Chikuto Chakumbuyo
Kodi ndi Buku Lina Liti
• limene lasonkhezera kwambiri maluso abwino kwambiri padziko lapansi ojambula, olemba mabuku, ndi a nyimbo, limenenso lakhudza kwambiri zamalamulo?
• limene lapulumuka zaka zikwi zambiri za kukopedwa pamanja komanso lafika kwa ife monga momwedi linalembedwera?
• limene lasonkhezera ena kukhala ndi mzimu wopanda dyera kwakuti akhala okonzeka kuvutika ngakhale kufa kuti alitembenuze?
• limene latembenuzidwa m’zinenero zoposa 2,100, likumapezeka kwa oposa 90 peresenti ya anthu onse padziko lapansi?
• limene limatchula zenizeni za sayansi zimene anthu anadzazitulukira pambuyo pake patapita zaka mazana ambiri?
• limene lili ndi mfundo zosasintha ndi nthaŵi zimene zingathandize anthu a fuko, mtundu, ndi dziko lililonse kuwongolera moyo wawo?
• limene lili ndi maulosi olondola amene anakwaniritsidwa, monga momwe mbiri ikusonyezera?
Kodi sikungakhale koyenera kulipenda buku limenelo?