Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Achichepere Amene ‘Amadalira Yehova’
    Nsanja ya Olonda—1994 | January 1
    • Achichepere Amene ‘Amadalira Yehova’

      ACHICHEPERE alibe ulamuliro wonse pakukongola, ndiponso achikulire sali ndi nzeru zonse. (Yerekezerani ndi Miyambo 11:22; Mlaliki 10:1.) Mmalo mwake, awo amene ali ndi kukongola kokhalitsa ndi nzeru yeniyeni ali awo amene amadalira Yehova ndipo ndi mtima wonse amanena za iye kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.”​—Salmo 31:14; Miyambo 9:10; 16:31.

      Kuzungulira dziko lonse pali unyinji wa anthu okongola umene ukuwonjezereka, achichepere ndi achikulire omwe, amene amasonyeza nzeru yawo mwa kutumikira Mulungu ndi kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Mwachitsanzo, talingalirani za Sabrina wazaka zisanu ndi zitatu.

      Sabrina amakhala ku Germany ndipo ali m’giredi lachiŵiri. Iye ndimmodzi wa Mboni za Yehova woyamba kuloŵa pasukulupo. Mwachisoni, iye anali munthu wotonzedwa ndi anzake akusukulu kufikira tsiku limene mphunzitsi anapempha ophunzira kuti adze ndi buku lawo lokondedwa m’kalasi. Sabrina anasankha kupita ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Usikuwo, ngakhale kuti anali ndi mantha, anakonzekera bwino lomwe zoti akachite m’kalasi. Popeza kuti panali ophunzira 26 m’kalasi mwake, iye anadziŵa kuti mwina sakakhala ndi nthaŵi yambiri. Koma anali wotsimikizira kusalola aliyense kudodometsa ulaliki wake ndipo anali wotsimikizira kuti Yehova akamthandiza. Patsiku losankhidwalo, mphunzitsi anafunsa za amene anali atadza ndi buku lake ndi amene akanakonda kukhala woyamba kulisonyeza. Modabwitsa, Sabrina yekha ndiye amene anadza ndi buku. Anaimirira patsogolo pa kalasiyo nayamba kulankhula, akumaŵerenga ndi kusonyeza zithunzithunzi za m’bukulo nafotokoza kuti zonsezo zinali zochokera m’Baibulo. Pomaliza iye anafunsa kuti: “Kodi ndani amene angakondwerere kukhala ndi buku limeneli?” Iye anagaŵira mphunzitsi kope limodzi, ndipo m’masiku angapo otsatira, anagaŵira mabuku ena owonjezereka khumi kwa anzake a m’kalasi. Ndemanga yokha ya mphunzitsiyo paulaliki wake inali yakuti: “Sindinaonepo zoterezi.” Anapatsa Sabrina giredi A chifukwa cha ntchito yake.

      Kunena zowona, Mboni zambiri zachichepere zili ofalitsa achimwemwe a mbiri yabwino kusukulu. Chitsanzo china ncha Erika, wofalitsa wa zaka 11 wa ku Mexico. Iye waphunzitsidwa kukonda Yehova kuyambira paubwana. Amachita bwino kwambiri pantchito yake ya kusukulu. Imodzi ya ntchito zake inali kukonzekera nkhani yonena za AIDS ndi kumwerekera ndi fodya ndi moŵa. Anakonzekera bwino lomwe, akumagwiritsira ntchito magazini a Galamukani!, ndipo analandira magiredi apamwamba koposa. Mphunzitsi wake anamfunsa za kumene anapeza chidziŵitsocho ndipo iyeyo anapatsidwa magazini amene anali ndi nkhani zimenezo. Pambuyo pake, mphunzitsiyo anagwiritsira ntchito magazini ameneŵa kufotokozera nkhaniyo kalasi yake yonse. Chifukwa cha khalidwe la Erika, kulemekeza aphunzitsi ake, ndi magiredi ake apamwamba, iye wayenerera kulandira mphatso, madipuloma, ndi kulandira ndalama pang’ono zopititsira maphunziro patsogolo. Komabe, iye akulingalira kuti zipambano zake zazikulu koposa zakhala zakuti wadzidziŵikitsa monga mmodzi wa Mboni za Yehova, wakhoza kugaŵira mabuku ofotokoza Baibulo, ndipo wakwezetsa dzina la Mulungu.

      Ndiyeno pali Shannon, mnyamata wazaka khumi amene amakhala ku New Zealand. Iye ali ndi diso limodzi lokha loona; lina linafa chifukwa cha kansa pamene anali kamwana. Pamene Shannon anali wazaka zisanu ndi ziŵiri amake anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komabe, pasanapite nthaŵi yaitali atayamba kuphunzira Baibulo, iwo anayamba kukhala ndi mwamuna wina popanda ukwati ndipo anasankha kuleka kuphunzira kwawo. Shannon anachonderera kuti phunziro lake Labaibulo lipitirizebe. Pempho lakelo linavomerezedwa. Mbonizo zinapitirizabe kufika, ndipo potsirizira pake ziŵalo zonse zitatu za banjalo zinaphunzira Baibulo ndi kupita patsogolo mwauzimu. Atakwatirana mwalamulo, amake Shannon ndi atate wake omlera anabatizidwa.

      Tsiku lina Shannon ndi mkazi wa woyang’anira dera anali muutumiki wakumunda. Mwininyumba wina anafunsa Shannon kuti: “Kodi nchiyani chimene chinachitikira diso lako?” “Linali ndi kansa, ndipo linachotsedwa,” iye anayankha motero. “Posachedwapa Yehova adzandipatsa latsopano m’Paradaiso, ndizo zimene tafikira pano kudzakuuzani.”

  • Kuchirimika Kudzetsa Mfupo Zazikulu
    Nsanja ya Olonda—1994 | January 1
    • Lipoti la Olengeza Ufumu

      Kuchirimika Kudzetsa Mfupo Zazikulu

      YESU ananeneratu kuti otsatira ake akazunzidwa, ndipo nayenso mtumwi Paulo anatero, monga momwe kwanenedwera pa 2 Timoteo 3:12 kuti: “Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” Koma kuchirimika potumikira Yehova Mulungu kumadzetsa mfupo zazikulu.

      ◻ Zimenezi zinali choncho m’tauni ina ya kugombe la kumpoto koma cha kummaŵa kwa Malaysia. Ngakhale kuti anali Mbuddha wolimba amene anaphunzitsa ana ake kwambiri, atateyo analephera kuletsa ana ake aakazi atatu ndi ana aamuna atatu kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Ngakhale mkazi wake anakondwereranso chowonadi. Ndiyeno tsiku lina mnansi wake wina anamnyodola akumati: “Kodi mungalephere motani kulamulira ana anu ndi kuwalola kukhala Mboni za Yehova? Inetu ana anga onse amandimvera ndipo ali m’chipembedzo cha Chibuddha cha makolo athu. Mumachititsa chisoni kwambiri!”

      Atatewo anamka kunyumba kwawo mofulumira akumawopseza kukamenya mlongo amene anali kuchititsa maphunziro kwa ana akewo. Komabe, anawo anawaletsa kuchita motero napitiriza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndi kufika pamisonkhano mochirikizidwa ndi amayi awo.

      Komabe, potsirizira pake, atatewo anaitana banja lonselo pamaso pawo. “Sankhani,” iwo analamula motero, “pakati pa ine ndi kukhala panyumba pano ndi kukhala Akristu ndi kuchoka panyumba pano.” Mwana wamkulu wamwamuna, mnyamata wolankhula mofatsa kwambiri, nthaŵi yomweyo anayamba kulongedza katundu kuti achoke. “Ayi!” atatewo anafuula motero. “Popeza kuti nonsenu ndinu ana opanduka, kuli bwino kuti ndingofa.” Ndiyeno anatuluka m’nyumbamo mofulumira, banjalo likumawalondola, ndi kuwachonderera kuti asadziphe. Atachita chidwi ndi kuchonderera kwawo, anabwerera kunyumba.

      Panapita nthaŵi. Atateyo anayamba kuona chiyambukiro chabwino cha chowonadi Chabaibulo pakhalidwe la ana ake. Tsiku lina anakumana ndi bwenzi lake lomnyodola lija, limene tsopano linali lachisoni, limene linati: “Ndagwiritsidwa mwala kwambiri ndi ana anga. Amandinamiza ndi kundibera zinthu.” Koma atate amene ana awo anali kuphunzira chowonadi ndi Mboni za Yehova anati: “O, ana anga sachita zimenezo! Iwo ngokoma mtima kwambiri kwa ine ndipo anandithandizadi kulipirira ndalama za galimoto langa pamene sindinali pantchito.”

      Lerolino, ana aakazi atatu ndi amayi awo ngobatizidwa. Mwana wamwamuna mmodzi ndimpainiya wapadera. Ndipo bwanji za amene kale anali atate wotsutsa ndi waukali kwambiriyo? Iye tsopano ngwaubwenzi ndipo anafika pa Chikumbutso.

      Yehova anafupa mwana wamwamunayo ndi alongo ake atatu limodzinso ndi amayi awo chifukwa cha kuchirimika kwawo kwa Iye. Iwo tsopano ali alaliki Aufumu achangu, akumakondweretsa mtima wa Yehova.​—Miyambo 27:11.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena