Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Dziperekeni pa Kuŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1996 | May 15
    • iwe ndiwe mkazi waulemu.” (Rute 3:11) Posapita nthaŵi, Boazi akukwatira Rute. Mogwirizana ndi makonzedwe a ukwati wapachilamu, mkaziyo ndi Boazi akubalira mwana “kwa Naomi.” Rute akukhala kholo la Davide ndipo potsirizira pake la Yesu Kristu. Motero iye analandira “mphotho yokwanira.” Ndiponso, awo amene amaŵerenga nkhani ya m’Malembayi amapezapo phunziro lofunika: Khalani okhulupirika kwa Yehova, ndipo mudzadalitsidwa kwambiri.​—Rute 2:12; 4:17-22; Miyambo 10:22; Mateyu 1:1, 5, 6.

      16. Kodi Ahebri atatu anakumana ndi chiyeso chotani, ndipo nkhani imeneyi ingatithandize motani?

      16 Nkhani ya Ahebri otchedwa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego ingatithandize kukhala okhulupirika kwa Mulungu m’mikhalidwe yoyesa. Onani m’maganizo chochitikacho pamene mukuŵerenga momveka Danieli chaputala 3. Fano lalikulu lagolidi lili thobo pachigwa cha Dura, kumene akuluakulu aboma a Babulo asonkhana. Pakumveka kwa ziŵiya za nyimbo, akugwada ndi kulambira fano limene Mfumu Nebukadinezara waliimika. Ndiko kuti, onse akuchita motero kusiyapo Sadrake, Mesake ndi Abedinego. Mwaulemu, koma mwamphamvu, iwo akuuza mfumu kuti sadzatumikira milungu yake ndi kulambira fano lagolidilo. Ahebri achichepere ameneŵa akuponyedwa m’ng’anjo yotentha yamoto. Koma kodi nchiyani chimene chikuchitika? Itayang’ana mkatimo, mfumu ikuona amuna anayi, mmodzi wa iwo “akunga mwana wa milungu.” (Danieli 3:25) Ahebri atatuwo akutulutsidwa m’nganjo, ndipo Nebukadinezara akulemekeza Mulungu wawo. Kuona m’maganizo chochitikacho kwakhala kofupa. Ndipo zimenezi zimapereka phunziro lofunika chotani nanga ponena za kukhulupirika kulinga kwa Yehova pansi pa chiyeso!

      Pindulani ndi Kuŵerenga Baibulo Monga Banja

      17. Tchulani mwachidule zinthu zina zopindulitsa zimene banja lanu lingaphunzire mwa kuŵerengera Baibulo pamodzi.

      17 Banja lanu lingathe kupeza mapindu ambiri ngati muthera nthaŵi mukuŵerenga Baibulo pamodzi nthaŵi zonse. Kuyambira ku Genesis, mukhoza kuona chilengedwe ndi kusuzumira m’mudzi woyamba wa munthu wa Paradaiso. Mungathe kukhala ndi phande m’zochitika za makolo okhulupirika ndi mabanja awo ndi kutsatira Aisrayeli pamene akuwoloka pouma pa Nyanja Yofiira. Mungathe kuona mnyamata mbusayo Davide akugonjetsa chimphona cha Afilisticho Goliati. Banja lanu lingathe kuona kumangidwa kwa kachisi wa Yehova mu Yerusalemu, lingathe kuona kupasulidwa kwake ndi magulu a Ababulo, ndipo lingathe kuona kumangidwanso kwake pansi pa Kazembe Zerubabele. Muli limodzi ndi abusa wamba pafupi ndi Betelehemu, mungathe kumva chilengezo cha mngelo cha kubadwa kwa Yesu. Mungathe kupeza tsatanetsatane wa ubatizo wake ndi utumiki wake, mungathe kumuona akupereka moyo wake waumunthu kaamba ka dipo, ndipo nanunso mungathe kukondwa nako kuuka kwake. Kenako, mungathe kuyenda ulendo ndi mtumwi Paulo ndi kuona kukhazikitsidwa kwa mipingo pamene Chikristu chikuwanda. Ndiyeno, m’buku la Chivumbulutso, banja lanu lingaone masomphenya aakulu a Yohane a zinthu zamtsogolo, kuphatikizapo Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi.

      18, 19. Kodi ndi malingaliro otani amene akuperekedwa ponena za kuŵerenga Baibulo kwa banja?

      18 Ngati mukuŵerenga Baibulo momveka monga banja, liŵerengeni momveka bwino ndiponso motenthedwa maganizo. Poŵerenga zigawo zina za Malemba, wa m’banja wina​—mwinamwake atate​—angaŵerenge mawu ofotokoza nkhaniyo. Ena a inu mungakhale anthu a m’Baibulo, mukumaŵerenga mbali zanu mwaumoyo woyenera.

      19 Pamene muŵerenga ndi ena Baibulo monga banja, luso lanu la kuŵerenga lingawongokere. Mwachionekere, kudziŵa kwanu Mulungu kudzawonjezereka, ndipo zimenezi ziyenera kukuchititsani kuyandikira kwambiri kwa iye. Asafu anaimba kuti: “Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu: ndimuyesa Ambuye Yehova pothaŵirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse.” (Salmo 73:28) Zimenezi zidzathandiza banja lanu kukhala ngati Mose, amene “anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo,” ndiko kuti, Yehova Mulungu.​—Ahebri 11:27.

      Kuŵerenga ndi Utumiki Wachikristu

      20, 21. Kodi ntchito yathu ya kulalikira njogwirizana motani ndi luso la kuŵerenga?

      20 Chikhumbo chathu cha kulambira “Wosaonekayo” chiyenera kutisonkhezera kulimbikira kukhala oŵerenga abwino. Luso la kuŵerenga bwino limatithandiza kuchitira umboni kuchokera m’Mawu a Mulungu. Limatithandizadi kupitirizabe mu ntchito yolalikira Ufumu imene Yesu analamulira otsatira ake kuchita pamene anati: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8) Kuchitira umboni ndiko ntchito yaikulu ya anthu a Yehova, ndipo luso la kuŵerenga limatithandiza kukwaniritsa zimenezi.

      21 Kuyesayesa kuli kofunika kuti munthu akhale woŵerenga wabwino ndi mphunzitsi waluso wa Mawu a Mulungu. (Aefeso 6:17) Chotero, ‘chitani changu kudzionetsera kwa Mulungu ovomerezeka, olunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Timoteo 2:15) Wonjezerani chidziŵitso chanu cha choonadi cha Malemba ndi luso lanu monga Mboni ya Yehova mwa kudzipereka pa kuŵerenga.

      Kodi Mayankho Anu Ngotani?

      ◻ Kodi chimwemwe chimadalira motani pa kuŵerenga Mawu a Mulungu?

      ◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kusinkhasinkha zimene mukuŵerenga m’Baibulo?

      ◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kugwirizanitsa mfundo ndiponso kuona zinthu m’maganizo pamene mukuŵerenga Malemba?

      ◻ Kodi ndi maphunziro ena otani amene angapezedwe m’kuŵerenga Baibulo?

      ◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kuŵerenga Baibulo momveka monga banja, ndipo ndi kugwirizana kotani kumene kulipo pakati pa kuŵerenga ndi utumiki wachikristu?

  • Ŵerengani Mawu a Mulungu ndi Kumtumikira M’choonadi
    Nsanja ya Olonda—1996 | May 15
    • Ŵerengani Mawu a Mulungu ndi Kumtumikira M’choonadi

      “Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’choonadi chanu.”​—SALMO 86:11.

      1. Kodi nchiyani makamaka chimene kope loyamba la magazini ano linanena ponena za choonadi?

      YEHOVA amatumiza kuunika ndi choonadi. (Salmo 43:3) Amatipatsanso luso la kuŵerenga Mawu ake, Baibulo, ndi kuphunzira choonadi. Kope loyamba la magazini ano​—July 1879​—linati: “Choonadi, monga momwe lilili duŵa wamba laling’ono m’chipululu cha moyo, nchozingidwa ndipo pafupifupi chotsamwitsidwa ndi zomera zina zomakula kwambiri za chinyengo. Kuti muchipeze muyenera kuyang’anitsitsa nthaŵi zonse. Kuti muone kukongola kwake muyenera kukankhira m’mbali zomera zinazo za chinyengo ndi ziyangoyango zaminga za liuma. Kuti chikhale chanu muyenera kuŵerama ndi kuchitola. Musakhutire ndi duŵa limodzi la choonadi. Duŵa limodzi likanakhala lokwanira sipakanakhalanso ena. Sonkhanitsani mosalekeza, funani ambiri.” Kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu kumatikhozetsa

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena