Kuthandiza Ofalitsa Osakhazikika ndi Ofooka
1 Yesu anati: “Yense amene akamva mawu anga ameneŵa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.” (Mat. 7:24) Munthu atawamvetsetsa bwino mawu a Yesu ndi kumsonkhezera moyenera, angamthandize kubala zipatso zabwino, kuphatikizapo kulalikira uthenga wabwino. Kumvera koteroko kuli maziko onga thanthwe, omwe sangakokoloke pamkuntho watsoka.
2 Tili ndi chifukwa chabwino chothandizira ena kugwira nawo ntchito yolalikira pamlingo wokwanira ndithu malinga ndi mmene mikhalidwe yathu ingatilolere. Ena mwa ife ali ofalitsa odumphadumpha, ndipo chimenecho nchodetsa nkhaŵa kwambiri. Kodi nchiyani chingampangitse munthu kulola mwezi wathunthu kutha popanda kugwira nawo ntchito yofunika yolalikira ndi kupanga ophunzira?
3 Mwina ena anali kudwala kwambiri, ndipo enanso ankafuna kudzaloŵa mu utumiki wakumunda pakati pamwezi, ndiyeno nkupeza kuti akumana ndi mikhalidwe ina yosayembekezereka, nkuwalepheretsa kupita ku utumiki. Ena angakhale asakudziŵa kuti utumikiwu uli chuma chimene tiyenera kuchisamala choyamba. (2 Akor. 4:7) Chinthu china chimene chakhala chofooketsa ndicho mavuto ochititsidwa ndi mwamuna kapena mkazi ndi achibale ena. Kulephera kuchita phunziro laumwini ndi kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse kwafooketsanso ena, moti akuiŵala kuti mapeto a dziko la Satana akuyandikira msanga. (2 Pet. 3:11) Kanthu kena kagwetsa mtima wawo mphwayi. Iwo sakulankhulanso monga mwa kusefukira kwake. (Mat. 12:34) Kaya chifukwa chake nchotani, koma afunikira kuthandizidwa.
4 Zimene Akulu Angachite: Akulu ayenera kuyesetsa kudziŵa mikhalidwe ya onse mumpingo ndi zosoŵa zawo kuti akhoze kuwathandiza mwachikondi. Pakukumana kwawo akulu azizindikira wofalitsa aliyense amene wayamba kudumphadumpha ndi kuona kuti ndani amene angawathandize ndi mmenenso wothandizayo angachitire zimenezo. Mwinanso angalitchule vutolo polongosola zosoŵa zapampingo pa Msonkhano Wautumiki. Mlembinso, podzaza makhadi a Cholembapo Ntchito za Wofalitsa cha Mpingo, ayenera kumazindikira umboni uliwonse wosonyeza kuti wofalitsa wayamba kudumphadumpha mu utumiki wakumunda.
5 Zimene Ochititsa Phunziro la Buku Angachite: Mwezi uliwonse mlembi ayenera kupatsa ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo mpambo wa omwe amalephera kupereka lipoti la ntchito yakumunda, kuti athandizidwe msanga. (Onani Utumiki Wathu Waufumu wa April 1998, tsamba 4, ndime 7.) Wochititsa phunziroyo angawafikire mwaulemu amene ali odumphadumphawo kuti adziŵe chimene chikuwapinga ndi mmene angawathandizire. (Miy. 27:23) Ambiri amene ali odumphadumpha adzayamikira atathandizidwa. Atadziŵa mikhalidwe ya munthuyo, wochititsa phunziroyo angalinganize kuti iyeyo agwire ntchito ndi munthuyo kapena kusankha wofalitsa wina wokhwima kapena mpainiya wina kuti atero. Zingathandizenso kuwapatsa anthu odumphadumphawo malingaliro othandiza ponena za kukonza ndandanda yoyenerana nawo malinga ndi mikhalidwe yawo. Kodi angakonzekere kugwira ntchito nthaŵi zonse mu utumiki wakumunda?
6 Pokachezera magulu a phunziro la buku, woyang’anira utumiki angalinganize zoti atengane ndi wochititsa phunziro kuti akachezere anthu odumphadumpha. Choncho abale aŵiri okhwima adzakhoza kuthandizana kupereka uphungu ndiyeno nkuthandiza anthu amenewo kumanga maziko onga thanthwe a kumvera lamulo la Kristu lakulalikira ndi kupanga ophunzira. Chotero iwo angasonkhezereke kumaika ntchito yolalikira patsogolo pa zinthu zawo zonse. (Aroma 10:10) Tiyeni tiyesetse kusonyeza kuti timakonda “a pa banja lachikhulupiriro.”—Agal. 6:10.
7 Kuthandiza Ofooka: Limodzi mwa mafanizo a Yesu likunena za mbusa wosiya nkhosa 99 nkukafunafuna imodzi yotayika. Kodi mukukumbukira zimene anati zidzachitika ngati imodzi yotayikayo inapezedwa? “Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi zosasokera.” (Mat. 18:13) Mipingo yambiri yakhala nacho chisangalalo choterocho pamene anthu ofooka anabwerera ku gulu lankhosa la Mulungu.
8 Pazaka zingapo zapitazo, tinayesanso kuthandiza awo amene anakhala ofooka. Oyang’anira ali ndi udindo wakupenyerera gulu lonse la nkhosa. (Mac. 20:28) Nchifukwa chake amakachezera anthu ofooka. Zotsatira zake zinali zakuti ambiri anayamikira kuyesayesa kwachikondi kumeneku ndipo anakhalanso olengeza Ufumu okangalika. Kodi mumpingo mwanu akalimo ena amene akhala ofooka m’zaka zaposachedwapa? Kodi mungatani kuti muwathandize?
9 Zimene Mungachite: Woyang’anira utumiki ndi mlembi amatsogolera kugwirizanitsa abale pakuyesayesa kuthandiza anthu ofooka. Akulu ayenera kulinganiza zochita zawo kuti oyamba akhale iwowo kukachezera anthuwo. Nthaŵi zina, mwina munthu wofookayo angakonde kuti wina azichita naye phunziro la Baibulo. Kapena wina amene ankaphunzira ndi munthuyo poyamba kapena wina amene munthuyo amadziŵa ndi kumlemekeza, angakhalenso wothandiza. Ngati lili banja lonse, mwina pangafunikire kupempha mkulu wina kapena mtumiki wotumikira wokhoza bwino kuti aziphunzira nawo. Mlongo wofooka angathandizidwe ndi mlongo wachidziŵitso. Wachinyamata zingamkhalire bwino kuchita ndi mtumiki wotumikira wachinyamata kapena mpainiya waluso. Mwina woyang’anira utumiki angalangize kuti nkhani zakutizakuti kapena buku lonse liphunziridwe. Cholinga nchakuthandiza. Woyang’anira utumiki angagwiritsire ntchito aliyense amene ali wokhoza bwino kuchita zimenezo.
10 Akulu ena aona kuti nkopindulitsa kuti paulendo woyamba azipenda nkhani yakuti ‘Bwererani kwa Mbusa wa Miyoyo Yanu’ mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1982, (Chingelezi). Mungawasonyeze chifundo cha Yehova ndipo mungawasimbire nkhani za anthu ena amene anabwerera kwa Yehova. Ngati ali wachinyamata yemwe wakhala wofooka, nkhani yakuti ‘Bwezerani Mtima Wanu kwa Yehova’ mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1982, (Chingelezi), ingamthandize. Kenako, mungalinganize zochita naye phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse.
11 Ofalitsa amene apatsidwa udindo ndi mwayi wochititsa maphunziro amenewo ayenera kuwasonyeza anthuwo kuti akukondwera nawo. Ayenera kuyanjana nawo. Kuwasonyeza kuti nkofunika kupezanso mphamvu yauzimu. Athandizeni kuzindikira kuti Yehova, mwa chikondi chake, ndi kuwadera nkhaŵa, wakonza kuti iwo athandizidwe payekhapayekha kudzera mwa gulu lake.
12 Ngakhale kuti ofalitsa ena ndi ena adzapemphedwa kuthandiza anthu ofooka, zimenezo sizikutanthauza kuti enanso sangathe kuthandiza. Onse angachite bwino kumawapatsa moni anthuwo pamene akufika pa Nyumba ya Ufumu ndi kumakambitsirana nawo nkhani zolimbikitsa. Asonyezeni kuti timakondwa kukhala nawo ndi kutinso tikuyembekezera kuwaona akupitabe patsogolo. Chidwi chowalimbikitsa chimenechi tiyenera kupitiriza kuchionetsa pamene iwo akupitabe patsogolo. Zotsatirapo zabwino zakhalapo chifukwa cha kuthandizana koteroko.—Aef. 4:16.
13 Indedi, timasangalala tikamaona anthu omwe kale anali ofooka akumasonkhananso nafe ndi omwe anali osakhazikika tsopano akumagwira ntchito mu utumiki mwezi uliwonse. Zimenezi zili choncho makamaka kwa aja amene iwo eniwo anakhozapo kuthandiza anthu ena. Tikupempherera kuti Yehova adalitse mooloŵa manja khama lathu ‘pochitira chokoma’ omwe anali ofooka kapena odumphadumpha ndiponso omwe ali “a pa banja lachikhulupiriro.”—Agal. 6:10.