Kodi Mukuona Kusoŵako?
1 Yehova amafotokozedwa kukhala Mthandizi ndi Ngaka. Tikudziŵa kuti tingathe kupita kwa iye panthaŵi ya kusoŵa ndipo adzatithandiza. (Sal. 18:2; 46:1) Tingatsanzire mkhalidwe wachifundo umenewu mwa kupereka thandizo kwa ena pamene tiona kusoŵa kwawo.
2 Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera munthu kudzipereka kuthandiza wina? Anthu ochuluka amadziŵa kuti kuchita zimenezi ndi chibadwa cha munthu cha chikondi. Indedi Mawu a Mulungu amalimbikitsa zimenezi. (Aroma 15:1) Paulo anatilimbikitsa ‘kusapenyerera zathu za ife tokha, koma kupenyerera za anzathu.’—Afil. 2:4.
3 Kuchita zimenezi kungatikondweretse tonsefe. (Mac. 20:35) Paulo anatchula mnyamatayo Timoteo monga chitsanzo cha munthu amene ‘akasamalira za kwa’ abale ake. (Afil. 2:20) Ndi bwino kuti tili ndi achichepere ambiri m’mipingo lerolino amene ali ndi khalidwe longa limenelo. Koma kaya ndife wachichepere kapena wachikulire, zilipo zinthu zimene tiyenera kuchita titaona kusoŵa kwina.
4 Kodi munalingalirapo kuti ena ali ndi zosoŵa zimene zingasamaliridwe bwinopo? Mwinamwake mbale kapena mlongo anali m’chipatala, ndipo oŵerengeka okha ndiwo anakamzonda; kapena wina anapuwala, koma panalibe wotumikira kapena wothandiza ntchito za panyumba. Yesu amaona aja amene akutumikira Yehova monga a m’banja limodzi amene amasamaliranadi. (Marko 3:33-35) M’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, iye anasonyeza kuti aja amene ali kudzanja lamanja la Mfumu ali oyanjidwa chifukwa cha kuthandiza kwawo abale a Mfumuyo.—Mat. 25:40.
5 Kodi Ndingathandize Motani? Kodi chingachitidwe nchiyani kuti thandizo liperekedwe pamene pali kusoŵa koonekeratu? Kodi ife tingayambe kuthandiza mwa njira ina? Mwinamwake pali okalamba amene afunikira chilimbikitso, koma alibe mabwenzi apafupi owathandiza. Pangakhale achichepere amene afunikira thandizo. Banja lokondwerera chatsopano la ana ambiri lingafike pa Nyumba Yaufumu pamene wofalitsa yemwe amaphunzira nawo palibe. Iwo angayamikire ngati wina angadzipereke kuthandiza ana awo.
6 Pamene chikondi chathu pa choonadi ndi gulu la Yehova chikukula, nakonso kuzindikira ena mumpingo ndi kuwadera nkhaŵa kumakula. Paulo anatilimbikitsa kukulitsa mikhalidweyo pankhaniyi. (2 Akor. 6:11-13) Yesu anagogomezera kuti kusonyezana kwathu chikondi ndiko njira yaikulu imene timasonyezera kuti tilidi otsatira ake.—Yoh. 13:35.
7 Chotero pamene tiona kusoŵa, chikondi chenicheni pa abale athu ndi mpingo chiyenera kutisonkhezera kuchitapo kanthu ndi kuwathandiza mwa njira iliyonse imene tingathe. (Agal. 6:9, 10) Kusamalira ena kumeneku kumatigwirizanitsa pamodzi m’zomangira zolimba za chikondi ndi umodzi. (1 Akor. 10:24) Mwa njira imeneyi, timachita mbali yathu ya kusamalira kusoŵa mumpingo.