Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 8/15 tsamba 21-23
  • “Tuluka ku Dziko Lako ndi kwa Abale Ako”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Tuluka ku Dziko Lako ndi kwa Abale Ako”
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nchifukwa Ninji Iwo Amachita Chimenecho?
  • Nchiyani Chomwe Chiyenera Kulingaliridwa Musanachoke?
  • Ndi Zovuta Zotani Zomwe Zingayenere Kukumanizidwa?
  • Ndi Madalitso Otani Amene Angasangalalidwe?
  • Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kusamuka?
    Galamukani!—1994
  • Kodi Muli ndi Chikhulupiriro Chonga cha Abrahamu?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi ‘Mungawolokere ku Makedoniya’?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • “Limbitsani Mitima Yanu”
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 8/15 tsamba 21-23

“Tuluka ku Dziko Lako ndi kwa Abale Ako”

MU November 1981, Tony ndi mkazi wake, Margaret, limodzi ndi ana awo aŵiri, a zaka 9 ndi 11, anachoka ku England kupita kumadzulo kwa Ireland. Nchifukwa ninji? Kukathandiza mu ntchito yophunzitsa poyera ya Mboni za Yehova. Kokha milungu yoŵerengeka pambuyo pake, iwo anali kukumanizana ndi mavuto. Inali nyengo yachisanu yozizira kwambiri. Ziyembekezo za ntchito sizinagwire ntchito, chotero Tony anayamba ntchito yoyeretsa chipata cha m’nyumba chotulutsira utsi kunja. Alibe luso lokwanira, iye anabwerera kunyumba atakutidwa ndi mwaye wakuda pambuyo pa ntchito ya tsiku yolimbika. Tangolingalirani kukwiitsidwa kwake pamene iye anapeza kuti madzi m’mipopi analimba ndi kuzizira, ndipo iye anali kokha ndi ketulo imodzi ya madzi kuti asambemo! “Kokha kwa kamphindi ndinayamba kudabwa chifukwa chimene timachokera kumudzi kwathu ndi kwa achibale anthu,” iye anavomereza tero.

Kuchoka ku banja ndi mabwenzi kupita kukatumikira Mulungu mokwanira koposa, ndipo kenaka kukapitirizabe mosasamala kathu za mavuto, kumatenga chikhulupiriro chenicheni. Winawake amene anasonyeza chikhulupiriro choterocho chifupifupi zaka 4,000 zapitazo anali kholo Abrahamu. Wophunzira Stefano ananena ponena za iye kuti: “Mulungu wa ulemerero anawonekera kwa kholo lathu Abrahamu pokhala iye m’Mesopotamiya, asanayambe kukhala m’Harana, ndipo [Mulungu] anati kwa iye, “Tuluka ku dziko lako ndi kwa abale ako ndipo tiye ku dziko limene ndizakusonyeza iwe.’”​—Machitidwe 7:2, 3.

Ndithudi, palibe aliyense lerolino amene ali ndi lamulo lachindunji loterolo kuchokera kwa Mulungu la kuchoka ku dziko lakwawo. Zikwi za Akristu m’zana lino la 20, ngakhale kuli tero, zakonza zochita zawo kuti zichite chimene Abrahamu anachita​—kupita ku magawo atsopano kukapititsa patsogolo zikondwerero za Mulungu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Aroma 10:13-15) Iwo azindikira kuti “munda ndiwo dziko lapansi” ndi kuti malo ambiri ali ndi kusowa kokulira kaamba ka thandizo lowonjezereka. (Mateyu 13:38) Mofanana ndi Yesaya, iwo avomereza ndi mphamvu ku mawu a Yehova, “Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife?” Akumawona chifunocho, iwo nawonso ayankha kuti, “Ndine pano! Munditumize ine.”​—Yesaya 6:8.

Nchifukwa Ninji Iwo Amachita Chimenecho?

Ndi anthu a mtundu wanji amene amatenga kayendedwe koteroko? Iwo sali ochokera ku gulu la msinkhu umodzi kapena chiyambi, ndiponso kwa sadzinenera kukhala ndi kuthekera kwapadera. Iwo ali kokha anthu amene kaamba ka chinthu chimodzi, ali ofunitsitsa kuika zikhumbo zaumwini m’malo achiŵiri ndi kupeza chitonthozo m’chikondwerero cha Ufumu wa Mulungu. Chiri mofanana ndi Abrahamu pamene iye anachoka ku mzinda wopita patsogolo mwa chuma cha kuthupi ndi ulemerero wa Uri kukakhala m’mahema m’dziko lachilendo.​—Ahebri 11:8-10.

“Nthaŵi zonse tinakhoza kuwona chifuno cha kuchita zochulukira monga mmene kungathekere mu utumiki wa Yehova,” anatero okwatirana ena omwe anasamuka ndi ana awo amuna aŵiri a zaka za pakati pa 13 ndi 19 mu 1983. “Tinadzimva monga mmene anachitira mtumwi Paulo pamene iye ananena kuti, ‘Nthaŵi yotsalira yafupikitsidwa’; chotero tinalingalira ‘kupita ku Ireland’ ndi kuthandiza ndi ntchito kumeneko.” (1 Akorinto 7:29; yerekezani ndi Machitidwe 16:9.) Mogwirizana ndi matembenuzidwe amodzi omasuka, lingaliro la mawu a mtumwi Paulo pa 1 Akorinto 7:29 liri: “Chinthu chofunika kwambiri kuchikumbukira chiri chakuti nthaŵi yathu yotsalira iri yaifupi kwambiri,” ndipo moteronso uli mwaŵi wathu wa kuchita ntchito ya Ambuye. (The Living Bible) Akristu ambiri okhulupirika asamukira kulikonse kumene iwo afunidwa ndi cholinga chofuna kugwira mwaŵi umenewu usanazimirike ndi kupanga kugwiritsira ntchito kwabwino koposa kwa nthaŵi yawo yofunika yotsalira.

“Tinawona uwu kukhala monga mwaŵi wabwino nthaŵi zonse ‘kukhala ndi zambiri zochita m’ntchito ya Ambuye.’” (1 Akorinto 15:58, NW) “Tinafuna kutumikira Yehova kumene tikanachita zabwino zokulira.” “Tinadzimva kuti tinali mu mkhalidwe wabwino wa chuma kuchoka ndipo kuti ngati tikakwaniritsa chifuno kwinakwake, chikakhala cholakwa kwa ife kusachita icho.” Malongosoledwe oterowo amalongosola malingaliro a ambiri omwe atenga masitepi a kutumikira kumene iwo ali ofunidwa mokulira. Akristu amenewa atenga ku mtima chenjezo lopezeka pa Miyambo 3:9, 27: “Lemekeza Yehova ndi chuma chako ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha. Oyenera kulandira zabwino usawamane, pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.” Pambuyo pa kusanthula mosamalitsa mikhalidwe yawo, iwo agamulapo kuti icho ‘chiri m’dzanja lawo kuchita’ zabwino zosatha kwa anansi awo m’mbali zina za dziko.​—Onaninso Aroma 1:14, 15; Luka 10:27-37.

Mungakhale mu mkhalidwe wa kuchita kachitidwe koteroko. Ngati ndi tero, mungakhale okondweretsedwa m’njira zimene ena omwe achita kale kachitidwe koteroko ayankhira mafunso otsatirawa.

Nchiyani Chomwe Chiyenera Kulingaliridwa Musanachoke?

Musanachoke, funsani akulu mu mpingo wakwanuko. Pezani chimene iwo akulingalira ponena za makonzedwe anu. (Miyambo 24:6) Pangakhale zifukwa zimene kusamuka koteroko sikukakhala koyenerera mu nkhani yanu, ndipo iwo adzakuthandizani inu kuanthulanso mkhalidwe wanu moyenerera. Mwachitsanzo, munthu yemwe akusamuka ayenera kukhala wamphamvu mwauzimu ngati akufuna kukhala chida chabwino ndipo osati chopanda pake m’malo atsopano.

Gwirani ntchito kupyolera mu ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko ku limene mukuyembekezera kusamukira​—kapena kupyolera mu ofesi ya nthambi ya kwanuko ngati mukuyembekezera kusamukira mkati mwa dziko lanu lomwelo. Ngati chiri chotheka, chezerani gawo loyembekezeredwalo kuti mukadziŵe chinachake ponena za dzikolo ndi anthu musanapange chosankha chomalizira.

Santhulani malingaliro anu musanasamuke. Abrahamu anasamuka chifukwa chakuti anali ndi chikhumbo chozama cha kukwaniritsa chifuno cha Mulungu, osati chifukwa cha mzimu wa kufuna kuchezera malo kapena chisonkhezero chaumwini kapena chosangulutsa. Mosamalitsa santhulani nsonga zonse zokhudzidwa. Kodi pangakhale vuto la chinenero? Kodi mungasinthire ku mkhalidwe wa moyo wosiyana ndi nyengo? Kodi muli ndi zifuno zapadera za umoyo? Kodi ziwalo zonse za banja ziri zodzilowetsamo mwa mtima wonse m’kusamukako? Kodi mwalinganiza mkhalidwe wanu wa zachuma kotero kuti mungapange kusamuka koteroko kukhala kwa chipambano? (Yerekezani ndi Luka 14:28.) Izi ndi nsonga zina zambiri zimafunikira kulingalira kosamalitsa ndi kwa pemphero.​—Aefeso 6:18.

Ndi Zovuta Zotani Zomwe Zingayenere Kukumanizidwa?

Ngakhale pamene musanasamuke, mungayenere kuyang’anizana ndi zovuta. Si aliyense amene adzawona zinthu mmene mumachitira. Inu mungamve ndemanga zopanda kulingalirapo kapena ndemanga zosalimbikitsa. Kumbukirani, ngakhale ndi tero, kuti ngakhale mtumwi Petro anachita mosalimbikitsa pamene iye anamva chimene chinali pafupi kuchitika kwa Yesu. M’malo molimbikitsa Yesu kukhala wosasunthika m’kuchita chifuniro cha Yehova, Petro ananena kuti: “Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa inu ayi.” Mofanana ndi Yesu, gamulanipo kupewa kulankhula kosalimbikitsa kulikonse kwa mtundu umenewo.​—Mateyu 16:22, 23.

Pambuyo pa kukhazikika m’gawo lanu latsopano, kukhumba kunyumba kungakhale vuto lalikulu. Chikondi kaamba ka Yehova ndi kaamba ka anthu omwe akufunikira kumva mbiri yabwino ya Ufumu wake chidzakuthandizani inu kuchita ndi chimenechi. Mavuto ambiri angachepetsedwe ngati inu mowonadi mupanga malo anu atsopano kukhala nyumba yanu. Pewani kupanga kuyerekeza kosalimbikitsa ndi kumudzi kwanu kwakale, popeza kuchita tero kungapangitse kusakhutiritsidwa ndi kudandaula. Pamene muyang’anizana ndi zovuta, kumbukirani chiitano cha Yehova pa Malaki 3:10: “Mundiyese nako tsono, . . . ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.”

Ndi Madalitso Otani Amene Angasangalalidwe?

Pamene kudzilowetsamo kwanu mu ntchito yolengeza mbiri yabwino kukula, moteronso mtundu wa utumiki wanu udzakula. Mudzakulitsa maluso ambiri monga mphunzitsi wa Mawu a Mulungu. Ichi chidzabweretsa mapindu osati kokha kwa inu koma kwa onse okumvetserani inu. (1 Timoteo 4:15, 16) Ndi mwaŵi wotani nanga kutsogoza maphunziro a Baibulo a panyumba ndi kuthandiza anthu owona mtima kumasuka ku ziphunzitso zonyenga za Chibabulo! Mungakhale ndi chimwemwe cholongosoledwa ndi mtumwi Paulo pamene iye analembera kwa ena amene anawathandiza kukhala Akristu: “Pakuti chiyembekezo chathu kapena chimwemwe kapena korona wa kudzitamandira naye​—nchiyani, si ndinu nanga?” (1 Atesalonika 2:19) Inde, chiri chimwemwe ndi dalitso kugawanamo m’kuthandiza anthu ndi mipingo kupita patsogolo mwauzimu.

Abrahamu anatchedwa “bwenzi la Yehova” chifukwa iye mofunitsitsa anamvera chitsogozo cha Mulungu. (Yakobo 2:21-23; Yesaya 41:8) Nanunso mungazamitse unansi wanu waumwini ndi Mulungu. Pamene mukudzikakamiza inu eni mu utumiki wake, mudzakumana ndi chisamaliro chake chachikondi ndi chichirikizo. Mudzamvetsetsa mokwanira koposa chimene wamasalmo anatanthauza pamene ananena kuti: “Talawani ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.”​—Masalmo 34:8.

Tony, Margaret, ndi ana awo anayang’anizana ndi mavuto pamene iwo anasamuka kukatumikira Yehova mokwanira koposa. Koma ndi thandizo la Yehova, iwo mwachipambano anachita nazo. “Sitinalole mavuto kutilanda ife chimwemwe chathu,” iwo anatero. “M’mikhalidwe yonga imene tinakumanizana nayo, tinaphunzira kudalira pa Yehova mokulira, ndipo tinawona dzanja lake m’chirichonse pamene vuto limodzi pambuyo pa linzake linatha.” Zikwi za atumiki amakono a Yehova zasonyeza chikhulupiriro chofananacho mwa kusamukira kulikonse kumene kuli chifuno chokulira. Kodi mungachite chofananacho?

[Chithunzi patsamba 23]

Kukambitsirana kwa banja kungapange kaamba ka kusamuka kwa chipambano kokulira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena