Mphunzitsi wa ku Moscow Anathandizidwa ndi Galamukani!
Mphunzitsi analembera ofesi ya Mboni za Yehova ku Russia kuti akufuna kumagwiritsira ntchito nkhani za mu Galamukani! m’kalasi mwake. Iye analongosola kuti:
“Ndimaona kuti Galamukani! amandilimbikitsa, kupangitsa mtima wanga kukhala pansi, ndi kundichotsera nkhaŵa. Ndikukuyamikani chifukwa cha nkhani zodabwitsa zonena za kulimbana pakati pa munthu ndi tizilombo toyambitsa matenda [kope la March 8, 1996]. Ndikukhulupirira kuti magazini anu amathandiza banja lililonse limene lili nawo.” Iye anawonjezera kuti: “Ndingakonde kumalandira Galamukani! . . . Mosakayikira magazini anu akhoza kundithandiza.”
Kalata inanso yokhala ngati yomweyi yomwe inachokera ku Stavropol, mzinda wa anthu oposa 250,000, womwe uli pamtunda woposa mamailosi 700 kumwera chakummaŵa kwa Moscow, inati: “Ndifuna kuoda Galamukani! Si kale kwambiri pamene ndinalandira makope aŵiri a magazini ameneŵa. Nkhani zake zinasonyeza kuti mmadziŵadi mavuto amene anthu amakumana nawo. Nkhani zina zinanena zinthu zomwe sindinazimvepo. Aka nkoyamba kuti ndione nkhani zolongosola bwino zinthu chotere.”
Ngati mufuna kulandira kope lina la Galamukani! kapena mukufuna kuti wina azibwera panyumba panu kudzakambitsirana nanu za m’Baibulo, chonde lemberani ku Watch Tower Society, Box 30749, Lilongwe 3, kapena ku keyala yoyenera patsamba 5.