Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chinsinsi cha bukhu Lamakedzana la Vatican
    Nsanja ya Olonda—1989 | May 1
    • lawo la Vaticanus linali m’ngozi ya kuzimiririka. Podzafika kumapeto kwa zanalo, makope abwino ojambulidwa potsirizira pake anapangidwa kukhalako.

      Manusikripitiyo iri ndi masamba 759. Iyo iribe mbali yokulira ya Genesis, masalmo ena, ndi mbali zomalizira za Malemba Achikristu a Chigriki. Iyo iri yolembedwa pa chikopa chopuntha chopyapyala, chabwino koposa, cholingaliridwa kukhala chochokera ku zikopa za nswala, mu mtundu wopepuka, wowongoka. Chizindikiritso chake chalamulo chiri Bukhu Lamakedzana B (Codex B), ndipo iyo ingawonedwe lerolino mu Laibulale ya Vatican. Iyo siri yobisidwanso, ndipo phindu lake potsirizira pake lamvetsetsedwa ndi kuyamikiridwa m’dziko lonse.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—1989 | May 1
    • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

      ◼ Kodi Yehova amagwiritsira ntchito machenjera kapena chinyengo ndi anthu, kuphatikizapo atumiki ake, monga mmene Yeremiya 4:10 ndi 20:7 ikuwonekera kulingalira?

      Ayi, Mlengi sali wachinyengo, wodyerekeza, kapena wamachenjera m’machitidwe ake. Iye angathe ndipo amakhoza, ngakhale ndi tero, kukwaniritsa chifuno chake cholungama mosasamala kanthu za chimene anthu angayembekezere.

      Timawona mbali imodzi ya ichi kuchokera pa Yeremiya 4:10, pamene mneneriyo ananena kuti: “Ha, [Mfumu Ambuye, NW] Yehova! ndithudi mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo.”

      Yehova anagwiritsira ntchito Yeremiya kuneneratu tsoka lomadzalo kaamba ka mtundu wokhotakhota umene unadzinenera kutumikira Iye. (Yeremiya 1:10, 15-19; 4:5-8; 5:20-30) Komabe, panalinso ena odzinenera kukhala aneneri. (Yeremiya 4:9) Kodi nchiyani chimene anthu anamva kuchokera kwa odzinenera kukhala aneneri oterowo? Mulungu anachiika icho mwanjira iyi: “Aneneri anenera monyenga . . . ndipo anthu anga akonda zotere.”​—Yeremiya 5:31; 20:6.

      Pamene kuli kwakuti Yehova sanatume aneneri onyengawio, iye sanawachinjirizenso iwo kuleka kufalitsa mauthenga, onga ngati: “Mudzakhala ndi mtendere” ndi, “Palibe choipa chidzagwera inu.” (Yeremiya 23:16, 17, 25-28, 32) Anthuwo anafunikira kusankha​—kulandira maulosi amphamvu koma owona oprekedwa ndi Yeremiya kapena kudzilola iwo eni kusokeretsedwa ndi aneneri onyenga, odzipanga okha, onga ngati Hananiya ndi Semaya. (Yeremiya 28:1-4, 11; 29:30-32) Chifukwa chakuti Mulungu sanaimitse aneneri osokeretsa amenewa, chinganenedwe za iye kuti: “Mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere.”

      Mu lingaliro losiyanako, Yeremiya anakopedwa. “Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa inu, ndipo mwalakika; ine ndikhala choseketsa dzuŵa lonse, onse andiseka.”​—Yeremiya 20:7.

      Pasuri, wansembe wotchuka kwambiri, anasautsa Yeremiya mwapoyera ndipo kenaka kumuika iye m’matangadza. Kuchokera ku kawonedwe ka umunthu, Yeremiya angakhale anadzimva kuti anali atafika polekezera pake, kuti iye kokha analibenso mphamvu ya kupitirizabe kuyang’anizana ndi kupanda chikondwerero, kukanidwa, kusekedwa, ndi chiwawa chakuthupi. Koma sichinali tero. Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu Yake motsutsana (kapena mosiyana ndi) zikhoterero zaumunthu za Yeremiya. Mulungu anakopa Yeremiya m’njira yakuti Iye anagwiritsira ntchito munthu wopanda ungwiro ameneyu kukwaniritsa chimene mneneriyo sakanakhoza kuchichita ndi mphamvu ya iyemwini. Wokopedwa kapena wodabwitsidwa monga mmene Yeremiya angakhale anakhalira ndi ichi, chinali ku zotulukapo zabwino: Awo omuzunza iye anachititsidwa manyazi, ndipo uthenga wa Mulungu unaperekedwa.​—Yeremiya 20:11.

      Chotero, atamvetsetsedwa m’mawu ozungulira,Yeremiya 4:10 ndi 20:7 amagwirizana ndi kumaliza kwa Elihu kwakuti: “Mulungu sangachite choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipsye mlandu.”​—Yobu 34:12.

  • Chiwiya Chofufuzira Chaphindu
    Nsanja ya Olonda—1989 | May 1
    • Chiwiya Chofufuzira Chaphindu

      “Ndikuyamikani kaamba ka zofalitsidwa zanu za mavolyumu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!,” akulemba tero wa msinkhu wa zaka 13 wa ku New Zealand. Mtsikanayo akulongosola kuti:

      “Mphunzitsi wanga anafunsa kalasi kuchita kufufuza pa tsoka lirilonse ndipo kenaka kuika ilo mu mtundu wa kabukhu. Ndinasankha kuphunzira ponena za Titanic. Ndinafunafuna kaamba ka mabukhu pa sukulu koma sindinapeze lirilonse loyenera. Chotero ndinayang‘ana mu volyumu ya Galamukani! (m’Chingelezi) ya ‘81. Ndinawerenga nkhani yonse yonena za Titanic, ndipo kenaka m’mawu anga, ndinaika iyo mu mtundu wa kabukhu. Pamene mphunzitsi wanga anachonga ntchito zonse, iye anasonyeza yanga ku kalasi. Ndinapambana onse.” Wachichepereyo akumaliza kuti: “Nthaŵi iriyonse pamene ndikhala ndi ntchito, ndidzagwiritsira zofalitsidwa zanu.”

      Mwakupeza mabound volyumu a magazini iyi, nanunso mudzakhala ndi chiwiya chofufuzira chaphindu. Bound volyumu ya Galamukani! (Chingelezi) ya 1988 tsopano iripo, limodzinso ndi bound volyumu ya Nsanja ya Olonda (Chignelezi), magazini inzake ya Galamukani! Landirani mavolyumu anu mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.

      Chongani kabokosi kalikonse, kapena tonse tiŵiri, ndi kutumiza chopereka choyenera. (Kunja kwa Zambia, lemberani ku nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso.)

      [ ] Chonde tumizani bound volyumu ya Galamukani! (Chingelezi) ya 1988. Ndatsekeramo K60 (Zambia).

      [ ] Chonde tumizani bound volyumu ya Nsanja ya Olonda (Chingelezi) ya 1988. Ndatsekeramo K60 (Zambia).

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena