Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 14 tsamba 110-116
  • ‘Ndichita Pangano ndi Inu la Ufumu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Ndichita Pangano ndi Inu la Ufumu’
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusonkhanitsa Olowa Nyumba a Ufumu
  • Ana Auzimu—Kodi Amadziwa Motani?
  • Kudya Moyenerera
  • “Tidzamuka Nanu Anthu Inu”
  • Kodi Mgonero wa Ambuye Uli ndi Phindu Lanji kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Ndani Kwenikweni Amene Ali ndi Chiitano Chakumwamba?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mwalandira “Mzimu wa Choonadi”?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 14 tsamba 110-116

Mutu 14

‘Ndichita Pangano ndi Inu la Ufumu’

1. Pausiku wa imfa ya Yesu isanachitike kodi nchiyembekezo chotani chimene anaika pamaso pa atumwi ake?

PANALI pausikuwo Yesu asanaphedwe pamene iye anauza atumwi ake okhulupirika kuti: ‘M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ndipita kukukonzerani inu malo, kuti kumene kuli ineko, mukakhale inunso.’ Iye anatinso kwa iwo: “Ndikuchita pangano ndi inu, monga momwe Atate wanga wachita pangano ndi ine, laufumu.” (Yoh. 14:2, 3; Luka 22:29, NW) Ha nchiyembekezo chodabwitsa chotani nanga chimene iye anaika pamaso pawo!

2. Kodi ndiangati amene adzakhala ndi mbali limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba?

2 Komabe, Yesu sanatanthauze kuti anali atumwi okhawo amene akalamulira limodzi naye mu ufumu wake wakumwamba. Pambuyo pake kunadziwitsidwa kuti okwanira 144 000 owomboledwa kuchokera kudziko lapansi apatsidwa mwayi waukulu umenewo. (Chiv. 5:9, 10; 14:1, 4) Kodi pali ena lerolino okalimira kupeza mphotoyo?

Kusonkhanitsa Olowa Nyumba a Ufumu

3. Mu uminisitala wake wapoyera, kodi Yesu anasonya za mwayi wotani?

3 Pambuyo pa kuikidwa kwa Yohane Mbatizi m’ndende ndi Herode Antipa, Yesu anayamba mkupiti waukulu wa kulalikira poyera mu umene anasumika chisamaliro pa “ufumu wakumwamba.” (Mat 4:12, 17) Anachititsa anthu kuzindikira kuti pakakhala mpata kwa iwo wa kulowa Ufumu umenewu, ndipo ophunzira ake anakalimira mwaphamphu mphotho imeneyo.—Mat. 5:3, 10, 20; 7:21; 11:12.

4. (a) Kodi ndiliti pamene ophunzira a Yesu oyamba anadzozedwa ndi mzimu woyera? (b) Kodi nchiyani chimasonyeza kuti chisamaliro chinali kulunjikitsidwa pa kusonkhanitsidwa kwa olowa nyumba a Ufumu kuyambira panthawiyo?

4 Pa Pentekoste wa 33 C.E. oyamba a amenewa anadzozedwa ndi mzimu woyera. (Mac. 2:1-4; 2 Akor. 1:21, 22) Makonzedwe a Mulungu a chipulumutso otsogolera ku moyo wakumwamba wosakhoza kufa anadziwikitsidwa. Petro anagwiritsira ntchito “mfungulo za ufumu wakumwamba” kutsegulira chidziwitso chimenechi—choyamba kwa Ayuda kenako kwa Asamariya, ndiyeno kwa anthu a mitundu Yachikunja. (Mat. 16:19) Chisamaliro chapadera chinali kuperekedwa kukupangidwa kwa boma limene likalamulira anthu kwa zaka 1 000, ndipo pafupifupi makalata onse ouziridwa mu Malemba Achikristu Achigriki kwakukulukulu alunjikitsidwa ku kagulu ka olowa nyumba a Ufumu kameneka—“oyera mtima,” “olandirana nawo maitanidwe akumwamba.”a

5. Kodi kuitanidwira kwawo kumoyo wakumwamba kunatanthauza kuti anali atumiki abwino kwambiri a Mulungu koposa amene anakhala ndi moyo iwo asanabadwe?

5 Kuitanidwira kwawo ku moyo wakumwamba sikunali chifukwa chakuti anali abwinopo kwambiri koposa atumiki onse a Mulungu amene adafa Pentekoste ya 33 C.E. isanachitike. (Mat. 11:11) M’malo mwake, Yehova tsopano anali atayamba kusankha awo amene akakhala olamulira limodzi ndi Yesu Kristu. Kwa zaka mazana 19 pambuyo pake panali chiitano chimodzi chokha, cha kumwamba. Kunali kukoma mtima kwa chifundo kumene Mulungu anasonyeza pachiwerengero chochepa m’kupititsa patsogolo zifuno za iyenwini zanzeru ndi zachikondi.—Aef. 2:8-10.

6. (a) Kodi nchifukwa ninji nthawi iyenera kudza pamene chiitano cha kumwamba chiyenera kutha? (b) Kodi ndani akatsogolera zochitika kotero kuti ulosi wonena za “khamu lalikulu” nawonso ukakwaniritsidwa, ndipo kodi nchiyani chimene chachitika?

6 M’nthawi yokwanira chiwerengero cholongosoledweratu koma chochepa cha 144 000 chikakwaniritsidwa. Kuikidwa chizindikiro kotsirizira kwa Aisrayeli auzimu amenewa monga momwe anavomerezedwera kukakhala kutayandikira. (Chiv. 7:1-8) Pamenepo Yehova, kupyolera mwa mzimu wake ndi kuzindikiridwa kwa Mawu ake kumene anatheketsa mwa gulu lake lowoneka, akayendetsa zinthu kotero kuti zikwaniritse mbali ina ya chifuno chake, monga yalongosoledwa m’Chivumbululutso 7:9-17. “Khamu lalikulu” lochokera m’mitundu yonse likasonkhanitsidwa ndi chiyembekezo chochititsa nthumanzi cha kupulumuka chisautso chachikulu ndi kukhala ndi moyo kosatha mu ungwiro pakati pa Paradaiso wadziko lapansi. Pamene tilingalira zimene kwenikweni zachitika, kukuwonekera kukhala kwachiwonekere kuti chiitano cha kumwamba kwakukulukulu chinatha podzafika chaka cha 1935 C.E., pamene chiyembekezo cha padziko lapansi cha “khamu lalikulu” chinazindikiridwa momvekera bwino. Kuyambira pa nthawiyo pakhala kugwirizanitsidwa ndi kagulu ka zikwi zowerengeka kwambiri za otsalira a kagulu ka kumwamba ndi mamiliyoni ambiri a olambira Yehova amene akuyembekezera mwaphamphu kukhala ndi moyo kosatha pompano padziko lapansi.

7. Kodi nkotheka kuti ena ngakhale lerolino angalandire chiitano cha kumwamba, ndipo kodi nchifukwa ninji mukuyankha motero?

7 Kodi izi zitanthauza kuti palibe aliyense tsopano amene akuitanidwa ndi Mulungu kaamba ka moyo wakumwamba? Kufikira kuikidwa chizindikiro kotsirizira kutachitidwa, kuli kotheka kuti owerengeka amene ali ndi chiyembekezo chimenecho angatsimikizire kukhala osakhulupirika, ndipo ena adzafunikira kusankhidwa kutenga malo awo. Koma kukuwonekera kukhala koyenera kuti ichi chikakhala chochitika cha kamodzikamodzi.

Ana Auzimu—Kodi Amadziwa Motani?

8. Kodi ndimalongosoledwe otani amene Paulo akupereka osonyeza mmene awo odzodzedwa ndi mzimu woyera amadziwira chenicheni chimenecho?

8 Mzimu wa Mulungu umapereka chitsimikiziro champhamvu cha kulandiridwa monga ana auzimu kwa Akristu obatizidwa amene alandira chiitano chakumwamba. Mtumwi Paulo anasonyeza ichi pamene analembera kwa “oyera mtima” m’Roma, akumalongosola chimene panthawiyo chinali mkhalidwe wa Akristu onse owona. Iye anati: “Onse amene amatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Pakuti inu simunalandire mzimu waukapolo wochititsa mantha kachiwiri, koma inu munalandira mzimu wa kulandiridwa monga ana, mwa mzimu umene ife timafuula nawo: ‘Abba, Atate’! Mzimu uwo wokha umachitira umboni ndi mzimu wathu kuti ife tiri ana a Mulungu. Pamenepa, ngati ife, tiri ana, ife tirinso olowa nyumba ogwirizana limodzi ndi Kristu, malinga ngati tivutika limodzi kuti tikalemekezedwenso limodzi.”—Aroma 1:7; 8:14-17, NW.

9. Kodi ndimotani mmene ‘mzimu uwo wokha umachitira umboni’ ndi mzimu wa awo amenedi ali ana a Mulungu?

9 Kugwiritsira ntchito kuwiri kwa mawu akuti “mzimu” panopa kukusonyezedwa kwa ife: “Mzimu uwo wokha” ndi “mzimu wathu.” Woyambawo ndiwo mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Umasonkhezera mwa ana ake auzimu chikhutiro cha kukhala atalandiridwa monga ana omasuka a Mulungu. Mzimu umenewo umachitiranso umboni kupyolera mwa Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo, amene ali ofanana ndi kalata yaumwini kwa ana ake auzimu. (1 Pet. 1:10-12) Pamene awo amene abadwa mwamzimu woyera awerenga zimene Malemba amanena kwa awo amene ali ana auzimu a Mulungu, amalabadira moyenerera kuti: ‘Izi zikugwira ntchito kwa ine.’ Chotero mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu mwini mwanjira zosiyanasiyana imachitira umboni ndi mzimu wawo, mphamvu yosonkhezera ya maganizo ndi mtima wawo kuti iwo ali ana a Mulungu. Chotero mogwirizana ndi zimene mzimu wa Mulungu umasonyeza, maganizo ndi mitima yawo zimasumikidwa pachiyembekezo cha kukhala olowa nyumba limodzi ndi Kristu, ndipo amavomereza mathayo akukhala ana auzimu a Mulungu.—Afil. 3:13, 14.

10. (a) Kodi ndizinthu ziti zimene mwa izo zokha sizimadziwikitsa munthu kukhala Mkristu wodzozedwa? (b) Kodi ndilingaliro lotani limene “nkhosa zina” zimakhala nalo ponena za malo awo m’chifuno cha Mulungu?

10 Kodi ziri choncho ponena za inu? Ngati ziri choncho, muli ndi mwayi wodabwitsa. Komabe, kukakhala kulakwa kwa aliyense kunena kuti chifukwa chakuti munthuyo ali ndi chidziwitso chozamirapo cha zinthu zauzimu kapena ali wachangu mu utumiki wa kufalitsa kapena ali ndi chikondi chachikulu cha paabale ake chifukwa cha chimenecho ayenera kukhala Mkristu wozodzedwa ndi mzimu. Zinthu zenizeni zimenezo zikupezeka pakati pa ambiri a “nkhosa zina.” Nawonso, mitima yawo, imasonkhezeredwa ndi zimene amawerenga m’Malemba ponena za olowa nyumba anzake a Kristu, koma iwo samayesa kudzinenera iwo eni kanthu kena kamene Mulungu sanawasungire. (Yerekezerani Numeri 16:1-40.) Amazindikira chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi ndipo moyamikira amagwira ntchito kulinga ku kukhala ndi phande m’chimenecho.

Kudya Moyenerera

11. Kodi ndani amafika pa kukumbukira imfa ya Yesu kwa chaka ndi chaka, ndipo chifukwa ninji?

11 Chaka chirichonse pa Nisan 14, pambuyo pa kulowa kwa dzuwa, otsatira odzodzedwa a Yesu Kristu m’mbali zonse zadziko lapansi amasunga imfa yake mogwirizana ndi malangizo amene iye anapereka kwa atumwi ake. (Luka 22:19, 20) “Nkhosa zina” nazonso zimafikapo, osati monga akudya mkate ndi kumwa vinyo, koma monga openyerera opereka ulemu.

12. Kodi ndimotani mmene Akristu ena oyambirira m’Korinto analepherera kusonyeza chiyamikiro choyenerera kaamba ka Mgonero wa Ambuye?

12 Iri siriri dzoma lachipembedzo lopanda pake koma liri lodzadzidwa ndi tanthauzo lamphamvu. Kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba m’Korinto, Grisi, ena amene analephera kusonyeza chiyamikiro choyenera cha nyengoyo, mtumwi Paulo analemba uphungu wamphamvu, akumati: “Yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye.” Kodi nchiyani chimene chinawapangitsa kukhala akudya ‘osayenera’? Sanali kudzikonzekeretsa bwino lomwe mu mtima ndi maganizo. Munali magawano mu mpingo. Ndiponso ena anadya mopambanitsa chakudya ndi kumwa mopambanitsa asanafike kumsonkhanowo. Anachitira Mgonero wa Ambuye mwamphwayi. Sanali mu mkhalidwe woti nkuzindikira tanthauzo lamphamvu lamkate ndi vinyo.—1 Akor 11:17-34.

13. Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la mkate ndi vinyo zogwiritsiridwa ntchito pa Chikumbutso?

13 Kodi tanthauzo limenelo nlotani? Sizikudalira m’kusandullzidwa kozizwitsa koyerekezedwa kwa mkate ndi vinyo. M’lingaliro lirilonse Kristu samaperekedwa nsembe kachiwiri pa Chikumbutso chirichonse. Malemba amalongosola kuti “Kristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri.” (Aheb. 9:28; 10:10; Aroma 6:9) Mtanda wamkate wopanda chotupitsa ndi vinyo wofiira ziri kokha zizindikiro zoimira thupi lenileni la Yesu loperekedwa nsembe ndi mwazi weniweni umene anakhetsa. Koma ha nzamtengo wapatali chotani nanga mmene zinthu zimenezi ziriri! Thupi lopanda uchimo laumunthu la Yesu linaperekedwa kotero kuti dziko la anthu likhale ndi mwayi wa kukhala ndi moyo kosatha. (Yoh. 6:51) Ndipo mwazi wake wokhetsedwa umatumikira mfundo ziwiri—kuyeretsa ku uchimo anthu amene amasonyeza chikhulupiriro mu uwo, ndiponso umachititsa kugwira ntchito kwa pangano latsopano pakati pa Mulungu ndi mpingo wa Israyeli wauzimu, umene wapangidwa ndi Akristu odzozedwa ndi mzimu. (1 Yoh. 1:7; 1 Akor. 11:25; Agal. 6:14-16) Ali makonzedwe amtengo wapatali amenewa amene amatheketsa ziwalo za “kagulu kankhosa” kulengezedwa kukhala olungama ndi Mulungu, makamaka kupatsidwa kwawo ungwiro waumunthu. (Luka 12:32) Izi zikuchitidwa kotero kuti abadwe ndi mzimu woyera monga ana a Mulungu, ncholinga cha kugawana ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba. Chotero pamene akudya zizindikiro za Chikumbutso chaka chirichonse, akumachitira umboni chiyembekezo chawo chakumwamba, chiyamikiro chawo cha kukhala mu “pangano latsopano” lochitiridwa unkhoswe ndi Kristu chimatsitsimulidwa ndi kuzamitsidwa.—Aheb. 8:6-12.

“Tidzamuka Nanu Anthu Inu”

14. (a) Kodi nchifukwa ninji “nkhosa zina” sizimadya zizindikiro pa Chikumbutso, koma kodi nchifukwa ninji zimakhala ndi phande mwaphamphu? (b) Kodi ndimotani mmene amawonera kugwirizana kwawo ndi otsalira a olowa nyumba a Ufumu?

14 “Nkhosa zina” zimazindikira mmene Yehova wakhala akuchitira ndi odzozedwa ake, ndipo izo zagwirizana nawo, kumati: “Tidzamuka nanu anthu inu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi anthu inu.” (Zek. 8:20-23, NW) Sikokha kuti amasonkhana pamodzi koma amagwirizana m’kudziwitsa mbiri yabwino ya Ufumu m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu. Komabe, “nkhosa zina” sizikulowetsedwa mu “pangano latsopano” ndi Israyeli wauzimu kapena kuphatikizidwa mu “pangano . . . laufumu” lopangidwa ndi Yesu ndi awo osankhidwa kukhala ndi mbali m’moyo wakumwamba limodzi naye, ndipo chifukwa chake, moyenerera, samadya zizindikiro pa Chikumbutso. (Luka 22:20, 29) Koma pamene “pangano latsopano” likwaniritsa chifuno chake, kusonkhanitsa ziwalo zotsirizira za “kagulu kankhosa” ku Ufumu wakumwamba, “nkhosa zina” zimazindikira kuti ichi chikusonyeza kuti madalitso amene iwo adzalandira padziko lapansi kupyolera mwa Ufumu umenewo ayandikira. Amauyesa mwayi, mkati mwa “masiku otsiriza,” kutumikira mogwirizana ndi otsalira okhulupirika a olowa nyumba aufumu.

[Mawu a M’munsi]

a Wonani mavesi oyambirira a Aroma, 1 ndi 2 Akorinto, Aefeso, Afilipi, Akolose, Tito, 1 ndi 2 Petro; ndiponso Agalatiya 3:26-29, 1 Atesalonika 2:12, 2 Atesalonika 2:14, 2 Timoteo 4:8, Abhetri 3:1, Yakobo 1:18, 1 Yohane 3:1, 2 ndi Yuda 1.

Makambitsirano Openda

● Kodi nchifukwa ninji mbali yaikulu ya Malemba Achigriki Achikristu imasonya ku chiyembekezo chakumwamba?

● Kodi ndimotani mmene awo amene abadwa monga ana a Mulungu amadziwira zimenezo? Kodi nchiyani chiri tanthauzo la zizindikiro za Chikumbutso zimene iwo amadya?

● Kodi ndimotani mmene “nkhosa zina” zimasonyezera kuti ziridi zogwirizana ndi “kagulu kankhosa”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena