Nyimbo 23
Chiyembekezo Chabaibulo cha Mtundu wa Anthu
1. Tsiku ladza; lowopsadi
Anthu ayembekeza motaya mtima.
Samawona, adzandira
Pamene dziko litha.
Koma m’Baibulo muli chifukwa
Chosangalalira Ufumu wadza.
Ya adzapukuta misozi yonse.
Tukulani mitu; musawopetu.
2. Moyowutu ngwamavuto,
Onse sangakane, anthu amafadi.
Sangapeŵe manda konse;
Ntchito zawo nzachabe.
Koma Baibulo liri nachotu
Chiyembekezo cha chiukiliro.
Anthu adzamka kumadzi a moyo.
Mbiriyi yanenedwa ndi Yehova.
3. Amanyoza Mulunguyo
Namtsutsa mwamwano, nayenda m’zoipa.
Satanayo alamula;
Kuipa kuli ponse.
Koma Baibulo limatiuza
Kuti Yehova adzaweruzadi,
Oipa adzachotsedwa kosatha,
Koma ofatsa adzadzaza dziko.