Mmene Mungagwiritsirire Ntchito “Kukambitsirana za m’Malemba”
Chitsanzo chotsatira m’kuthandiza ena kumvetsetsa Baibulo ndicho chija choperekedwa ndi Yesu Kristu ndi atumwi ake. Poyankha mafunso, Yesu anagwira mawu malemba ndipo panthaŵi zina anagwiritsira ntchito mafanizo oyenerera amene akathandiza anthu owona mtima kulandira zimene Baibulo limanena. (Mat. 12:1-12) Mtumwi Paulo anapanga kukhala chizoloŵezi ‘kukambitsirana za m’Malemba, kufotokoza ndi kutsimikizira mwa maumboni’ zimene anaphunzitsa. (Machitidwe 17:2, 3, NW) Mawu a m’bukhu lino angakuthandizeni kuchita zofananazo.
Mmalo mwa kupereka kufoledwa kokulira, ndi kofala kwa nkhani iriyonse, Kukambitsirana za m’Malemba limasumika chisamaliro chachikulu pa mafunso amene akufunsidwa tsopano lino ndi anthu ambiri.
Bukhu lino silinalinganizidwire kuthandiza aliyense “kuwina mikangano” ndi anthu amene samalemekeza chowonadi. Mmalo mwake, limapereka chidziŵitso chofunika cholinganizidwira kugwiritsiridwa ntchito m’kukambitsirana ndi anthu amene adzakulolani kuchita motero. Ena a iwo angafunse mafunso amene akuwafuniradi mayankho okhutiritsa. Ena, m’nthaŵi ya kukambitsiranako, angafotokoze zikhulupiriro zawo ndipo angatero mokhutira kwambiri. Koma kodi iwo ali anthu olingalira amene ali ofunitsitsa kumvetsera lingaliro lina? Ngati ali otero, mungathe kugaŵana nawo zimene Baibulo limanena, mukumatero ndi chikhutiro chakuti zidzalandiridwa mokondwa ndi mitima ya okonda chowonadi.
Kodi mungapeze motani nkhani yeniyeni imene mufuna m’bukhu lino lamaumboni? Kaŵirikaŵiri mudzaipeza mosavuta konse mwa kutembenukira mwachindunji kumutu waukulu umene umaimira nkhani yomwe ikukambitsiridwa. Pansi pa mitu yankhani yaikulu yonseyo, mafunso okulira ngosavuta kuwalekanitsa; alembedwa m’zilembo zakuda zimene zimayambira m’mphepete kudzanja lamanzere. Ngati simupeza mofulumira zimene mufuna, yang’anani ku Zosonyezera kothera kwa bukhuli.
Kukonzekera makambitsiranowo pasadakhale kuli kopindulitsa nthaŵi zonse. Koma ngati muli wosazoloŵerana konse ndi zigawo zina za bukhuli, mungazigwiritsirebe ntchito bwino lomwe. Motani? Pamene mupeza funso limene liri pafupifupi loyenderana ndi mfundo imene mufuna kukambitsirana, yang’anani mutu wankhani waung’ono uliwonse pa mfundoyo. Mitu yankhani imeneyi yalembedwa m’mawu a kanyenye wodera ndipo alembedwa pansi pa mafunso ogwirizana nawo. Ngati inu muli kale ndi chidziŵitso cha nkhaniyo, kupendedwa kwa mitu yankhani yaing’ono imeneyo ndi kuyang’ana mofulumira mfundo zina za mituyo kungakhale zokha zimene mufunikira, chifukwa chakuti zimapereka ganizo lothandiza la chigomeko limene lingagwiritsiridwe ntchito. Musazengeleze kutchula mfundozo m’mawu a inumwini.
Kodi mulingalira kuti mufunikira zowonjezereka—mwinamwake malemba enieni, chigomeko chochigwiritsira ntchito mogwirizana ndi malemba amenewo, mafanizo ena okuthandizani kuchititsa kukambitsirana zimene Baibulo limanena kukhala komvekera bwino, ndi zina zotero? Ngati ziri choncho, mungafune kusonyeza munthu amene mukulankhula naye zimene muli nazo m’bukhu lino ndiyeno ŵerengerani pamodzi kachigawo kamene kakuyankha funso limene wafunsa. Ngakhale ngati simunaphunzire nkhaniyo pasadakhale, mungaigwiritsire ntchito kuperekera yankho lokhutiritsa. Chirichonse chikupezeka m’bukhu mommuno, chalongosoledwa mu mpangidwe wokhweka ndi wachidule.
Kumbukirani kuti bukhu lino liri kokha chithandizo. Baibulo ndilo chilimbilimbi. Ndiro Mawu a Mulungu. Pamene kugwidwa mawu m’bukhuli kwachokera m’Baibulo, khomerezani chenicheni chimenechi pa amene mukulankhula nawo. Pamene kuli kotheka, afunseni kutulutsa Baibulo lawo ndi kuyang’ana malemba kotero kuti adzawona kuti zimene mukunena ziridi m’makope awo a Malemba Opatulika. Ngati matembenuzidwe a Baibulo ogwiritsiridwa ntchito mofala atembenuza mfundo zazikulu za malemba ena m’njira yosiyana, kaŵirikaŵiri zimenezi zimasonyezedwa, ndipo mamasuliridwe a matembenuzidwe osiyanasiyana amaperekedwa kaamba ka kuyerekezera.
Mogwirizana ndi chitsanzo choperekedwa ndi mtumwi Paulo posonya kuguwa lansembe “Kwa Mulungu Wosadziŵika” ndi pogwira mawu maumboni akudziko ovomerezedwa ndi anthu onse polalikira kunzika za Atene (Mac. 17:22-28), bukhuli likugwira mawu mochepa kumbiri yakale ya kudziko, mabukhu a nazonse, mabukhu a maumboni achipembedzo, ndi mabukhu omasulira mawu a Baibulo. Chotero, mmalo mwa kupanga zitsimikiziro ponena za magwero a zizoloŵezi zachipembedzo chonyenga, kuyambika kwa ziphunzitso zina, ndi matanthauzo a mawu Achihebri ndi Chigriki, bukhuli limasonyeza zifukwa zimene mawuwo anenedwera. Komabe, limasonyeza Baibulo kukhala magwero aakulu a chowonadi.
Monga chithandizo chowonjezereka m’kulambula njira ya kugaŵira chowonadi Chabaibulo kwa ena, zigawo zoyambirira za bukhuli ziri ndi ndandanda ya “Mawu Oyambirira Ogwiritsidwa Ntchito mu Uminisitala Wakumunda” ndi kusonkhanitsidwa kwa malingaliro onena za “Mmene Mungayankhire Oyembekezera Kuimitsa Kukambitsirana.” “Oimitsa kukambitsirana” ena ambiri oyembekezeredwa amaphatikizapo zikhulupiriro zina, ndipo zimenezi zafotokozedwa pamapeto a chigawo chachikulu chirichonse chofotokoza zikhulupiriro zimenezo. Sikunalinganizidwire kuti muloŵeze pamtima mayankho amenewa, koma mosakaikira mudzakupeza kukhala kothandiza kupenda chifukwa chake ena awapeza kukhala ogwira mtima; ndiyeno lankhulani malingalirowo mmawu a inu mwini.
Kugwiritsiridwa ntchito kwa bukhu lamaumboni iri kuyenera kukuthandizani kukulitsa luso la kukambitsirana za m’Malemba ndi kuzigwiritsira ntchito mogwira mtima m’kuthandiza ena kuphunzira “zazikulu za Mulungu.”—Mac. 2:11.