Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 7/1 tsamba 13
  • Umphumphu Pansi pa Chiletso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Umphumphu Pansi pa Chiletso
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amadalitsa Kwambiri Amene Amasunga Njira Yake
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Tizilambirabe Yehova Ngakhale Boma Litatiletsa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mulungu Samaiŵala ‘Chikondi Chimene Munachiwonetsera ku Dzina Lake’
    Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1988
w88 7/1 tsamba 13

Ripoti la Olengeza Ufumu

Umphumphu Pansi pa Chiletso

KWA zaka 11 ntchito yolalikira m’dziko limodzi la Kum’mwera cha kum’mawa kwa Asia yakhala iri pansi pa chiletso cha nduna za boma. Zaka zaposachedwapa, ngakhale kuli tero, abale akhala ndi chifukwa cha kukhulupirira kuti anthu ena athayo m’bomalo angakonde kusintha mkhalidwewo. Chiletsocho chikuwoneka kukhala chinasonkhezeredwa ndi chisonkhezero champhamvu cha zipembedzo za Chikristu cha Dziko m’mabwalo a boma.

Pa nthaŵi zina abale anagonjetseredwa ku kuvutitsidwa, kumangidwa, ndi kufunsidwa kwamphamvu. Awo ogwira ntchito m’malo a boma awopsyedwa ndi kutsitsidwa pa ntchito kapena kukakamizidwa kuleka ntchito ngati iwo sadzagwirizana ndi Boma m’chipani cha ndale zadziko. Gulu la ofalitsa linamenyedwa kwambiri.

Mboni zalandidwanso kuyenera kwa lamulo, monga ngati mautumiki a bwalo lamilandu ndi kuyenera kwa kutsogoza kuika maliro. (Olamulirawo amaika mtsogoleri wa chipembedzo kuchita ichi.) M’malo ena, ngakhale kulembetsa kwa ukwati kumakanizidwa kwa Mboni!

Komabe, awo amene akuyang’anira ntchito kumeneko akusimba kuti: “Mosiyanako, kumene abale amayang’anizana ndi nkhaniyo molimba mtima, mwaulemu akumapereka umboni kuchokera m’Baibulo, kufunsidwako kenaka kumaleka ndipo kuvutitsidwa kumachepetsedwako, kuwatheketsa abalewo kupitirizabe mokhutiritsa ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira.”​—Mateyu 28:19, 20.

Mwachitsanzo, mlongo pansi pa kufunsidwa anafunsidwa kumene angapeze dzina la Yehova. Molimba mtima iye anatsegula Baibulo lake pa Eksodo 15:3, kumene dzinalo limapezeka. Wofunsayo, mkulu wa gulu lankhondo, anatsatira m’Baibulomo, akumanena kuti: “Inde, ndithudi. Ilo liri m’Baibulo.” Kenaka, akutembenukira kwa mtsogoleri wa chipembedzo yemwenso anali kutengamo mbali m’kufunsako, iye anafunsa: “Nchifukwa ninji simudziŵitsa anthu ponena za dzinalo?” Mtsogoleri wa chipembedzoyo mwamanyazi anayankha kuti: “Aha, inde, dzinalo liri m’Chipangano Chakale. Koma chifukwa dziko lino siliri ndi kugwirizana kulikonse ndi Israyeli, sitigwiritsira ntchito dzinalo.” Mlongoyo anamasulidwa panthaŵi yomweyo!

Mwakumachitapo kanthu pa kudziŵitsidwa ndi munthu “wokondwerera,” apolisi analetsa woyambirira wa misonkhano itatu ya chigawo usiku umodzi usanayambike! Ngakhale kuli tero, anthu ena amalingaliro a chiyanjo pa gulu la apolisilo anathandiza kuletsa kuyambitsa kufunsa. Mopanda mantha, abalewo anachita misonkhano ina iŵiriyo.

Mosasamala kanthu za chitsutso champhamvu cha chipembedzo m’dziko iri, padakali awo amene amakonda chilungamo. Wolemba ntchito mmodzi, mwachitsanzo, pambuyo pa kuwona kukhulupirika kwa abalewo ku maprinsipulo awo ndi chikhulupiriro, iye wafikira pa kukulitsa chidaliro chokulira mwa abalewo. Iwo amapatsidwa mathayo ochulukira pa ntchito.

Zinthu zofananazo zimachitika kwa ana opita ku sukulu. Aphunzitsi owona mtima amawasirira iwo kaamba ka kaimidwe kawo kamphamvu kotengedwa kaamba ka chikhulupiriro chawo.

Ngakhale kuti mkhalidwe m’munda wakhala ukukhalako bwino kaamba ka abalewa, matchalitchi akadapitirizabe kuvutitsa kwawo ndi kuyesera njira iriyonse yothekera kuimitsa ntchito ya umboni. Nthaŵi zina iwo amayesera kuvulaza mwakuthupi awo amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni. Ngakhale kuli tero, okondwerera adakali kupitabe ku gulu la Yehova. Chokumana nacho chimodzi chiri cha gogo wachikazi m’zaka zake za mu ma-70. Pamene limodzi la maso ake linatumbulidwa, iye analongosola chikhumbo chake cha kuchita upainiya wothandizira. Chifukwa cha msinkhu wake, iye poyamba anadzimva kuti chifuno cha maora 60 chinali chachikulu koposa kwa iye, koma pambuyo pa kuyesera icho, iye anapeza kuti angachite tero. M’chenicheni, m’masiku khumi oyambirira, anaika maora 38 mu utumiki wa m’munda; kugawira mabukhu aŵiri, timabukhu titatu, ndi magazini aŵiri m’gawo lovuta; ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo aŵiri. Iye anali wachimwemwe!

Mwa zonse, mkhalidwe mu utumiki wa m’munda m’dzikoli uli wabwino kwambiri. Makamaka pambuyo pa masankho, abalewo akhala okhoza kulondola mbali zosiyanasiyana za umboni. Ichi mowonadi chapititsa patsogolo ntchitoyo. Wofalitsa wokhazikika ali wokhoza kukhala ndi maphunziro a Baibulo asanu ndi aŵiri kufika ku khumi. Kale, eninyumba anali ofunitsitsa kudziŵa ponena za amene ife tinali, kumene tinachokera, ndi zina zotero. Tsopano abale safunikira kudzidziŵikitsa iwo eni. Anthu ali anjala kaamba ka chakudya chauzimu chokhutiritsa. Munda ndithudi uli wokonzekera kaamba ka kututa.​—Mateyu 9:37, 38.

Ndithudi, abale m’dziko iri asunga umphumphu wawo pansi pa chiyeso, posachedwapa akumasangalala ndi chiwonjezeko cha 7 peresenti mwa ofalitsa! Iwo amatenga kaimidwe kamodzimodziko kamene wamasalmo Davide anatenga pamene ananena kuti: “Koma ine ndidzayenda mu [umphumphu, NW] wanga.”​—Masalmo 26:11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena