Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 84
  • Thayo la Kukhala Wophunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thayo la Kukhala Wophunzira
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Thayo la Kukhala Wophunzira
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kukhala Wophunzira wa Yesu Ndi Udindo Waukulu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Amene Anakhala Ophunzira a Yesu
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Ulaliki Wotchuka Woposa Wonse Umene Unaperekedwa
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 84

Mutu 84

Thayo la Kukhala Wophunzira

ATACHOKA m’nyumba ya Mfarisi wotchuka, amene mwachiwonekere ali chiŵalo cha Sanhedrin, Yesu akupitirizabe kumka ku Yerusalemu. Makamu aakulu akumtsatira. Koma kodi zolinga zawo nzotani? Kodi nchiyani kwenikweni chimaphatikizidwa m’kukhala wotsatira wake wowona?

Pamene iwo akuyenda limodzi naye Yesu akutembenukira kukhamulo ndipo mwinamwake akuwadabwitsa pamene akuti: “Munthu akadza kwa ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.”

Kodi Yesu akutanthauzanji? Yesu panopa sakunena kuti otsatira ake ayenera kuda kwenikweni achibale awo. Mmalomwake, iwo ayenera kuwada m’lingaliro la kuwakonda mocheperapo kuposa mmene amamkondera iye. Kholo la Yesu Yakobo likunenedwa kukhala “litada” Leya ndi kukonda Rakele, zimene zitanthauza kuti Leya anakondedwa mocheperapo kuposa mchemwali wake Rakele.

Lingaliraninso, kuti Yesu anati wophunzira ayenera kuda ‘ngakhale moyo wake womwe wa iye mwini,’ kapena umoyo. Kachiŵirinso zimene Yesu akutanthauza nzakuti wophunzira wowona ayenera kukonda Iye mowonjezereka koposa mmene amakondera moyo wa iye mwini. Motero Yesu akugogomezera kuti kukhala wophunzira wake liri thayo lalikulu. Siliri kanthu kena kochitidwa popanda kulingalira mosamalitsa.

Mavuto ndi chizunzo zimaphatikizidwa m’kukhala wophunzira wa Yesu, monga momwe akupitirizira kusonyeza kuti: ‘Yense amene sanyamula mtengo wake wonzunzirapo nanditsata ine sangakhale wophunzira wanga.’ Motero, wophunzira wowona ayenera kukhala wofunitsitsa kukumana ndi vuto limodzimodzilo la chitonzo chimene Yesu anapirira, ngakhale kuphatikizapo ngati kuli koyenelera, kufera m’manja mwa adani a Mulungu, zimene Yesu ati achite mwamsanga.

Chifukwa cha chimenecho, kukhala wophunzira wa Kristu, iri nkhani imene makamu omtsatirawo afunikira kupenda mosamalitsa. Yesu akugogomezera chenicheni chimenechi mwakusimba fanizo. “Pakuti,” iye akutero, “ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, awone ngati ali nazo zakuimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, wosakhoza kuimaliza, anthu onse akuyang’ana adzayamba kumseka iye, ndi kunena kuti, munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.”

Chotero Yesu akufotokozera mwafanizo khamu limene likumtsatira kuti asanakhale ophunzira ake, ayenera kukhala otsimikizira kusankha kuti angathe kukwaniritsa zophatikizidwamo, monga momwedi munthu amene afuna kumanga nsanja amatsimikizirira asanayambe kuti ali nazo ndalama zakuimaliza. Akumapereka fanizo lina, Yesu akupitiriza kuti:

“Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi aŵiri? Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere.”

Pamenepo Yesu akugogomezera mfundo ya mafanizo ake, akumati: “Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga.” Zimenezo ndizo zimene khamu lomtsatiralo, ndipo inde, wina aliyense amene aphunzira za Kristu, ayenera kukhala wofunitsitsa kuchita. Iwo ayenera kukhala okonzekera kudzimana zonse zimene iwo ali nazo—chuma chawo chonse, kuphatikizapo moyo weniweniwo—ngati iwo ati akhale ophunzira ake. Kodi inu muli wofunitsitsa kuchita zimenezi?

“Kotero mchere uli wokoma,” Yesu akupitiriza motero. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, iye ananena kuti ophunzira ake ndiwo “mchere wa dziko lapansi,” kutanthauza kuti iwo ali ndi chiyambukiro chotetezera pa anthu, monga momwedi mchere uliri wotetezera. “Koma ngati mcherewo utasukuluka adzaukoleretsa ndi chiyani? Suyenera kuthiridwa pamunda kapena padzala,” Yesu akumaliza. “Autaya kunja. Amene alinawo makutu akumva, amve.”

Chotero Yesu akusonyeza kuti ngakhale awo amene akhala ali ophunzira ake kwanthaŵi yakutiyakuti sayenera kufooka m’chitsimikizo chawo cha kupitirizabe. Ngati iwo atero, adzakhala opanda pake, munthu wosekedwa wa dziko lino ndi wosayenerera pamaso pa Mulungu, kwenikweni, wochititsa mtonzo kwa Mulungu. Chifukwa chake, mofanana ndi mchere wosukuluka, woipitsidwa, iwo adzatayidwa kunja, inde kuwonongedwa. Luka 14:25-35; Genesis 29:30-33; Mateyu 5:13.

▪ Kodi ‘kuda’ anansi a munthu ndi iwe mwini kumatanthauzanji?

▪ Kodi ndimafanizo aŵiri otani amene Yesu akupereka, ndipo kodi amatanthauzanji?

▪ Kodi nchiyani chimene chiri mfundo ya ndemanga zomalizira za Yesu ponena za mchere?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena