Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 13 tsamba 103-109
  • Khamu Lalikulu Pamaso pa Mpando Wachifumu wa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khamu Lalikulu Pamaso pa Mpando Wachifumu wa Yehova
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziwikitsa “Khamu Lalikulu”
  • Oyesedwa Ponena za Kuyenerera Kupulumuka
  • Kukhala ndi Moyo m’Paradaiso Wauzimu
  • Khamu Lalikulu Loimirira ku Mpando Wachifumu wa Yehova
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Khamu Lalikulu Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • “Ndinaona Khamu Lalikulu la Anthu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Khamu Lalikulu Lopereka Utumiki Wopatulika
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 13 tsamba 103-109

Mutu 13

Khamu Lalikulu Pamaso pa Mpando Wachifumu wa Yehova

1. (a) Atumiki a Mulungu apatsogolo kapena pambuyo pa Chikristu kapena a 144 000 asanalandire mphoto yawo, kodi ayenera kukomana ndi chiyani? (b) Kodi nchiyani chidzakhala chotheka kwa khamu lalikulu limene likukhala ndi moyo pamene “chisautso chachikulu” chikantha?

NGAKHALE kuli kwakuti atumiki okhulupirika a Mulungu kuyambira kwa Abele mpaka kwa Yohane Mbatizi anaika kuchitidwa kwa chifuniro cha Mulungu poyamba m’miyoyo yawo, iwo onse anafunikira kufa ndi kuyembekezera chiukiriro. A 144 000 amene adzakhala ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba nawonso ayenera kufa asanalandire mphoto yawo. Mosiyana, mtumwi Yohane anasonyezedwa masomphenya akuti kukakhala khamu lalikulu limene kwenikweni likapulumuka “chisautso chachikulu” ndipo, popanda kufa, kukhala ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha.—Chiv. 7:9-17.

Kudziwikitsa “Khamu Lalikulu”

2. Kodi nchiyani chinatsogolera kukumveketsedwa bwino kwa a “khamu lalikulu” la Chivumbulutso 7:9?

2 Kwa zaka mazana ambiri kudziwika kwa “khamu lalikulu” sikunazindikiridwe. Koma chidziwitso chopita patsogolo cha maulosi otero chinalambula njira. Mu 1923 kunazindikiridwa kuti “nkhosa” za fanizo la Yesu pa Mateyu 25:31-46 ndi “nkhosa zina” zotchulidwa pa Yohane 10:16 zinali anthu amoyo pa tsopano lino amene akakhala ndi mwayi wa kukhala ndi moyo kosatha pano padziko lapansi. Mu 1931 awo olongosoledwa mu Ezekieli 9:1-11 monga olembedwa chizindikiro pamphumi zawo ndi mwamuna wokhala ndi cholembera cha inki cha mlembi anadziwikitsidwa kukhala “nkhosa” za pa Mateyu mutu 25. Ndiyeno, mu 1935, “chikhamu chachikulu,” kapena “khamu lalikulu,” la Chivumbulutso 7:9-17 linawonedwa kukhala lofanana ndi “nkhosa” za fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi. Ngakhale kuli kwakuti kalelo mu 1923 kunadziwika kuti anthu ena onga nkhosa otere anali atayamba kale kudziwonetsera iwo eni, sikunachitike kufikira 1935 kuti ziwerengero zawo zinayamba kukula mofulumira. Lerolino pali mamiliyoni enieni amene akufunafuna kudziwikitsidwa monga mbali ya “khamu lalikulu” loyanjidwa ndi Mulungu limenelo la “nkhosa zina.”

3. Kodi nchifukwa ninji “kuimirira pamaso pampando wachifumu” kwawo sikumatanthauza kuti ali akagulu kakumwamba?

3 A “nkhosa zina” ali olekanitsidwa ndi ziwalo za 144 000 za Israyeli wauzimu, wotchulidwa koyambirira kwa mutu umodzimodziwo wa Chivumbulutso. M’masomphenya ake Yohane sanawone “khamu lalikulu” limeneli monga lokhala m’mwamba. “Kuimirira pamaso pa mpando wachifumu” kwawo (Chigriki: e·noʹpi·on tou throʹnou, “mowonekera kumpando wachifumu”) wa Mulungu sikumawafunikiritsa kuti akhale kumwamba. Malo awo ali kokha “owoneka” kwa Mulungu, amene amatiuza kuti kuchokera kumwamba amawona ana a anthu. (Chiv. 7:9; Sal. 11:4; yerekezerani ndi Salmo 100:1, 2, ndiponso Luka 1:74, 75 ndi Machitidwe 10:33, Kingdom Interlinear.) Mofananamo, kuli kofunikira kwa “mitundu yonse” kukhala m’mwamba kuti iwo akhale pamaso pa mpando wa Kristu (“pamaso pake,” m’thupi,), monga momwe kwalongosoledwera pa Mateyu 25:31, 32. Chenicheni chakuti “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga,” siriri kagulu ka kumwamba chasonyezedwa moyerekezera pa Chivumbulutso 7:4-8 ndi 14:1-4, kumene chiwerengero chenicheni cha otengedwa kuchokera kudziko lapansi kukakhala kumwamba chavumbulutsidwa.

4. (a) Kodi nchiyani chiri “chisautso chachikulu” chimene akupulumuka? (b) Monga momwe kwalongosoledwera pa Chivumbulutso 7:11, 12, kodi ndani amene akuwona “khamu lalikulu” nagawana nawo m’kulambira?

4 M’kudziwikitsa “khamu lalikulu,” Yohane analemba kuti: “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu.” Chimene akupulumuka, chidzakhaladi, chitsautso chachikulu koposa chimene chinachitikapo ndi kale lonse padziko lapansi. (Chiv. 7:13, 14; Mat. 24:21) Opulumuka tsiku lochititsa mantha limenelo la Yehova sadzakhala ndi chikaikiro ponena za amene ali ndi thayo lakupulumutsidwa kwao. Pamene mothokoza anena za chipulumutso chawo kukhala chochokera kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa, pamenepo, monga momwe Yohane anawonera m’masomphenya, zolengedwa zokhulupirika zonse m’mwamba zidzagwirizana ndi mawu awo m’kulambiridwa kwa Mulungu wowona yekha, zikumati: “Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi zanthawi. Amen.”—Chiv. 7:11, 12.

Oyesedwa Ponena za Kuyenerera Kupulumuka

5. (a) Kodi ndimotani mmene tingadziwire chimene chikufunika kuti tikhale mbali ya “khamu lalikulu” limene lidzatetezeredwa? (b) Mwakuyankha mafunso kumapeto a ndime ino, longosolani chimene chiri chofunika kupulumuka “chisautso chachikulu.”

5 Kupulumutsidwa kwa “khamu lalikulu” kumachitika mogwirizana ndi miyezo yolungama ya Yehova iyemwiniyo. Zisonyezero zowoneka zamikhalidwe yodziwikitsa ya awo amene adzawomboledwa nzophatikizidwa m’malemba olosera a Baibulo kwa iwo. Chotero kuli kotheka kwa okonda chilungamo kuchitapo kanthu tsopano ali ndi chiyembekezo cha kupulumuka. Tatchula kale malemba amene akutsatirawa. Koma tsopano apendeni mosamalitsa, mwachithandizo chamalemba owonjezereka olembedwa, ndipo lingalirani chimene muyenera kuchita kuti muyenerere malongosoledwe olosera amenewa.

“Nkhosa zina” zotchulidwa pa Yohane 10:16

Kodi kumatanthauzanji kwa munthu kumvetseradi mawu a Yesu? (Yoh. 10:27; Mat. 9:9; Aef. 4:17-24)

Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti tikuvomereza Kristu monga ‘mbusa wathu mmodzi’? (Mat. 23:10, 11)

“Nkhosa” m’fanizo la Yesu lankhosa ndi mbuzi (Mat. 25:31-46)

Kodi ndani amene ali “abale” a Kristu kwa amene amenewa akuchitira zabwino? (Aheb. 2:10, 11; 3:1)

Kodi ndi pansi pamikhalidwe yovuta yotani pa imene iwo akufunikira kuzidziwikitsa ndi abale a Kristu padziko lapansi? Ndipo kodi iwo amakupereka chithandizo chokhulupirika m’ntchito yotani? (Chiv. 12:12, 17; Mat. 24:14; 28:19, 20)

Anthu olembedwa chizindikiro cha kupulumuka ndi munthu wokhala ndi cholembera cha inki cha mlembi (Ezek. 9:1-11)

Kodi ndimotani mmene amasonyezera kuti saali ogwirizana ndi zinthu zonyansa zochitidwa mu Yerusalemu wophiphiritsiridwa, kapena Dziko Lachikristu? (Chiv. 18:4, 5)

Kodi nchiyani chikuphatikizidwa mu “chizindikiro” chimene chimawalekanitsa iwo ndi Akristu m’dzina lokha ndi kuwaika m’mzera wa kupulumutsidwa? (1 Pet. 3:21; Mat. 7:21-27; Yoh. 13:35)

6. Kodi ndimotani mmene malongosoledwe a Yohane a “khamu lalikulu” amatithandizira kuzindikira chifukwa chake iwo anapulumutsidwa?

6 Kulongosola “khamu lalikulu” kopezeka pa Chivumbulutso 7:9-15 kumawonjezera mfundo zina zofunika. Potiuza za “khamu lalikulu” limenelo lowonekera pambuyo pa “chisautso chachikulu,” Malemba amasonyanso ku zenizeni zimene zinatsogolera kukupulumutsidwa kwawo.

7. Kodi nchiyani chimene anachita “chisautso chachikulu,” chisanachitike ndipo kodi ichi chikusonyezedwa motani?

7 Ngakhale kuli kwakuti akuchokera m’mitundu yonse, mafuko, anthu ndi manenedwe, akusonyezedwa “akuimirira pamaso pa mpando wachifumu,” mogwirizana kuvomereza Yehova, Uyo wokhala pampando wachifumu, monga Wolamulira Wachilengedwe chonse. Iwo atsimikizira mwanjira yawo ya moyo kuti ali ochirikiza okhulupirika a ulamuliro wake. Chenicheni chakuti “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa” chimasonyeza kuti akuvomereza kufunikira kwawo mtengo wansembe ya Yesu yotetezera machimo monga Mwanawankhosa wa Mulungu. (Yoh. 1:29; 1 Yoh. 2:2) Mwachikhulupiriro iwo adzipatulira kwa Mulungu pamaziko ansembe imeneyo, akusonyeza mwa kumizidwa m’madzi ndipo tsopano akusangalala ndi kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu, monga momwe kanachitiridwa chithunzi ndi miinjiro yoyera. Sanaleke kusonyeza poyera chikhulupiriro chawo mwa Mwana wa Mulungu. (Mat. 10:32, 33) Mogwirizana ndi zonsezi, iwo asonyezedwa monga okhala m’kachisi wa Mulungu, kapena nyumba yolambirira ya m’chilengedwe chonse, monga olambira opereka kwa Mulungu “utumiki wopatulika usana ndi usiku.” Chotero apanga mbiri ya kukhala ochirikiza okhulupirika a kulambira kowona ndi olengeza Ufumu wake.—Yes. 2:2, 3.

8. Kuti chidziwitso ichi chitipindulitse, kodi tiyenera kuchitanji?

8 Kodi tsatanetsatane wa zithunzi zolosera izi akukuyenerani? Kodi pali njira m’zimene mufunikira kugwirizanitsa mokwanira moyo wanu ndi zimene zalongosoledwa pano? Ngati ziri choncho, tsopano ndiyo nthawi ya kutero!

Kukhala ndi Moyo m’Paradaiso Wauzimu

9. Kodi ndimotani mmene Yohane amalongosolera madalitso auzimu amene “khamu lalikulu” liri nawo ngakhale tsopano?

9 Kodi inu ndinu mmodzi woyembekezera kupulumuka monga mbali ya “khamu lalikulu”? Ngati mwagwirizana ndi njira zolungama za Yehova, pamenepo mosakaikira mwayamba kale kusangalala ndi mikhalidwe yolonjezedwa imene moyenerera yatchedwa paradaiso wauzimu. Mtumwi Yohane anauzidwa kuti: “Sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena chitungu chirichonse; chifukwa Mwanawankhosa wa kukhala pakati pampando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pawo.” (Chiv. 7:16, 17) Kodi ndimotani mmene izi zatsimikizirira kukhala zowona kwa inu?

10. (a) M’lingaliro lauzimu kodi nzowona kuti “khamu lalikulu” “silikumvanso njala, kapena ludzu”? (b) Kodi mkhalidwewo wakuchitikirani?

10 Musanadze pansi pa chisamaliro chachikondi cha Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, kodi munali kumva njala ndi kumva ludzu kaamba ka chilungamo? (Yerekezerani Mateyu 5:6.) Ngati ziri choncho, zimene munalakalaka zinali kanthu kena kamene kakanaperekedwa kokha ndi Yehova kupyolera mwa Mwana wake. Pamene munaphunzira za njira zolungama za Yehova—chifuno chake cha kuwononga oipa, komabe kukoma mtima kwake kwa chifundo m’kuchititsa chipulumutso kukhala chothekera kaamba ka mbadwa za Adamu—pamenepa, mosakaikira, kwa nthawi yoyamba m’moyo wanu munamvadi chikhutiro. Chakudya chauzimu ndi chakumwa chochokera m’Mawu a Mulungu, monga momwe chikuperekedwera ndi gulu lake, chapitirizabe kukubweretserani chikhutiro. (Yes. 65:13, 14) Ndipo ngati inu mwadzipatulira kwa Mulungu kupyolera mwa Kristu tsopano muli ndi chifuno chenicheni m’moyo. (Yerekezerani Yohane 4:32-34.) Pamaso panu pali chiyembekezo chachisangalalo cha moyo wamuyaya m’Paradaiso pa dziko lapansi, chifukwa chakuti Mwanawankhosa “adzatsogolera [khamu lalikulu] ku akasupe a madzi a moyo.”

11. (a) Kodi ndim’njira yotani mmene ziriri zowona kuti ‘dzuwa kapena kutentha kowaula kulikonse sikumagweranso pa iwo’? (b) Kodi zimenezo nzofunika motani kwa inu?

11 Monga “nkhosa” zodalirika a “khamu lalikulu” akutetezeredwanso ndi kutsogozedwa bwino lomwe ndi Mbusa Wamkulu. Ndicho chifukwa chake, mophiphiritsira, ‘silidzawatentha dzuwa kapena kukanthidwa ndi kutentha kowaula kulikonse.’ Izi sizitanthauza kuti, monga mmodzi wa “khamu lalikulu,” simudzavutika ndi chizunzo kuchokera kudziko. M’malo mwake, chikutanthauza kuti muli otetezereka kuchokera kukutentha kowaula kwa mkwiyo wa Mulungu iyemwiniyo. Ndipo pamene avumbitsa chiwonongeko pa oipa, sichidzakuvulazani. Unansi woyanjika uwu ungapitirizebe kosatha.—Ezek. 38:22, 23; yerekezerani ndi Salmo 11:6; 85:3, 4.

12. Kodi ndimotani mmene misozi yapukutidwira m’maso mwanu ngakhale tsopano?

12 Ha nzifukwa zabwino kwambiri zotani nanga za kusangalalira zimene ziri zanu ngati zowonadi muli mmodzi wa “khamu lalikulu”! Muli ndi chiyembekezo chodabwitsa cha kuwona kuipa kukuchotsedwa kotheratu ndiyeno maganizo anu ndi thupi nkuonjoledwa ku ziyambukiro zonse za uchimo. Koma ngakhale tsopano chisoni chimene chimakantha anthu chifukwa chakuti ali osazindikira Mulungu sichimakukanthani inu. Mukuyanba kudziwa chisangalalo chimene chimadza kokha kwa anthu amene Mulungu wawo ali Yehova. (Sal. 144:15b) Mwanjira iyi mwayamba kale kusangalala ndi kukwaniritsidwa kwa lonjezo lakuti: “Mulungu adzapukuta misodzi yonse kuichotsa pamaso pawo.”

13. Kodi nchiyani chidzawonjezera zisangalalo za paradaiso wauzimu pamene ulamuliro wazaka chikwi wa Kristu ukupita patsogolo?

13 Monga momwe a “khamu lalikulu” adzapulumukira mapeto adongosolo lino lazinthu, choteronso paradaiso wauzimu. Ngati muli mmodzi wa iwo, pamenepo mudzapitirizabe kusangalala ndi phwando lauzimu lazinthu zonona pamene ulamuliro wazaka chikwi wa Kristu ukupita patsogolo. Chidziwitso chanu cha Mulungu iye mwiniyo chidzazamirapo pamene mukuwona chifuno chake chosalephera chikukwaniritsidwa mwaulemerero. Chisangalalo chanu chidzakulitsidwa pamene mukukhala ndi mbali m’kuchingamira khamu lomakulakula lochokera kwa akufa limene lidzagwirizana nanu m’kulambira kowona. Ndipo madalitso akuthupi amene panthawiyo adzaperekedwa adzakhala amtengo wapatalidi kwa atumiki onse okhulupirika a Mulungu pamene akuwonedwa kukhala chisonyezero cha chikondi cha Yehova iyemwiniyo.—Yes. 25:6-9; Yak. 1:17.

Makambitsirano Openda

● Kodi nchochitika chapadera chotani chimene Baibulo limagwirizanitsa nacho ndi “khamu lalikulu,” ndipo motani?

● Ngati ife tifunadi kuphatikizidwa mu “khamu lalikulu,” loyanjidwa ndi Mulungu limenelo kodi tiyenera kuchitanji tsopano?

● Kodi madalitso a paradaiso wauzimu ali ofunika motani kwa inu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena