyense.” Anthu omwe ali paulendo komanso ziweto zawo ankatha kupeza malo ogona m’nyumba zimenezi. Eni nyumbazo ankapereka zina ndi zina kwa mlendoyo kwaulere. Koma ngati munthu wapaulendoyo wasiya zinthu zina kuti amusungire, ankayenera kulipira ndalama.

w98 7/1 31 ¶2

Msamariya Anali Munthu Wachifundo

Fanizo la Yesuli limasonyeza kuti munthu wabwino amayesetsa kumvera malamulo a Mulungu komanso kutsanzira makhalidwe ake. (Aefeso 5:1) Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti “Mulungu alibe tsankho.” (Machitidwe 10:34) Kodi nafenso timatengera Yehova poyesetsa kukhala opanda tsankho? Fanizo la Yesuli limasonyeza kuti tiyenera kumakonda aliyense posaganizira dziko, chikhalidwe kapena chipembedzo. Akhristu ayenera ‘kumachitira onse zabwino,’ osati anthu amaphunziro, mtundu, fuko kapena chipembedzo chawo chokha. Sitiyenera kumangosonyeza chikondi kwa abale ndi alongo okha.​—Agalatiya 6:10.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 10:18

Ndinayamba kuona Satana atagwa kale ngati mphezi kuchokera kumwamba: Yesu ankanena zinthu zomwe zidzachitike m’tsogolo. Iye ankatha kuona Satana atagwetsedwa pansi kuchokera kumwamba ndipo zinkangokhala ngati zachitika kale. Lemba la Chiv. 12:7-9 limanena za nkhondo yomwe inachitika kumwamba Ufumu wa Mesiya utangoyamba kulamulira ndipo limasonyeza kuti Satana anagwetsedwa pansi. Apa Yesu ankanena za kugonjetsedwa kwa Satana ndi ziwanda zake pa nkhondo yomwe inkayenera kudzachitika m’tsogolo chifukwa anali ataona kuti Mulungu wapereka mphamvu yotulutsa ziwanda kwa ophunzira ake 70 aja, omwe anali opanda ungwiro.​—Luka 10:17.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 11:5-9

Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate: Kale ku Middle East, anthu ankaona kuti kulandira bwino alendo n’kofunika kwambiri ngati mmene fanizoli limasonyezera. Ngakhale mlendo atafika pakati pa usiku, mwina chifukwa cha mavuto ena okhudzana ndi mayendedwe, munthu yemwe walandira mlendoyo ankayenera kumupatsa chakudya. Iye ankaona kuti kupatsa mlendo wakeyo chakudya n’kofunika kwambiri kuposa kusokoneza tulo ta mnzake yemwe ankamugogodera pakati pa usiku kuti amubwereke chakudyacho.

Usandivutitse ine: Mnzake amene anapita kukamugogodera m’fanizoli ankaoneka kuti sankafuna kumuthandiza osati chifukwa choti anali wovuta. Zikuoneka kuti anachita zimenezi chifukwa anali atagona kale. Nyumba za nthawi imeneyo, makamaka za anthu osauka, zinkakhala zopanda chipinda. Ndiye ngati munthu yemwe ankagogoderedwayo akanadzuka, ndiye kuti akanadzutsa banja lake lonse kuphatikizapo ana.

chifukwa cha kukakamira kwake: Mawuwa m’Chigiriki amatanthauza “kupanda ulemu” kapena “kupanda manyazi.” Komabe, pavesili amatanthauza kupitirizabe kupempha kapena kusagonja msanga. Munthu wa mufanizo la Yesuli, sanachite manyazi kapena kugonja pamene ankakagogoda kwa mnzake uja. Apa Yesu ankafuna kuti nawonso ophunzira ake azipemphera mobwerezabwereza kapena kuti mosalekeza.​—Luka 11:9, 10.

JULY 23-29

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 12-13

“Ndinu Ofunika Kwambiri Kuposa Mpheta Zambiri”

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 12:6

mpheta: Mawu achigiriki akuti strou·thiʹon amatanthauza mbalame zazing’ono. Koma nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito ponena za mpheta zomwe zinali mbalame zotsika mtengo zimene anthu ankagula kuti akadye.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 12:7

ngakhale tsitsi lonse la m’mutu mwanu analiwerenga: Anthu ena amanena kuti m’mutu mwa munthu muli tsitsi loposa 100,000. Popeza Yehova amadziwa zinthu zing’onozing’ono ngati zimenezi, ayenera kuti amaganizira kwambiri wotsatira aliyense wa Khristu.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 13:24

Yesetsani mwamphamvu: Kapena kuti “Chitani khama.” Mawu a Yesuwa amasonyeza kuti n’zofunika kwambiri kuti tizichita zonse zomwe tingathe kuti tilowe pakhomo lopapatiza. Mabaibulo ena amamasulira mawuwa kuti “Muyesetse ndi mphamvu zanu zonse” kapena “Muchite khama kwambiri.” Mawu achigiriki akuti a·go·niʹzo·mai amafanana ndi mawu enanso achigiriki akuti a·gonʹ, omwe ankakonda kugwiritsidwa ntchito akamanena zamasewera. Pa Aheberi 12:1, mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa ponena za mpikisano wa moyo wosatha. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito ponena za “nkhondo” (Afil. 1:30; Akol. 2:1) kapena “kumenya” (1 Tim. 6:12; 2 Tim. 4:7). Mawu achigiriki omwe ali pa Luka 13:24 angamasuliridwenso kuti “wochita nawo mpikisano” (1 Akor. 9:25), “poyesetsa kwambiri” (Akol. 1:29; 4:12; 1 Tim. 4:10) komanso “Menya nkhondo” (1 Tim. 6:12). Ndiye popeza mawuwa ankanena za mipikisano yomwe inkachitika kale, ena amaona kuti Yesu ankayerekezera khama limene munthu amafunika kuchita kuti alowe pakhomo lopapatiza ndi zimene munthu wochita masewera ankachita. Iye ankayesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti apambane.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 13:33

n’kosayenera: Kapena kuti “sizingatheke.” Ngakhale kuti palibe ulosi womwe umanena kuti Mesiya adzaphedwera ku Yerusalemu, mawu amenewa ayenera anachokera pa Danieli 9:24-26. Komanso, anthu ankayembekezera kuti ngati Ayuda angadzaphe mneneri, kapena Mesiya, akanamuphera mumzindawu. Khoti Lalikulu la Ayuda lomwe linapangidwa ndi oweruza 71, linkakumana ku Yerusalemu ndipo anthu onse omwe ankazengedwa mlandu woti ndi aneneri onyenga ankakaweruzidwa kumeneko. Yesu ayeneranso ankadziwa kuti ku Yerusalemu n’kumene anthu ankapereka nsembe kwa Mulungu komanso kumene mwana wankhosa wa Pasika ankaphedwa. Mawu a Yesuwa anakwaniritsidwadi. Iye anaweruzidwa ndi Khoti Lalikulu la Ayuda kuti aphedwe. Ndipo ndi ku Yerusalemu komweko pafupi ndi mpanda wa mzinda komwe Yesu anaphedwa ngati ‘nsembe ya pasika.’​—1 Akor. 5:7.

JULY 30–AUGUST 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 14-16

“Fanizo la Mwana Wolowerera”

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 15:11-16

Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri: Zinthu zina zimene zinafotokozedwa m’fanizo la mwana wolowerera ndi zochititsa chidwi kwambiri. Fanizoli ndi limodzi mwa mafanizo aatali kwambiri amene Yesu anapereka. Chinthu chochititsa chidwi kwambiri ndi choti anafotokoza za anthu a m’banja limodzi. M’mafanizo ena, Yesu ankakonda kugwiritsa ntchito zinthu monga mbewu, nthaka kapena anthu ena omwe si apachibale kwenikweni monga munthu ndi antchito ake. (Mat. 13:18-30; 25:14-30; Luka 19:12-27) M’fanizoli, Yesu anasonyeza bwino kwambiri mmene bambo ankakondera ana ake. N’kutheka kuti anthu ambiri amene anamva fanizoli sanaleredwe ndi bambo wachikondi ngati ameneyu. Fanizoli limasonyeza mmene Atate wathu wakumwamba amakondera ana ake apadziko lapansi omwe amayesetsa kumumvera komanso amene amabwerera kwa iye akasochera.

Wamng’ono: Malinga ndi chilamulo cha Mose, mwana ankalandira magawo awiri a cholowa cha bambo ake. (Deut. 21:17) Choncho ngati mwana wamkulu ankayenera kulandira magawo awiri, mwana wamng’ono ankayenera kulandira hafu ya cholowa cha wamkuluyo.

anasakaza: Mawuwa m’Chigiriki amatanthauza “kumwaza zinthu.” (Luka 1:51; Mac. 5:37) Pa Mat. 25:24, 26, mawuwa anamasuliridwa kuti “kupeta.” Palembali mawuwa amatanthauza kuwononga kapena kugwiritsa ntchito ndalama mopanda nzeru.

m’makhalidwe oipa: Kapena kuti “moyo woipa (khalidwe lotayirira; moyo wangati nyama).” Mawu ofanana ndi amenewa anagwiritsidwa ntchito pa Aef. 5:18; Tito 1:6; 1 Pet. 4:4 ndipo amatanthauza zomwezi. Ndiye popeza mawuwa amanenanso za kuchita zinthu mowononga, Mabaibulo ena amamasulira mawuwa kuti “moyo wolowerera.”

kuti azikaweta nkhumba: Malinga ndi Chilamulo, nkhumba zinali zodetsedwa. Choncho ntchito yoweta nyamazi inali yonyozeka komanso yosayenera kwa Ayuda.​—Lev. 11:7, 8.

chakudya cha nkhumba: Chakudya chimene chikutchulidwa apa ndi mtundu wina wa zipatso zooneka ngati chitimbe. Zimaoneka zabulawuni, zokhota ngati nyanga ndipo izi n’zogwirizana ndi tanthauzo la mawu achigiriki otchulira chakudyachi (ke·raʹti·on, kapena kuti “nyanga yaing’ono.”) Zakudya zimenezi zimagwiritsidwabe ntchito masiku ano ngati chakudya cha mahatchi, ng’ombe komanso nkhumba. Zikuoneka kuti mnyamatayu anakumana ndi mavuto aakulu moti mpaka anafika posirira chakudya cha nkhumba.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 15:17-24

ndachimwira inu: Kapena kuti “pamaso panu.” Mawu achigiriki akuti e·noʹpi·on, amatanthauza “munthu wina akuona,” ndipo mawuwa anagwiritsidwanso ntchito pa 1 Sam. 20:1, m’Baibulo la Septuagint. Palemba limeneli, Davide anafunsa Yonatani kuti: “Bambo ako ndawachimwira chiyani?”

aganyu: Atabwerera kwawo, mwana wamng’onoyo anapempha bambo ake kuti azimutenga ngati waganyu wawo, osati ngati mwana wawo. Pa nthawiyo aganyu sankawerengedwa ngati antchito okhazikika ngati mmene zinalili ndi akapolo. Nthawi zambiri ankakhala anthu omwe ankawalemba ntchito kwa tsiku limodzi lokha.​—Mat. 20:1, 2, 8.

anamupsompsona mwachikondi: Kapena kuti “anamukisa.” Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “anamupsompsona mwachikondi” ndi mawu otsindika ochokera ku mawu akuti phi·leʹo, omwe nthawi zina amatanthauza “kupsompsona.” (Mat. 26:48; Maliko 14:44; Luka 22:47) Koma nthawi zambiri mawuwa amatanthauza “kukonda kwambiri” munthu wina. (Yoh. 5:20; 11:3; 16:27) Popeza m’fanizo lija bambo analandiranso mwana wakeyo mwachikondi, anasonyeza kuti anali atam’khululukira ndi mtima wonse.

kutchedwa mwana wanu: M’mipukutu ina anawonjezera mawu akuti: “Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.” Komabe mu Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso mulibe mawuwa chifukwa sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yakale kwambiri. Akatswiri ena amanena kuti mawu akuti “Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu” anawonjezeredwa kuti zifanane ndi zimene zimapezeka pa Luka 15:19.

mkanjo . . . mphete . . . nsapato: Mkanjo umenewu sunali chovala wamba. Chinali chovala chapamwamba kwambiri, chokongoletsedwa bwino chomwe ankapereka kwa alendo olemekezeka kwambiri. Kuveka mwanayo mphete kunkasonyeza kuti bamboyo amamukondabe komanso kumulemekeza ngati mwana wake. Kawirikawiri akapolo sankavala mphete komanso nsapato. Choncho pomupatsa mwanayo zinthu zimenezi, bamboyo ankasonyeza kuti wamulandiranso ngati mwana wake weniweni.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 14:26

osadana: M’Baibulo, mawu akuti “kudana” ali ndi matanthauzo ambiri. Mawuwa angatanthauze kuwawidwa mtima ndi munthu mpaka kufika pomuchitira zoipa. Kapena akhoza kutanthauza kunyansidwa ndi munthu kapena chinthu chinachake n’kufika posafuna kuchiyandikira kapena kuchiona n’komwe. Akhozanso kutanthauza kukonda chinthu pang’ono poyerekeza ndi china. Mwachitsanzo, Baibulo lachingerezi limanena kuti Yakobo anali “kudana” ndi Leya koma ankakonda Rakele. Mawu amenewa amatanthauza kuti Leya sanali kukondedwa kwenikweni tikayerekeza ndi mmene Yakobo ankakondera Rakele. (Gen. 29:31; Deut. 21:15) Mawuwa anagwiritsidwanso ntchito m’mabuku ena achiyuda akale kwambiri. Choncho, Yesu sankatanthauza kuti otsatira ake azinyansidwa ndi achibale awo ngakhalenso moyo wawo umene, chifukwa zimenezi zikanakhala zosemphana ndi Malemba. (Yerekezani ndi Maliko 12:29-31; Aef. 5:28, 29, 33.) Palembali, mawu akuti “kudana” angatanthauze “kukonda chinthu pang’ono poyerekeza ndi chinthu china.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena