Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuyankha Kuitana kwa Zisumbu za Micronesia
    Nsanja ya Olonda—1987
    • “ndipo enawo akupita patsogolo kulinga ku ubatizo. Ntchito yopulumutsa moyo yoteroyo iri ndi phindu lalikulu m’maso mwathu.” James, mishonale kwa zaka zoposa khumi, akunena kuti: “Kuwona kupirira kwa abale athu a ku Kosrea chaka ndi chaka kuli dalitso lenileni.” Mu Belau, Roger akuchitira ndemanga kuti: “Tadalitsidwa ndi Nyumba ya Ufumu yatsopano ndi gulu lomvera la ofalitsa.” Ndipo kuyang’ana m’mbuyo mkati mwa zaka, Placido akunena kuti: “Chitsogozo cha Yehova ndi mzimu woyera zatsimikiziridwa m’miyoyo yathu. Ichi chatithandiza ife kutsendera kufupi kwa iye.”

      Zokumana nazo zoterozo zalimbikitsa amishonale kukhalabe m’magawo awo. Ambiri a iwo angayang’ane m’mbuyo ndi kukumbukira kupangidwa kwa mpingo woyamba m’dera lawo. Mofanana ndi mtumwi Paulo, iwo ali ndi chimwemwe chapadera ‘cha kusamanga pa maziko a munthu wina.’ (Aroma 15:20) Kudzimva kwawo kukulongosoledwa bwino ndi ndemanga iyi: “Padakali ntchito yambiri yoti ichitidwe. Ndikhulupirira kuti Yehova adzatsegula mwaŵi wambiri kubweretsa ena ambiri onga nkhosa mu zisumbu izi, ndipo tiri ndi mwaŵi kugawana mu icho.”

      “Madalitso a Yehova​—alemeretsa, sawonjezerapo chisoni,” likutero Baibulo pa Miyambo 10:22. Awo amene ayankha ku chiitano cha umishonale mu zisumbu za Micronesia mowonadi akumana ndi dalitso limeneli limodzi ndi chimwemwe ndi zikhutiritso zomwe zimabwera kuchokera ku kutumikira Yehova.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1987
    • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

      ◼ Kodi Paulo anali kulozera kwa Yehova kapena kwa Yesu pamene iye analemba kuti: ‘Ambuye anati kwa iye: “Mphamvu yanga ikupangidwa kukhala yangwiro mu ufoko”’?

      Chikuwoneka kuti mtumwi Paulo anali kulozera kwa Ambuye Yehova. Mwakudziŵa mawu a Paulo m’lembalo, sitingawone kokha nchifukwa ninji ichi chiri tero komanso tingazamitse chiyamikiro chathu kaamba ka unansi pakati pa Mulungu ndi Mwana wake. Paulo akulemba kuti:

      “Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m’thupi, ndi mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa. Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine. Ndipo ananena kwa ine: ‘Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga [ikupangidwa kukhala yangwiro mu ufoko, NW].’ Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m’maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine.”​—2 Akorinto 12:7-9.

      Munga m’thupi la Paulo ungakhale unali kaya umphaŵi wa maso kapena atumwi onyenga omwe anatokosa utumwi wake. (Agalatiya 4:15; 6:11; 2 Akorinto 11:5, 12-15) Chirichonse chomwe chinali, icho chinafuna kukhumudwitsa Paulo kapena kumulefula iye kudzitamandira pa utumiki wake. Chotero iye katatu anafunsa kuti icho chichotsedwe. Koma kodi ndani amene iye anafunsa, ndipo kodi ndani amene anayankha mwakulankhula za “mphamvu yanga”?

      Popeza nkhani ikutchula “mphamvu ya Kristu,” chingawoneke ngati kuti Paulo anafunsa Ambuye Yesu. Mosakaikira, iye ali ndi mphamvu ndipo angaipereke iyo kwa ophunzira ake. (Marko 5:30; 13:26; 1 Timoteo 1:12) M’chenicheni, Mwana wa Mulungu “amakwaniritsa zinthu zonse ndi mawu amphamvu yake.”​—Ahebri 1:3; Akolose 1:17, 29.

      Ngakhale kuli tero, Ambuye Mulungu ali magwero a akulu koposa amphamvu, amene iye angathe ndipo amapereka kwa olambira ake. (Masalmo 147:5; Yesaya 40:26, 29-31) Mphamvu yoteroyo yochokera kwa Mulungu inamutheketsa Yesu kuchita zozizwitsa ndipo idzamutheketsanso iye kuchitapo kanthu. (Luka 5:17; Machitidwe 10:38) Mofananamo, atumwi a Yesu ndi ophunzira ena analandira mphamvu kuchokera kwa Yehova. (Luka 24:49; Aefeso 3:14-16; 2 Timoteo 1:7, 8) Ichi chinaphatikizapo Paulo, yemwe anachitira utumiki “monga mwamphatso ya chisomo cha Mulungu chimene anapatsidwa [mtumwiyo] monga mwamachitidwe amphamvu yake.”​—Aefeso 3:7.

      Popeza Paulo anapempha kaamba ka kuchotsedwa kwa ‘munga m’thupi mwake, mngelo wa Satana,’ chiri chanzeru kuti iye anayang’ana kwa Ambuye Mulungu kuchita ichi, Yehova akumakhala amene mapemphero amalunjikitsidwako. (Afilipi 4:6; Masalmo 145:18) Kuwonjezerapo, kulimbikitsa Paulo kwa Yehova ndi mawu akuti, “Mphamvu yanga [ikupangidwa kukhala yangwiro mu ufoko, NW] sikumusiya Kristu. Mphamvu yochokera kwa Ambuye Mulungu ingalongosoledwe monga “mphamvu ya Kristu [yomwe inali] yonga chihema” pa Paulo, popeza ‘Kristu ali mphamvu ya Mulungu ndi nzeru ya Mulungu.’ (1 Akorinto 1:24) Chotero, 2 Akorinto 12:7-9 amatithandiza ife kuyamikira bwino njira yokhoza kukhota mu imene Yehova amagwiritsira ntchito Mwana wake m’kukwaniritsa chifuno chaumulungu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena