Mfundo Zazikulu za Baibulo Nyimbo ya Solomo 1:1–8:14
Chikondi Chowona Chiri Chachipambano!
Pali chikondi chimene sichilephera. Icho chiri chokhazikika, chopirira, chopambana. Chikondi chosagwedezeka chimenecho chiripo pakati pa Yesu Kristu ndi “mkwatibwi,” wake kapena mpingo wodzozedwa ndi mzimu. (Chivumbulutso 21:2, 9; Aefeso 5:21-33) Ndipo ndi mokongola chotani nanga mmene chikondi chimenechi chasonyezedwera mu Nyimbo ya Solomo!
Yopangidwa zaka 3,000 zapita ndi Mfumu yanzeru Solomo ya Israyeli, “nyimbo yoposa” imeneyi (1:1) imanena za chikondi chomwe chinalipo pakati pa mbusa ndi mtsikana wa ku mudzi wa m’mudzi wa Sunemu (Sulemu). Ndi chuma chake chonse ndi ulemerero, mfumuyo inali yosakhoza kupeza chikondi cha Msulami, popeza iye anali wokhulupirika kwa mbusa wokondedwa wake.
Pamene bukhu la ndakatulo limeneli liŵerengedwa ndi chisamaliro chenicheni ndi chiyamikiro, ilo limapereka kwa atumiki a Yehova osakwatira ndi okwatira chakudya chambiri kaamba ka lingaliro ponena za kuyera, kukoma mtima, kukhulupirika, ndi chikondi chomangira chomwe chiyenera kukhala maziko aukwati Wachikristu. Ndithudi, tonsefe tingapindule kuchokera ku nyimbo imeneyi yonena za chipambano cha chikondi chowona.
Msulami mu Msasa wa Solomo
Chonde ŵerengani Nyimbo ya Solomo 1:1-14. Mu mahema a chifumu, Msulamiyo akulankhula ngati kuti mbusa wake wokondedwa alipo. Solomo akuyamikira kukongola kwake ndi kumlonjeza kumkometsera iye ndi zinthu za golidi ndi siliva. Koma mtsikanayo akupewa zifikiro zake ndi kumlola iye kudziŵa kuti iye ali ndi chikondi chowona kokha kwa mbusa.
◆1:2, 3—Nchifukwa ninji ziyerekezo zimenezi pakati pa vinyo ndi mafuta zinali zoyenera?
Vinyo amasangalatsa mtima ndi kulimbikitsa moyo wopsyinjika. (Masalmo 104:15; Miyambo 31:6) Mafuta anali kuthiridwa pa alendo oyanjidwa kaamba ka kuthekera kwake kwa kusalalitsa. (Masalmo 23:5; Luka 7:38) Chotero Msulami wopsyinjikayo analimbikitsidwa ndi kutonthozedwa mwa kukumbukira “chikondi choposa” cha mbusa ndi “dzina” lake. Mofananamo, otsalira a atsatiri odzozedwa a Kristu akulimbikitsidwa mwakusinkhasinkha pa chikondi ndi zitsimikiziro za mbusa wawo, Yesu Kristu, ngakhale kuti iwo adakali padziko lapansi ndipo opatulidwa kuchokera kwa iye.
phunziro kwa Ife: Solomo akanalemeretsa Msulami ndi “nkhata zagolidi” ndi “njumu zasiliva,” koma iye anakana ziyeso za zinthu zakuthupi zimenezi ndi kutsimikizira za chikondi chake chosalephera kaamba ka mbusa. (1:11-14) Kuwunikira pa khalidwe lake kungalimbikitse chigamulo cha gulu la “mkwatibwi” kukana mkhalidwe wokondetsa zinthu zakuthupi wonyenga wa dziko ndi kukhalabe okhulupirika kwa mkwati wawo wa kumwamba. Ngati ziyembekezo zathu ziri zapadziko lapansi ndipo tikulingalira kukwatira, lolani kuti chitsanzo cha mtsikana chimenechi chitisonkhezere ife kupanga zinthu zauzimu, ndipo osati zinthu zakuthupi, zikondwerero zathu zodera nkhaŵa zoyamba.
Kulakalaka Kwaubwenzi
Ŵerengani 1:15–3:5. Mbusayo alowa m’msasa wachifumu ndi kunena chikondi chake kaamba ka Msulami wodzichepetsa, yemwe anamlemekeza iye pamwamba pa ena onse. Pamene iwo anapatukana, mtsikanayo anakumbukira nthaŵi za chisangalalo ndi wokondedwa wake ndi kuchonderera kuti iye afulumire kusendera kumbali yake. Usiku, iye anamlakalaka iye.
◆ 2:1-3—Nchiyani chimene mawu ophiphiritsira amenewo akutanthauza?
Msulami anadzitcha iyemwini “nduŵa lofiira la ku Saroni,” chifukwa anali wodzichepetsa, mkazi wachichepere wodekha yemwe anadziwona iyemwini monga kokha mmodzi wa maluŵa ofala ambiri. Mbusayo, ngakhale kuli tero, anazindikira kuti iye anali “kakombo pakati pa minga,” popeza iye anali wokongola wokhoza kuchita zinthu, ndipo wokhulupirika kwa Yehova. Kwa mtsikanayo, mbusayo anali monga “maula pakati pa mitengo ya m’nkhalango” chifukwa iye anali mwamuna wachichepere woyedzamira ku zinthu zauzimu mofananamo wodzipereka kwa Mulungu ndipo wokhala ndi zikhoterero ndi kuthekera kokhumbirika kwambiri. Mkristu wosakwatira wofunafuna mnzake m’moyo ayenera kuyang’ana kokha kaamba ka wokhulupirira mnzake wokhulupirika wokhala ndi mikhalidwe yonga ija ya Msulami kapena mbusa wake wokondedwa.
◆ 3:5—Nchifukwa ninji lumbiro limeneli linagwirizanitsidwa ndi nyama zimenezi?
Mphoyo ndi nswala ziri nyama zodekha, zofatsa, ndi zokongola zomwe zirinso za liŵiro ndi zoyenda motsimikizira. M’chenicheni, chotero, mtsikanayo anali kumangirira “ana akazi a Yerusalemu” mu chilumbiro ndi zonse zomwe ziri zokongola ndi zodekha. Ndi zolengedwa zimenezi, iye anali kukakamiza akazi amenewo kupewa kuyesera kudzutsa chikondi mwa iye kaamba ka wina aliyense wosakhala mbusa wake wokondedwa.
Phunziro kwa Ife: Mtsikanayo anaika “ana akazi a Yerusalemu,” kapena akazi a m’mabwalo omwe anali kudikirira pa mfumu, pansi pa chilumbiro ‘kusagalamutsa chikondi mwa iye mpaka chitafuna mwini.’ (2:7; 3:5) Ichi chikusonyeza kuti sichiri chothekera kukhala ndi chikondi cha mwambi kaamba ka wina aliyense. Mtsikana iyemwiniyo sanadzimve kukhala wokopedwa ndi Solomo. Chiri chanzeru chotani, nanga, kwa Mkristu wosakwatira yemwe akulingalira kukwatira kulingalira kokha wolambira wa Yehova wabwino ndi wokhulupirira yemwe angakondedwedi!—1 Akorinto 7:39.
Mtsikanayo mu Yerusalemu
Ŵerengani 3:6–6:3. Solomo anabwerera ku Yerusalemu mu ulemerero. Mbusayo analankhula ndi mtsikanayo kumeneko ndi kumlimbikitsa iye ndi chikondi choposa. M’maloto, iye mochedwa anayankha ku kugogoda kwa wokondedwa wake ndipo anavutitsidwa ndi alonda pamene iye anali kufunafuna osaphula kanthu kaamba ka iye. Pamene anafunsidwa nchiyani chimene chinapangitsa wokondedwa wake kukhala wotchuka, iye anapatsa “ana akazi a Yerusalemu” kalongosoledwe kowala ka iye.
◆5:12—Ndimotani mmene maso a mbusayo analiri monga ‘nkhunda zotsukidwa ndi mkaka’?
Kumayambiriro, maso a Msulami anayerekezedwa ndi aja a nkhunda chifukwa cha kukhala ofewa, odekha. (1:15; 4:1) Kaamba ka chimenecho, mbusayo anamutcha mtsikanayo “nkhunda” yake. (5:2) Pano mkazi wachichepere wodwala chikondiyo anayerekezera maso a mbusayo ndi nkhunda zobiliŵira motuŵira zikusamba mu madziwe a mkaka. (5:8, 12) Mwinamwake, mawu ofanana amenewa analozera ku mbali yakuda ya diso yozunguliridwa ndi mbali yoyera yowala ya maso ake.
Phunziro kwa Ife: Msulami anali monga “munda wotsekedwa.” (4:12) Kaŵirikaŵiri munda m’Israyeli wakale unali monga munda wa maluŵa wokongola, paradaiso wokongola wokhala ndi magwero abwino a madzi ndi mitundu yosiyanasiyana ya ndiwo zamasamba, maluŵa ndi mitengo. Kaŵirikaŵiri, unali kutsekedwa ndi mpanda kapena khoma ndipo ukanalowedwa kokha kupyolera pa chipata chotsekedwa. (Yesaya 5:5) Kwa mbusayo, kuyera kwa makhalidwe kwa Msulamiyo ndi chikondi chake chinali monga munda wokongola mwapadera, wokhala ndi zipatso zabwino, fungo losangalatsa, ndi kusangalatsa kowonjezereka. Chikondi chake sichinali chopezeka kwa munthu aliyense, popeza iye anali woyera, monga “munda wotsekedwa” kusalandira olowerera ndi kutseguka kokha kwa mwini wake walamulo. M’kuwongolera kwa makhalidwe abwino ndi kumvera Msulamiyo chotero anakhazikitsa chitsanzo chabwino kaamba ka akazi Achikristu osakwatiwa lerolino.
“Mphezi ya Ya”
Ŵerengani 6:4–8:14. Solomo analemekeza kukongola kwa mtsikanayo, koma anamukana iye ndi kulongosola kudzipereka kwake kwa mbusa. Wosakhoza kupeza chikondi chake, Solomo anamlola iye kupita kunyumba. Ndi “wokondedwa wake” pambali pake, iye anabwerera ku Sunemu monga mkazi wachikulire wokhala ndi kukhazikika kotsimikiziridwa. Chikondi pakati pake ndi mbusa chinali cholimba monga imfa, ndipo kung’anima kwake kunali ngati “mphezi ya [Ya, NW].”
◆6:4, NW—Nchiyani chimene chinali “Mzinda Wokoma”?
Kalongosoledwe kameneka kangatchulidwe “Tiriza,” kutanthauza “Wokoma, Wosangalatsa.” Tiriza unali mzinda wodziŵika chifukwa cha kukongola womwe unakhala likulu loyamba la ufumu wa kumpoto wa Israyeli.—1 Mafumu 14:17; 16:5, 6, 8, 15.
◆7:4—Ndimotani mmene khosi la mtsikanayo linaliri ngati “nsanja yaminyanga”?
Mwachiwonekere linali ndi kusalala kwa minyanga ndi kuwongoka kwa nsanja. Kumayambiriro, khosi lake linayerekezedwa ndi “nsanja ya Davide,” mwinamwake nsanja ya Nyumba ya Mfumuyo m’mphepete mwa khoma la kum’mawa la Yerusalemu. Pa iyo ‘panapachikidwa zikopa [zozungulira, NW] zikwi za amuna amphamvu,’ kusonyeza kuti khosi laufumu la Msulamilo linalemekezedwa ndi nthendele yokometseredwa ndi zokometsera zozungulira kapena miyala yokongola.—4:4; Nehemiya 3:25-27.
◆8:6, 7—Kodi ndimotani mmene chikondi chiliri “cholimba ngati imfa”?
Imfa mosalephera yatenga miyoyo ya anthu ochimwa, ndipo chikondi chowona chiri cholimba motero. Pa kuwumirira kwake pa kudzipereka kotheratu, chikondi choterocho chiri chosagonjera monga mmene aliri Sheol (manda) m’kulamulira matupi a anthu akufa. Popeza Yehova Mulungu anaika ukulu wa chikondi mkati mwa anthu, mtundu umenewu umachokera kwa iye ndipo moyenerera umatchedwa “mphezi ya [Ya, NW].” Osati ngakhale Mfumu yolemera Solomo ingagule chikondi choterocho.
Phunziro kwa Ife: Chokumana nacho cha Msulami ndi Mfumu Solomo chinali chiyeso chofufuza chomwe iye anachilaka mwachipambano. Iye sanali wosakhazikika mu chikondi ndi kuwona mtima, monga chitseko chotembenuka mopepuka pa maziko ake ndipo chofunikira chidutswa cha mkungudza kuchichinjiriza icho kuti chisatsegukire kwa winawake wosalandiridwa kapena wosayenerera. Ayi, mtsikanayo anapambana pa zinyengo za mfumuyo, akumaima monga khoma molimbana ndi zocheutsa zakuthupi zadziko iri. Ndii chidaliro pa Mulungu ndi kukumbukira chitsanzo chabwino cha Msulami, akazi Achikristu lerolino mofananamo angatsimikizire kaimidwe kawo monga anthu olimba m’maprinsipulo abwino ku chilemekezo cha Yehova.—8:8-10.
Ndithudi, “nyimbo yoposa” imeneyi, yokhala ndi chikondi monga mutu wake, imakweza chiyamikiro chathu kaamba ka chomangira chomwe chiripo pakati pa Yesu ndi awo osankhidwa kukhala “mkwatibwi” wake wa kumwamba. Koma amuna ndi akazi achichepere onse limodzinso ndi amuna okwatira ndi akazi okwatiwa odzipereka kwa Yehova angapindule kuchokera ku kufunafuna kutsanzira umphumphu wa Msulami ndi mbusa pamene ayang’anizana ndi zizunzo ndi mayeso. Ndipo mbali iyi yosangalatsa ya Mawu a Mulungu iyenera kutisonkhezera tonse a ife kukhalabe okhulupirika kwa Yehova, Magwero a chikondi chachipambano.